Mfundo Zazikulu Zabaibulo Miyambo 1:1-31:31
Opani Yehova ndipo Mudzakhala Achimwemwe
“Chiyambi cha nzeru ndicho kuopa Yehova.”(9:10) Ndi motani nanga mmene ichi chasonyezedwera bwino lomwe mu Miyambol Bukhu iri la Baibulo. lotsirizidwa chifupifupi 716 B. C.E., limatithandiza kusonyeza nzeru, kugwiritslra ntchito chidziwitso molongosoka. Labadirani zonena za nzeru zimenezi ndipo mudzakhala achimwemwe.
Tcherani Khutu ku Nzeru
Werengani Miyambo 1:1-2:22. “Kuopa Yehova” chiri chofunika chenicheni cha chidziwtso. Ngati tilandira malangizo, sitidzatsagana ndi ochimwa m’kuchita zoipa. Kwa awo owopa Yehova, amawapatsa nzeru imene imawachinjiriza kwa ochita zoipa.
◆ 1:7—Kodi “kuopa Yehova“ nchiyani?
Kuli mantha, ulemu wakuya, ndi kuwopa kwenikweni kwa kusamukondweretsa chifukwa timayamikira ubwino ndi kukoma mtima kwake. “Kuopa Yehova“ kumatanthauza kuvomereza kuti ali Woweruza Wamkulu ndi Wamphamvuyonse, amene alindi kuyenera ndi mphamvu ya kubweretsa chilango kapena Imfa pa osamumvera iye. Chimatanthauzanso kutumikira Mulungu mokhulupirika, kudalira mwa iye kotheratu, ndi kudana ndi chimene chiri ohoipa m’maso mwake.—Masalmo 2:11; 115:11; Miyambo 8:13.
◆ 2:7—Kodi umphumphu nchiyani?-
Mawu a Chihebri kulinga ku umphumphu ali ndi tanthauzo limodzimodzi la chija chimene chiri “chathunthu“ kapena “chotsirizika.” Iwo kaŵirikaŵiri amasonyeza mkhalidwe wabwino ndi wolungama. “Awo oyenda mu umphumphu“ ali osagwedezeka mu kudzipereka kwawo kwaYehova. Kwa “olungama“ ali “chikopa“ chotetezera chifukwa amawonetsa nzeru yowona ndi kumamatira ku malamulo ake olungama.
Phunziro kwa Ife: Ngati tiopa Yehova, tidzalandira malangizo amene iye amapereka kupyolera mu Mawu ake ndi gulu lake. Kulephera kuchita tero kungatiike ife pamodzi ndi “opusa,“ ochimwa opanda umulungu. Chotero tiyeni tliandire malangizo ake achikondi.—Miyambo 1:7; Ahebri 12:6.
Kondani Nzeru
Werengani Miyambo 3:1-4:27. Kukhala ndi kawonedwe kabwino, “khulupirira Yehova ndi mtima wako wonse.” Chimwemwe chimasangalalidwa ndi awo okuza nzeru kwambiri. Njira yawo Iri monga kuunika komawala nthawi zonse, koma amafunikira kuchinjiriza mitima yawo.
◆ 4:18—Kodi ’mayendedwe a olungama’ awalitsa motani?
Kuunika kwa dzuwa kunkabe kuwala kuchokera ku mbanda kucha kufikira “usana woti mbe.” Mofananamo, kuunlka kwauzimu kunkabe kuwala kwa anthu a Yehova pamene nthawi ipita. Pamene tikuyandikira kwambiri ku zochitika, kumvetsetsa kwathu kwakugwira ntchito kwa zifuno za Yehova kumveketsedwa. Maulosi a umulungu amatitsegukira pamene mzimu woyera wa Mulungu uuniktra pa iwo, ndi pamene akukwaniritsidwa mu zochitika za dziko kapena mu zokumana nazo za anthu a Yehova. Chotero ’mayendedwe awo ankabe nawala.’
Phunziro kwa Ife: Kusonyeza nzeru yowona ndi kuchita mogwirizana ndi malamulo aumulungu kudzatichinjlriza ife kukutsatira njira zopusa zimene zlngatitsogolere ku imfa ya mwamsanga. Mwachitsanzo, awo onyalanyaza malamulo a Yehova oletsa chisembwere angatenge nthenda yopatsiridwa kupyolera mu kugonana chimene chingatanthauze Imfa yosayembekezereka. Chotero tiyeni tichite mogwirizana ndi zofuna za Mulungu, titatero nzeru idzakhala “mtengo wa moyo“ kwa Ife.—Miyambo 3:18.
