Kodi Muli Woyeneretsedwa Kutumikira?
“Kukhala kwathu oyeneretsedwa mokwanira kumachokera kwa Mulungu.”—2 AKORINTO 3:5, “NW.”
1. Kodi mpingo Wachikristu ulibe malo a anthu amtundu wotani?
YEHOVA MULUNGU ndi Yesu Kristu ali antchito. Yesu anati: “Atate wanga amagwira ntchito kufikira tsopano, inenso ndigwira ntchito.” (Yohane 5:17) Mulungu samavomereza anthu okana kugwira ntchito; ndiponso iye samavomereza ofunafuna mathayo kotero kuti apeze ulamuliro pa ena. Mpingo Wachikristu ulibe malo kwa aulesi kapena kwa okhala ndi chikhumbo chadyera.—Mateyu 20:25-27; 2 Atesalonika 3:10.
2. Kodi nchifukwa ninji tsopano pali kufunika kwakukulu kwa amuna osenza mathayo mumpingo Wachikristu?
2 Mboni za Yehova ziri ndi ‘zochita zochuluka m’tchito ya Ambuye,’ makamaka tsopano pamene anthu ambiri akukwera kumka ku “phiri” la kulambira kowona. (1 Akorinto 15:58; Yesaya 2:2-4) Pali kufunika kwakukulu kwa amuna oyeneretsedwa mwauzimu kuti asenze mathayo mumpingo. Amuna oterowo, mosasonkhezeredwa ndi chikhumbo chadyera amalemekeza Yehova, osati iwo okha. (Miyambo 8:13) Amadziŵa kuti Mulungu amawathandiza kuyeneretsedwa kaamba ka mathayo ampingo, monga momwedi ‘amayeneretsera mokwanira aminisitala a pangano latsopano.’—2 Akorinto 3:4-6.
3. Kwakukulukulu, kodi ndiati amene ali mathayo a akulu ndi a atumiki otumikira?
3 Lerolino, monga momwe zinaliri kwa Akristu oyambirira, amuna akuikidwa ndi mzimu woyera ndi kupyolera mwamakonzedwe a gulu la Yehova kuti atumikire monga akulu ndi atumiki otumikira. (Machitidwe 20:28; Afilipi 1:1; Tito 1:5) Akulu amaŵeta nkhosa za Mulungu mwauzimu, kumapereka chiyang’aniro chotetezera. Amathandizidwa ndi atumiki otumikira, amene mathayo awo samaphatikizapo uyang’aniro wauzimu mwachindunji. (1 Petro 5:2; yerekezerani ndi Machitidwe 6:1-6.) Mofanana ndi Mwana wa Mulungu, yemwe anabwera kudzatumikira, oikidwa oterowo amakhumba kutumikira okhukulupirira anzawo. (Marko 10:45) Ngati ndinu mwamuna Wachikristu, kodi muli ndi mzimu umenewo?
Ziyeneretso za Onse
4. Kodi nkuti makamaka kumene timapezako mpambo wa ziyeneretso za awo oikiziridwa mathayo ampingo?
4 Makamaka pali ziyeneretso kwa awo oikiziridwa mathayo ampingo zoperekedwa ndi mtumwi Paulo pa 1 Timoteo 3:1-10, 12, 13 ndi Tito 1:5-9. Pamene tipenda ziyeneretso zimenezi, zimene zina zimagwira ntchito ponse paŵiri kwa akulu ndi atumiki otumikira, sitiyenera kuziwona mogwirizana ndi miyezo yakudziko. Mmalo mwake, tiyenera kuziwona mwamakhazikitsidwe ake a m’zaka za zana loyamba ndipo monga zogwira ntchito pakati pa anthu a Yehova. Kuzifikira ziyeneretso zimenezi sikumafuna ungwiro, popeza kuti ngati zinali zotero palibe munthu amene akanayeneretsedwa. (1 Yohane 1:8) Koma ngati ndinu mwamuna Wachikristu, mosasamala kanthu kuti inu tsopano muli ndi mathayo ampingo kapena ayi, bwanji osapenda ziyeneretso za inu mwini.
