Wosakwatira Koma Wokwanira Kaamba ka Utumiki wa Mulungu
“Iye amene apereka unamwali wake mu ukwati achita bwino, koma iye amene saupereka adzachita bwino koposa.”—1 AKORINTO 7:38, NW.
1. Kodi ndimotani mmene ukwati watsimikizirira kukhala dalitso?
YEHOVA sanayembekezere nkomwe munthu woyamba kukhala wosakwatira. M’malo mwake, Mulungu analenga mnzake wa mu ukwati kaamba ka Adamu, m’yambitsi wa mtundu wa anthu. (Genesis 2:20-24; Machitidwe 17:26) Ndipo ndi dalitso lotani nanga mmene ukwati unatsimikizira kukhala! Iwo unapereka wokhala naye, unapangitsa kuthekera kwathandizo lofunikira, unali makonzedwe olemekezedwa kaamba ka kutulutsa mbadwa, ndipo unathandizira mokulira ku chimwemwe cha munthu. Nkulekelanji, popeza ngakhale osauka ndi anthu apansi angasangalale ndi zimene unyinji uliwonse wa ndalama sungagule—chikondi cha mu ukwati!—Nyimbo ya Solomo 8:6, 7.
2, 3. (a) Ndi kawonedwe kotani kamene chofalitsidwa chimodzi cha chipembedzo chinatenga ponena za umbeta ndi ukwati? (b) Mwa Malemba, ndimotani mmene ukwati uyenera kuwonedwera?
2 Ena, ngakhale kuli tero, amawona ukwati m’njira yosiyana. Chikutero chofalitsidwa cha chipembedzo chimodzi: “Umbeta uli lamulo la ulaliki mu Matchalitchi a Kumadzulo loikidwa pa atsogoleri a chipembedzo amene amakaniza awo amene ali m’mkhalidwe wokwatira kusaikidwa m’mathayo ndi awo amene ali m’mathayo opatulika kusakwatira. Ilo limaphatikizapo thayo la kusunga kuyera kwa ungwiro pansi pa chilumbiro. Zifukwa kaamba ka izi ziri zakuti: awo oikidwa angatumikire Mulungu ndi chifuno chimodzi chokulira (1 Akor. 7:32), ndipo chotero mwakukhala ndi moyo wodzimana mwa zilakolako iwo angasunge mkhalidwe wa unamwali, womwe uli wopatulika koposa ndi wapamwamba kuposa uja wa mu ukwati. Mu CC [Chipangano Chatsopano] umbeta kapena mkhalidwe wa unamwali umakwezedwa kuchiitano chapamwamba kuposa chija cha ukwati.”—The Catholic Encyclopedia, yokonzekeretsedwa ndi Robert C. Broderick.
3 Kodi chiridi chothekera kuti umbeta wokakamizidwa uli ‘wopatulika koposa ndi wapamwamba kuposa ukwati’? Osati molingana ndi “Chipangano Chatsopano,” chimene chimanena mu Catholic Jerusalem Bible: “Mzimu wanena mosabisira kuti mkati mwa nthaŵi zomaliza padzakhala ena omwe adzachoka ku chikhulupiriro ndi kusankha kumvetsera mizimu yonyenga ndi ziphunzitso zomwe zimachokera kwa ziwanda; ndipo choyambitsa cha izi chidzakhala bodza lonenedwa ndi onyenga amene zikumbumtima zawo zapsyerezedwa ndi chitsulo chotentha: iwo adzanena kuti ukwati uli woletsedwa, ndipo adzakhazikitsa malamulo ponena za kusala zakudya zimene Mulungu anazilenga kuti zilandiridwe ndi chiyamiko ndi onse okhulupirira ndi awo odziŵa chowonadi.” (1 Timoteo 4:1-3) M’chenicheni, ukwati uli mphatso yochokera kwa Mulungu, ndipo uli wabwino.—Rute 1:9.
