Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Pamene Mwana Wotayika Apezeka
PAMENE mwana wotayika, kapena wolowerera, m’fanizo la Yesu abwerera kunyumba ya atate wake, ndi kulandiridwa kotani kumene akulandira? Mvetserani pamene Yesu akulongosola:
“Koma pakudza iye kutali, atate wake anamuwona nagwidwa chifundo, nathamanga namkupatira pakhosi lake nampsyopsyonetsa.” Ndi atate wachifundo, wokoma mtima, wotani nanga yemwe moyenerera akuimira Atate wathu wa kumwamba, Yehova!
Mwachidziŵikire atatewo anamva za mkhalidwe wa chitaiko wa mwana wake. Komabe iye akumulandira mwanayo kunyumba popanda kudikira kaamba ka kulongosola kwa tsatanetsatane. Yesu alinso ndi mzimu wolandira woterowo, kuyambitsa kufikira ochimwa ndi osonkhetsa msonkho, omwe akuimiridwa m’fanizolo ndi mwana wolowerera.
Zowona, atate wozindikira wa m’fanizo la Yesu mosakaikira ali ndi lingaliro lina la kutembenuka mtima kwa mwana wake mwa kuwona nkhope yake ya chisoni, ya kugwa pansi pamene akubwerera. Koma chiyambi cha chikondi cha atatewo chipangitsa icho kukhala chopepuka kwa mwanayo kuwulula machimo ake, monga mmene Yesu akusimbira: “Ndipo mwanayo anati kwa iye, ‘Atate, ndinachimwira kumwamba ndi pamaso panu. Sindiyeneranso konse kutchulidwa mwana wanu. [Mundiyese ine ngati mmodzi wa antchito anu, NW].’”
Komabe, mawuwo anali asanatuluke nkomwe pakamwa pa mwanayo pamene atate wake akuchitapo kanthu, kulamulira akapolo ake: “‘Tulutsani! msanga mwinjiro, wokometsetsa, nimumveke, ndipo mpatseni mphete ku dzanja lake ndi nsapato ku mapazi ake. Ndipo idzani naye mwana wang’ombe wonenepa, mumuphe ndipo tidye tisekerere, chifukwa mwana wanga uyu anali wakufa ndipo akhalanso wamoyo; anali wotayika ndipo wapezedwa.’ Ndipo anayamba kusekera.”
Pa nthaŵiyo, “mwana wamkulu wa [atateyo] anali kumunda.” Onani ngati mungazindikire amene iye akuimira mwa kumvetsera ku yotsalira ya nkhaniyo. Yesu akunena za mwana wamkuluyo: “Ndipo pakubwera iye ndi kuyandikira kunyumba anamva kuyimba ndi kuvina. Ndipo anaitana mmodzi wa anyamata namfunsa zinthu izi nzotani. Ndipo uyu anati kwa iye, ‘M’ng’ono wako wafika, ndipo atate wako anapha mwana wa ng’ombe wonenepa, chifukwa anamulandira iye wamoyo.’ Koma anakwiya ndipo sanafuna kuloŵamo.
“Ndipo atate wake anatuluka namudandaulira. Koma anayankha nati kwa atate wake, ‘Onani ine ndinakhala kapolo wanu zaka zambiri zotere ndipo sindinalakwira lamulo lanu nthaŵi iriyonse, ndipo simunandipatsa ine kamodzi konse mwana wambuzi kuti ndisekere ndi abwenzi anga. Koma pamene anadza mwana wanu uyu wakutha zamoyo zanu ndi akazi achiwerewere, munaphera iye mwana wa ng’ombe wonenepa.’”
Ndani, mofanana ndi mwana wamkulu, wakhala wosuliza za chifundo ndi chisamaliro choperekedwa kwa ochimwa? Kodi si alembi ndi Afarisi? Popeza chiri chisulizo chawo cha Yesu chifukwa iye akulandira ochimwa chomwe chadzutsa fanizo limeneli, iwo mwachimvekere ayenera kukhala amene akuimiridwa ndi mwana wamkuluyo.
Yesu akumaliza nkhani yake ndi pembedzero la atatewo kwa mwana wake wamkulu: “Mwana wanga, iwe uli ndi ine nthaŵi zonse, ndipo zanga zonse ziri zako; koma kudayenera kuti tisangalale ndi kukondwerera, chifukwa m’ng’ono wako uyu anali wakufa ndipo ali ndi moyo, anatayika ndipo wapezeka.”
Yesu chotero akusiya chosamasuliridwa chimene mwana wamkuluyo potsirizira pake anachita. Ndithudi, pambuyo pake, pambuyo pa imfa ndi kuwuka kwa Yesu, “khamu lalikulu la ansembe linayamba kukhala lomvera ku chikhulupiriro,” mothekera kuphatikizapo ena a awa a gulu la “mwana wamkulu” kwa amene Yesu akulankhula pano.
Koma ndani mu nthaŵi zamakono amene akuimira ana aŵiri amenewo? Chiyenera kukhala awo omwe adziŵa mokwanira ponena za zifuno za Yehova kukhala ndi maziko kaamba ka kulowa kwawo mu unansi ndi iye. Mwana wamkulu amaimira ziwalo zina za “kagulu ka nkhosa,” kapena “mpingo wa obadwa oyamba olembedwa m’mwamba.” Awa anatengera mkhalidwe wofanana ndi uja wa mwana wamkulu. Iwo analibe chikhumbo cha kulandira gulu la pa dziko lapansi, “nkhosa zina,” omwe anawalingalira kukhala anali kuba chidziŵitso.
Mwana wolowerera, ku mbali ina, akuimira awo a anthu a Mulungu omwe achoka kukasangalala ndi zosangulutsa zomwe dziko likupereka. M’kupita kwa nthaŵi, ngakhale kuli tero, awa molapa amabwerera ndipo kachiŵirinso kukhala atumiki okangalika a Mulungu. Ndithudi, ndi wachikondi ndi wachifundo chotani nanga mmene Atate aliri kulinga kwa awo omwe amazindikira chifuno chawo cha kukhululukidwa ndi kubwerera kwa iye! Luka 15:20-32; Machitidwe 6:7; Luka 12:32; Ahebri 12:23; Yohane 10:16.
◆ Ndimotani mmene Yesu akutsanzirira chitsanzo cha tate wachifundo m’fanizo lake?
◆ Nkati komwe kali kawonedwe ka mwana wamkulu ka kulandiridwa kwa mbale wake, ndipo ndimotani mmene Afarisi akuchitira mofanana ndi mwana wamkuluyo?
◆ Ndi kugwiritsidwa ntchito kotani kumene fanizo la Yesu liri nako m’tsiku lathu?