Tsanzirani Chifundo cha Yehova
“Khalani inu achifundo monga Atate wanu ali wachifundo.”—LUKA 6:36.
1. Kodi Afarisi anaonetsa motani kuti analibe chifundo?
NGAKHALE kuti anthu analengedwa m’chifanizo cha Mulungu, nthaŵi zambiri iwo amalephera kutsanzira chifundo chake. (Genesis 1:27) Mwachitsanzo, tatengani Afarisi. Monga gulu, sanafune kukondwera pamene Yesu mwachifundo anachiritsa dzanja lopuwala la munthu wina pa Sabata. M’malo mwake, anakhala upo womchitira Yesu pofuna “kumuwononga.” (Mateyu 12:9-14) Nthaŵi ina, Yesu anachiritsa munthu wakhungu chibadwire. Apanso ‘ena mwa Afarisi’ sanakondwere ndi chifundo chimene Yesu anaonetsa. Koma anadandaula kuti: “Munthu uyu sachokera kwa Mulungu, chifukwa sasunga Sabata.”—Yohane 9:1-7, 16.
2, 3. Kodi Yesu anatanthauzanji ndi mawu akuti, “Yang’anirani mupewe chotupitsa mkate cha Afarisi”?
2 Kuuma mtima kwa Afarisi kunali kulakwira anthu ndi Mulungu. (Yohane 9:39-41) Pachifukwa chabwino, Yesu anachenjeza ophunzira ake kuti, “Yang’anirani mupewe chotupitsa mkate” cha gulu limeneli lamphamvu ndi azipembedzo ena, monga Asaduki. (Mateyu 16:6) Baibulo limagwiritsa ntchito chotupitsa mkate kuimira uchimo kapena chivundi. Chotero Yesu anali kunena kuti chiphunzitso cha “alembi ndi Asaduki” chikanavunditsa kulambira koyera. Motani? M’lingaliro lakuti chinaphunzitsa anthu kuona Chilamulo cha Mulungu kukhala malamulo awo okhwima ndi miyambo yawo, pamene ananyalanyaza “zolemera” zake, kuphatikizapo chifundo. (Mateyu 23:23) Kupembedza kumeneku kwamwambo kunapangitsa kulambira Mulungu kukhala mtolo wosapiririka.
3 M’mbali yachiŵiri ya fanizo lake la mwana wosakaza, Yesu anavumbula kulingalira koipa kwa atsogoleri achipembedzo achiyuda. M’fanizolo atate, yemwe akuimira Yehova, anali wofunitsitsa kukhululukira mwana wake wolapayo. Koma mbale wa mnyamatayo, amene anaimira “Afarisi ndi alembi,” anaganiza zosiyana kwambiri pankhaniyo.—Luka 15:2.
Mkwiyo wa Mbale Wake
4, 5. Kodi mbale wa mwana wosakaza anali ‘wotayika’ motani?
4 “Koma mwana wake wamkulu anali kumunda. Ndipo pakubwera iye ndi kuyandikira kunyumba, anamva kuimba ndi kuvina. Ndipo anaitana mmodzi wa anyamata, namfunsa, Zinthu izi nzotani? Ndipo uyu anati kwa iye, Mng’ono wako wafika; ndipo atate wako anapha mwana wa ng’ombe wonenepa, chifukwa anamlandira iye wamoyo. Koma anakwiya, ndipo sanafuna kuloŵamo.”—Luka 15:25-28.
5 Mwachionekere mwana wosakaza sindiye yekha amene anali ndi vuto m’fanizo la Yesu ayi. “Ana onse aŵiri ofotokozedwawo ngotayika,” limatero buku lina la maumboni, “winayo chifukwa cha kusalungama kumene kumuwonongera mbiri, winayo chifukwa cha kudzilungamitsa kumene kumchititsa khungu.” Onani kuti mbale wa mwana wosakazayo sanangokana kukondwera nawo komanso “anakwiya.” Tsinde lachigiriki la liwulo “mkwiyo” silimanena kwenikweni za mkwiyo woti nkulalata nawo, koma kuŵaŵidwa mtima kopitiriza. Mwachionekere, mbale wa mwana wosakaza anasunga chakukhosi, choncho anaganiza kuti sikunali bwino kukondwerera kubwera kwa munthu amene sanayenera kuchoka panyumba.
