Maphunziro Kuchokera ku Malemba: Mika 1:1–7:20
Chilungamo cha Yehova ndi Dzina Zikwezedwa
MNENERI Mika anakhalako mu zana lachisanu ndi chitatu B.C.E., nthaŵi ya kulambira mafano ndi kupanda chilungamo mu Israyeli ndi Yuda. Mikhalidwe pa nthaŵiyo inafanana kotheratu ndi iyo yomwe iripo pa nthaŵi ino kotero kuti mauthenga ndi machenjezo a Mika ali oyenerera ku nthaŵi yathu. Ndipo mbiri yabwino imene iye anaiperekanso imatipatsa ife chiyembekezo chenicheni m’dziko lolamulidwa ndi Satana.—1 Yohane 5:19.
Uthenga wa Mika uli mwinamwake wofupikitsidwa bwino kwambiri m’malongosoledwe atatu otsatirawa: “Tsoka iwo . . . okonza choipa.” “Ndipo Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako?” “Ife tidzayenda m’dzina la Yehova Mulungu wathu . . . kwamuyaya.”—Mika 2:1; 6:8; 4:5.
Kulambira Mafano Kutsutsidwa
Yehova salekerera ochita choipa mopanda mapeto. Kulambira mafano ndi kuwukira ziri zofala mu Israyeli ndi Yuda. Chotero, Yehova akutumikira monga mboni motsutsana nawo. Mafano awo adzaphwanyidwa. Olambira mafanowo adzakhala ‘adazi ngati chiwombankhanga’ ndipo adzavutika ndi kutengedwa ndende.—1:1-16.
Kwa okhulupirika, Yehova amatsimikizira kukhala Mulungu wa chiyembekezo. Olamulira okonzekera chiwembu akutsutsidwa monga mbala ndi olanda. Tsoka lidzawakantha iwo. Komabe lonjezo la kubwezeretsedwa likupangidwa kwa “otsalira a Israyeli.” “Mu umodzi ndidzawaika iwo ngati zoŵeta m’khola,” akutero Yehova.—2:1-13, NW.
Yehova amayembekezera chilungamo kuchitidwa ndi awo okhala ndi thayo pakati pa anthu ake. Kwa atsogoleri oipsya a Israyeli, chikunenedwa kuti: “Simuyenera kodi kudziŵa [chilungamo,NW]? Inu amene mudana nacho chokoma ndi kukondana nacho choipa; inu akumyula khungu lawo la pathupi pawo, ndi mnofu wawo pa mafupa awo.” Mika, “ndi mzimu wa Yehova, ndi [chilungamo, NW] ndi chamuna,” akulengeza ziweruzo za Mulungu motsutsana nawo. Atsogoleri opanda chilungamowo, iye akutero, amaweruza kaamba ka chiphuphu, ansembe amalangiza kaamba ka malipiro, ndipo aneneri amalosera chifukwa cha ndalama. Chotero, Yerusalemu “adzasanduka miunda.”—3:1-12.
Uthenga wa Chiyembekezo
Kulambira kowona kudzachitidwa pa dziko lonse lapansi. Mika akulosera kuti “m’masiku otsiriza,” anthu a mitundu yambiri adzalangizidwa m’njira za Yehova. Mulungu adzapereka chiweruzo, ndipo nkhondo sidzakhalaponso. Alambiri owona ‘adzayenda m’dzina la Yehova Mulungu wawo kwamuyaya.’ Mosasamala kanthu za chilango ndi kuwawa, anthu ake adzapulumutsidwa kuchoka mu dzanja la adani awo.—4:1-13.
Tingakhale ndi chidaliro mwa Wopulumutsa wolonjezedwa ndi Mulungu. wolamulira wa ku Betelehemu adzaŵeta mu mphamvu ya Yehova. “Chipulumutso kuchokera kwa Asuri” chikunenedweratu. Otsalira a alambiri owona adzakhala ngati mame opatsa mpumulo ndi mvula ya mvumbi, ndipo mitundu yonse ya chipembedzo chonyenga ndi ya uchiwanda idzazulidwa.—5:1-15.
