MUTU 7
Anthu a Mitundu Ina “Adzadziwa Kuti Ine Ndine Yehova”
MFUNDO YAIKULU: Zimene tikuphunzira pa zochita za Aisiraeli ndi anthu a mitundu ina amene ankanyoza dzina la Yehova
1, 2. (a) Kodi Aisiraeli anakhala bwanji ngati nkhosa imene ili yokhayokha pakati pa mimbulu? (Onani chithunzi choyambirira) (b) Kodi Aisiraeli komanso mafumu awo analola kuti pachitike chiyani?
KWA zaka zambiri, Aisiraeli anali ngati nkhosa imene yazunguliridwa ndi mimbulu. Aamoni, Amowabu ndi Aedomu ankaukira Aisiraeli kuchokera kumalire akum’mawa. Afilisiti amene nthawi zonse ankadana ndi Isiraeli, anakhazikika kumadzulo. Kumpoto kunali mzinda wa Turo umene unali wamphamvu komanso wolemera chifukwa kunali kuchimake kwa malonda. Kumwera kunali dziko la Iguputo limene linkalamuliridwa ndi Farao amene anthu ankamuona ngati mulungu.
2 Aisiraeli akamadalira Yehova, iye ankawateteza kwa adani awo. Koma mobwerezabwereza anthu a Mulungu komanso mafumu awo ankatengera makhalidwe oipa a mitundu ya anthu owazungulira. Mfumu Ahabu ndi chitsanzo chimodzi cha olamulira amene anatengera makhalidwe oipa a mitundu ya anthu owazungulira. Ahabu ankalamulira ufumu wa Isiraeli wa mafuko 10 pa nthawi imene Mfumu Yehosafati ankalamulira Yuda. Iye anakwatira mwana wa mfumu ya ku Sidoni imene inkalamulira mzinda wotchuka wa Turo. Mkazi ameneyu amene dzina lake anali Yezebeli, analimbikitsa anthu kuti azilambira Baala mu Isiraeli ndipo anachititsa kuti mwamuna wake adetse kwambiri kulambira koyera.—1 Maf. 16:30-33; 18:4, 19.
3, 4. (a) Kodi tsopano Ezekieli anayamba kufotokoza za ndani? (b) Kodi tikambirana mafunso ati?
3 Yehova anali atachenjeza anthu ake kuti adzakumana ndi mavuto akakhala osakhulupirika kwa iye. Tsopano kuleza mtima kwake kunatha. (Yer. 21:7, 10; Ezek. 5:7-9) Mu 609 B.C.E., asilikali a Babulo anabweranso kachitatu kudzaukira Dziko Lolonjezedwa. Panali patadutsa zaka pafupifupi 10 kuchokera pamene anabwera komaliza kudzaukira mzindawo. Ulendo umenewu anagwetsa mpanda wa Yerusalemu ndiponso anazunza kwambiri anthu onse amene anapandukira Nebukadinezara. Adani atayamba kuukira mzindawo ndipo maulosi ouziridwa a Ezekieli atakwaniritsidwa mochititsa mantha, mneneriyu anayamba kufotokoza zimene zidzachitikire mitundu imene inazungulira Dziko Lolonjezedwa.
Anthu a mitundu ina amene akunyoza dzina la Yehova sadzalephera kulangidwa
4 Yehova anauza Ezekieli kuti adani a Yuda adzasangalala Yerusalemu akadzawonongedwa ndipo adzazunza anthu amene adzapulumuke. Koma mitundu imene inkanyoza dzina la Yehova komanso kuzunza kapena kusokoneza makhalidwe a anthu ake, sidzalephera kulangidwa. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Aisiraeli ankachita ndi mitundu imeneyo? Kodi maulosi a Ezekieli onena za anthu a mitundu ina akutipatsa bwanji chiyembekezo masiku ano?
Achibale a Aisiraeli Amene ‘Ankawanyoza’
5, 6. Kodi panali ubale wotani pakati pa Aamoni ndi Aisiraeli?
5 Aamoni, Amowabu ndi Aedomu anali pa chibale ndi Aisiraeli. Ngakhale kuti anthuwa anali pa chibale, kwa nthawi yaitali mitundu imeneyi inkadana kwambiri ndi anthu a Mulungu ndipo ‘inkawanyoza.’—Ezek. 25:6.
