PHUNZIRO 16
Kodi Atumiki Othandiza Ali Ndi Udindo Wotani?
Baibulo limatchula magulu awiri a amuna achikhristu amene amakhala ndi maudindo mumpingo. Gulu loyamba ndi la “oyang’anira” ndipo lachiwiri ndi la “atumiki othandiza.” (Afilipi 1:1) Kawirikawiri mumpingo uliwonse mumakhala abale angapo amene ndi akulu komanso atumiki othandiza. Kodi atumiki othandiza amagwira ntchito zotani mumpingo?
Amathandiza bungwe la akulu. Atumiki othandiza, achinyamata ndi achikulire omwe, ndi amuna omwe ali paubwenzi wabwino ndi Yehova. Iwo amakhala odalirika komanso amachita zinthu mosamala. Atumiki othandiza amagwira ntchito zofunika zosiyanasiyana zomwe zimayenera kuchitika nthawi zonse. Zimenezi zimathandiza akulu kuti akwaniritse udindo wawo wophunzitsa komanso kuweta nkhosa za Mulungu.
Amagwira ntchito zosiyanasiyana pampingo. Atumiki othandiza amapatsidwa ntchito zosiyanasiyana, monga kulandira anthu amene akufika kumisonkhano, kusamalira zokuzira mawu, kusamalira mabuku. Komanso amasamalira ndalama za mpingo ndiponso amapatsa Akhristu anzawo dera loti azikalalikira. Iwo amathandizanso pa ntchito yokonza zinthu pa Nyumba ya Ufumu. Nthawi zina angapemphedwe ndi akulu kuti athandize okalamba. Atumiki othandiza amakhala ofunitsitsa kugwira ntchito iliyonse imene apatsidwa, ndipo zimenezi zimachititsa kuti onse mumpingo aziwalemekeza.—1 Timoteyo 3:13.
Monga amuna achikhristu, iwo amapereka chitsanzo chabwino kwa ena. Atumiki othandiza amasankhidwa chifukwa cha makhalidwe awo achikhristu. Iwo amalimbitsa chikhulupiriro chathu akamakamba nkhani pamisonkhano. Komanso akamasonyeza chitsanzo chabwino pa ntchito yolalikira, amatithandiza kuti ifenso tikhale akhama. Popeza kuti iwo amamvera bungwe la akulu, zimenezi zimathandiza kuti onse azisangalala komanso kugwirizana. (Aefeso 4:16) Pakapita nthawi, iwonso angayenerere kukhala akulu.
Kodi atumiki othandiza ndi anthu otani?
Kodi atumiki amathandiza bwanji kuti mpingo uziyenda bwino?