Njira za Kusonyezera Nzeru
Werengani Miyambo 5:1-9:18. Kupewa chisembwere kuli kusonyeza nzeru ndipo kondwera ndi mkazi wokula naye.” Zinthu zisanu ndi ziwiri zonyansa kwa Yehova zasonyezedwa, ndipo machenjezo aperekedwa olimbana ndi kunyenga kwa mkazi wa chigololo. Nzeru yolimbikltsidwa iri “mmisiri” wa Mulungu. Ndipo “kuopa Yehova chiri chiyambi chanzeru.”
◆ 6:1-5—Kodi uphungu umenewu uli wosivana ndi mzlmu wa kuolowa manja?Mwambo umenewu siukuletsa kuolowa manja, ngakhale kuti ukupereka uphungu wa kulowerera mu zochitachita za malonda za ena, makamaka alendo. Aisrayeli anayenera kuthandiza mbale wawo amene ’anasauka chuma.’ (Levitiko 25:35-38) Koma ena analowerera mu ziwonetsero za malonda ndipo anapeza chirikizo la ndalama mwa kugonjetsa ena kupereka ’chikole’ kwa iwo, kulonjeza kulipira angongole awo ngati kunali kofunika. Ngati munthu analowerera mu kachitidwe koipa kotero, mwinamwake mwa kudzitukumula, kuweruza kwanzeru kunall kudzipulumutsa iyemwini kuchokera ku icho popanda kuchedwa.—Miyambo 11:16.
◆ 8:22-31—Kodi uku kuli kulongosola kokha kwa nzeru?
Ayi, popeza nzeru yakhalabe chikhalire monga mkhalidwe wa Mulungu wamuyaya. (Yobu 12:13). Pano, ngakhale kuli tero, panenedwa kuti nzeru “Inatulutsidwa ndipo Inali “pambali pa [Yehova] monga mmisiri”pa kulenga dziko lapansi. Kuzindikira nzeru ya umunthu monga Mwana wa Mulungu kumagwlrizana ndi nsonga yakuti “amene zolemera zonse za nzeru ndi chidziwitso zibisika mwa iye.”—Akolose 1:15, 16; 2:3.
Phunziro kwa Ife: Mwakutchula kwake “nsembe za mtendere“ ndi “zowinda,“ mkazi wa chisembwere wa Miyambo mutu 7 angakhale anali kulankhula mosalunjika kuti sanali wosowa mwauzimu. Nsembe za mtendere zinaphatikizapo nyama, Ufa, mafuta, ndi vinyo. (Levitiko 19:5, 6; 22:21; Numeri 15:8-10) Chotero anali kusonyeza kuti panali zambiri zakudya ndi kumwa ku nyumba yake, ndipo “mnyamata wopanda nzeru“ akakhala ndi nthawi yabwino kumeneko. ichi chiri cholingana ndi mmene munthu wosonknezeredwa molakwa angatsogozedwere ku chisembwere. Chiri chofunika chotani nanga kulabadira chenjezo iri ndi kupewa machimo otere olimbana ndi Mulungu!—Genesis 39:7-12.
Kusiyana Kodzutsa Maganizo Werengani
WerenganiMiyambo 10:1-15: 33. Miyambo ya Solomo iyamba kwakukulu ndi kusiyanitsa malamulo abwino. “Kuopa Yehova” kwagogomezeredwa.—10:27; 14:26, 27; 15:16, 33.
◆ 10:25—kodi nchifukwa ninji chisonyezero chapangidwa ku“kabvumvulu”?
Kusowa maziko mu maprinsipulo olungama, oipa ali ngati nyumba zosakhazikika zomwe zingagwe mu kabvumvulu wachiwawa. Koma olungama ali okhazikika chifukwa kuganiza kwawo molimba kwazikidwa pa maprinsipulo aumulungu. Monga chinthu chimene chiri ndi maziko abwino, iwo sagwedezeka pansi pa zitsenderezo.—Mateyu 7:24-27.
◆11:22—Kodi ndimotani mmene mkazi angakhalire ngati chipini m’mphuno ya nkhumba?
Chipini cha golide cha m’mphuno choikidwa pambali pa mphuno kapena pakati polekanitsa zimbuwa za mphuno chinasonyeza kuti wovalayo anali munthu wa mwambo. Koma Aisrayeli anawona nkhumba kukhala zopanda ukhondo ndipo zonyansa. Chotero mkazi wokongola koma wopanda nzeru ali ngati chipini chosayenera cha golide pa mphuno ya nkhumba
◆14:14—Kodi ndimotani mmene wosakhulupirira wakhutiritsidwira?