5. Kodi kukhala wopanda chifukwa kumatanthauzanji?
5 Wopanda chifukwa; wokhala ndi umboni wabwino kuchokera kwa anthu akunja; wopanda chinenezo. (1 Timoteo 3:2, 7, 8, 10, NW; Tito 1:6, 7, NW) Pamene aikidwa ndi pamene akutumikira, atumikira otumikira ndi akulu ayenera kukhala opanda chifukwa, ndiko kuti, opanda chinenezo ndipo osafunikira kudzudzulidwa kaamba ka chinenezo chotsimikiziridwa cha khalidwe loipa kapena chiphunzitso. Zinenezo zonama zopangidwa ndi “abale onyenga” kapena ena sizimapangitsa munthu kukhala ndi chifukwa. Kuti munthu asayeneretsedwe kutumikira mumpingo, chinenezocho sichiyenera kukhala chosanunkha kanthu, ndipo chiyenera kutsimikiziridwa mogwirizana ndi miyezo Yamalemba. (2 Akorinto 11:26; 1 Timoteo 5:19) Munthu woikidwa mumpingo “ayeneranso kukhala ndi umboni wabwino kuchokera kwa anthu akunja, mmalo mwakuti asagwere m’chitonzo ndi mumsampha wa Mdyerekezi.” Ngati munthu anachita tchimo lalikulu kalelo, angaikidwe kokha ngati wakhala ndi moyo umene wamchotsera chitonzo chirichonse ndipo wadzipezera dzina labwino.
6. Kodi kukhala mwamuna wamkazi mmodzi kumatanthauzanji?
6 Mwamuna wa mkazi mmodzi. (1 Timoteo 3:2, 12, NW; Tito 1:6, NW) Izi sizitanthauza kuti amuna okwatira ndiwo okha angakhale atumiki otumikira ndi akulu. Komabe, ngati ngwokwatira, mwamunayo ayenera kukhala ndi mkazi wamoyo mmodzi yekha ndikukhala wokhulupirika kwa iye. (Ahebri 13:4) Mosiyana ndi amuna ambiri osakhala Achikristu m’zaka za zana loyamba, iye sangakhale wamitala.a
7. (a) Kodi uli msinkhu wakuthupi umene umayeneretsa mwamuna kukhala mkulu? (b) Kodi nchiyani chimene chikuphatikizidwa m’kutsogoza banja mumkhalidwe wabwino kwambiri?
7 Wotsogoza banja lake la iye yekha mumkhalidwe wabwino kwambiri, wokhala ndi ana ogonjera. (1 Timoteo 3:4, 5, 12, NW; Tito 1:6, NW) Ena angalingalire kuti akulu ayenera kukhala azaka zosachepera 30 zakubadwa, koma Baibulo silimanena zaka zoyambirapo. Komabe, mwamunayo ayenera kuchita zinthu monga mwamuna wokhwima m’lingaliro lauzimu. Atumiki otumikira ndi akulu ayenera kukhala okhwima mokwanira kukhala ndi ana. Ngati ali wokwatira, mwamunayo samayeneretsedwa ngati achita zinthu mwanjira yaumulungu ku malo ena komabe nakhala wotsendereza panyumba. Ayenera kukhala atapeza ulemu kaamba ka kutsogoza bwino banja lake mogwirizana ndi malamulo amakhalidwe abwino a Baibulo, ndipo cholinga chake chiyenera kukhala chipambano chauzimu ndi chiŵalo chirichonse chabanja. Kaŵirikaŵiri, mkulu amenenso ali atate ayenera kukhala ndi ana achichepere odzisungira bwino amene ali “okhulupirira.” Ayenera kukhala akumapita patsogolo kulinga kukudzipereka kwa Mulungu kapena ngobatizidwa kale monga Mboni za Yehova. Mwamuna wosakhoza kupereka chikhulupiriro kwa ana ake sikukuwonekera kuti angatero kwa ena.