6. Kodi mbale wa mwana wosakaza amaimira ndani, ndipo chifukwa chiyani?
6 Mbale wa mwana wosakaza amaimira aja omwe anaipidwa ndi Yesu pamene anaonetsa chifundo ndi chisamaliro kwa ochimwa. Anthu odzilungamitsa ameneŵa sanakhudzike ndi chifundo cha Yesu; ndipo sanaonetse chimwemwe chimene chimakhala kumwamba pamene wochimwa akhululukidwa. Koma chifundo cha Yesu chinaputa mkwiyo wawo, ndipo anayamba “kuganizira zoipa” m’mitima yawo. (Mateyu 9:2-4) Nthaŵi ina mkwiyo wa Afarisi ena unakula moti analephera kuupirira mpaka ataitana munthu amene Yesu anachiritsa ndiyeno “anamtaya kunja” kwa sunagoge—mwachionekere kumchotsa! (Yohane 9:22, 34) Mofanana ndi mbale wa mwana wosakaza uja, amene “sanafuna kuloŵamo,” atsogoleri achipembedzo achiyuda anazemba pamene anali ndi mpata ‘wokondwa nawo iwo akukondwera.’ (Aroma 12:15) Yesu anavumbulanso kulingalira kwawo koipa pamene anapitiriza fanizo lake.
Kulingalira Kolakwika
7, 8. (a) Kodi mbale wa mwana wosakaza analiphonya motani tanthauzo la umwana? (b) Kodi mwana wamkuluyo anasiyana motani ndi atate wake?
7 “Ndipo atate wake anatuluka namdandaulira. Koma anayankha nati kwa atate wake, Onani, ine ndinakhala kapolo wanu zaka zambiri zotere, ndipo sindinalakwira lamulo lanu nthaŵi iliyonse; ndipo simunandipatsa ine kamodzi konse mwana wa mbuzi, kuti ndisekere ndi abwenzi anga. Koma pamene anadza mwana wanu uyu, wakutha zamoyo zanu ndi akazi achiwerewere, munamphera iye mwana wa ng’ombe wonenepa.”—Luka 15:28-30.
8 Mwa mawu ameneŵa, mbale wa mwana wosakaza anaonetsa poyera kuti anaphonya tanthauzo lenileni la umwana. Anatumikira atate wake monga momwe wantchito amatumikirira womlemba ntchito. Nzimenedi anauza atate wake kuti: “Ine ndinakhala kapolo wanu.” Inde, mwana wamkulu ameneyu sanachokepo panyumba kapena kulakwira lamulo la atate wake. Koma kodi ndi chikondi chomwe chinamsonkhezera kumvera? Kodi kutumikira atate wake kunamsangalatsadi, kapena kodi anafika poti nkudzikhulupirira kwambiri, namaganiza kuti anali mwana wabwino chabe chifukwa chakuti anachita ntchito yake “kumunda”? Ngati iyeyo analidi mwana wodzipereka, bwanji sanaonetse maganizo a atate wake? Atakhala ndi mpata woonetsa chifundo kwa mbale wake, bwanji sanamve chisoni mumtima mwake?—Yerekezerani ndi Salmo 50:20-22.
9. Fotokozani kufanana kwa atsogoleri achipembedzo achiyuda ndi mwana wamkulu uja.
9 Atsogoleri achipembedzo achiyuda anafanana ndi mwana wamkulu ameneyu. Ankakhulupirira kuti anali okhulupirika kwa Mulungu chifukwa chakuti ankatsata kwambiri mpambo wa malamulo. Inde, kumvera nkofunika kwambiri. (1 Samueli 15:22) Koma kugogomezera kwawo ntchito mopambanitsa kunasandutsa kulambira Mulungu kukhala chizoloŵezi wamba, kungoonetsera kudzipereka popanda uzimu weniweni. Iwo anasumika maganizo awo pamiyambo. Mtima wawo sunali wachikondi. Ee, anaona anthu wamba monga fumbi lakumapazi kwawo, nafika pakutcha anthuwo mwachipongwe kuti “otembereredwa.” (Yohane 7:49) Kunena zoona, kodi Mulungu akanakondwera nazo motani ntchito za atsogoleri ngati amenewo pamene mitima yawo inali kutali ndi iye?—Mateyu 15:7, 8.