(Wopanda chikhulupiriro NW) m’mtima” amakhala wokwaniritsidwa ndi njira yake ya kuthupi. (Masalmo 144:11-15a) Kuchita chimene chiri cholungama m’maso mwa Mulungu kulibe chotulukapo chiri chonse kwa iye, ndipo saganizirapo ponena za kudzaziwerengera mlandu wake kwa Yehova (1 Petro 4:3-5) Koma “munthu wabwino“ amakana zizolowezi za osakhulupirira ndipo amakhutiritsidwa “ndi [zotulukapo za NW] njira zake.” lye amasunga zinthu zauzimu choyamba, ndi kumamatira ku malamulo a Mulungu, ali ndi chisangalalo chachikulu cha kutumikira iye, ndipo ali wokhutiritsidwa ndi madalitso a umulungu.—Masalmo 144:15b.
◆ 15:23—Kodi ndimotani mmene ’tingakondwere ndi yankho lam’kamwa mwathu’?
Ichi chingachitike ngati uphungu wathu walabadiridwa ndipo watulutsa zotulukapo zabwino. Koma kuti tithandize wina, tiyenera kumvetsera mosamalitsa, kupima nsonga zimene zinapangitsa vuto lake, ndi kuzika uphungu wathu pa Baibulo. “Ndipo ndi mawu a panthawi yake kodi Sali abwino?’
Phunziro kwa Ife: “Munthu wopusa” mwamsanga amayankha mwaukali pa kutukwanidwa kapena kunyazitsa, “mtsiku lomwelo.” Koma “wanzeru“—munthu wochenjera—amapemphera kaamba ka mzimu wa Mulungu kuti agwiritsire ntchito kudziletsa ndi kutsatira mawu ake. (Miyambo 12:16) Mwakuchita motero, tingapewe kupikisana kowonjezereka kumene kungakhale ndi zotulukapo za kuwononga mwa malingaliro kapena mwa kuthupi kwa ife eni kapena kwa ena.
Miyambo Imene Iri ndi Kulingana Nako
Werengani Miyambo 16:1-24:34. Zonena zanzeru zimenezi za Solomo zimapatsa chitsogozo makamaka kupyolera mmalingaliro olinganako. Chogogomezedwanso ndi “kuopa Yehova.”—16:6; 19:23; 22:4; 23:17; 24:21.
◆ 17:19—Kodi nchiyani chimene chiri cholakwika ndi khomo lotalika?
Awo amene sanapange zitseko zazifupi ku nyumba zawo ndi mabwalo awo anali pangozi ya kulowamo kwa okwera pa akavalo ndi kutenga zinthu zawo. Miyambo iyi ingakhale inasonyanso pakamwa monga khomo lotalikitsidwa ndi kulankhula kodzitamandira ndi kudzitukumula. Kulankhula kotero kumadzutsa ndewu ndipo potsirizira pake kumatsogolera ku tsoka.
◆ 19:17—Kodi nchifukwa ninji kuthandiza aumphaŵi kuli monga kubwereka Yehova?
Aumphawi ali a Mulungu, ndipo chimene timachita kwa iwo chimawonedwa monga chachitidwa kwa iye. (Miyambo 14:31) Ngati chikondi ndi kuolowa manja kutifulumiza ife kuwonetsa chiyanjo kwa aumphawi kapena kupatsa mphatso kwa osauka, osayembekezera chobwezera chirichonse kuchokera kwa iwo, Yehova amawona kupatsa koteroko monga zomubwereka iye zimene amabwezera ndi chiyanjo ndi madalitso.—Luka 14:12-14.
◆ 20:1—Kodi ndimotani mmene vinyo “aliri chiphwete”?
Vinyo angapangitse wina kulowerera mopambanitsa mu iyo kuchita mnjira ya chiphwete ndi yosokosa. Popeza kuti kumwa mopambanitsa kumabweretsa zotulukapo zoipa zoterozo, Akristu afunikira kuzipewa izo.—1 Timoteo 3:2, 3, 8; l Akorinto 6:9, 10; Miyambo 23:20, 21.
◆ 23:27—Kodi ndimotani mmene mkazi wadama aliri “dzenje” ndi [chitsimeNW]?
Monga mmene nyama zinali kugwidwira mu Ynaenje akuya’ okumbidwa ndi osaka nyama, choteronso awo olondoia mkazi wadama amagwidwa mu chisembwere. “Mkazi [wa chilendo” NW]amatanthauza mkazi wadama, mosakaikira chifukwa chakuti akazi adama ambiri mu Israyeli anali alendo. Kutunga madzi kuchokera “[mchitsime NW] chopapatiza“ kunaphatikizapo mavuto chifukwa zikho zotungira zadothi zinali kubenthuka m’mbali mosavuta. Mofananamo, awo amene ali ndi zochita ndi akazi adama angakumane ndi matsoka mwa malingaliro ndi mwakuthupi.—Miyambo 7:21-27.