6 Taganizirani za Aamoni. Iwo anali mbadwa za Loti, kudzera mwa mwana wake wamng’ono ndipo Lotiyo anali mwana wa mchimwene wake wa Abulahamu. (Gen. 19:38) Chilankhulo chawo chinali chofanana kwambiri ndi Chiheberi moti anthu a Mulungu ayenera kuti ankamva chilankhulo chawocho. Chifukwa chakuti anthuwa anali pa chibale, Yehova anauza Aisiraeli kuti asayambitse nkhondo yomenyana ndi Aamoni. (Deut. 2:19) Koma m’masiku a Oweruza, Aamoni anagwirizana ndi Mfumu Egiloni ya ku Mowabu imene inkazunza Aisiraeli. (Ower. 3:12-15, 27-30) Patapita nthawi, Sauli atakhala mfumu Aamoni anaukira Aisiraeli. (1 Sam. 11:1-4) Ndipo m’masiku a Mfumu Yehosafati, Aamoni anagwirizananso ndi Amowabu n’kukaukira Dziko Lolonjezedwa.—2 Mbiri 20:1, 2.
7. Kodi Amowabu anawachitira chiyani abale awo omwe anali mbadwa za Isiraeli?
7 Amowabu nawonso anali mbadwa za Loti koma kudzera mwa mwana wake wamkulu. (Gen. 19:36, 37) Yehova anauza Aisiraeli kuti asamenyane ndi Amowabu. (Deut. 2:9) Koma Amowabu sanasonyeze chifundo kwa Aisiraeli. M’malo mothandiza abale awo omwe ankathawa ukapolo ku Iguputo, iwo anayesetsa kuti awalepheretse kulowa m’Dziko Lolonjezedwa. Balaki mfumu ya Amowabu, analemba ganyu Balamu kuti akatemberere Aisiraeli ndipo Balamu anauza Balaki zoyenera kuchita kuti apusitse Aisiraeliwo n’cholinga choti achite chiwerewere komanso kulambira mafano. (Num. 22:1-8; 25:1-9; Chiv. 2:14) Kwa zaka zambiri Amowabu anapitiriza kuzunza abale awo mpaka m’nthawi ya Ezekieli.—2 Maf. 24:1, 2.
8. N’chifukwa chiyani Yehova ananena kuti Aedomu anali abale awo a Aisiraeli, nanga kodi Aedomuwo anachita chiyani?
8 Aedomu anali mbadwa za Esau amene anali mchimwene wake wa Yakobo. Chibale cha mafuko awiriwa chinali chapafupi kwambiri moti Yehova ananena kuti Aedomu anali abale awo a Aisiraeli. (Deut. 2:1-5; 23:7, 8) Ngakhale zinali choncho, Aedomu anapitiriza kuzunza Aisiraeli kuchokera pamene anachoka ku Iguputo kudzafika nthawi imene Yerusalemu anawonongedwa mu 607 B.C.E. (Num. 20:14, 18; Ezek. 25:12) Pa nthawi imeneyo, Aedomu anasangalala ataona kuti Aisiraeli akuzunzika ndipo anauza Ababulo kuti awononge Yerusalemu. Kuwonjezera pamenepo, ankagwira Aisiraeli amene ankathawa n’kumakawapereka kwa adani awo.—Sal. 137:7; Obad. 11, 14.
9, 10. (a) Kodi n’chiyani chimene chinachitikira Aamoni, Amowabu ndi Aedomu? (b) Kodi ndi zitsanzo ziti zimene zikusonyeza kuti si anthu onse a mitundu imeneyi amene ankachitira nkhanza Aisiraeli?
