Mutu 8
Kodi “Mudzakhalabe ndi Moyo” Ngati Yeremiya?
1, 2. N’chifukwa chiyani m’pake kuti tiyenera kudera nkhawa za moyo wauzimu wa munthu aliyense payekha komanso wa banja lathu lonse?
YOSWA atalimbikitsa Aisiraeli kuti asankhe Mulungu amene akufuna kumutumikira, iye ananenanso kuti: “Ine ndi a m’nyumba yanga, tizitumikira Yehova.” (Yos. 24:15) Apa Yoswa anatsimikiza ndi mtima wonse kuti apitiriza kutumikira Mulungu mokhulupirika, ndipo sankakayikira kuti nawonso anthu a m’banja lake akhalabe okhulupirika. Patapita zaka, Yerusalemu atatsala pang’ono kuwonongedwa, Yeremiya anauza Mfumu Zedekiya kuti, “inuyo ndi banja lanu mudzakhalabe ndi moyo,” ngati mungadzipereke m’manja mwa Ababulo. (Yer. 38:17) Zedekiya sanamvere zimenezi, ndipo zotsatirapo zake zinakhudza iyeyo, akazi ake komanso ana ake. Mwachitsanzo, ana ake anaphedwa iye akuona, komanso iyeyo anavulazidwa m’maso n’kuchititsidwa khungu, ndipo kenako anatengedwa kupita ku ukapolo ku Babulo.—Yer. 38:18-23; 39:6, 7.
2 Pa mfundo ziwiri zomwe zili m’mawu akuda kwambiriwa, munthu mmodzi ndi yemwe ankakhudzidwa kwambiri m’nkhani iliyonse. Koma banja lake linatchulidwanso ndipo zimenezi n’zomveka. Munthu aliyense wamkulu adzayankha yekha mlandu kwa Mulungu. Komabe, Aisiraeli ambiri ankachokera m’mabanja. Nawonso Akhristu amaona kuti banja ndi chinthu chofunika kwambiri. Mfundo imeneyi timaiona tikaganizira zimene timawerenga m’Baibulo ndiponso zimene timaphunzira kumisonkhano yachikhristu pa nkhani yokhudza kulowa m’banja, kulera ana komanso kulemekeza anthu a m’banja lathu.—1 Akor. 7:36-39; 1 Tim. 5:8.
LAMULO LODABWITSA
3, 4. Kodi mmene zinthu zinalili pa moyo wa Yeremiya zinali zosiyana bwanji ndi anthu ena onse, ndipo zimenezo zinamuthandiza bwanji?
3 Yeremiya ‘anakhalabe ndi moyo’ m’nthawi yake. Iye anapulumuka pamene Yerusalemu ankawonongedwa, ngakhale kuti moyo wake unali wosiyana kwambiri ndi anthu ambiri. (Yer. 21:9; 40:1-4) Mulungu anamuuza kuti asakwatire kapena kukhala ndi ana, ndiponso anamuuza kuti asamachite nawo zinthu zina zimene Ayuda ambiri ankachita pa nthawiyo.—Werengani Yeremiya 16:1-4.