Chilungamo cha Yehova Chidzalakika
Yehova amayembekezera anthu ake kugwirizana ndi miyezo yake yolungama ndi yowongoka. Nchiyani chomwe iye wachita kuyenerera kulambira kopanda pake? Iye wachita zinthu zabwino kaamba ka anthu ake. ‘Ndipo Yehova afunanji nawo koma kuti achite cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wawo?’ Ngati iwo apitiriza mu chiwawa chawo choipa ndi kudyerera, iwo angayembekezere kokha chiweruzo chake chowopsya.—6:1-16.
Tiyenera kukhulupirira m’chilungamo ndi chifundo cha Yehova. Ngakhale ziwalo za banja zidzakhala adani. Koma Mika akunena kuti: “Ndidzalindirira Mulungu wa chipulumutso changa; Mulungu wanga adzandimvera.” Mneneriyo akukhulupirira m’chilungamo cha Yehova, akumadziŵa kuti Mulungu “sadzasunga mkwiyo wake ku nthaŵi yonse, popeza akondwera nacho chifundo.”—7:1-20.
Maphunziro kaamba ka lerolino: Yehova amayembekezera anthu ake kusonyeza chilungamo. M’chilozero ku machitachita a zamalonda, m’chenicheni Mkristu ayenera kudzifunsa iyemwini: “Kodi ndikhoza kuyera ndi miyeso yoipa, ndi thumba la miyala yonyenga?” (6:11) M’masiku otsiriza ano, anthu onse a Yehova ayenera kuthandizira ku umodzi wa gulu lake la padziko lapansi ndi kulandira malangizo m’njira zake za mtendere. Tiyenera kuchita chirichonse chothekera kukweza dzina la Yehova ndi kupititsa patsogolo kulambira kowona.—2:12; 4:1-4.
[Bokosi patsamba 14]
MALEMBA A BAIBULO OSANTHULIDWA
○ 1:16—Mu Israyeli, dazi linagwirizanitsidwa ndi manyazi, kulira, ndi nsautso. (Yesaya 3:24-26; 15:2, 3; Yeremiya 47:5) Mitundu ina yachikunja inapanga kachitidwe kometa mitu yawo mpala mu nthaŵi ya chisoni kaamba ka wachibale womwalira. Pamene kuli kwakuti dazi lachibadwa silinalingaliridwe kukhala lodetsedwa pansi pa Chilamulo, Aisrayeli sanafunikire kumeta mitu yawo polira chifukwa iwo anali “anthu oyera kwa Yehova.” (Deuteronomo 14:1, 2) Ngakhale kuli tero, Mika anawuza Israyeli ndi Yuda kumeta tsitsi lawo chifukwa cha njira yawo yochimwa ya kulambira mafano yomwe sinawayeneretse iwo monga anthu oyera ndi kuwapanga iwo ndi mbadwa zawo kukhala oyenera ukapolo. Liwu la Chihebri pano lotembenuzidwa “chiwombankhanga” lingalozere ku muimba waukulu wa kumapiri, womwe uli kokha ndi mbali yoyera yofewa pamutu pake. Ngakhale kuti suli wa m’gulu limodzi monga chiwombankhanga, iwo ukulingaliridwa kukhala wa m’banja limodzimodzilo.
○ 2:12—Mawu awa amapeza kukwaniritsidwa kwamakono mu Israyeli wauzimu. (Agalatiya 6:16) Makamaka kuyambira 1919 kupita kutsogolo, njira inatsegulidwa kaamba ka otsalira odzozedwa kupulumuka kochoka ku ukapolo wawo mu Babulo Wamkulu wachipembedzo. (Chivumbulutso 18:2) Monga mmene Mika ananeneratu, iwo anasonkhanitsidwa ‘monga nkhosa mu khola, monga zoŵeta pabusa pake.’ Popeza kuti iwo agwirizanitsidwa chiyambire 1935 ndi “khamu lalikulu” la “nkhosa zina,” iwo ndithudi akhala “phokoso chifukwa cha kuchuluka anthu.”—Chibvumbulutso 7:9; Yohane 10:16.