9 Yehova anapereka chilango kwa achibale a Aisiraeliwo chifukwa cha zimene anachitira anthu ake. Iye anati: “Ndidzapereka . . . Aamoni kwa anthu a Kumʼmawa kuti akhale chuma chawo. Ndidzachita zimenezi kuti Aamoni asadzakumbukiridwenso pakati pa mitundu ya anthu.” Iye ananenanso kuti: “Ndidzapereka chiweruzo mʼdziko la Mowabu ndipo adzadziwa kuti ine ndine Yehova.” (Ezek. 25:10, 11) Patadutsa zaka 5 Yerusalemu atawonongedwa, maulosi amenewa anayamba kukwaniritsidwa pamene Ababulo anagonjetsa Aamoni ndi Amowabu. Ponena za Edomu, Yehova ananena kuti ‘adzapha anthu ndi ziweto mʼdzikolo’ komanso kuti ‘adzalisandutsa bwinja.’ (Ezek. 25:13) Mogwirizana ndi zimene analoserazi, patapita nthawi, Aamoni, Amowabu ndi Aedomu anatha onse.—Yer. 9:25, 26; 48:42; 49:17, 18.
10 Komabe si anthu onse a m’mitundu imeneyi amene ankachitira nkhanza anthu a Mulungu. Mwachitsanzo, Zeleki amene anali mbadwa ya Amoni komanso Itima wa ku Mowabu, anali m’gulu la asilikali amphamvu a Mfumu Davide. (1 Mbiri 11:26, 39, 46; 12:1) Komanso Rute wa ku Mowabu anayamba kulambira Yehova ndipo anali wokhulupirika.—Rute 1:4, 16, 17.
Tisasiye ngakhale pang’ono kutsatira mfundo zimene timayendera
11. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Aisiraeli ankachita ndi Aamoni, Amowabu komanso Aedomu?
11 Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Aisiraeli ankachita ndi mitundu imeneyi? Choyamba, Aisiraeli atayamba kuchita zinthu motayirira, anayamba kutengera miyambo ya zipembedzo zabodza za abale awowo moti anayamba kulambira Baala wa ku Peori yemwe ndi mulungu wa Amowabu komanso Moleki yemwe ndi mulungu wa Aamoni. (Num. 25:1-3; 1 Maf. 11:7) Ifenso zoterezi zikhoza kutichitikira. Achibale athu omwe si Mboni akhoza kumatikakamiza kuti tichite zinthu zolakwika. Mwachitsanzo, sangamvetse chifukwa chake sitikondwerera nawo Isitala, kupatsana mphatso pa Khirisimasi kapena kuchita nawo miyambo ina yotchuka imene imagwirizana ndi zikhulupiriro za zipembedzo zabodza. Ngakhale kuti angakhale ndi zolinga zabwino, angayese kutikakamiza kuti tichite pang’ono pokha zinthu zosemphana ndi zimene timakhulupirira. Choncho n’zofunika kwambiri kuti tisagonje ngati zimenezi zitatichitikira. Monga mmene tikuonera kuchokera kwa Aisiraeli, kungosiya pang’ono kutsatira mfundo zimene timayendera kungabweretse mavuto aakulu.
12, 13. Kodi tingatsutsidwe ndi ndani, nanga chingachitike n’chiyani ngati titakhalabe okhulupirika?
12 Tingaphunzirenso chinthu china kuchokera pa zimene Aamoni, Amowabu ndi Aedomu anachitira Aisiraeli. Ifenso tikhoza kumatsutsidwa kwambiri ndi achibale athu omwe si Mboni. Yesu anachenjeza kuti nthawi zina uthenga umene timalalikira ‘ungagawanitse anthu.’ Ungachititse kuti “mwana wamwamuna atsutsane ndi bambo ake, mwana wamkazi atsutsane ndi mayi ake.” (Mat. 10:35, 36) Yehova anauza Aisiraeli kuti asamakangane ndi abale awo. Ifenso sitifuna kuti tizikangana ndi anthu a m’banja lathu omwe si Mboni. Koma sitiyenera kudabwa ngati atayamba kutitsutsa.—2 Tim. 3:12.
13 Ngakhale zitakhala kuti achibale athu satitsutsa tikamalambira Yehova, tisamalole kuti tiziyendera maganizo awo kuposa maganizo a Yehova. Chifukwa chiyani? Chifukwa chakuti tiyenera kukonda kwambiri Yehova kuposa wina aliyense. (Werengani Mateyu 10:37.) Kuwonjezera pamenepo tikakhala okhulupirika kwa Yehova, achibale athu ena angakhale ngati Zeleki, Itima ndi Rute ndipo angagwirizane nafe n’kuyamba kulambira Mulungu woona. (1 Tim. 4:16) Zikatero iwonso angamasangalale polambira Mulungu woona yekha amene angawakonde komanso kuwateteza.
