Nyimbo 102
Tiyeni Tiimbe Nyimbo ya Ufumu!
1. Iyi ndi nyimbo yachisangalalo
Yolemekeza M’lungu wamkulu.
Imatipatsadi chiyembekezo,
Imba nafe nyimbo ya Ufumu.
(KOLASI)
‘Lambirani M’lungu wathu,
Mwana waketu ndi mfumu!
Dzaphunzireni nyimbo ya Ufumu
Tamandani dzina la Mulungu.’
2. Ndi nyimboyi tilengeza Ufumu
Khristu Yesu ndi wolamulira.
Ndipo mtundu watsopano wabadwa
Nawo ukumusangalalira.
(KOLASI)
‘Lambirani M’lungu wathu,
Mwana waketu ndi mfumu!
Dzaphunzireni nyimbo ya Ufumu
Tamandani dzina la Mulungu.’
3. Nyimboyi omwe angaiphunzire
Ndi amene amadzichepetsa.
M’dziko lonse ambiri aphunzira.
Akuitananso anthu ena.
(KOLASI)
‘Lambirani M’lungu wathu,
Mwana waketu ndi mfumu!
Dzaphunzireni nyimbo ya Ufumu
Tamandani dzina la Mulungu.’
(Onaninso Sal. 95:6; 1 Pet. 2:9, 10; Chiv. 12:10.)