“Zinthu Zomangilira Ziyembekezo Zathu”
PANALI pa Sande m’mawa mofunda, September 10, pamene 4,155 anasonkhana m’Holo Yosonkhanira yokongola ya Mboni za Yehova mu Mzinda wa Jersey, New Jersey, kaamba ka chochitika chomaliza maphunziro a kalasi ya 87 ya Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower. Pa opezekapo panali ophunzira 24 ndi alendo awo oitanidwa limodzi ndi ziŵalo za banja la Beteli zochokera ku Brooklyn ndi ku mafamu a Sosaite.
Gululo linakhalitsidwa bata panthaŵi imodzi pa 10:00 a.m. ndi Albert Schroeder, amene anatumikira monga tcheyamani pa tsikulo. Pambuyo pa nyimbo yotsegulira, pemphero linaperekedwa ndi John Barr. Abale aŵiriwo ali ziŵalo za Bungwe Lolamulira. Mbale Schroeder analongosola mwachidule ndandanda ya kalasiyo ndipo anachitira ndemanga kuti omaliza maphunzirowo anali “okonzekera kukhala ndi phande m’ntchito ya dzikolonse ya Mboni za Yehova, tsopano m’maiko 210.” Iye kenaka anapitiriza kudziŵikitsa alankhuli asanu ndi aŵiri.
Robert Wallen, yemwe amagwira ntchito m’Maofesi Oyendetsa Ntchito pa malikulu a Brooklyn, anazika mutu wake wakuti, “Mukhale Nacho Chikondano Chenicheni mwa Inu Nokha,” pa 1 Petro 4:8. Iye adatero kuti amishonale afunikira kuthandizana, ndipo popeza kuti ophunzira onse a kalasi imeneyi anali okwatira, iye analunjikitsa ndemanga zake makamaka kwa okwatira. “Mkazi ayenera kukonda mwamuna wake ngakhale kuti mkaziyo angaphunzire chinenero chachilendo mwamsanga kuposa mmene iye angachitire,” iye analangiza tero. “Mkaziyo ayenera kukhala womvetsetsa ndi wachifundo. Ndiponso, ayenera kuyesera kum’mvetsetsa iye pamene ali ndi tsiku lake lophika la mlungu ndi mlungu!” (Kaŵirikaŵiri, m’mishonale aliyense amagaŵiridwa tsiku lokhazikika kuphika chakudya cha tsikulo cha onse okhala m’nyumba ya amishonale.) Kenaka mlankhuliyo anafotokoza zokumana nazo zolefulitsa ndi zosangalatsa zimene amuna ena amakhala nazo pophunzira kuphika, monga chokumana nacho cha mwamuna amene anagwiritsira ntchito baking soda m’malo mwa baking powder. Mbale Wallen anatchulanso nsonga yakuti mwamuna ayenera “kulingalira bwino za zosoŵa za mkazi wake,” popeza kuti nthaŵi yochuluka ya mwamuna ingawonongedwe pa kusamalira mathayo a mpingo. Ponse paŵiri kwa amuna ndi akazi, iye anati: “Nthaŵi zonse khalani omangirira; musapange ndemanga zokhumudwitsana. Peŵani kudzipatula nokha. Ndipo pamene mupanga zophophonya, zivomerezeni izo.”
Mlankhuli wotsatira, Daniel Sydlik, chiŵalo cha Bungwe Lolamulira, anasankha mutu wakuti: “Musazime Moto wa Mzimu wa Mulungu,” wozikidwa pa 1 Atesalonika 5:19. “Moto ponse paŵiri ungafunditse ndi kuwononga,” iye anatero. “Nthaŵi zina amishonale amalimbikitsa ndipo nthaŵi zina amawopsyeza. Mwamuna wokalamba wa ku Africa nthaŵi zina ananena kuti: ‘Uzirani pang’onopang’ono,’ monga pa kamoto kakang’ono pamene muyesera kubweretsa moyo! Pamene mukulankhula za zinthu zimene mungapeze m’gawo lanu—malo a zonyansa otseguka, ntchentche, phokoso la magalimoto, dziko latsopano, chipembedzo chachilendo—sonyezani ulemu. Mungagwire ntchentche zambiri ndi uchi kuposa ndi vinegar. Phunzirani ‘kuuzira pang’onopang’ono’ ndipo musazime moto wa mzimu wa Yehova.”