Yehova Analanga Adani Ake “Mwaukali”
14, 15. Kodi Afilisiti ankawachitira chiyani Aisiraeli?
14 Afilisiti anachoka ku chilumba cha Kirete n’kukakhala m’dziko limene Yehova analonjeza kuti adzalipereka kwa Abulahamu ndi mbadwa zake. Abulahamu ndi Isaki, onse ankachita zinthu zina ndi anthu amenewa. (Gen. 21:29-32; 26:1) Pofika nthawi imene Aisiraeli ankalowa m’Dziko Lolonjezedwa, Afilisiti anali atakhala mtundu wamphamvu ndipo anali ndi asilikali odziwa kumenya nkhondo. Iwo ankalambira milungu yabodza ngati Baala-zebabu ndi Dagoni. (1 Sam. 5:1-4; 2 Maf. 1:2, 3) Nthawi zina Aisiraeli ankalambiranso milungu imeneyi.—Ower. 10:6.
15 Chifukwa cha kusakhulupirika kwa Aisiraeli, Yehova analola kuti Afilisiti apondereze anthu akewo kwa zaka zambiri. (Ower. 10:7, 8; Ezek. 25:15) Iwo anawaikira malamulo ovuta ndipo Aisiraelia ambiri anaphedwa. (1 Sam. 4:10) Koma Aisiraeli atalapa n’kubwerera kwa Yehova, iye anawapulumutsa. Iye anagwiritsa ntchito Samisoni, Sauli ndi Davide kuti apulumutse anthu akewo. (Ower. 13:5, 24; 1 Sam. 9:15-17; 18:6, 7) Ndipo mogwirizana ndi zimene Ezekieli analosera, Afilisiti analangidwa “mwaukali” pamene Ababulo komanso pambuyo pake Agiriki analanda dziko lawo.—Ezek. 25:15-17.
16, 17. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Afilisiti ankachitira Aisiraeli?
16 Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Afilisiti ankachitira Aisiraeli? Anthu a Yehova masiku ano akhalanso akutsutsidwa ndi maulamuliro amphamvu kwambiri komanso opondereza. Koma mosiyana ndi Aisiraeli, ife takhala okhulupirika kwa Yehova. Ngakhale zili choncho, nthawi zina zingaoneke ngati anthu amene amadana ndi kulambira koyera akupambana. Mwachitsanzo, kumayambiriro kwa zaka za m’ma 1900, boma la United States linkafuna kuletsa ntchito ya anthu a Yehova polamula kuti anthu amene ankatsogolera gulu lathu akakhale m’ndende kwa zaka zambiri. Pa nthawi ya nkhondo yachiwiri yapadziko lonse, chipani cha Nazi ku Germany chinkafuna kuwonongeratu anthu onse a Mulungu, moti abale ndi alongo athu masauzande ambiri anaikidwa m’ndende ndipo ambiri anaphedwa. Nkhondo imeneyo itatha, boma la Soviet Union linayamba kampeni yolimbana ndi Mboni za Yehova, imene inachitika kwa zaka zambiri. Zimenezi zinachititsa kuti abale athu ambiri awapititse kumakampu amene ankazunzirako anthu kapena kumadera akutali m’dzikomo.
17 Maboma angapitirize kuletsa ntchito yathu yolalikira, kutitsekera m’ndende komanso ngakhale kupha ena a ife. Kodi zimenezi ziyenera kutichititsa mantha kapena kuchititsa kuti chikhulupiriro chathu chichepe? Ayi. Yehova adzateteza anthu ake okhulupirika. (Werengani Mateyu 10:28-31.) Taona kale maboma amphamvu komanso opondereza akutha, koma anthu a Mulungu akupitirizabe kuwonjezereka. Posachedwapa, maboma onse a anthu adzakakamizika kudziwa Yehova ngati mmene zinachitikira ndi Afilisiti. Ndipo mofanana ndi Afilisiti, iwo adzatheratu.
