NYIMBO 74
Tiimbire Limodzi Nyimbo ya Ufumu
1. Iyi ndi nyimbo yachisangalalo
Yolemekeza M’lungu wamkulu.
Imatipatsadi chiyembekezo.
Imbani nafe nyimbo yathuyi.
(KOLASI)
Lambirani M’lungu wathu.
Mwana wake ndiye Mfumu.
Dzaphunzireni nyimbo ya Ufumu.
Tamandani dzina la Mulungu.
2. Nyimboyi ikulengeza Ufumu.
Yesu Khristu ndi wolamulira
Ndipo mtundu watsopano wabadwa,
Nawo ukumusangalalira.
(KOLASI)
Lambirani M’lungu wathu.
Mwana wake ndiye Mfumu.
Dzaphunzireni nyimbo ya Ufumu.
Tamandani dzina la Mulungu.
3. Amene angaphunzire nyimboyi
Ndi amene amadzichepetsa.
Ambiri m’dzikoli aiphunzira
Ndipo akuphunzitsanso ena.
(KOLASI)
Lambirani M’lungu wathu.
Mwana wake ndiye Mfumu.
Dzaphunzireni nyimbo ya Ufumu.
Tamandani dzina la Mulungu.
(Onaninso Sal. 95:6; 1 Pet. 2:9, 10; Chiv. 12:10.)