Phunziro kwa Ife: “Mboni yonama” imasonyeza kusalemekeza Mulungu ndipo ikanafunikira kuphedwa pansi pa Chilamulo. Chotero akafunikira “kufa” pa manja a anthu kapena Yehova. (Miyambo 21:28; Deutronomo 5:20; 19:16-21; yerekezani ndi Machitidwe 5:1 -11. ) Koma ’munthu womvetsera’ mosamalitsa analankhula kokha pambuyo potsimikiza chimene anamva. Umboni wake unaima “kosatha,” osati pambuyo pake kukanidwa monga wabodza. Ndiponso, sanali kuphedwa mwalamulo monga mboni ya bodza. Awo ochitira umboni pa kumvetsera kwa chiweruzo pakati pa Mboni za Yehova afunikira kukhala atamvetsera mosamalitsa kotero kuti akhale okhoza kupereka chidziwitso cholongosoka, popeza umboni wosalongosoka kapena wabodza ungakhale wovulaza mwauzimu.
Zoyerekeza Zothandiza
Werengani 25:1-29:27. Miyambo ya Solomo yolembedwa ndi amuna a Mfumu Hezekiya imaphunzitsa kwakukulu mwa kuyerekezera. Pakati pa zinthu zina, chidaliro pa Yehova chimalimbikitsidwa.
26:6—Nchifukwa ninji kuyerekeza kwapangidwa ndi ’kudula mapazi ake’?
Munthu wodula mapazi ake angadzipundule iyemwini, monga mmene munthwolowetsa ntchito “wopusa“ achita kupundula kwa chiwawa ku zikondwerero za iyemwini. Ntchito yoikidwa mmanja mwa munthu wopusa idzalephera. Ndi kwanzeruchotani nanga[’kuwayesa amunaponena za kuyenera’NW]musanawayamikie, kaamba ka mathayo a mpingo!—1 Timoteo3:10.
◆ 27:17—Kodi ndi motani mmenenkhope ‘Imanoledwera’?
Monga mmene chitsulo chingagwiritsidwire ntchito kunola mpeni wopangidwa ndi chitsulo chimodzimodzicho, munthu mmodzi angapambane mu kunola kaimidwe ka chidziwitso ndi kauzimu ka wina. Ngatikugwiritsa mwala ndi kukumana ndianthu osatifuna kwatididikiza, kuyang’ana kwa kutonthoza ndi kusonkhezera mwa Malemba kwa mnzathu wa mu chikhuluplriro kungakhale kolimbitsa kwenikweni. Kawonekedwe kathu ka chisoni kamasinthira ku ubwino, ndipo timadzutsidwanso ndi chiyembekezo chatsopano cha kachitidwe katsopano.—Miyambo13:12.
◆ 28:5—Kodi nchiyanl chimene “zinthu zonse” zimaphatikizapo?
Awo ochita chimene chiri choipa ali akhungu mwauzimu. (Miyambo 4: 14-17; 2 Akorinto 4:4) Iwo “samvetsetsa chiweruzo,” kapena chimene chiri chabwino malinga ndi malamulo a Mulungu. Chotero sangaweruze milandu mwaubwino ndi kupangazosankha zabwino. Koma awo“omwe akufuna Yehova“ mwapemphero ndi kuphunzira Mawu ake“amvetsetsa zonse”zofunika kumuumiklra iye molandirika.—Aefeso 5: 15-17.
◆ 29:8—Kodi ndimotani mmene olankhula modzikuza “amatenthera mudzi”?
Anthu onyoza amene salemekeza maulamuliro amalankhula mwachipongwe. Mwakutero amasonkhezera moto wa kutsutsana ndi kukolezera kwambiri malawi a moto chakuti okhala m’mudzi onse amatenthedwa. Koma anthu anzeru “alezetsa mkwiyo,“ kulankhula mofatsa ndi mwanzeru, kumazima malawi aukali ndi kubweretsa mtendere.—Miyambo 15:1.