4. M’chiyang’aniro cha 1 Akorinto 7:38, ndi mafunso otani amene amabuka?
4 Ngakhale kuti ukwati uli mphatso yochokera kwa Mulungu, mtumwi Paulo analemba kuti: “Iye wopereka unamwali wake mu ukwati achita bwino, koma iye amene saupereka mu ukwati adzachita bwino koposa.” (1 Akorinto 7:38, NW) Nchifukwa ninji Paulo anasonyeza kuti chingakhale bwino koposa kukhala wosakwatira? Kodi munthu wosakwatira ayenera kudzimva kukhala wosakwanira? Ndipo kodi umbeta ungakhale wopatsa mphoto?
Maziko a Moyo Wachikristu
5. Nchiyani chimene chiyenera kukhala maziko a moyo Wachikristu?
5 Kutumikira Yehova kuyenera kukhala maziko enieni a moyo wathu Wachikristu, kaya ndife osakwatira kapena okwatira. Utumiki wopatulika woperekedwa kwa Mulungu mwachimwemwe umapereka chitsimikiziro cha kugwirizana kwathu ndi iye monga Wolamulira wa Chilengedwe. Kumvera kwa mtima wonse ndi kutengamo mbali kwachangu mu utumiki Wachikristu ziri njira za kusonyezera kugwirizana koteroko. (1 Yohane 5:2, 3; 1 Akorinto 9:16) Ponse paŵiri utumiki ndi machitidwe ena omvera m’chigwirizano ndi chifuno chaumulungu angakwaniritsidwe ngati munthu ali wosakwatira.
6. Kaya ndife okwatira kapena osakwatira, utumiki wachangu umatitheketsa ife kuchita chiyani?
6 Olalikira tsopano akutenga ntchito yolalikira Ufumu ku chilemekezo cha Yehova. Ndipo kaya ndife okwatira kapena osakwatira, utumiki wachangu umapereka mwaŵi wa kulunjikitsa chifupifupi zina za magwero athu aumwini ndi zoyesayesa zathu pa utumiki wa Yehova. Koma tiyenera kukulitsa ndi kulamulira mikhalidwe yathu kotero kuti utumiki sukuikidwa pamalo amene mochepera sali maziko a moyo wathu. Tiyenera ‘kufuna Ufumu choyamba.’ (Mateyu 6:33) Muli chimwemwe m’kumamatira pa zikondwerero zaumulungu m’malo mwa kungomamatira pa zikondwerero zaumwini.
Wokwanira kaamba ka Utumiki
7. Ndi chitsanzo chotani chimene chiripo chosonyeza kuti Mkristu wosakwatira angakhale wokwanira kaamba ka utumiki?
7 Akristu angakhale okwanira kaamba ka utumiki kaya ndi osakwatira kapena okwatira. Chotero mkhalidwe wosakwatira uli maziko osati kwenikweni ofunikira masinthidwe. (Yerekezani ndi 1 Akorinto 7:24, 27.) Mawu a Mulungu samatenga kawonedwe ka mafuko ena kakuti munthu safika ku mkhalidwe wake wa chikwanekwane kokha ngati wakwatira. Yesu Kristu anafa wosakwatira, ndipo mkwatibwi wauzimu kumwamba ali mkazi yekha amene Yehova wamuvomereza Yesu kukhala naye. (Chivumbulutso 21:2, 9) Komabe, Mwana wa Mulungu, ngakhale kuti anali wosakwatira monga munthu, anali chitsanzo chabwino koposa cha munthu wokwanira kaamba ka utumiki.
8. Monga mmene Paulo anasonyezera, kukhala wosakwatira kumatheketsa kaamba ka chiyani?
8 M’chenicheni, kukhala osakwatira kumapereka ufulu wokulira waumwini ndi nthaŵi kaamba ka utumiki. Akuyamikira umbeta, Paulo ananena kuti: “Koma ndifuna kuti mukhale osalabadira. Iye amene wosakwatira alabadira zinthu za Ambuye, kuti akondweretse Ambuye. . . . Ndi mkazi wokwatiwa ndi namwali asiyananso. Iye wosakwatiwa alabadira za Ambuye.” (1 Akorinto 7:32-34) Ichi chimagwira ntchito kwa Akristu osakwatira ndi kwa awo poyamba anakwatiwa koma mikhalidwe yawo yasintha, kuwabwezera iwo ku mkhalidwe wosakwatira.—Mateyu 19:9; Aroma 7:2, 3.