10. (a) Kodi nchifukwa chiyani mawu akuti “ndifuna chifundo, si nsembe ayi” anali uphungu woyenera? (b) Kodi kupanda chifundo ili nkhani yaikulu motani?
10 Yesu anauza Afarisi kuti “mukani muphunzire nchiyani ichi, ndifuna chifundo, si nsembe ayi.” (Mateyu 9:13; Hoseya 6:6) Iwo sanazindikire kuti zofunika nziti, pakuti popanda chifundo nsembe zawo zikakhala zopanda pake. Nkhani imeneyi njaikuludi, pakuti Baibulo limatero kuti “opanda chifundo” amaŵerengeredwa limodzi ndi aja amene Mulungu awayesa kuti “ayenera imfa.” (Aroma 1:31, 32) Choncho nzosadabwitsa kuti Yesu anatero kuti monga gulu atsogoleri achipembedzowo adzawonongedwa kotheratu. Mwachionekere, kupanda kwawo chifundo kunathandizira kwambiri kuti alandire chiweruzo chimenechi. (Mateyu 23:33) Koma mwina ena mwa gulu limeneli akanathandizidwa. Pomaliza fanizo lake, Yesu anayesetsa kusintha kulingalira kwa Ayuda ngati amenewo mwa mawu a atateyo kwa mwana wake wamkulu. Tione mmene anachitira zimenezo.
Chifundo cha Atate
11, 12. Kodi atateyo m’fanizo la Yesu akuyesa motani kumthandiza kulingalira mwana wake wamkulu, ndipo pogwiritsa ntchito mawu akuti “mng’ono wako” angakhale akutanthauza chiyani?
11 “Koma iye ananena naye, Mwana wanga, iwe uli ndine nthaŵi zonse, ndipo zanga zonse zili zako. Koma kudayenera kuti tisangalale ndi kukondwerera: chifukwa mng’ono wako uyu anali wakufa ndipo ali ndi moyo; anatayika, ndipo wapezeka.”—Luka 15:31, 32.
12 Onani kuti atateyo anagwiritsa ntchito mawu akuti “mng’ono wako.” Chifukwa? Chabwino, kumbukirani kuti poyamba, pamene anali kulankhula ndi atate wake, mnyamata wamkuluyu anatcha mwana wosakaza uja “mwana wanu”—osati “mng’ono wanga.” Zikukhala ngati sanauzindikire ubale umene unalipo pakati pa iye ndi mng’ono wakeyo. Tsopano, tingati atateyo akumuuza mnyamata wamkuluyo kuti: ‘Ameneyutu si mwana wanga chabe. Ndi mbale wako, mbale wako weniweni. Uyenera kukondwera kuti iye wabwera!’ Mfundo ya Yesu iyenera kuti inamveka bwino kwa atsogoleri achiyudawo. Anthu ochimwa omwe iwo ananyoza analidi “abale” awo. Inde, “kulibe wolungama pansi pano amene achita zabwino osachimwa.” (Mlaliki 7:20) Chifukwa chake, Ayuda omvekawo anayenera kukondwera pamene ochimwa analapa.
13. Kodi kutha mwadzidzidzi kwa fanizo la Yesu kukutisiya ndi funso lotani lalikulu?
13 Atateyo atamdandaulira, fanizolo likutha mwadzidzidzi. Zikukhala ngati Yesu akupempha omvetsera ake kupeza mapeto a nthanoyo paokha. Kaya mwana wamkuluyo anayankha zotani, womvetsera aliyense anayenera kuyankha funso lakuti, ‘Kodi inu mudzakhala nacho chimwemwe chimene amakhala nacho kumwamba akalapa munthu wochimwa?’ Akristunso ali ndi mpata lero woyankha funso lomwelo. Motani?