8. Mwamuna wokhala ndi banja lake asanakhale mkulu, kodi ayenera kuphunzira kuchitanji?
8 Mwamuna wokhala ndi banja asanakhale mkulu wokhoza kupereka uyang’aniro wauzimu mumpingo, ayenera kuphunzira kutsogoza banja lake. ‘Ngati mwamuna aliyense sadziŵa kutsogoza banja lake la iye yekha, kodi adzasamalira bwanji mpingo wa Mulungu?’ (1 Timoteo 3:5) Zowona, mwamuna angatsutsidwe ndi mkazi wosakhulupirira. (Mateyu 10:36; Luka 12:52) Kapena mmodzi wa ana ake angakhale ndi liwongo latchimo lalikulu, ngakhale kuti enawo akuchita bwino mwauzimu. Ndiponso, ngati mwamunayo wachita zonse zimene zingayembekezeredwe, ndipo makamaka ngati wakhala ndi chipambano chauzimu kwa ena am’banja lake, kukanidwa kwa chilangizo chake chabwinocho ndi mmodzi wa banja lake sikungampangitse kusayeneretsedwa monga mtumiki wotumikira kapena mkulu.
9. Kodi mkulu kapena mtumiki wotumikira ayenera kukhala ndi chisamaliro chotani ponena za zakumwa zoledzeretsa?
9 Osati wakumwa waphokoso kapena wokonda kumwa vinyo kwambiri. (1 Timoteo 3:3, 8, NW; Tito 1:7, NW) Mtumiki wotumikira kapena mkulu sayenera kumwerekera m’zakumwa zoledzeretsa. Kumwerekera nazo kungatulukire m’kulephera kulamulira maganizo ndi malingaliro, kukumatsogolera kukuchita phokoso kapena ndewu. Sayenera kukhala ‘wokonda kumwa vinyo kwambiri’ kapena kukhala ndi mbiri ya chizoloŵezi chakuledzera kapena uchidakwa. (Miyambo 23:20, 21, 29-35) Nkwaupandu chotani nanga ngati ulendo waubusa unaipitsidwa ndi kusadziretsa! Ngati mbale amamwa konse, sayenera kutero pamene akugaŵanamo m’misonkhano, uminisitala, kapena utumiki uliwonse wopatulika.—Levitiko 10:8-11; Ezekieli 44:21.
10. Kodi nchifukwa ninji okonda ndalama ndi aumbombo wofuna phindu losawona mtima sakuyeneretsedwa kukhala akulu kapena atumiki otumikira?
10 Osati wokonda ndalama kapena phindu losawona mtima. (1 Timoteo 3:3, 8, NW; Tito 1:7, NW) Okonda ndalama ali pangozi yauzimu, ndipo “osirira” sadzaloŵa Ufumu wa Mulungu. Chifukwa chake, amuna oterowo sakuyeneretsedwa kukhala akulu kapena atumiki otumikira. (1 Akorinto 6:9, 10; 1 Timoteo 6:9, 10) Liwu Lachigiriki lotembenuzidwa “kusawona mtima” kwakukulukulu limatanthauza “chamanyazi,” ndipo liwu lotembenuzidwa “phindu” limasonya ku phindu lamtundu uliwonse kapena geni. (Afilipi 1:21; 3:4-8) Ndithudi, mwamuna amene maganizo ake amasonyeza kuti akachitira “nkhosa” za Mulungu mosawona mtima saali woyeneretsedwa kaamba ka mathayo ampingo. (Ezekieli 34:7-10; Machitidwe 20:33-35; Yuda 16) Kufunika kwakukhala wochenjera popanga mavomerezedwe kumagogomezeredwa pamene tizindikira kuti mwamuna ataikidwa, angaikiziridwe thayo losunga ndalama ndipo angayesedwe kufuna kuba zina za ndalamazo.—Yohane 12:4-6.
