Moyo ndi Uminisitala za Yesu
Chiyembekezo cha Chiwukiriro
YESU pomalizira akufika kumalire a Betaniya, mudzi wokhala chifupifupi makilomita atatu kuchokera ku Yerusalemu. Chakhala kokha masiku oŵerengeka chiyambire imfa ndi kuikidwa kwa Lazaro. Alongo ake Mariya ndi Marita akali kulirabe, ndipo ambiri abwera kunyumba yawo kudzawatonthoza.
Pamene akulira, winawake akudziŵitsa Marita kuti Yesu ali m’njira. Chotero iye akunyamuka ndi kufulumira kukakumana naye, mwachiwonekere popanda kuwuza mbale wake. Akubwera kwa Yesu, Marita akubwereza chimene iye ndi mbale wake ayenera kukhala atachinena nthaŵi zambiri mkati mwa masiku anayi apita: “Mukadakhala kuno mlongo wanga sakadafa.”
Marita, ngakhale kuli tero, akusonyeza chiyembekezo, akumasonyeza kuti Yesu angachitebe chinachake kaamba ka mlongo wake. “Ndidziŵa kuti zinthu zirizonse mukapempha Mulungu, adzakupatsani Mulungu,” iye akutero.
“Mlonga wako adzawuka,” Yesu akulonjeza.
Marita akumvetsetsa Yesu kukhala akulankhula za chiwukiriro cha pa dziko lapansi chamtsogolo, ku chimene Abrahamu ndi atumiki a Mulungu ena anayang’ana kutsogolo. Chotero iye akuyankha kuti: “Ndidziŵa kuti adzawuka m’kuwuka tsiku lomaliza.”
Ngakhale kuli tero, Yesu akupereka chiyembekezo kaamba ka chitonthozo cha mwamsanga, akumayankha kuti: “Ine ndine kuwuka ndi moyo.” Iye akumbutsa Marita kuti Mulungu wampatsa mphamvu pa imfa, akumanena kuti: “Wokhulupirira Ine, angakhale amwalira, adzakhala ndi moyo; ndipo yense wakukhala ndi moyo, nakhulupirira Ine, sadzamwalira nthaŵi yonse.”
Yesu sakulingalira kwa Marita kuti okhulupirika okhala ndi moyo nthaŵi imeneyo sadzafa konse. Ayi, koma nsonga imene iye akupanga iri yakuti kusonyeza chikhulupiriro mwa iye kungatsogolere ku moyo wosatha. Moyo woterowo udzasangalalidwa ndi anthu ochuluka koposa monga chotulukapo cha kuwukitsidwa kwawo pa tsiku lomaliza. Koma ena omwe ali okhulupirika adzapulumuka mapeto a dongosolo iri la kachitidwe ka zinthu pa dziko lapansi, ndipo kaamba ka amenewa mawu a Yesu adzakhala owona m’lingaliro lenileni. Iwo sadzafa konse! Pambuyo pa ndemanga yodabwitsa imeneyi, Yesu akufunsa Marita kuti, “Kodi ukhulupirira ichi?”
“Inde Ambuye,” iye akuyankha tero. “Ndakhulupirira ine kuti Inu ndinu Kristu, Mwana wa Mulungu, Wakudza m’dziko lapansi.”
Marita kenaka akufulumira kubwerera kukadziŵitsa mbale wake, kumuwuza iye mwamseri: “Wafika Mphunzitsi, akuitana iwe.” Mwamsanga Mariya achoka panyumba. Pamene ena amuwopa iye ali nkupita, akutsatira, akulingalira kuti iye akupita kumanda a chikumbukiro.
Akubwera kwa Yesu, Mariya akugwa pansi pa mapazi ake ndi kulira. “Ambuye, mukadakhala kuno Inu, mlongo wanga sakadamwalira,” iye akutero. Yesu akukhudzidwa mwakuya pamene akuwona kuti Mariya ndi makamu a anthu omtsatira iye akulira. “Mwamuika iye kuti?” iye akufunsa tero.
“Ambuye, tiyeni, mukawone,” iwo akuyankha.
Yesu nayenso atulutsa misozi, kuchititsa Ayuda kunena kuti: “Tawonani, anamkondadi!”
Ena akukumbukira kuti Yesu, mkati mwa Phwando la Misasa miyezi ingapo pasadakhale, anachiritsa mwamuna wachichepere wobadwa wakhungu, ndipo iwo akufunsa kuti: “Kodi uyu wotsegulira maso wosawona uja, sanakhoza kodi kuchita kuti sakadafa ameneyonso?” Yohane 5:21; 6:40; 9:1-7; 11:17-37.
◆ Kodi ndi liti pamene Yesu pomalizira akufika pafupi ndi Betaniya, ndipo kodi mkhalidwe uli wotani kumeneko?
◆ Kodi ndi maziko otani amene Marita ali nawo kaamba ka kukhulupirira m’chiwukiriro?
◆ Kodi Yesu akuyambukiridwa motani ndi imfa ya Lazaro?