Kutsanzira Chifundo cha Mulungu Lero
14. (a) Kodi tingagwiritsire ntchito motani uphungu wa Paulo wa pa Aefeso 5:1 pankhani yokhudzana ndi chifundo? (b) Kodi tiyenera kupewa lingaliro liti lolakwika ponena za chifundo cha Mulungu?
14 Paulo analangiza Aefeso kuti: “Khalani akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa.” (Aefeso 5:1) Ndiye pokhala Akristu, tiyenera kuzindikira chifundo cha Mulungu, kuchikhomereza zolimba m’mitima yathu, kenako kuonetsa khalidwe limeneli kwa ena. Komabe, pafunika kusamala. Chifundo cha Mulungu chisaonedwe monga chifukwa chochepetsera uchimo. Mwachitsanzo, ena mtima uli phe angaganize kuti, ‘Nditalakwa, ndizingopemphera kwa Mulungu kuti andikhululukire, ndipo adzandimvera chifundo.’ Maganizo ngati amenewo akufanana ndi zimene wolemba Baibulo Yuda anatcha “kusandutsa chisomo cha Mulungu wathu chikhale chilakolako chonyansa.” (Yuda 4) Ngakhale kuti Yehova ngwachifundo, ‘sadzamasula wopalamula’ pochita ndi anthu ochimwa amene salapa.—Eksodo 34:7; yerekezerani ndi Yoswa 24:19; 1 Yohane 5:16.
15. (a) Nchifukwa chiyani akulu makamaka afunika kusamala pankhani ya chifundo? (b) Pamene salekerera kuchimwa dala, kodi akulu ayenera kuyesetsa kutani, ndipo nchifukwa chiyani?
15 Komanso, tifunikira kusamala kuti tisapambanitsenso—kukhala ndi chizoloŵezi chowaumitsira zinthu kapena kukonda kuwaweruza aja amene amaonetsa kulapa kwenikweni ndi chisoni chaumulungu pamachimo awo. (2 Akorinto 7:11) Popeza akulu aikizidwa udindo wosamalira nkhosa za Yehova, afunika kusamala pankhaniyi, makamaka posamalira milandu yachiweruzo. Mpingo wachikristu uyenera kukhala woyera, ndipo nkoyenera mwa Malemba ‘kuchotsa woipayo.’ (1 Akorinto 5:11-13) Komanso, kuli bwino kuonetsa chifundo pamene maziko ake oonekeratu alipo. Chotero pamene akulu salekerera kuchimwa dala, amayesetsa kutsata njira yachikondi ndi yachifundo, malingana ndi chilungamo. Nthaŵi zonse amakumbukira pulinsipulo la Baibulo lakuti: “Chiweruziro chilibe chifundo kwa iye amene sanachita chifundo; chifundo chidzitamandira kutsutsana nacho chiweruziro.”—Yakobo 2:13; Miyambo 19:17; Mateyu 5:7.
16. (a) Mwa kugwiritsa ntchito Baibulo, sonyezani mmene Yehova amafunira kwambiri kuti olakwa abwerere kwa iye. (b) Kodi ifenso tingaonetse motani kuti timalandira olakwa amene alapa akabwerera?
16 Fanizo la mwana wosakaza limasonyeza bwino kuti Yehova amafuna kuti olakwa abwerere kwa iye. Inde, amawaitanabe kufikira iwo ataonetsa kuti ali osalapa. (Ezekieli 33:11; Malaki 3:7; Aroma 2:4, 5; 2 Petro 3:9) Mofanana ndi atate wa mwana wosakaza, Yehova amaŵerengera aja amene abwerera, kuwalandira monga ana a m’nyumba ndithu. Kodi mukutsanzira Yehova pankhani iyi? Pamene wokhulupirira mnzanu, amene kwanthaŵi yaitali anali wochotsedwa, wabwezeretsedwa, kodi mumatani? Tikudziŵa kuti kumakhala “chimwemwe Kumwamba.” (Luka 15:7) Koma kodi pamakhala chimwemwe padziko lapansi, mumpingo wanu, ndi mumtima mwanu? Kapena, monga mwana wamkulu m’fanizo lija, kodi pamakhala kuipidwa, monga ngati kuti sayenera kulandiridwa uja amene poyamba sanayenera kusiya gulu la Mulungu?