9. Kodi ndimotani mmene chitsanzo cha Yesu chimasonyezera kuti kukhala wosakwatira sikumapangitsa munthu kukhala wosakwanira kaamba ka utumiki Wachikristu?
9 Kufikira uchikulire wa kuthupi, maganizo, ndi uzimu kumabweretsa kukwanira kaamba ka utumiki wa Mulungu. Yesu Kristu sanafunikire mnzake wa mu ukwati kuti akhale wokwanira kaamba ka ntchito ya Mtumiki Wamkulu wa Mulungu ndi mmodzi amene kupyolera mwa iye dipo lidzaperekedwa. (Mateyu 20:28) Kukhala wosakwatira, Yesu anali womasuka kulunjikitsa mphamvu zake zonse pa utumiki wake. Mkhalidwe wake wosakwatira unasiyana kotheratu ndi chikhulupiriro chaunyinji cha Chiyuda, pansi pa chimene ukwati ndi ana zinali kugogomezeredwa. Mosasamala kanthu za chimenecho, Yesu anali wokhoza kumaliza ntchito yake yopatsidwa ndi Mulungu. (Luka 3:23; Yohane 17:3, 4) Chotero, kukhala wosakwatira sikumapangitsa munthu kukhala wosakwanira kaamba ka utumiki Wachikristu.
Anthu Okwatirana “Ogawanika”
10. Chifukwa cha chomangira cha “thupi limodzi”, nchiyani chimene Paulo ananena ponena za awo omwe ali okwatira kuyerekeza ndi awo amene ali osakwatira?
10 Mosiyana ndi munthu wosakwatira, Akristu okwatira ayenera kulondola utumiki akumazindikira chomangira chawo cha “thupi limodzi”. (Mateyu 19:5, 6) Chifukwa cha chomangira chimenecho ndi mathayo ake osiyanasiyana, Paulo ananena kuti anthu okwatira ali “ogawanika.” Iye analemba kuti: “Koma ndifuna kuti mukhale osalabadira. Iye amene ali wosakwatira alabadira zinthu za Ambuye, kuti akondweretse Ambuye. Koma iye wokwatira alabadira zinthu za dziko lapansi, kuti akondweretse mkazi wake. Ndi mkazi wokwatiwa ndi namwali asiyananso. Iye wosakwatiwa alabadira za Ambuye, kuti akhale woyera m’thupi ndi mumzimu; koma wokwatiwayo, alabadira za dziko lapansi, kuti akondweretse mwamunayo. Koma ichi ndinena mwa kupindula kwanu kwa inu nokha; sikuti ndikakutchereni msampha, koma kukuthandizani kuchita chimene chiyenera, ndi kutsata chitsatire Ambuye, opanda chocheukitsa.”—1 Akorinto 7:32-35.
11. Nchiyani chimene Paulo anali kusonyeza pa 1 Akorinto 7:32-35?
11 Mwachimvekere, kaamba ka moyo wosacheukitsa, Paulo anayamikira kusakwatira. Iye iyemwini angakhale anali wamasiye yemwe sanasankhe kukwatiranso. (1 Akorinto 9:5) M’njira iriyonse, iye anadziŵa kuti panali zodetsa nkhaŵa zogwirizanitsidwa ndi moyo wokwatira m’dziko lino. Iye anali kusonyeza ufulu wocheperapo umene Akristu osakwatira angasangalale nawo ndi mmene zikondwerero za akhulupiriri okwatira moyenerera zimagawanikirana pakati pa zinthu zakuthupi ndi zauzimu. Munthu wokwatira saika ulamuliro wotheratu pa thupi lake, popeza kuti mnzake wa mu ukwati ali thupi limodzi ndi iye ndipo chotero ali ndi kuyenera pathupi lake. (1 Akorinto 7:3-5) M’chiyang’aniro cha ichi, Paulo molondola ananena kuti Mkristu wosakwatira ali wokhoza kukhala wopatulika, kunena kuti, woikidwa pambali kotheratu ndi kusungidwa kaamba ka kugwiritsidwa ntchito mwachindunji ndi Yehova Mulungu, ponse paŵiri m’thupi ndi mumzimu.