4 Malinga ndi chikhalidwe cha Ayuda m’masiku a Yeremiya, anthu ankayembekezera kuti munthu aliyense akakula ayenera kulowa m’banja ndi kubereka ana. Amuna ambiri achiyuda ankachitadi zimenezi, ndipo akatero, ankatetezera malo a makolo awo kuti asachoke m’manja mwa banja lawo komanso fuko lawo.a (Deut. 7:14) Nanga n’chifukwa chiyani Yeremiya sanakwatire ndi kubereka ana? Poganizira zimene zinayenera kuchitika m’tsogolo, Mulungu anamuuza kuti asamachite nawo zinthu zimene anthu ambiri ankachita, monga za pa nthawi yachisoni kapena yachisangalalo. Iye anauzidwa kuti asamatonthoze anthu olira maliro ndiponso asamadye nawo chakudya pambuyo pa malirowo. Anauzidwanso kuti asamapite nawo kumaphwando a Ayuda, monga ku ukwati. Yeremiya anauzidwa zimenezi chifukwa panali patangotsala nthawi yochepa kuti maphwando ndi zisangalalo zoterozo zithetsedwe. (Yer. 7:33; 16:5-9) Zimene Yeremiya anauzidwa kuchitazo zikanathandiza ena kuti akhulupirire uthenga wake. Komanso zinasonyezeratu kuti kukubwera chiweruzo choopsa kwambiri, ndipo patapita nthawi, chinafikadi. Pa nthawiyo, anthu ena anasowa pogwira chifukwa cha njala, moti anafika pomadya nyama ya anthu anzawo. Komanso anthu ankaona mitembo ya abale awo ikuwola pamtunda, osaikidwa m’manda. Kodi mukuganiza kuti anthuwo ankamva bwanji mumtima chifukwa cha zimenezi? (Werengani Yeremiya 14:16; Maliro 2:20.) Yeremiya anapewa mavuto omvetsa chisoniwa chifukwa anali wosakwatira. Pa miyezi yonse 18 imene Ababulo anazungulira mzinda wa Yerusalemu komanso pamene iwo anayamba kupha mwankhanza kwambiri anthu a mumzindawo, Yeremiya sanakhudzidwe kwambiri chifukwa analibe mkazi kapena ana.
5. Kodi Akhristu akukhudzidwa bwanji ndi malangizo amene ali pa Yeremiya 16:5-9?
5 Koma kodi tinganene kuti ifenso masiku ano tikuyenera kutsatira zimene Yeremiya anauzidwa, pa Yeremiya 16:5-9? Ayi. Zili choncho chifukwa Akhristu akulimbikitsidwa “kutonthoza amene ali m’masautso amtundu uliwonse” ndiponso ‘kusangalala ndi anthu amene akusangalala.’ (2 Akor. 1:4; Aroma 12:15) Mwachitsanzo, nthawi ina Yesu anapita ku ukwati ndipo anachita zinthu zimene zinathandizira kuti anthu asangalale pa ukwatiwo. Komabe, posachedwapa dziko loipali likumana ndi tsoka loopsa. Ndipo Akhristu masiku ano amatha kukumana ndi mavuto osiyanasiyana. Yesu anatilimbikitsa kuti tiyesetse kupirira ndiponso kukhalabe okhulupirika, ngati mmene anachitira abale athu omwe anathawa mu Yudeya m’nthawi ya atumwi. Choncho aliyense ayenera kuganizira mozama nkhani yokhudza kukhalabe wosakwatira, kukwatira, kapena kukhala ndi ana.—Werengani Mateyu 24:17, 18.
6. Kodi ndani amene angapindule ndi malangizo omwe Mulungu anapatsa Yeremiya?
6 Kodi tingaphunzirepo chiyani pa lamulo limene Mulungu anauza Yeremiya loti asakwatire kapena kukhala ndi ana? Masiku ano, Akhristu ena okhulupirika sali pa banja kapena alibe ana. Kodi iwo angaphunzirepo chiyani pa chitsanzo cha Yeremiya? Ndipo n’chifukwa chiyani ngakhale Akhristu amene ali pa banja ndipo ali ndi ana, ayenerabe kuganizira mofatsa za chitsanzo cha Yeremiya, yemwe sanakwatire kapena kukhala ndi ana?
7. Kodi n’chifukwa chiyani masiku ano tiyenera kuganizira mofatsa lamulo limene Mulungu anapatsa Yeremiya lakuti asakhale ndi ana?
7 Choyamba, ganizirani mfundo yakuti Yeremiya anauzidwa kuti asakhale ndi ana. Yesu sanalamule otsatira ake kuti asamakhale ndi ana. Komabe, n’zochititsa chidwi kuti iye ananena kuti “tsoka” kwa akazi apakati kapena oyamwitsa ana pa nthawi ya chisautso. Chisautso chimenechi chinayamba mumzinda wa Yerusalemu m’chaka cha 66 C.E. mpaka mu 70 C.E. Nthawi imeneyo inali yovuta kwambiri, makamaka kwa akazi apakati komanso oyamwitsa ana. (Mat. 24:19) Ifenso tikumana ndi chisautso chachikulu posachedwapa. Choncho Akhristu omwe ali pa banja ayenera kuganizira mfundo imeneyi mozama ngati akufuna kukhala ndi ana. Kodi simukuvomereza kuti zinthu zikuipiraipira m’masiku ovuta ano? Ndipo makolo afika povomereza kuti akuvutika kwambiri pothandiza ana awo kuti ‘adzakhalebe ndi moyo’ pamene dziko loipali lizidzawonongedwa. Ngakhale kuti mwamuna ndi mkazi wake amasankha okha ngati akufuna kukhala ndi ana kapena ayi, angachite bwino kuganizira mofatsa chitsanzo cha Yeremiya. Tsopano tiyeni tikambirane lamulo limene Mulungu anapatsa Yeremiya lakuti asakwatire n’komwe.