17. (a) Kodi ku Korinto wa m’zaka za zana loyamba kunachitika zotani, ndipo kodi Paulo anawauza kuti aisamalire motani nkhaniyo mumpingo? (b) Kodi nchifukwa chiyani uphungu wa Paulo unali woyenera, ndipo tingaugwiritse ntchito motani lero? (Onaninso bokosi lili kulamanja.)
17 Chimene chingatithandize pankhaniyi ndi kulingalira zimene zinachitika pafupifupi m’chaka cha 55 C.E. ku Korinto. Kumeneko mwamuna wina amene anachotsedwa mumpingo pomaliza pake anayeretsa moyo wake. Kodi abale anayenera kuchita chiyani? Kodi anayenera kukayikira za kulapa kwake ndi kupitiriza kumpeŵa. Kusiyana ndi zimenezo, Paulo analimbikitsa Akorinto kuti: “Mumkhululukire ndi kumtonthoza, kuti wotereyo angamizidwe ndi chisoni chochulukacho. Chifukwa chake ndikupemphani inu kuti mumtsimikizire ameneyo chikondi chanu.” (2 Akorinto 2:7, 8) Nthaŵi zambiri, munthu amene walapa atachimwa amachita manyazi ndipo amathedwa nzeru. Chotero munthu wotereyu amafunikira kuona kuti okhulupirira anzake ngakhalenso Yehova akumkonda. (Yeremiya 31:3; Aroma 1:12) Zimenezi nzofunika kwambiri. Chifukwa?
18, 19. (a) Kodi Akorinto poyamba anaonetsa motani kuti anapambanitsa kulekerera? (b) Kodi zikanatheka motani kuti kupanda chifundo kwa Akorinto kukanachititsa ‘Satana kuwachenjerera’?
18 Pouza Akorinto kuti amkhululukire, chifukwa chimodzi chimene Paulo anapereka nchakuti “asatichenjerere Satana; pakuti sitikhala osadziŵa machenjerero ake.” (2 Akorinto 2:11) Anatanthauzanji? Chabwino, poyamba Paulo anadzudzula mpingo wa Akorinto chifukwa chopambanitsa kulekerera. Iwo analola mwamuna ameneyu kuchitabe tchimo lake popanda kumlanga. Pakutero, mpingo—makamaka akulu—anakondweretsa Satana, pakuti iye akanafuna kuti mpingo ukhale ndi mbiri yoipa.—1 Akorinto 5:1-5.
19 Ngati iwo pambuyo pake akanapambanitsa nkukana kumkhululukira munthu wolapayo, ndiye kuti Satana akanakhala akuwachenjereranso. M’njira yotani? M’njira yakuti iye akanadyerera kuumitsa kwawo zinthu ndi kupanda kwawo chifundo. Ngati munthu wochimwa uja amene analapa ‘akanamizidwa ndi chisoni chochulukacho’—kapena malinga ndi Today’s English Version, ‘akanachita chisoni kwambiri moti nkulekeratu’—akuluwo akanakhala ndi mlandu waukulu chotani nanga kwa Yehova! (Yerekezerani ndi Ezekieli 34:6; Yakobo 3:1) Yesu atachenjeza otsatira ake za kusakhumudwitsa “aang’ono awa,” anali ndi chifukwa chabwino chonenera kuti: ‘Kadzichenjerani nokha; akachimwa mbale wako umdzudzule; akalapa, umkhululukire.’a—Luka 17:1-4.