Ndiyeno mutu wakuti “Khalirirani m’Magawo Anu ndi Chisangalalo Limodzi ndi Kuchenjera” unali mutu wolongosoledwa ndi Kenneth Flodin, woyang’anira Nyumba ya Beteli ku Watchtower Farms. Popeza kuti tsopano Sukulu ya Gileadi inakhazikitsidwa ku Watchtower Farms, omaliza maphunziro onse anazoloŵerana bwino lomwe ndi Mbale Flodin. Mbali ziŵiri zachenjezo zinagogomezeredwa m’nkhani yake: (1) kukondetsa zinthu zakuthupi ndi (2) kalankhulidwe koipa ndi maganizo oipa. Uphungu wake unali wakuti, “Peŵani kudzikonda ndipo khalani okonda ena.” “Penyani kutsogolo ku zitonthozo ndi zinthu zokoma m’dziko latsopano; musazifunefune izo tsopano,” iye anatero. Kuti athandize ophunzirawo kupeŵa zinthu zoipa, mlankhuliyo anagwira mawu Numeri 13:28, 32. Iye anati, “Nthaŵi zina, anthu amawona chinthu chimodzimodzicho, ndipo ena adzakhala ndi kapenyedwe koipa, koma ena adzakhala ndi kapenyedwe kabwino. Mofanana ndi Kalebi wakale, dalirani mwa Yehova. Wuzani ena malingaliro anu abwino. Ndipo patabwera nkhani yoipa, sinthani nkhaniyo kupeŵa malingaliro oipa.”
Lloyd Barry, chiŵalo cha Bungwe Lolamulira amene kale anali mishonale iyemwini, anapereka uphungu wogwira ntchito. “Chikondi, chimwemwe, ndi mtendere iri mikhalidwe yofunika kwa amishonale atsopano,” iye anatero. “Mudzakhala mukuwona zifooko za ena m’nyumba yanu ya umishonale, koma sumikani pa zifooko za inumwini.” Iye anakumbukira masiku ake oyambirira mu Japan pamene amishonale anasangalala ndi kudya nsomba tsiku ndi tsiku, koma kenaka amishonale atsopano anafika amene ankadwala ngati adya nsomba. Chotero mpambo wa zakudya unasintha kaamba ka chikondi kwa atsopanowo. Iye analangizanso kuti: “Sungani maganizo anu achisangalalo; musalole konse dzuŵa kuloŵa muli ndi vuto lirilonse. Sungani mtendere m’nyumbayo, ndipo mudzakhala wachimwemwe m’moyo wanu wa umishonale.”—Aefeso 4:26.
Jack Redford, m’modzi wa alangizi a Gileadi, analankhulanso pa nkhani yakuti: “Yehova Adzamaliza Kuphunzira Kwanu,” akuzika ndemanga zake pa 1 Petro 5:10. Iye adati: “Yehova angakuphunzitseni mwakulola mikhalidwe yovuta kuchita nayo kubuka. Monga mmene anaphunzitsira atumwi kusamalira mikangano yaumwini, adzakuphunzitsaninso. Musataye mtima pamene pali kusiyana kwa malingaliro. Khalani okonzekera kusintha umunthu wanu. Kunyada kumachititsa chimenechi kukhala chovuta, koma kudzichepetsa kumachitheketsa icho. Phunzirani kukhala wosinthika. Yehova adzakuphunzitsaninso kuchita ndi ena. Inu mungofunikira ‘kusasunga ku mtima mawu onse amene anthu angalankhule’ ponena za inu.” (Mlaliki 7:21, 22) Chizunzo nachonso chimatumikira monga kuphunzitsa. Amishonale amene apirira chizunzo ali achimwemwe ndipo alibe zodandaula, amangokhala ndi chisangalalo pokhala ataphunzitsidwa ndi chizunzocho.
Ulysses Glass, mlangizi wina, anaperekanso mawu ake omalizira kwa omaliza maphunzirowo. Iye anasumika pa Aefeso 4:1-3, akumayamikira kalasiyo chifukwa chosonyeza mikhalidwe ya chigwirizano yolongosoledwa pamenepo ndi kuwalimbikitsa kupitirizabe kuchita tero, akumati: “Mtendere uli chinthu chomangirira, ndipo uli wofunikira kaamba ka chigwirizano.” Iye kenaka anapitiriza ndi Aefeso 4:4-6 ndipo anabwereramo mu ubwino wa mzimu wa Mulungu, akumakumbutsa onse kuti “Yehova ali Magwero a nyonga yogwira ntchito. Tiyenera kumuwopa iye; kugwa m’manja mwake nkoopsya.”—Ahebri 10:31.
