MUTU 76
Anakadya Kunyumba kwa Mfarisi
YESU ANADZUDZULA AFARISI ACHINYENGO
Yesu adakali ku Yudeya, Mfarisi wina anamuitana kuti akadye chakudya kunyumba kwake ndipo Yesu anavomera. Zikuoneka kuti anakadya chakudyachi masana osati madzulo. (Luka 11:37, 38; yerekezerani ndi Luka 14:12.) Asanayambe kudya, Afarisi anali ndi mwambo wosamba m’manja mpaka m’zigongono koma Yesu sankachita nawo zimenezi. (Mateyu 15:1, 2) Ngati munthu akanasamba m’manja kufika m’zigongono sakanaphwanya Chilamulo koma si zimene Mulungu analamula kuti anthu azichita.
Mfarisi uja anadabwa kuona kuti Yesu sanatsatire mwambo umenewu. Yesu anadziwa zimene Mfarisiyo ankaganiza ndipo anamuuza kuti: “Inu Afarisi mumayeretsa kunja kwa kapu ndi mbale, koma mkati mwanu mwadzaza maganizo ofuna kulanda zinthu za anthu ndi kuchita zinthu zoipa. Anthu opanda nzeru inu! Amene anapanga kunja anapanganso mkati, si choncho kodi?”—Luka 11:39, 40.
Pamenepatu nkhani siinali yosamba m’manja munthu asanayambe kudya koma inali yonena za zinthu zachinyengo zimene zinkachitika m’chipembedzo. Afarisi komanso anthu ena amene ankasamba m’manja pongotsatira mwambo ankalephera kuyeretsa mitima yawo kuti asamachite zinthu zoipa. N’chifukwa chake Yesu anawauza kuti: “Koma inu, perekani zimene zili mkati monga mphatso zachifundo, mukatero zina zonse zokhudza inuyo zidzakhala zoyera.” (Luka 11:41) Zimenezitu n’zoona chifukwa munthu ayenera kupereka mphatso chifukwa chokonda munthu amene akumupatsa mphatsoyo, osati n’cholinga chofuna kugometsa anthu kuti azimuona ngati wolungama.
Sikuti Afarisi sankapereka mphatso. Yesu ananena kuti: “Mumapereka chakhumi cha timbewu ta minti ndi ta luwe, ndi cha mbewu zakudimba zamtundu uliwonse. Koma mumanyalanyaza chilungamo ndi chikondi cha Mulungu! Unalidi udindo wanu kuchita zinthu zimenezi, koma simunayenera kusiya zinazo.” (Luka 11:42) Chilamulo cha Mulungu chinkanena kuti anthu azipereka chakhumi (kapena kuti gawo limodzi la magawo 10) pa zokolola zawo. (Deuteronomo 14:22) Zina mwa zinthu zimene ankapereka zinali minti ndi luwe zomwe zinali zitsamba zimene ankazigwiritsa ntchito pokometsera kapena kununkhiritsa zakudya. Afarisi ankayesetsa kupereka chakhumi cha zitsamba zimenezi koma ankanyalanyaza zinthu zofunika kwambiri za m’Chilamulo ngati kuchita chilungamo komanso kukhala wodzichepetsa kwa Mulungu.—Mika 6:8.
Yesu ananenanso kuti: “Tsoka inu Afarisi, chifukwa mumakonda mipando yakutsogolo m’masunagoge ndi kupatsidwa moni m’misika! Tsoka inu, chifukwa muli ngati manda achikumbutso osaonekera, moti anthu amayenda pamwamba pake koma osadziwa!” (Luka 11:43, 44) Anthu ankakhala odetsedwa akayenda pamwamba pa manda. Choncho Yesu anagwiritsa ntchito mfundo imeneyi pofuna kusonyeza kuti Afarisiwo ankachita zinthu zachinyengo mosaonetsera.—Mateyu 23:27
Munthu wina amene ankadziwa Chilamulo cha Mulungu ananena kuti: “Mphunzitsi, izi mukunenazi mukunyoza ndi ife tomwe.” Komatu Yesu ananena dala zimenezi chifukwa atsogoleriwa anayenera kudziwa kuti ankalephera kuthandiza anthu. Ndiyeno Yesu ananena kuti: “Tsoka inunso odziwa Chilamulo, chifukwa mumasenzetsa anthu katundu wovuta kunyamula, koma inuyo simukhudza katunduyo ngakhale ndi chala chokha! “Tsoka inu, chifukwa mumamanga manda achikumbutso a aneneri, komatu makolo anu ndi amene anawapha!”—Luka 11:45-47.
Katundu wovuta kunyamula amene Yesu ankanena inali miyambo imene Afarisi anakhazikitsa okha komanso zinthu zimene iwo ankanena pomasulira Chilamulo. Afarisi amenewa ankachititsa kuti anthu azipanikizika kwambiri moti ankawakakamiza kuti azitsatirabe zinthu zovutazo. Makolo a Afarisiwa anapha aneneri a Mulungu kuyambira pa Abele. Ngakhale kuti Afarisiwa ankaoneka ngati ankalemekeza aneneri powamangira manda koma ankaganiza ndiponso kuchita zinthu ngati makolo awo. Pa nthawiyi ankafunanso kupha Mneneri wamkulu wa Mulungu. Yesu ananena kuti Mulungu adzawalanga chifukwa cha zimenezi. Ndipo anawalangadi m’chaka cha 70 C.E., patadutsa zaka 38.
Yesu ananenanso kuti: “Tsoka inu odziwa Chilamulo, chifukwa munalanda anthu kiyi yowathandiza kudziwa zinthu. Inuyo simunalowemo, ndipo ofuna kulowamo munawatsekereza!” (Luka 11:52) Afarisi amenewa, amene anali ndi udindo wothandiza anthu kumvetsa Mawu a Mulungu, ankalepheretsa anthuwo kudziwa komanso kumvetsa mawuwo.
Kodi Afarisi ndi alembi anatani atamva zimenezi? Pamene Yesu ankafuna kuchoka, Afarisi ndi alembiwo anakwiya kwambiri ndipo anayamba kumutsutsa komanso kum’panikiza ndi mafunso. Sikuti ankafunsa mafunso kuti aphunzirepo kenakake koma iwo ankafuna kuti Yesu anene zinazake n’cholinga choti amupezere chifukwa kuti amumange.