Anachita Chifuniro cha Yehova
Mose ndi Aroni—Alengezi Olimba Mtima a Mawu a Mulungu
TALINGALIRANI chochitikacho: Mose wazaka makumi asanu ndi atatu ndi mbale wake, Aroni, aimirira pamaso pa munthu wamphamvu koposa padziko lapansi—Farao wa Igupto. Kwa Aigupto munthu ameneyu saali chabe woimira milungu. Amakhulupirira kuti iyeyo ali mulungu. Amamuona monga Horus wobadwanso m’thupi, mulungu wokhala ndi mutu wa mphamba. Pamodzi ndi Isis ndi Osiris, Horus anali mbali ya milungu itatu yaikulu pakati pa milungu ya Igupto yachimuna ndi yachikazi.
Aliyense wofika kwa Farao sanali kulephera kuona chifanizo chowopsa cha mutu wa mamba chomaonekera pakati pa chisoti chake. Anthu anakhulupirira kuti njoka imeneyi inali kulavula moto ndi chiwonongeko pa mdani aliyense wa Farao. Tsopano Mose ndi Aroni adza pamaso pa mfumu mulungu imeneyi ndi pempho limene siinalimvepo—kuti alole Aisrayeli omangidwa ukapolo kupita kukachitira madyerero Mulungu wawo, Yehova.—Eksodo 5:1.
Yehova anali ataneneratu kuti Farao adzauma mtima. Motero, Mose ndi Aroni sanadabwe ndi yankho lake lonyozera lakuti: “Yehova ndani, kuti ndimvere mawu ake ndi kulola Israyeli apite? Sindimdziŵa Yehova, ndiponso sindidzalola Israyeli apite.” (Eksodo 4:21; 5:2) Motero, bwalo linatseguka kaamba ka zochitika zochititsa chidwi. Pakukumana kotsatira, Mose ndi Aroni anasonyeza umboni wodabwitsa kwa Farao kuti iwo anali kuimira Mulungu woona ndi wamphamvuyonse.
Chozizwitsa Chichitika
Monga momwe Yehova anawalangizira, Aroni anachita chozizwitsa chimene chinasonyezadi ukulu wa Yehova pa milungu ya Igupto. Anaponya ndodo yake pansi pamaso pa Farao, ndipo pamenepo inakhala chinjoka chachikulu! Atadabwa ndi chozizwitsa chimenechi, Farao anaitana amatsenga ake.a Mothandizidwa ndi mphamvu ya ziŵanda, amuna ameneŵa anachita zofananazo ndi ndodo zawo.
Ngati Farao ndi amatsenga ake ananyada, zinali kwa kamphindi kochepa chabe. Tayerekezerani kaonekedwe ka nkhope zawo pamene chinjoka cha Aroni chinameza njoka zawo imodziimodzi! Onse amene analipo anaona kuti milungu ya Aigupto sinali kulingana ndi Mulungu woona, Yehova.—Eksodo 7:8-13.
Ngakhale pambuyo pa zimenezi, mtima wa Farao unaumabe. Panali kokha pambuyo poti Mulungu wabweretsa nkhonya zowononga, kapena miliri khumi pa Igupto pamene Farao potsirizira pake anauza Mose ndi Aroni kuti: “Ukani, tulukani pakati pa anthu anga, inu ndi ana a Israyeli; ndipo mukani katumikireni Yehova, monga mwanena.”—Eksodo 12:31.
Zimene Tiphunzirapo
Kodi nchiyani chinakhozetsa Mose ndi Aroni kufikira Farao wa Igupto wamphamvuyo? Poyamba, Mose anasonyeza kuti analibe chidaliro pa kukhoza kwake, akumanena kuti ali “wa m’kamwa molemera, ndi wa lilime lolemera.” Ngakhale pambuyo poti Yehova wamtsimikizira kuti adzamchirikiza, iye anapempha kuti: “Tumizani pa dzanja la iye amene mudzamtuma.” M’mawu ena, Mose anali kupempha kuti Mulungu atume wina. (Eksodo 4:10, 13) Ngakhale zinali motero, Yehova anagwiritsira ntchito Mose wofatsayo, akumampatsa nzeru ndi nyonga zofunikira kuti achite ntchito yake.—Numeri 12:3.
Lerolino, atumiki a Yehova Mulungu ndi Yesu Kristu akutsatira lamulo la ‘kuphunzitsa anthu amitundu yonse.’ (Mateyu 28:19, 20) Kuti tichite mbali yathu pakukwaniritsa ntchito imeneyi, tiyenera kugwiritsira ntchito bwino koposa chidziŵitso chathu cha Malemba ndi kukhoza kwina kulikonse kumene tingakhale nako. (1 Timoteo 4:13-16) M’malo mwa kusumika maganizo pa zinthu zimene timalephera kuchita, tiyeni tivomereze ndi chikhulupiriro ntchito iliyonse imene Mulungu watipatsa. Akhoza kutiyeneretsa ndi kutilimbitsa kuti tichite chifuniro chake.—2 Akorinto 3:5, 6; Afilipi 4:13.
Pakuti Mose anayang’anizana ndi mphamvu zaumunthu ndi zauchiŵanda, mosakayikira iye anafunikira chithandizo cha Mulungu. Chotero, Yehova anamtsimikizira kuti: “Taona, ndakuika ngati Mulungu kwa Farao.” (Eksodo 7:1) Inde, Mose anali ndi chichirikizo cha Mulungu ndi ulamuliro wake. Pokhala nawo mzimu wa Yehova, Mose analibe chifukwa chowopera Farao kapena atsamwali a wolamulira wonyadayo.
Ifenso tiyenera kudalira mzimu woyera wa Yehova, kapena mphamvu yogwira ntchito, kuti tikwaniritse utumiki wathu. (Yohane 14:26; 15:26, 27) Pokhala ndi chichirikizo chaumulungu tinganenenso mawu a Davide, amene anaimba kuti: “Pa Mulungu ndakhulupirira, sindidzawopa; munthu adzandichitanji?”—Salmo 56:11.
Popeza Yehova ngwachifundo sanamsiye yekha Mose pantchito yake. M’malo mwake, Mulungu ananena kuti: “Aroni mkulu wako adzakhala mneneri wako. Iwe uzilankhula zonse ndikulamulira; ndi Aroni mkulu wako azilankhula kwa Farao.” (Eksodo 7:1, 2) Chinalidi chikondi cha Yehova kuchita zinthu malinga ndi zimene Mose anatha kuchita!
Mulungu watipatsa mayanjano a Akristu anzathu amene avomereza chitokoso cha kukhala Mboni za Yehova Wam’mwambamwambayo. (1 Petro 5:9) Motero, mosasamala kanthu za zopinga zimene tingakumane nazo, tiyeni tikhale ngati Mose ndi Aroni—alengezi olimba mtima a mawu a Mulungu.
[Mawu a M’munsi]
a Liwu lachihebri lotembenuzidwa “amatsenga” limasonya ku kagulu ka amatsenga amene anali kunena kuti anali ndi mphamvu kuposa ziŵanda. Anthu anali kukhulupirira kuti amuna ameneŵa ankalamula ziŵanda ndipo izo zinkamva ndi kuti ziŵanda zinalibe mphamvu pa amatsenga ameneŵa.
[Chithunzi patsamba 25]
Mose ndi Aroni anaimira Yehova molimba mtima pamaso pa Farao