Ziyembekezo Zapamwamba
Ndiyeno onse anamvetsera ndi chikondwerero chenicheni kwa Theodore Jaracz, chiŵalo cha Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova, yemwe analankhula pa mutu wosonyezedwawo wakuti: “Zinthu Zomangilira Ziyembekezo Zathu.” Kulingalira pa 1 Akorinto 2:9, iye adati: “Vesi limeneli silikulankhula ponena za zinthu za mtundu wakuthupi, popeza kuti vesi lotsatira, 1 Akorinto 2:10, likulankhula za ‘zinthu zakuya za Mulungu.’ Zimenezi zimaloŵetsamo ‘nzeru ya Mulungu’ mogwirizana ndi ‘chinsinsi chopatulika,’ ‘nzeru [yake] yobisika’ imene inachokera kutali kupyola dongosolo iri la dzuŵa, inde, yochokera kwa Mulungu iyemwini.” (1 Akorinto 2:7) Gululo kenaka linalozeretsedwa ku Yesaya 64:4, limene linali chokumbutsa ‘kuyembekezerabe’ Mulungu ndi zinthu zimene wakonza.
Ndi ziyembekezo zotani nanga zimene anthu a Mulungu alidi nazo! Mbale Jaracz anatchula zotsatirazi: “Mu 1919 panali kugwa kwa Babulo Wamkulu; mu 1922 chisonkhezero chodzutsa maganizo cha ‘kubukitsa Mfumu ndi Ufumuwo,’ kulalikira Ufumu wokhazikitsidwa pa dziko lonse; mu 1935 anthu a Mulungu anaphunzira kufunika kwa ‘khamu lalikulu’ la pa Chibvumbulutso 7:9; mu 1943 iwo anawona Sukulu ya Gileadi ikuyamba kutumiza amishonale kumalekerezo a dziko lapansi; lerolino, mu 1989, omaliza maphunziro inu muli ndi mwaŵi wa kuwuza zinthu zabwino kwa anthu ofunitsitsa kumvetsera m’magawo anu.”
Pambuyo pa kupatsidwa madipuloma, mmodzi wa ophunzirawo anaŵerenga kalata yogwira mtima ya chiyamikiro kuchokera ku kalasiyo.
Masanawo, Lon Schilling, m’gwirizanitsi wa Komiti ya Watchtower Farms, anatsogoza Phunziro lachidule la Nsanja ya Olonda. Kenaka ophunzirawo anawonetsa programu ya kuimba yosangalatsa ndipo anaseŵera zina za zokumana nazo zawo mu utumiki wakumunda. Motsatira chimenechi, ofalitsa a kumaloko anawonetsa drama ya panthaŵi yake ya mutu wakuti: “Kuchita Ndi Machenjera a Satana.” Pomalizira, pambuyo pomvetsera ku kufunsidwa kwa asanu ndi mmodzi a omaliza maphunziro atsopanowo, khamu lachimwemwelo linaimba nyimbo yotsekera ndipo anasangalala kugwirizana m’pemphero ndi prezidenti wa zaka 96 zakubadwa wa Sukulu ya Gileadi, Frederick Franz.
[Bokosi patsamba 23]
CHIŴERENGERO CHA KALASI
Chiŵerengero cha maiko oimiridwa: 5
Chiŵerengero cha maiko ogaŵiridwako: 10
Chiŵerengero cha okwatirana: 12
Chiwonkhetso cha ophunzira: 24
Avereji ya msinkhu: 30.9
Avereji ya zaka m’chowonadi: 13.4
Avereji ya zaka mu uminisitala wa nthaŵi zonse: 9.2
[Chithunzi patsamba 23]
Kalasi ya Omaliza Maphunziro ya 87 ya Sukulu ya Gileadi ya Baibulo ya Watchtower
Mundandanda pansipa, mizera yaŵerengedwa kuyambira kutsogolo kunka kumbuyo, ndipo maina andandalitsidwa kuchokera kulamanzere kunka kulamanja mu mzera uliwonse.
(1) Heindel, E.; Andrews, D.; Casavant, D.; Montanez, E.; Nale, P.; Koukaras, S. (2) Miell, T.; Heithaus, M.; Melton, T.; Hagberg, N.; Kettinen, M. (3) Kettinen, L.; Andrews, W.; Koukaras, E.; McCollough, S.; Melton, G.; McCollough, J. (4) Heindel, W.; Casavant, G.; Miell, G.; Montanez, J.; Nale, M.; Hagberg, I.; Heithaus, K.