MUTU 19
Miliri Itatu Yoyambirira
Aiguputo ankaumiriza Aisiraeli kuti azigwira ntchito ngati akapolo. Yehova anatumiza Mose ndi Aroni kwa Farao kukanena kuti: ‘Yehova akuti mulole kuti anthu ake apite kuchipululu kuti akamulambire.’ Koma Farao anayankha mwamwano kuti: ‘Zimene Yehova wanenazo ndilibe nazo ntchito. Sindilola kuti Aisiraeli apite.’ Atatero anawonjezera ntchito zimene Aisiraeli ankagwira. Choncho Yehova anafuna kuti Farao adziwe kuti iye ndi wamkulu kuposa milungu yonse. Kodi ukudziwa zimene anachita? Anabweretsa Miliri 10 ku Iguputo. Yehova anauza Mose kuti: ‘Farao sakufuna kundimvera. Mawa m’mawa akhala ali kumtsinje wa Nailo. Upite ukamuuze kuti popeza sakufuna kuti anthu anga apite, madzi onse a mumtsinje wa Nailo asanduka magazi.’ Mose anamvera Yehova ndipo anapitadi kwa Farao. Kumeneko Aroni anamenya ndi ndodo madzi a mumtsinje wa Nailo, Farao akuona ndipo madziwo anasanduka magazi. Madziwo anayamba kununkha, nsomba zonse zinafa ndipo anthu anasowa madzi akumwa. Koma Farao sanalolebe kuti Aisiraeli apite.
Patatha masiku 7, Yehova anatumanso Mose kwa Farao kukamuuza kuti: ‘Ukapanda kulola kuti anthu anga apite, m’dziko la Iguputo mudzakhala achule paliponse.’ Aroni anakweza ndodo yake m’mwamba ndipo achule anayamba kudzaza m’dziko lonse. Achulewo ankapezeka m’nyumba, pabedi, m’mbale, tingoti paliponse. Zitatero Farao anauza Mose kuti akapemphe kwa Yehova kuti mliriwu uthe ndipo analonjeza kuti alola Aisiraeli kuti apite. Choncho Yehova anathetsadi mliriwo ndipo achulewo anayamba kufa. Aiguputo anaunjika achulewo milumilu moti dziko lonse linkanunkha. Koma Farao ataona kuti mliri watha, sanalolebe kuti Aisiraeli apite.
Ndiyeno Yehova anauza Mose kuti: ‘Aroni amenye pansi ndi ndodo ndipo fumbi lisanduka tizilombo toyamwa magazi.’ Aroni anachitadi zimenezi ndipo paliponse panagwa tizilombo toyamwa magazi. Aiguputo ena anauza Farao kuti: ‘Mliriwu wachokera kwa Mulungu.’ Koma Farao sanalolebe kuti Aisiraeli apite.
“Ndiwachititsa kuti adziwe mphamvu ndi nyonga zanga, ndipo adziwa kuti dzina langa ndine Yehova.”—Yeremiya 16:21