Kodi Yeremiya anapatsidwa lamulo lodabwitsa lotani, ndipo lamulo limeneli liyenera kutilimbikitsa kuganizira chiyani?
KODI TIKUPHUNZIRA CHIYANI KWA YEREMIYA, AMENE ANAKHALABE WOSAKWATIRA?
8. N’chifukwa chiyani tinganene kuti munthu sachita kufunikira kukwatira kapena kukwatiwa kuti asangalatse Mulungu?
8 Popeza Mulungu anauza Yeremiya kuti asakwatire, kodi zimenezi zikutanthauza kuti atumiki ake onse ayenera kukhala osakwatira? Ayi, si choncho. Palibe cholakwika chilichonse ndi kukwatira kapena kukwatiwa. Ndipotu Yehova ndi amene anayambitsa ukwati n’cholinga choti anthu achulukane padzikoli, komanso kuti anthu okwatiranawo azisangalala. (Miy. 5:18) Komabe, sikuti anthu onse m’nthawi ya mneneri Yeremiya anali okwatira kapena okwatiwa. Zikuoneka kuti pa gulu la atumiki a Mulungu panalinso anthu ena amene sakanatha kukwatira.b Komanso sitikukayikira kuti panalinso akazi ndi amuna amasiye. Choncho pa gulu la olambira oona a Mulungu, sikuti ndi Yeremiya yekha amene sanali pa banja. Ndipo panali zifukwa zimene zinam’chititsa kuti asakwatire, ngati mmene zililinso ndi Akhristu ena masiku ano.
9. Kodi ndi malangizo ouziridwa ati okhudza kulowa m’banja amene tiyenera kuwaganizira mofatsa?
9 Akhristu ambiri amakwatira kapena kukwatiwa, koma osati onse. Mukudziwa kuti Yesu sanakwatire, ndipo ananena kuti ophunzira ake ena ali ndi mphatso yoti “angathe” kukhala osakwatira kapena osakwatiwa. Iye analimbikitsa anthu amene akanatha kukhala osakwatira kuti asakwatire. (Werengani Mateyu 19:11, 12.) Choncho, ndi bwino kuyamikira, osati kunyoza, anthu amene asankha kukhalabe osakwatira kapena osakwatiwa n’cholinga choti azichita zambiri potumikira Mulungu. Akhristu ena amakhala osakwatira kapena osakwatiwa, mwina kwa zaka zingapo, chifukwa cha mavuto ena. Mwachitsanzo, iwo angakhale asanapeze Mkhristu mnzawo woti angamange naye banja, ndipo akuyesetsa ndi mtima wonse kutsatira mfundo ya Mulungu yakuti ayenera kukwatira kapena kukwatiwa “mwa Ambuye” basi. (1 Akor. 7:39) Komanso, ena mwa atumiki a Mulungu ndi akazi kapena amuna amasiye, motero sali pa banja.c Anthu onsewa sayenera kuiwala kuti kuyambira kale kwambiri, Mulungu (ndiponso Yesu) wakhala akudera nkhawa komanso kusamalira anthu ngati amenewa, omwe sali pa banja.—Yer. 22:3; werengani 1 Akorinto 7:8, 9.
10, 11. (a) N’chiyani chinathandiza Yeremiya kuti akhalebe wosakwatira ndiponso kuti apitirizebe kukhala wosangalala? (b) Kodi zitsanzo za masiku ano zikutsimikizira bwanji kuti anthu amene sali pa banja angakhalebe moyo wosangalala?
