BOKOSI 7A
Mitundu Imene Inazungulira Yerusalemu
cha m’ma 650-300 B.C.E.
TCHATI CHOSONYEZA NTHAWI (ZAKA ZONSE NDI ZA MU B.C.E.)
620: Ababulo anayamba kulamulira Yerusalemu
Nebukadinezara anachititsa kuti mfumu ya ku Yerusalemu ikhale pansi pa ulamuliro wake
617: Ababulo anatenga gulu loyamba la akapolo kuchokera ku Yerusalemu
Anatenga olamulira, asilikali amphamvu ndi amisiri n’kupita nawo ku Babulo
607: Ababulo anawononga Yerusalemu
Mzindawo ndi kachisi wake zinawotchedwa
Pambuyo pa 607: Mzinda wa Turo wakumtunda
Nebukadinezara anaukira mzinda wa Turo kwa zaka 13. Iye anagonjetsa mzinda wa Turo wakumtunda koma mzinda wa Turo wapachilumba anausiya
602: Aamoni ndi Amowabu
Nebukadinezara anaukira Aamoni ndi Amowabu
588: Ababulo anagonjetsa Aiguputo
M’chaka cha 37 cha ulamuliro wake, Nebukadinezara anaukira Aiguputo
332: Mzinda wa Turo wapachilumba
Gulu lankhondo la Agiriki limene ankalitsogolera ndi Alekizanda Wamkulu, linawononga mzinda wa Turo wapachilumba
332 kapena chakachi chisanafike: Filisitiya
Alekizanda anagonjetsa mzinda wa Gaza umene unali likulu la Afilisiti
Malo amene ali pa Mapu
GIRISI
NYANJA YAIKULU
(NYANJA YA MEDITERRANEAN)
TURO
Sidoni
Turo
Samariya
Yerusalemu
Gaza
FILISITIYA
IGUPUTO
BABULO
AMONI
MOWABU
EDOMU