Phunziro kwa Ife: Ngati tiri onyada, kudzitamandirako kudzatulukapo mkuchepetsedwa kwathu. (Miyambo 29:23) Munthu wodzitamandira angathe kukhala wodzitukumula, ndipo ichi chingatsogoze ku kusalemekeza, kukhumudwitsa, ndi kuwonongeka. (Miyambo 11:2; 16:18; 18:12) Mulungu angawone ku icho kuti munthu wodzitukumula wachepetsedwa, kubweretsedwa pans) mnjira Ina, mwinamwake ku mlingo wa chiwonongeko. Munthu woteroyo amafuna ulemerero, koma anthu apeza njira zake kukhala zonyansa. Komabe, munthu “wofatsa mu mzimu (potsirizira pake] adzagwira ulemerero.”
‘Uthenga [Wolemera, NW]
Werengani Miyambo 30:1-31: 31. Uthenga [wolemera, NW] wa Aguri umavomereza kuti “mawu onse a Mulungu ali oyengeka.” Ndiponso zolembedwa ziri zinthu zabwino kwambiri kuzizindikira, ndi zina zotero. (30:1-33) “Uthenga [wolemera, NW] umene Lemuel! anaulandira kuchokera kwa mayi wake umachenjeza kuti kumwa zakumwa zoledzeretsa kungasinthe chiweruzo, kusonkhezera wina kuweruza molungama, ndi kulongosola mkazi wabwlno.-31:1-31.
◆ 30:15, 16—Kodi ndi iti yomwe iri nsonga ya zitsanzo zimenezi?
Zimachitira chitsanzo kusakwaniritsidwa kwa umbombo. Misundu imazikwaniritsa yokha ndi mwazi, monga mmenedi munthu wa umbombo nthawi zonse amafuna ndalama kapena mphamvu. Mofananamo, Manda sakwaniritsidwa, koma amakhala otseguka kulandira mikhole yambiri ya imfa. Mimba yosabala ‘imalirira’ ana (Genesis 30:1) Dziko louma limamwa madzi a mvula ndipo mwamsanga limawonekanso louma. Ndipo moto womwe watha zinthu zimene zaponyedwa pa iwo, umadzutsa malawi amene amayatsanso zina zomwe zingagwire moto mwamsanga zimene ziri pafupi. Ndi mmene ziriri ndi munthu waumbombo. Koma awo otsogozedwa ndi nzeru ya umulungu sakalipitsidwa kosathandi umbombo wotero.
◆ 31:6, 7—Nchifukwa ninji kupatsa vinyo kwa “owawa mtima”?
Chakumwa chaukali ndi vinyo zirizogonetsa. Chotero zikanapatsidwa kwa “[amene ali pafupi kutsirizika, NW],“ kapena kufa, kapena ’owawa m’mtima’ kuwapangitsa iwo kuiwala kupweteka kwawo ndi kuvutika. Mwambo wakale wa kupatsa achifwamba vinyo wosanganiza kuletsa kuwawa kwa kunyongedwa kungalongosole chifukwa chimene asirikali a Chiroma anapereka vinyoyo kwa Ye8u Kristu panthawi ya kumpachika lye anakana vinyoyo chifukwa anafuna kukhala nazo nzeru zake zonse panthawi ija ya kuyesa ndipo mwakutero kusunga umphumpnu kwa Mulungu.—Marko 15:22-24.
◆ 31:15—Kodi “adzakaziwo“ndani?
Atumiki achikazi a panyumba akutanthauzidwa pano. Analibe chifukwa cha kudandaulira pa chakudya kapena ntchito yopatsidwa. Mkazi wachangu anapatsa chakudya kwa a mnyumba yake ndipo anatsimikizira kuti akaziwa anapatsidwa china chake chakudya ndi ntchito yochita.
Phunziro kwa Ife: Monga opanda ungwiro, panthawi zina mopanda nzeru ’tingadzikweze,’ kupanga mphamvu za kudzitukumula. Ngati tichita ichi kapena kulankhula mwaukali, “tifunlkira kugwira pakamwa,“ kuleka kulankhulanso mawu ena amene angakalipitse yemwe tamulakwira. Monga mmene mkaka ufunikira kutakasidwa kuti upange mafuta oyengeka ndipo mphuno yotulutsa mwazi nthawi zambiri imatero chifukwa chakuipsyinja, mkangano umabuka pamene anthu alekerera mkwiyo. (Miyambo 30:32, 33) M’nkhani zotero, chiri chanzeru chotani nanga kukhala odekha ndi kuchinjiriza mavuto ena ochulukira!
Ndi mapindu otani nanga amene tingatenge mu bukhu la Miyambo! Tiyeni tikonde zonena izi za nzeru zimene zimadzetsa mantha okulira a Yehova. Kuwagwiritsira ntchito ndithudi kudzatipanga ife kukhala achimwemwe.