10 Choncho, Yeremiya ankadalira Mulungu kuti azimuthandiza pa moyo wake monga munthu wosakwatira. Kodi iye anathandizidwa bwanji? Kumbukirani kuti Yeremiya ankakonda kwambiri mawu a Yehova. Zimenezi ziyenera kuti zinalimbikitsa kwambiri Yeremiya kwa zaka zambiri, ndipo zinamuthandiza kuti apitirizebe kuchita utumiki wake umene anapatsidwa ndi Mulungu. Komanso, iye ankayesetsa kupewa kucheza ndi anthu amene akanayamba kumunyoza chifukwa choti anali wosakwatira. Yeremiya ankalolera ‘kukhala pansi yekhayekha’ kusiyana ndi kukhala ndi anthu ngati amenewo.—Werengani Yeremiya 15:17.
11 Akhristu ambiri osakwatira kapena osakwatiwa, kaya ndi achinyamata kapena achikulire, akutsatira chitsanzo chabwino cha Yeremiya. Zitsanzo za abale ndi alongo omwe sali pa banja zikusonyeza kuti kutumikira Mulungu mwakhama kwambiri, kapena kuti kutanganidwa ndi zinthu zauzimu, n’kothandiza kwambiri. Mwachitsanzo, mlongo wina amene akutumikira mumpingo wachinenero cha Chitchaina ananena kuti: “Kuchita upainiya kukundithandiza kwambiri pa moyo wanga. Popeza ndine wosakwatiwa, ndimakhala ndi mpata wotha kuchita zinthu zambiri, ndipo zimenezi zimandithandiza kuti ndisamasungulumwe. Tsiku lililonse kukada, ndimakhala wosangalala kwambiri chifukwa ndimaona kuti utumiki wanga ukuthandizadi anthu.” Mlongo wina wa zaka 38 yemwenso ndi mpainiya ananena kuti: “N’zotheka kuti munthu akhaledi wosangalala ndipo ndikuona kuti chinsinsi chake n’chakuti aziona zinthu zabwino pa chilichonse chimene akuchita kapena chimene chikumuchitikira.” Mkhristu winanso yemwe sali pa banja m’dera lina lakum’mwera ku Ulaya, ananena moona mtima kuti: “Sikuti ndili mwana ndinkafuna kuti zinthu zikhale mmene zililimu pa moyo wanga. Komabe, ndikusangalala ndipo ndipitiriza kukhalabe wosangalala.”
12, 13. (a) Kodi tiyenera kuona bwanji nkhani yokhudza kukhala pa banja komanso kusakhala pa banja? (b) Kodi moyo wa Paulo ndiponso malangizo amene anapereka, akutsimikizira chiyani chokhudza kusakhala pa banja?
12 Mwina n’kutheka kuti Yeremiya ankaona kuti zimene zinkachitika pa moyo wake si zimene ankayembekezera ali mwana. Komabe, mwina anaonanso kuti anthu ambiri omwe anali pa banja ndipo anali ndi ana, sankayembekezeranso kuti moyo wawo udzakhala wotero. Mlongo wina wa ku Spain, amenenso ndi mpainiya ananena kuti: “Ndikudziwa anthu ena amene ali pa banja ndipo akusangalala komanso ndikudziwa ena amene sakusangalala. Zimenezi zimandichititsa kukhulupirira kuti kukwatiwa kapena kusakwatiwa si kumene kumachititsa munthu kukhaladi wosangalala.” Ndipo tikaona za moyo wa Yeremiya, yemwe ndi chitsanzo chimodzi chokha cha anthu ambirimbiri omwe sanali pa banja, sitikayikira kuti n’zotheka kukhala ndi moyo wosangalala kwambiri ngakhale munthu atakhala kuti sali pa banja. Komanso chitsanzo cha mtumwi Paulo ndiponso zimene ananena, zikutsimikiziranso mfundo imeneyi. Iye analemba kuti: “Ndikunena kwa osakwatira ndi kwa akazi amasiye kuti, ndi bwino akhalebe mmene ineyo ndililimu.” (1 Akor. 7:8) N’kutheka kuti Paulo anakhalapo pa banja koma mkazi wake anamwalira. Kaya zinalidi choncho kapena ayi, iye anali wosakwatira pamene ankachita zambiri mu utumiki wake waumishonale. (1 Akor. 9:5) Choncho, zikuonekeratu kuti zinthu zinamuyendera bwino kwambiri pa utumiki wake chifukwa anali wosakwatira. Iye ankatha “kutumikira Ambuye nthawi zonse popanda chododometsa,” ndipo anachita zambiri pa utumiki wake.—1 Akor. 7:35.