12. Kukhala wopanda mkazi, nchiyani chimene munthu wosakwatira angachite?
12 Mzimu wa Mkristu wosakwatira, kapena chikhoterero cha maganizo, chimamusonkhezera iye ku utumiki wokangalika, wosacheutsa wa Ufumu wa Mulungu. Pokhala wopanda mkazi wokhala ndi ulamuliro wochepa pa thupi lake, iye angatsatire mzimu, kapena chikhoterero, cha malingaliro ake ndi mtima. Iye angakhale katswiri mu utumiki wa Yehova ndi kusumika kwathupi ndi maganizo. Chotero mwamuna wosakwatira kapena mkazi angayang’ane kokha ku kusangalatsa Ambuye ndi ufulu waumwini waukulu koposa. Moyenerera sitingapatule ku zimene Paulo ananena, popeza Yehova anachiwona icho kukhala choyenera kulembedwa kaamba ka chilangizo chathu.
Munthu Wokwatira Wosakwanira?
13, 14. Ndi njira yolakwika yotani imene imagawa pakati chomangira cha “thupi limodzi” ndi imene ingapange munthu wokwatira kukhala wosakwanira kaamba ka utumiki Wachikristu?
13 Ndi lingaliro lolakwika lakuti angachite zochulukira mu utumiki wa Mulungu, Akristu ena okwatira angaike pambali ukwati wawo kumalo osazindikirika m’moyo. Mwachitsanzo, mkazi angayambe kuchita zinthu wosadalira mwamuna wake m’njira yodzilemekeza iyemwini. Mwamuna angakhale wotanganitsidwa koposa ndi machitachita a mpingo. Pansi pa mikhalidwe yoteroyo, iwo angamalize kuti iwo akuchita bwino mu utumiki wa Yehova. M’chenicheni, ngakhale kuli tero, iwo angakhale akutenga njira yomwe imagawa pakati chomangira cha “thupi limodzi”. Ngati ndi tero, chimenecho sichingakhale chokondweretsa Yehova.
14 M’chenicheni, kugawa pakati chomangira cha “thupi limodzi” kungapangitse munthu wokwatira kukhala wosakwanira kaamba ka utumiki Wachikristu. Ukwati sumawonjezera ku kukwanira kwa utumiki koma umachepetsako chisamaliro chaumwini chomwe chingaperekedwe ku utumiki. (Yerekezani ndi Luka 14:16, 17, 20.) Komabe, ngati anthu okwatira ayenera kusangalatsa Mulungu ndi kukhala okwanira monga atumiki, iwo ayenera kukhala ndi moyo ku mathayo awo aukwati.
Wosakwatira kaamba ka Ufumu
15. (a) Akristu osakwatira ayenera kukulitsa mtundu wanji wa khalidwe? (b) Ndi nsonga yeniyeni iti imene imanena ponena za ukwati ndi kusakwatira imene Paulo anali kupanga pa 1 Akorinto 7:36, 37?
