Atumiki Otumikira Amachita Ntchito Yofunika
1 “Adzisonyeza kukhala amuna odzipatuliradi amene chikhulupiriro chawo chasonyezedwa mu utumiki Waufumu wachangu ndi m’kuthandiza ena kulimbitsidwa m’chikhulupiriro.” Limatero buku la Olinganizidwa Kutsiriza Uminisitala Wathu, patsamba 57, ponena za atumiki otumikira. Zoonadi, chitsanzo chauzimu chimene atumiki otumikira athu amasonyeza n’choyeneradi kuchitsatira. Kugwira nawo ntchito komanso ndi akulu ‘kumachita makulidwe a thupi, kufikira chimango chake mwa chikondi.’—Aef. 4:16.
2 Atumiki otumikira amachita ntchito yofunika kwambiri mumpingo. Tangolingalirani mautumiki awo onse ofunika! Amasamalira maakaunti, mabuku, magazini, masabusikiripishoni, ndi magawo; amakhala monga akalinde; kusamalira zokuzira mawu; ndi kusamalira Nyumba ya Ufumu. Amatenga mbali mu Sukulu ya Utumiki Wateokalase ndi Msonkhano wa Utumiki. Ena a iwo amapereka nkhani zapoyera kapenanso kuchititsa misonkhano ina ya mpingo. Monga ziwalo za thupi lenileni, atumiki otumikira amachita utumiki umene timafunikira.—1 Akor. 12:12-26.
3 Kuona atumiki otumikira akugwira ntchito pamodzi ndi akulu mwaulemu ndi momvera monga bungwe limodzi la atumiki kumalimbikitsa ena kuchita zofananazo. (Aef. 2:19) Mwa kukwaniritsa maudindo awo mokhulupirika nthaŵi zonse ndiponso mwa kusonyeza chidwi chawo mwa ena, amathandiza mpingo kupita patsogolo mwauzimu.
4 Kodi tingachite chiyani kuti tisonyeze chiyamikiro chathu kwa atumiki otumikira ogwira ntchito molimbikawa? Tiyenera kudziŵa ntchito yawo ndi kukhala okonzeka kugwirizana nawo pamene afuna thandizo lathu. Mwa mawu kapena zochita zathu, tingawasonyeze kuti ntchito yawo timaiyamikira. (Miy. 15:23) Amene amatigwirira ntchito molimbika n’ngoyenera kuwayamikira kwambiri.—1 Ates. 5:12, 13.
5 Mawu a Mulungu amanena ntchito ndi ziyeneretso za atumiki otumikira. (1 Tim. 3:8-10, 12, 13) Utumiki wawo wopatulika n’ngwofunika kwambiri kuti mpingo uyende bwino. Amuna amenewa ndi ofunika chilimbikitso chathu nthaŵi zonse, popeza onse ali ndi ‘zochuluka mu ntchito ya Ambuye.’—1 Akor. 15:58.