13 Mouziridwa, Paulo anawonjezera mfundo ina polemba kuti: “Olowa m’banjawo adzakhala ndi nsautso m’thupi mwawo.” Mulungu anauziranso Paulo kuti alembe mfundo yofunika kwambiri yomwe ndi yoona, yakuti: “Ngati wina ndi wokhazikika mumtima mwake . . . ndipo wasankha . . . kukhalabe wosakwatira, wachita bwino. Nayenso amene walekana ndi moyo wokhala yekha n’kulowa m’banja wachita bwino, koma amene sanalowe m’banja wachita bwino koposa.” (1 Akor. 7:28, 37, 38) Yeremiya sanawerenge mawu amenewa, koma mmene ankakhalira pa moyo wake kwa zaka zambiri zinasonyeza kuti kukhala wosakwatira kapena wosakwatiwa sikulepheretsa munthu kukhala wosangalala potumikira Mulungu. Ndipotu munthu yemwe sali pa banja angachite zambiri polambira Mulungu woona, ndipo angakhale wosangalala kwambiri. Mwachitsanzo, Mfumu Zedekiya, yemwe anali wokwatira, sanamvere malangizo a Yeremiya amene akanamuthandiza kuti ‘akhalebe ndi moyo,’ koma mneneri wosakwatirayu anachita zinthu zimene zinamuthandiza kuti ‘akhalebe ndi moyo.’
Kodi mungaphunzire chiyani kwa Yeremiya amene anakhalabe wosakwatira kwa zaka zambirimbiri?
MUZILIMBIKITSA ENA KUTI INUNSO MUZILIMBIKITSIDWA
14. Kodi ubwenzi umene unali pakati pa Paulo ndi banja la Akula ukusonyeza chiyani?
14 Monga mmene taonera, amuna ndi akazi ambiri m’nthawi ya Yeremiya anali okwatira ndipo anali ndi mabanja. Zinalinso chimodzimodzi m’nthawi ya Paulo. N’zodziwikiratu kuti Akhristu ambiri omwe anali ndi mabanja sakanatha kupita m’mayiko ena pochita utumiki wawo ngati mmene ankachitira Paulo. Koma iwo anali ndi ntchito yambiri pa utumiki wawo m’madera amene iwowo ankakhala, monga kuthandiza abale ndi alongo omwe sanali pa banja. Mwachitsanzo, kumbukirani kuti Paulo atafika ku Korinto, Akula ndi Purisikila anamulandira n’kumakhala naye m’nyumba yawo ndiponso ankagwira naye ntchito popeza onsewa anali osoka mahema. Koma si zokhazi. Ubwenzi umene unalipo pakati pa Paulo ndi banja la Akula uyenera kuti unali wolimbikitsa kwambiri. Iwo ayenera kuti ankadyera limodzi chakudya chokoma komanso ankacheza bwino kwambiri n’kumalimbikitsana. Koma kodi nayenso Yeremiya ankacheza ndi anthu ngati mmene ankachitira Paulo? Iye ankagwiritsira ntchito nthawi yake yambiri monga munthu wosakwatira potumikira Mulungu. Komabe, tisaganize kuti iye anali munthu wosafuna kucheza ndi anzake. Yeremiya ayenera kuti ankasangalala kucheza ndi mabanja a atumiki a Mulungu odzipereka kwambiri, monga banja la Baruki, Ebedi-meleki ndi enanso.—Aroma 16:3; werengani Machitidwe 18:1-3.