15 Pamene kuli kwakuti atumiki okwatira a Yehova ayenera kukhala ndi moyo kulinga ku mathayo awo aukwati, Akristu osakwatira ayenera kukulitsa chikhutiritso m’kukwanira kwawo kosakwatira. Monga mmene Paulo ananenera: “Koma ndinena kwa osakwatira, ndi kwa akazi amasiye, kuti kuli kwabwino kwa iwo ngati akhala monganso ine [wosakwatira]. Kodi wamangika kwa mkazi? Usafune kumasuka. Kodi wamasuka kwa mkazi? Usafune mkazi.” (1 Akorinto 7:8, 27) Ndi thandizo la Yehova, monga munthu wosakwatira, kulitsani mkhalidwe wokhazikika umene Mulungu amautheketsa. Kusintha kulikonse kwa khalidwe lathu sikuyenera kukhala chinthu chonenedweratu, kokha monga mwambo kapena chivomerezo kuchitsenderezo cha anzanu a zaka zofanana. M’malo mwake, chiyenera kubuka kuchokera ku kuyenera kwa m’Malemba, popeza Paulo ananena kuti: “Koma wina akayesa kuti achitira chosayenera unamwali wake, ngati apitirira pa unamwali, ndipo kukafunika kutero, achite chimene afuna, sachimwa; lolani iwo akwatire. Koma iye amene aima wokhazikika mumtima mwake, wopanda chikakamizo, koma ali nawo ulamuliro wa zifuniro za iye yekha, natsimikiza ichi m’mtima mwa iye yekha, kusunga unamwali wake, adzachita bwino.”—1 Akorinto 7:36, 37, NW.
16. (a) Nchiyani chimene chimatanthauza “kupitirira unamwali”? (b) Mkristu wokhala wosakwatira ayenera kudzitsimikizira za chiyani?
16 Chotero Paulo anasonyeza kuti sichingakhale cholakwa kukwatira ngati munthu anali kuchita mkhalidwe wosayenera kulinga ku unamwali wake, ngakhale kuti mtumwiyo mosakaikira sanali kulozera ku cholakwa chachikulu. Monga mmene iye ananenera poyambirira, “Nkwabwino kukwatira koposa kutentha mtima.” (1 Akorinto 7:9) Ndithudi, iye anali kulozera ku ukwati pansi pa mikhalidwe imeneyo ngati munthu anali “wopitirira unamwali,” kupyola nthaŵi imene zikondwerero za kugonana zinakhala zamphamvu choyamba. Ngati munthu wachikulire ali “ndi ulamuliro pa chifuno chake” ndipo molimba mtima walingalira mumtima mwake kupanga malo kaamba ka umbeta, iye angachite bwino. Umbeta wachipambano sumatanthauza kutsendereza chikhumbo chochepa ndipo chifupifupi champhamvu kaamba ka ukwati ndi moyo wa banja. M’malo mwake, Mkristu wosankha kukhala wosakwatira ayenera kukhala wotsimikizira kotheratu mumtima kuti kusunga umbeta kuli kolondola m’njira yake kaya wamwamuna kapena wamkazi ndipo ayenera kukhala wofunitsitsa kuika kuyesetsa kulikonse kofunikira kusunga mkhalidwe woterowo m’chiyero. Mkristu wochita tero adzakhala ndi zocheutsa zochepa ndi ufulu wochulukira kutumikira Ambuye.
17. Molingana ndi Yesu, nchifukwa ninji ena amakhala osakwatira?
17 Akristu osakwatira adzathandizidwa kusunga mkhalidwe wosakwatira ngati iwo akulitsa maganizo a Yesu Kristu. Ngakhale kuti iye anali wosakwatira mu mwambo umene unagogomezera ukwati, iye anasumika nthaŵi yake ndi mphatso pa utumiki wake wosabwerezedwa. Mofanana ndi Yesu, Mkristu wosakwatira angasangalale ndi mphatso ya kusakwatira imene Mulungu wapereka kwa awo amene angapange malo kaamba ka iyo. Ponena za ichi, Yesu ananena kuti: “Onse sangathe kulandira chonena ichi, koma kwa iwo omwe chapatsidwa. Pakuti pali osabala, amene anabadwa otero m’mimba ya amawo; ndipo pali osabala anawafula anthu; ndipo pali osabala amene anadzifula okha chifukwa cha Ufumu wa kumwamba. Amene angathe kulandira ichi achilandire.”—Mateyu 19:11, 12.