○ 3:1-3—Pano pali kusiyanitsa kodabwitsa pakati pa Yehova, Mbusa wachifundo, ndi atsogoleri ankhalwe a anthu akale m’tsiku la Mika. Awa analephera mu ntchito yawo ya kutetezera nkhosa mwa kusonyeza chilungamo. Iwo mwankhalwe anapondereza nkhosa zophiphiritsirazo osati kokha mwa kuzidyerera izo komanso mwa ‘kumyula khungu lawo’—monga mimbulu. Abusa oipawo analanda anthuwo chilungamo, kuwagonjetsera iwo ku “machitachita okhetsa mwazi.” (3:10, NW) Kupyolera mu ziweruzo zokhotetsedwa, opanda chinjirizo analandidwa nyumba zawo ndi umoyo.—2:2; yerekezani ndi Ezekieli 34:1-5.
○ 4:3—“Mitundu yambiri ya anthu” imeneyi ndi “amitundu amphamvu” sayenera kuzindikiritsidwa ndi mitundu ya ndale zadziko ndi maboma. M’malomwake, awa ali anthu ochokera ku mitundu yonse, anthu omwe asweka kuchoka ku utundu wawo ndi kutembenukira ku utumiki wogwirizana m’phiri la Yehova la kulambira kowona. (Yesaya 2:2-4) Yehova ‘apereka chiweruzo ndi kulungamitsa zinthu’ m’njira yauzimu kaamba ka okhulupirira amenewa omwe atenga kaimidwe kawo kaamba ka Ufumu wa Mulungu. Anthu amenewa a “khamu lalikulu” amagonjera ku ziweruzo zaumulungu, kusula malupanga awo kukhala makasu ndipo mwakutero kukhala pa mtendere ndi mboni zinzawo za Yehova.
○ 5:2—Betelehemu Efrata mwinamwake anazindikiritsidwa monga tero chifukwa panali matauni aŵiri otchedwa Betelehemu. Mika akuzindikiritsa imodzi mu Yuda, kokha kum’mwera kwa Yerusalemu. Tauni inayo inali kumpoto, mu Zebuloni. (Yoswa 19:10, 15) “Efrata,” kapena “Efrati,” linali dzina loyambirira kaamba ka Betelehemu mu Yuda kapena dera lozungulira iyo. (Genesis 48:7; Rute 4:11) Kuzindikiritsa kwa tsatanetsatane koteroko kumakwaniritsa kulongosoka kwa malonjezo a ulosi wa Mulungu ponena za Mesiya.
○ 6:8—Mika sanali kuchepetsa phindu la nsembe zochotsera chimo koma anali kuwunikira chomwe mowonadi chinali cha mtengo wapatali m’maso mwa Yehova. (Yerekezani ndi Deuteronomo 10:12.) Kaamba ka nsembezo kuti zikhale zolandirika kwa Yehova, wochimwayo anayenera kusonyeza mikhalidwe ya chilungamo, chifundo, ndi kudzichepetsa. Lerolino, Yehova amayang’ana kaamba ka zofananazo mu utumiki wathu.—1 Akorinto 13:4-8.
○ 7:4—Mtungwi ndi mpanda wa minga ziri zomera zomwe zingakole zovala ndi kung’amba thupi. Mika pano anali kulongosola kuwola kwa mkhalidwe wa mtunduwo m’tsiku lake. Chotero iye mwachiwonekere anatanthauza kuti ngakhale abwino koposa pakati pa Aisrayeli osokerawo anali opanda pake kapena owawitsa monga mtungwi kapena mpanda wa minga kwa aliyense wofika pafupi kwambiri.
[Chithunzi patsamba 15]
Mika ananeneratu malo obadwira a Yesu