15. Kodi mabanja achikhristu angathandize bwanji Akhristu amene sali pa banja?
15 Masiku anonso, Akhristu omwe sali pa banja amasangalala kucheza ndi mabanja ena ngati mmene Paulo ankachitira ndi banja la Akula. Ngati inuyo muli pa banja, kodi mumayesetsa kucheza ndi anthu amene sali pa banja? Mlongo wina anadandaula kuti: “Ndinasiyana ndi dziko ndipo sindikufuna kubwereranso. Koma ndikufunikirabe kukondedwa. Ndimapemphera kuti Yehova apitirize kupereka chakudya chauzimu chothandiza Akhristu omwe sitili pa banjafe ndiponso kuti apitirize kutilimbikitsa. Tikufunikira kulimbikitsidwa, ndipo sikuti ndi tonse amene timafunitsitsa titalowa m’banja tsiku lina. Koma pamene tikuyesetsa kuchita zimenezi, zikuoneka kuti palibe amene akutilimbikitsa. N’zoona kuti tingalankhule ndi Yehova nthawi ina iliyonse, komabe tikafuna kucheza ndi anthu anzathu, kodi banja lathu lauzimu limakhala lokonzeka kuti tilankhule nalo?” Abale ndi alongo ambirimbiri omwe sali pa banja angayankhe moona mtima kuti inde. Iwo amakhala ndi mwayi wocheza ndi Akhristu anzawo mumpingo wawo. Koma sikuti iwo amangocheza ndi abale ndi alongo ofanana nawo msinkhu basi. Popeza iwo amakonda anthu, amasangalala kucheza ndi anthu a misinkhu yosiyanasiyana, monga achikulire, kapena ana a m’mabanja achikhristu amene ali m’dera lawo.
16. Kodi mungachite zinthu ziti zing’onozing’ono polimbikitsa Akhristu amene sali pa banja mumpingo wanu?
16 Mutaganizira mofatsa, mungaone kuti mungathe kulimbikitsa ena amene sali pa banja. Mungachite zimenezi powaitana kuti mudzakhale nawo limodzi pamene banja lanu likuchita zinthu zina monga Kulambira kwa Pabanja. Ngati mutaitana m’bale kapena mlongo amene sali pa banja kuti mudzadye naye limodzi chakudya, angalimbikitsidwe kwambiri, osati ndi chakudya chokhacho, koma ndi macheza amene mungakhale nawo. Komanso kodi mungagwirizane ndi m’bale kapena mlongo amene sali pa banja kuti mudzalowe naye limodzi mu utumiki tsiku lina? Mwinanso mukhoza kuitana Mkhristu yemwe sali pa banja kuti mugwire naye limodzi ntchito yoyeretsa kapena kukonza zina n’zina pa Nyumba ya Ufumu. Nthawi zina mukhozanso kumutenga mukamapita kogula zinthu. Mabanja ena akakhala ndi ulendo wopita kumsonkhano wachigawo kapena kutchuthi, amatenga m’bale kapena mlongo wamasiye, kapenanso mpainiya yemwe sali pa banja. Mabanja achikhristu akamacheza mwanjira imeneyi ndi Akhristu omwe sali pa banja, amalimbikitsana kwambiri.
17-19. (a) Kodi n’chifukwa chiyani ana ayenera kuchita zinthu mwachikondi pamene akukonza zosamalira makolo okalamba kapena amene sangathe kudzisamalira okha? (b) Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Yesu anachita poonetsetsa kuti mayi ake akusamalidwa?
17 Nkhani ina yofunika kuiganizira yokhudza abale ndi alongo omwe sali pa banja, ndi yosamalira makolo okalamba. M’masiku a Yesu, Ayuda ena otchuka ankazemba udindo wosamalira makolo awo. Iwo ankanena kuti kutsatira malamulo achipembedzo amene ankadziikira okha kunali kofunika kwambiri kuposa udindo wopatsidwa ndi Mulungu, wosamalira makolo awo. (Maliko 7:9-13) Mabanja achikhristu ayenera kupewa khalidwe limeneli.—1 Tim. 5:3-8.