18. Nchiyani chimene chimapangitsa “osabala” kaamba ka Ufumu kusakwatira?
18 Yesu sananene kuti munthu wosakwatira ali wapamwamba kuposa munthu wokwatira. Iye sanakakamize umbeta kokha kuti akhale ndi moyo waufulu, ndipo iye mowonadi sanachiyamikire icho kotero kuti munthu wosakwatira angafalitse zisamaliro zake ku unyinji wa anthu osiyana nawo ziwalo. Ayi, koma awo amene anadzipanga iwo eni “osabala” kaamba ka Ufumu ali anthu amakhalidwe abwino amene amapanga malo kaamba ka ichi mu mitima mwawo. Nchiyani chimene chimapangitsa iwo kusakwatira? Osati kupunduka kwina kwa kuthupi koma chikhumbo champhamvu chodzigwiritsira ntchito iwo eni mokwanira monga mmene kungathekere mu utumiki wa Mulungu. Utumiki umenewu uli chofunika mwapadera nthaŵi ino popeza Ufumu unakhazikitsidwa kumwamba mu 1914 ndipo “mbiri imeneyi yabwino ya ufumu” iyenera kulalikidwa padziko lonse kaamba ka umboni asanafike mapeto omwe akudza mofulumira a dongosolo lamdima iri la kachitidwe ka zinthu.—Mateyu 24:14.
Yamikirani Akristu Osakwatira
19. Ponena za awo omwe amakhala osakwatira kaamba ka Ufumu, nchiyani chimene Akristu onse ayenera kuchita?
19 Akristu onse ayenera kuyamikira ndi kulimbikitsa awo amene amakhalabe osakwatira kaamba ka Ufumu. Ndiko nkomwe, kukhala wosakwatira “kumatanthauza kutsata chitsatire Ambuye, opanda chocheukitsa.” (1 Akorinto 7:35) Makolo angachite bwino kuphunzitsa ana awo zimene Baibulo limanena ponena za mkhalidwe wosakwatira ndi ubwino wake kaamba ka utumiki wa Yehova. Tonse a ife tingalimbikitse okhulupirira anzathu osakwatira ndipo sitiyenera kufooketsa chigamulo chawo cha kukhala osakwatira kaamba ka Ufumu.
20. Ngati muli Mkristu wosakwatira, nchiyani chimene muyenera kuchita?
20 Akristu osakwatira angasangalale monga atumiki okwanira a Mulungu. Mu nthaŵi zino zovuta, iwo amasangalatsidwa kugawana mu ntchito yofunika kwambiri ya kulalikira Ufumu. Chotero, ngati muli wosakwatira, sangalalani m’kukhala mukugwiritsiridwa ntchito ndi Yehova monga mtumiki Wachikristu wosakwatira wokwanira. ‘Gwirirani ntchito chipulumutso chanu ndi mantha ndi kunthunthumira, pamene mukuwala monga miuni ku dziko lapansi, gwiritsani pa mawu a moyo.’ (Afilipi 2:12-16) Sumikani malingaliro anu pa zikondwerero za Ufumu pamene mukukhalabe ogwirizana ndi ubale wa mitundu yonse wa Mboni za Yehova ndi kukwaniritsa utumiki Wachikristu. Kuchita tero monga munthu wosakwatira iri njira yopatsa mphoto, monga mmene tidzawonera.
Ndi Ati Omwe Ali Mayankho Anu?
◻ Nchiyani chimene chiyenera kukhala maziko a moyo Wachikristu?
◻ Nchifukwa ninji atumiki osakwatira a Yehova ayenera kukhala okwanira kaamba ka utumiki?
◻ Ndi mwanjira yotani mmene munthu wokwatira angakhalire wosakwanira?
◻ Nchiyani chimene chimatanthauza kukhala “wosabala” kaamba ka Ufumu?
◻ Nchifukwa ninji tiyenera kulimbikitsa Akristu osakwatira?
[Chithunzi patsamba 10]
Ngakhale anali wosakwatira,mtumwi Paulo anali wokwanira
[Chithunzi patsamba 12]
Yesu anali chitsanzo choyambirira cha munthu wokwanira kaamba ka utumiki
[Chithunzi patsamba 15]
Kodi mumayamikira awo amene amakhalabe osakwatira kaamba ka Ufumu?