‘Chuma Chochuluka’ Sichinawateteze
18. Kodi mzinda wa Turo unali wotchuka chifukwa chiyani?
18 Mzinda wakale wa Turob unali wotchuka kwambiri pa nkhani za malonda pa nthawiyo. Kumbali yakumadzulo, mzinda wa Turo unali ndi njira zambiri zimene amalonda ankadutsa kudzera pa Nyanja ya Mediterranean. Mbali ya kum’mawa, mzinda wa Turo unali ndi njira zambiri zapamtunda zimene zinkalumikiza dzikoli ndi maulamuliro ena akutali. Kwa zaka zambiri, mzindawu unapeza chuma chambiri chimene chinkachokera m’madera akutaliwa. Anthu amalonda amumzindawu analemera kwambiri moti ankadziona ngati akalonga.—Yes. 23:8.
19, 20. Kodi anthu a ku Turo anali osiyana bwanji ndi anthu a ku Gibiyoni?
19 M’nthawi ya ulamuliro wa Mfumu Davide ndi Solomo, Aisiraeli ankagwirizana kwambiri ndi anthu a ku Turo, omwe ankawapatsa katundu ndi amisiri amene anawathandiza kumanga nyumba ya Mfumu Davide ndiponso pambuyo pake kachisi wa Solomo. (2 Mbiri 2:1, 3, 7-16) Anthu a ku Turo ankagwirizana ndi Aisiraeli pa nthawi imene anali okhulupirika kwa Yehova ndipo ankawadalitsa. (1 Maf. 3:10-12; 10:4-9) Taganizirani mwayi umene anthu masauzande a ku Turo anali nawo wophunzira zokhudza kulambira koyera, wodziwa Yehova komanso kuona okha ubwino wotumikira Mulungu woona.
20 Komabe ngakhale kuti anali ndi mwayi umenewu, anthu a ku Turo anapitiriza kukonda chuma. Sanatsatire chitsanzo cha anthu amumzinda wa ku Kanani wa Gibiyoni. Anthu amumzinda umenewu ankafunitsitsa kukhala atumiki a Yehova, atangomva zinthu zochepa chabe zokhudza ntchito zazikulu za Yehova. (Yos. 9:2, 3, 22–10:2) Ndipotu anthu a ku Turo anayamba kutsutsa anthu a Mulungu moti anafika pogulitsa ena a iwo ku ukapolo.—Sal. 83:2, 7; Yow. 3:4, 6; Amosi 1:9.
Tisamaone chuma ngati khoma lotiteteza
21, 22. Kodi n’chiyani chinachitikira mzinda wa Turo, nanga n’chifukwa chiyani?
21 Kudzera mwa Ezekieli, Yehova anauza otsutsawo kuti: “Ine ndikuukira iwe Turo ndipo ndikutumizira mayiko ambiri kuti adzamenyane nawe. Iwo adzabwera ngati mafunde amʼnyanja. Mayikowo adzagwetsa mipanda ya Turo komanso kugumula nsanja zake. Ine ndidzapala dothi lake nʼkumusandutsa thanthwe losalala lopanda kanthu.” (Ezek. 26:1-5.) Pa nkhani ya chitetezo, anthu a ku Turo ankadalira chuma chawo chimene ankaona kuti chikuwapatsa chitetezo chofanana ndi cha mpanda wa mzindawo womwe unali wautali mamita 46. Iwo akanachita bwino kwambiri akanamvera chenjezo la Solomo lakuti: “Chuma cha munthu wolemera chili ngati mzinda wokhala ndi mpanda wolimba. Ndipo m’maganizo mwake chili ngati mpanda umene ukumuteteza.”—Miy. 18:11.
