Mutu 97
Ogwira Ntchito m’Munda Wampesa
“AMBIRI oyamba,” Yesu anali atanena motero, “adzakhala akuthungo ndi akuthungo, adzakhala oyamba.” Iye tsopano akufotokoza mwa fanizo zimenezi mwa kusimba fanizo lina. “Ufumu wakumwamba,” iye akuyamba motero, “ufanana ndi munthu mwini banja, amene anatuluka mamaŵa ku kalemba antchito a m’munda wake wampesa.”
Yesu akupiritiza kuti: “Pamene [mwini banjayo] anapangana ndi antchito pa lupiya latheka limodzi tsiku limodzi, anawatumiza kumunda wake. Atatulukanso pafupifupi ora lachitatu, anawona ena ataimilira pamalo a msika ali osalembedwa ntchito; ndipo kwa ameneŵa anati, ‘Nanunso, pitani kumunda wampesa, ndipo zirizonse zimene ziri zoyenerera ndidzakupatsani.’ Chotero anamuka. Anatulukanso kachiŵiri pafupifupi ora lachisanu ndi chimodzi ndi ora lachisanu ndi chinayi nachita chimodzimodzi. Potsirizira pake, pafupifupi pa ora lakhumi ndi chimodzi anatuluka napeza ena ataimirira, ndipo anati kwa iwo, ‘Kodi mwaimiranji pano tsiku lonse osalembedwa ntchito?’ Iwo anati kwa iye, ‘Chifukwa palibe munthu watilemba ntchito.’ Iye anati kwa iwo, ‘Pitani inunso kumunda wampesawo.’ ”—NW.
Mwini banjayo, kapena mwini munda wampesa, ndiye Yehova Mulungu, ndipo munda wampesawo ndiwo mtundu wa Israyeli. Antchito m’munda wampesawo ndiwo anthu oloŵetsedwa mpangano la Chilamulo; kwakukulukulu iwo ali Ayudawo amene akukhala ndi moyo m’nthaŵi ya atumwi. Pangano la malipiro limachitidwa kokha kwa wantchito wogwira tsiku lathunthu. Malipirowo ndiwo lupiya la theka kaamba ka ntchito ya tsiku limodzi. Popeza kuti “ora lachitatu” ndilo 9:00 mmaŵa, awo amene aitanidwa pa ora la ntchito la 3, 6, 9 ndi 11, akugwira ntchito maora 9, 6, 3, ndi 1 malinga ndi nthaŵi yawo.
Ogwira ntchito maora 12, kapena tsiku lathunthu, akuimira atsogoleri Achiyuda amene akhala otanganitsidwa mosalekeza m’ntchito zachipembedzo. Iwo sali ofanana ndi ophunzira a Yesu, amene, kwa moyo wawo wochuluka, akhala olembedwa ntchito ya kusodza kapena ntchito zina zakudziko. Osati kufikira m’mphakasa ya 29 C.E. pamene “mwini banja” akutumiza Yesu Kristu kudzasonkhanitsa ameneŵa kuti akhale ophunzira. Motero iwo akukhala “akuthungo,” kapena ogwira ntchito a ora la 11.
Potsirizira, tsiku la ntchito lophiphiritsira likutha limodzi ndi imfa ya Yesu, ndipo nthaŵi ikufika ya kulipira antchitowo. Lamulo lachilendo la kulipira omalizira choyamba likutsatiridwa, monga momwe kwafotokozeredwa kuti: “Ndipo pamadzulo, mwini munda anati kwa kapitawo wake, Kaitane antchito, nuwapatse iwo kulipira kwawo, uyambe kwa omalizira kufikira kwa oyamba. Ndipo pamene iwo olembedwa poyandikira madzulo anadza, analandira munthu aliyense lupiya latheka limodzi. Ndipo mmene oyamba anadza, analingalira kuti adzalandira kopambana, ndipo iwonso analandira onse lupiya la theka. Koma mmene iwo analilandira, anaderera kwa mwini banja, nati, Omalizira awa anagwira ntchito mphindi yaing’ono, ndipo munawalinganiza ndi ife amene tinapilira kuwawa kwa dzuŵa ndi kutentha kwake. Koma iye anayankha, nati kwa mmodzi wa iwo, Mnzanga, sindikunyenga iwe; kodi iwe sunapangana ndi ine pa lupiya latheka limodzi? Tenga lako, numuke; pakuti ine ndifuna kupatsa kwa uyu womalizira monga kwa iwe. Sikuloleka kwa ine kodi kuchita chimene ndifuna ndi zanga? Kapena kodi diso lako laipa chifukwa ndiri wabwino?” Pomaliza, Yesu akubwereza mfundo yonenedwa payambirirapo, akumati: “Chomwecho omalizira adzakhala oyamba, ndipo oyamba adzakhala omalizira.”
Kulandiridwa kwa theka la lupiya kukuchitika, osati paimfa ya Yesu, koma pa Pentekoste wa 33 C.E. pamene Kristu, “kapitawo,” atsanulira mzimu woyera pa ophunzira ake. Ophunzira a Yesu ameneŵa ali ngati “omalizira,” kapena ogwira ntchito a ora la 11. Lupiya la theka silimaimira mphatso ya mzimu woyera weniweniwo. Lupiya la theka ndilo kanthu kena kamene ophunzirawo amagwiritsira ntchito pano padziko lapansi. Ndilo kanthu kena kamene kamatanthauza chochirikiza moyo, moyo wawo wosatha. Ndilo mwaŵi wa kukhala Mwisrayeli wauzimu, wodzodzedwera kulalikira Ufumu wa Mulungu.
Mwamsanga awo amene alembedwa ntchito choyamba akuwona kuti ophunzira a Yesu alandira malipiro, ndipo akuwawona akugwiritsira ntchito lupiya la theka lophiphiritsiralo. Koma iwo akufuna zowonjezereka koposa mzimu woyera ndi mwaŵi wake wogwirizanitsidwa ndi Ufumu. Kung’ung’udza kwawo ndi zitsutso kukuchitidwa mumpangidwe wa kuzunza ophunzira a Kristu, antchito “omalizira” m’munda wampesa.
Kodi kukwaniritsidwa kumeneko kwa m’zaka za zana loyamba ndiko kukwaniritsidwa kokha kwa fanizo la Yesu? Ayi, atsogoleri a Chikristu Chadziko m’zaka za zana la 20 lino, mwa lingaliro lawo la malo awo antchito ndi mathayo akhala, “oyamba” kulembedwa ntchito m’munda wampesa wophiphiritsira wa Mulungu. Iwo analingalira ofalitsa odzipatulira ogwirizana ndi Watch Tower Bible and Tract Society kukhala “omalizira” kulandira gawo lirilonse lovomerezeka m’ntchito ya Mulungu. Koma, ndiwo kwenikweni, anthu enieni ameneŵa, amene atsogoleri achipembedzo amanyoza, amene analandira lupiya la theka—mwaŵi wa kutumikira monga oimira odzozedwa a Ufumu wakumwamba wa Mulungu. Mateyu 19:30–20:16.
▪ Kodi nchiyani chimene chikuimiridwa ndi munda wampesa? Kodi ndani amene akuimiridwa ndi mwini munda wampesa ndiponso ndi ogwira ntchito maora 12 ndi 1?
▪ Kodi ndiliti pamene tsiku lophiphiritsiralo litha, ndipo kodi ndiliti pamene malipiro anaperekedwa?
▪ Kodi nchiyani chimene chikuimiridwa ndi malipiro a lupiya la theka?