20. Kodi kumakhala motani chimwemwe kumwamba ndiponso padziko lapansi wochimwa akalapa?
20 Anthu zikwizikwi amene amayambiranso kulambira koyera chaka chilichonse amathokoza Yehova kaamba ka chifundo chimene wawachitira. “Sindikukumbukira nthaŵi ina iliyonse pamoyo wanga imene inandisangalatsa kwambiri kusiyapo imeneyi,” anatero mlongo wina wachikristu atabwezeretsedwa. Inde, chimwemwe chake nchimenenso angelo ali nacho. Ifenso tigwirizane nawo pa ‘chimwemwe chimene amakhala nacho Kumwamba’ munthu wochimwa akalapa. (Luka 15:7) Tikatero, tidzatsanzira chifundo cha Yehova.
[Mawu a M’munsi]
a Ngakhale kuti zikukhala ngati wolakwayo ku Korinto anabwezeretsedwa patapita nthaŵi yaifupi, zimenezi zisatengedwe monga njira yotsatira pamilandu yonse ya kuchotsa. Mlandu uliwonse ngwosiyana. Anthu ena olakwa amayamba kuonetsa kulapa koona mwamsanga atachotsedwa. Ena zimawatengera nthaŵi yaitali kuti aonetse mkhalidwe umenewo. Komabe, m’milandu yonse, aja amene amabwezeretsedwa ayenera choyamba kuonetsa umboni wakuti ali ndi chisoni chaumulungu ndipo, ngati kutheka, aonetse ntchito zoyenera kulapa.—Machitidwe 26:20; 2 Akorinto 7:11.
Kubwereza
◻ Kodi mbale wa mwana wosakaza anafanana motani ndi atsogoleri achipembedzo achiyuda?
◻ Kodi mbale wa mwana wosakaza analiphonya motani tanthauzo la umwana?
◻ Polingalira za chifundo cha Mulungu, kodi tiyenera kupeŵa kusapambanitsa pambali ziŵiri ziti?
◻ Kodi tingachitsanzire motani chifundo cha Mulungu lero?
[Bokosi patsamba 17]
“MUMTSIMIKIZIRE AMENEYO CHIKONDI CHANU”
Za munthu wolakwa amene anachotsedwa kenako nkuonetsa kulapa, Paulo anauza mpingo wa ku Korinto kuti: “Ndikupemphani inu kuti mumtsimikizire ameneyo chikondi chanu.” (2 Akorinto 2:8) Liwu lachigiriki lotembenuzidwa kuti “mumtsimikizire” ndi liwu logwiritsidwa ntchito pa zamalamulo ndipo limatanthauza “kupereka umboni wotsimikiza.” Inde, anthu olapa amene abwezeretsedwa afunikira kuona kuti akukondedwa ndi kuti alandiridwanso mumpingo.
Komabe, tikumbukire kuti ambiri mumpingo sakudziŵa zimene zinachotsetsa munthuyo kapena zimene zachititsa kuti abwezeretsedwe. Ndiponso, pangakhale ena amene anakhudzidwa mtima kwambiri kapena kukhumudwa—mwina kwanthaŵi yaitali—chifukwa cha tchimo la munthu wolapayo. Chifukwa chozindikira zinthu ngati zimenezo, tidzapeŵa mawu akuti tamlandira polengeza kubwezeretsedwa kwake. Tidzasiyira nkhani imeneyo kwa munthu aliyense payekha kuti adzilankhulire yekha pokambitsirana naye wochotsedwayo.
Zimalimbitsa chikhulupiriro chotani nanga pamene aja obwezeretsedwa azindikira kuti alandiridwanso kukhala mumpingo wachikristu! Titha kuwalimbitsa anthu amenewo olapa mwa kulankhula nawo ndi kuyanjana nawo pa Nyumba ya Ufumu, muutumiki, ndi panthaŵi zina zoyenera. Mwa kuwatsimikizira mwanjira imeneyi, kapena kupereka umboni wotsimikiza chikondi chathu pa okondedwa ameneŵa, sitikhala tikuchepetsa kukula kwa machimo omwe anachita. Koma timasangalala limodzi ndi makamu akumwamba kuti iwo asiya njira yawo yauchimo ndi kubwerera kwa Yehova.—Luka 15:7.
[Chithunzi patsamba 15]
Mwana wamkulu anakana kukondwera mbale wake atabwerera