22 Pamene Ababulo kenako Agiriki ankakwaniritsa ulosi wa Ezekieli, anthu a ku Turo anazindikira kuti chitetezo chimene chuma cha mzindawo komanso mpanda wake chinkapereka sichinali chenicheni. Ababulo atawononga Yerusalemu, anayamba kulimbana ndi mzinda wa Turo kwa zaka 13. (Ezek. 29:17, 18) Kenako mu 332 B.C.E., Alekizanda Wamkulu anakwaniritsa mbali yaikulu ya maulosi a Ezekieli.c Asilikali ake anakokolola zinthu zimene zinatsala mzinda wa Turo utawonongedwa kenako anaponyera m’madzi miyala, zinthu zamatabwa komanso dothi. Izi zinapangitsa kuti apange njira yokafikira pamzinda wa Turo umene unali pachilumba. (Ezek. 26:4, 12) Alekizanda anagumula mpanda n’kutenga zinthu zimene zinali mumzindamo, anapha asilikali ndi anthu amumzindawo masauzande ambiri ndipo anthu ena ambiri anawagulitsa kuti akhale akapolo. Anthu a ku Turo anakakamizika kudziwa Yehova pamene anaphunzira mowawa kuti ‘chuma chochuluka’ sichingawateteze mpaka kalekale.—Ezek. 27:33, 34.
23. Kodi tikuphunzira chiyani kwa anthu a ku Turo?
23 Kodi tikuphunzira chiyani kwa anthu a ku Turo? Tisalole kuti “chinyengo champhamvu cha chuma” chitipangitse kuti tizidalira kwambiri chumacho n’kumachiona ngati khoma limene lingatiteteze. (Mat. 13:22) Sitingathe “kutumikira Mulungu ndi Chuma.” (Werengani Mateyu 6:24.) Anthu okhawo amene amatumikira Yehova ndi mtima wonse ndi amene amakhala otetezeka. (Mat. 6:31-33; Yoh. 10:27-29) Maulosi onse okhudza kutha kwa dziko loipali adzakwaniritsidwa ngati mmene maulosi okhudza kuwonongedwa kwa Turo anakwaniritsidwira. Pa nthawi imeneyo, amene amadalira chuma chawo adzakakamizika kudziwa Yehova, iye akadzawononga amalonda am’dzikoli omwe ndi adyera komanso odzikonda.
Ulamuliro Wandale Unali “Ngati Tsekera”
24-26. (a) N’chifukwa chiyani Yehova ananena kuti Iguputo anali “ngati tsekera”? (b) Kodi Mfumu Zedekiya ananyalanyaza bwanji malangizo a Yehova, nanga zotsatira zake zinali zotani?
24 Kuyambira kale Yosefe asanabadwe kudzafika nthawi imene Ababulo analowa mu Yerusalemu, ulamuliro wa Iguputo unkakhudza kwambiri zochitika za m’Dziko Lolonjezedwa. Ulamulirowu unkaoneka ngati wolimba chifukwa chakuti unakhala kwa nthawi yayitali ngati mtengo. Koma tikauyerekezera ndi Yehova, ulamulirowu unali wosalimba ngati “tsekera.”—Ezek. 29:6.
25 Mfumu Zedekiya amene anapanduka sanadziwe kuti Iguputo anali ngati tsekera losalimba. Kudzera mwa mneneri Yeremiya, Yehova anauza Zedekiya kuti azitumikira mfumu ya Babulo. (Yer. 27:12) Zedekiya anachita kulumbira m’dzina la Yehova kuti sadzapandukira Nebukadinezara. Koma sanatsatire malangizo a Yehova komanso anaphwanya lumbiro limene anachita ndi Nebukadinezara ndipo anapempha Aiguputo kuti amuthandize kumenyana ndi Ababulo. (2 Mbiri 36:13; Ezek. 17:12-20) Koma Aisiraeli amene ankadalira mphamvu za Iguputo anadzibweretsera mavuto. (Ezek. 29:7) N’kutheka kuti Iguputo ankaoneka wamphamvu kwambiri ngati “chilombo chachikulu chamʼnyanja.” (Ezek. 29:3, 4) Koma Yehova ananena kuti adzathana naye ngati mmene osaka nyama amagwirira ng’ona za mumtsinje wa Nailo. Ananena kuti adzamukola ndi ngowe munsagwada zake n’kupita naye kokamuwononga. Mulungu anachita zimenezi pamene anatuma Ababulo kuti akagonjetse dziko lakaleli.—Ezek. 29:9-12, 19.