18 Nanga bwanji ngati makolo okalamba ali ndi ana angapo achikhristu? Kodi ngati mmodzi mwa anawo sali pa banja, ndiye kuti basi udindo wonse wosamalira makolowo uyenera kukhala m’manja mwake? Taganizirani zimene mlongo wina wa ku Japan analemba. Iye anati: “Ndikufuna n’takwatiwa, koma chifukwa choti ndili ndi udindo wosamalira makolo anga, sindingathe kukwatiwa. Sindikukayikira kuti Yehova amamvetsa mavuto amene munthu amakumana nawo posamalira makolo, ndiponso ululu umene anthu omwe sitili pa banjafe timamva mumtima mwathu.” Kodi mwina mlongoyu ali ndi azichimwene ndi azichemwali ake omwe ali pa banja amene anangoganiza kuti iyeyo ndi amene azisamalira makolowo, osamufunsa maganizo ake? Zimenezi n’zofanana ndi mmene zinalili ndi Yeremiya, chifukwa nayenso anali ndi abale ake amene ankamuchitira zinthu mosamuganizira.—Werengani Yeremiya 12:6.
19 Yehova amamvetsa bwino mavuto amene anthu amene sali pa banja amakumana nawo ndiponso amamvera chisoni anthu amene akukumana ndi mavuto osiyanasiyana. (Sal. 103:11-14) Komabe, makolo okalamba kapena amene sangathe kudzisamalira okha, amakhalabe makolo a ana awo onse, osati makolo a ana okha omwe sali pa banja. N’zoona kuti ena mwa ana awo angakhale ali pa banja ndipo mwina angakhalenso ndi ana awo. Komabe, zimenezo sizimathetsa chikondi chachibadwa chimene ayenera kukhala nacho kwa makolo awo. Komanso sizithetsa udindo wawo wachikhristu wowathandiza pamene akufunikira thandizo. Tisaiwale kuti ngakhale Yesu atatsala pang’ono kufa pamtengo wozunzikirapo, sanaiwale udindo wake wosamalira mayi ake ndipo anachitapo kanthu. (Yoh. 19:25-27) Baibulo silitiuza malamulo atsatanetsatane pa nkhani yogawana udindo wosamalira makolo okalamba kapena amene sangathe kudzisamalira okha. Komanso silinena kuti ngati makolowo ali ndi ana omwe sali pa banja, ndiye kuti basi, iwo ndi amene ali ndi udindo waukulu wowasamalira. Pa nkhani yosamalira makoloyi, yomwe ndi yovuta komanso yofunika kwambiri, anthu onse apachibale amene nkhaniyi ikuwakhudza ayenera kukambirana momvetsetsana ndiponso moganizirana. Pochita zimenezi, ayenera kukumbukira chitsanzo chimene Yesu anapereka pa nkhani yosamalira mayi ake.
20. Kodi mumaiona bwanji nkhani yocheza ndi anthu amene sali pa banja mumpingo wanu?
20 Mouziridwa, Yeremiya analosera kuti: “Munthu sadzaphunzitsanso mnzake kapena m’bale wake kuti, ‘Mum’dziwe Yehova!’ pakuti aliyense wa iwo adzandidziwa.” (Yer. 31:34) Mofanana ndi anthu amenewo, ifeyo tayamba kale kukhala ndi anzathu oterowo chifukwa timacheza ndi anthu osiyanasiyana mumpingo wachikhristu, kuphatikizapo abale ndi alongo omwe sali pa banja. Mosakayikira, tonsefe tikufunitsitsa kulimbikitsana ndi anthu amene sali pa banja, ndipo tikufunitsitsanso kuwaona ‘akukhalabe ndi moyo.’
Kodi mungachite zinthu zina ziti kuti muzilimbikitsa komanso kulimbikitsidwa ndi abale ndiponso alongo ena amene sali pa banja?
a M’Malemba Achiheberi oyambirira mulibe mawu otanthauza “munthu wosakwatira.”
b Yesaya ananena ulosi wopita kwa anthu omwe sakanatha kukwatira m’masiku ake, amenenso sankaloledwa kuchita nawo zinthu zina polambira Mulungu m’nthawi ya Aisiraeli. Iye analosera kuti ngati anthuwo angapitirize kukhalabe omvera, adzapatsidwa zinthu “zabwino kuposa ana aamuna ndi aakazi,” zomwe ndi “dzina limene silidzatha mpaka kalekale” m’nyumba ya Mulungu.—Yes. 56:4, 5.
c Ena sali pa banja chifukwa choti mwamuna kapena mkazi wawo, mwina yemwe ndi wosakhulupirira, anapatukana nawo kapena anawasudzula n’kuwasiya.