26 Kodi n’chiyani chinachitikira Zedekiya wosakhulupirika uja? Chifukwa chakuti anapandukira Yehova, Ezekieli analosera kuti ‘mtsogoleri woipayu’ adzalandidwa chisoti chake chachifumu ndipo ulamuliro wake udzatha. Koma Ezekieli anaperekanso chiyembekezo. (Ezek. 21:25-27) Yehova anamuuza kuti alosere kuti winawake wa m’banja lachifumu, amene “ali woyenerera mwalamulo,” adzatenga ufumu wake. M’mutu wotsatira wa bukuli tiona kuti munthu ameneyo anali ndani.
27. Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Aisiraeli ankachita ndi Aiguputo?
27 Kodi tikuphunzira chiyani pa zimene Aisiraeli ankachita ndi Aiguputo? Anthu a Yehova masiku ano akuyenera kupewa kudalira maulamuliro andale, n’kumaganiza kuti maulamuliro amenewo akhoza kuwateteza mpaka kalekale. Ngakhale pa zimene tikuganiza tikuyenera kupewa kukhala “mbali ya dzikoli.” (Yoh. 15:19; Yak. 4:4) Maulamuliro andalewa akhoza kuoneka ngati amphamvu koma mofanana ndi dziko lakale la Iguputo, iwo ndi osalimba ngati tsekera. Kudalira anthu amene amafa m’malo modalira Wolamulira Wamphamvuyonse wa chilengedwe chonse, kungakhale kusaona patali.—Werengani Salimo 146:3-6.
Anthu a Mitundu Ina “Adzadziwa”
28-30. Kodi mmene anthu a mitundu ina ‘adzadziwire’ Yehova zikusiyana bwanji ndi mmene ifeyo timadziwira Yehova?
28 M’malo ambiri m’buku la Ezekieli, Yehova ananena kuti anthu a mitundu ina “adzadziwa kuti ine ndine Yehova.” (Ezek. 25:17) Mawu amenewa anakwaniritsidwa kalelo pamene Yehova anapereka chiweruzo kwa adani a anthu ake. Koma kukwaniritsidwa kwakukulu kuchitika mu nthawi yathu ino. Kodi kuchitika bwanji?
29 Mofanana ndi anthu akale a Mulungu, ifenso tazunguliridwa ndi mitundu ya anthu imene imationa kuti ndife osatetezeka ngati nkhosa imene ili yokhayokha. (Ezek. 38:10-13) Monga mmene tidzaonere m’Mutu 17 ndi 18 wa buku lino, anthu amenewa posachedwapa aukira mwankhaza anthu a Mulungu. Koma akadzachita zimenezi adzadziwa tanthauzo la mphamvu zenizeni. Mulungu akamadzawawononga pa nkhondo ya Aramagedo, iwo adzakakamizika kudziwa Yehova komanso kuzindikira kuti ndi woyenera kulamulira.—Chiv. 16:16; 19:17-21.
30 Koma mosiyana ndi anthu amenewa, ife Yehova adzatiteteza komanso kutidalitsa. Chifukwa chiyani? Chifukwa choti panopa tikusonyeza kuti timadziwa Yehova pomudalira, kumumvera ndi kulambira iye yekha.—Werengani Ezekieli 28:26.
a Mwachitsanzo, Afilisiti analetsa kuti pasapezeke aliyense wosula zitsulo mu Isiraeli. Aisiraeli ankayenera kupita kwa Afilisiti kuti akawanolere zipangizo zawo zolimira ndipo ankawalipiritsa ndalama zimene munthu ankalandira akagwira ntchito masiku ambiri.—1 Sam. 13:19-22.
b Zikuoneka kuti mzinda woyambirira wa Turo unamangidwa pamalo okwera amiyala amene anali m’mbali mwa nyanja pafupifupi makilomita 50 kumpoto kwa phiri la Karimeli. Patapita nthawi anamanga mbali ina ya mzindawu kumtunda. Dzina la mzindawu m’Chiheberi ndi Sur, kutanthauza “Thanthwe.”
c Yesaya, Yeremiya, Yoweli komanso Zekariya ananenanso maulosi okhudza Turo amene anakwaniritsidwa mwatsatanetsatane.—Yes. 23:1-8; Yer. 25:15, 22, 27; Yow. 3:4; Amosi 1:10; Zek. 9:3, 4.