11. Kodi nchifukwa ninji “mwamuna wotembenuzidwa chatsopano” sayenera kuvomerezedwa kaamba ka mathayo ampingo?
11 Osati wotembenuzidwa chatsopano; woyesedwa. (1 Timoteo 3:6, 10, NW) Munthu wobatizidwa chatsopano sanakhale ndi nthaŵi yotsimikizira kuti adzasamalira mokhulupirika mathayo ake ogaŵiridwa. Iye angakhale wopanda chifundo kwa ovutika kapena kupanda nzeru yofunika kuthandiza olambira anzake ndipo ngakhale kululuza ena. Chotero, asanavomerezedwe monga mtumiki wotumikira ndipo makamaka monga mkulu, mwamunayo ayenera “kuyesedwa” ndipo ayenera kupereka umboni wakukhala wokhoza kupanga zosankha zabwino ndi kudalirika. Palibe nthaŵi yoikika yakuyesa kumeneku, ndipo anthu amasiyana pamlingo wakukula kwauzimu. Koma akulu sayenera kufulumira kuvomereza mwamuna watsopano “kuwopera kuti iye angatukumuke ndi kunyada ndi kugwera m’chiweruzo choperekedwa kwa Mdyerekezi.” Mwamunayo ayambe wasonyeza kudzichepetsa konga kwa Kristu.—Afilipi 2:5-8.
Kusumika Chisamaliro pa Atumiki Otumikira
12. Kodi ziyeneretso zondandalitsidwira atumiki otumikira ziyenera kufikiridwa ndi iwo okha?
12 Ziyeneretso zina zandandalikidwa kaamba ka atumiki otumikira, komabe, ngati ziyeneretso zoterozo sizinafikiridwe ndi akulu, sakayeneretsedwa kutumikira. Monga mwamuna Wachikristu, kodi mukuyeneretsedwa m’mbali izi?
13. Kodi kukhala wolingalira kumatanthauzanji?
13 Wolingalira. (1 Timoteo 3:8) Mwamuna woyeneretsedwa kutumikira monga mtumiki wotumikira sayenera kuwona mathayo mopepuka. Ayenera kuchita zinthu mumkhalidwe waulemu womdzetseranso ulemu. Ngakhale kuti kuseka kwa apa ndi apo kuli kovomerezedwa, iye sakayeneretsedwa ngati nthaŵi zonse achita zinthu mwanjira yopeputsa.
14. (a) Kodi kukhala wosanena paŵiri kuli nditanthazo lotani? (b) Kodi kukhala ndi chikumbumtima choyera kumafunikiritsa chiyani?
14 Wosanena paŵiri; wokhala nacho chikumbumtima chowona. (1 Timoteo 3:8, 9) Atumiki otumikira (ndi akulu omwe) ayenera kunena zowona, osati amiseche kapena amdyera kuŵiri. Popeza kuti sayenera kukhala onena paŵiri, sayenera kunena mwachinyengo chinthu china kwa munthu wina ndi chosiyana nacho kwa wina. (Miyambo 3:32; Yakobo 3:17) Amuna ameneŵa ayeneranso kukhala ochirikiza chowonadi chovumbulutsidwa osasunthika, “okhala nacho chinsinsi cha chikhulupiriro m’chikumbumtima chowona.” Pamaso pa Mulungu, chikumbumtima cha mwamuna choterocho chiyenera kupereka umboni wakuti iye ali wakaimidwe kabwino ndipo sakuchita chirichonse chobisa kapena chodetsa. (Aroma 9:1; 2 Akorinto 1:12; 4:2; 7:1) Palibe aliyense amene angayeneretsedwe kutumikira nkhosa za Mulungu kusiyapo ngati amamatira kuchowonadi ndi kumalamulo a makhalidwe abwino a Mulungu.
Kusumika Chisamaliro Paziyeneretso za Akulu
15. Kodi ndi ziyeneretso za ayani zimene zikupendedwa tsopano, ndipo kodi makamaka zimenezi zimaphatikizapo chiyani?
15 Ziyeneretso zina zimagwira ntchito mwachindunji kwa akulu ndipo kwakukulukulu zimaphatikizapo ntchito yawo monga abusa ndi aphunzitsi. Monga mwamuna Wachikristu, kodi mumazifikira ziyeneretso izi?
16. (a)Kodi nchiyani chimene chiri chofunika kukhala wachikatikati m’zizolowezi? (b) Kodi ndimotani mmene mkulu angasungire kudziletsa?
16 Wachikatikati m’zizolowezi; wodziletsa. (1 Timoteo 3:2, NW; Tito 1:8, NW) Mkulu ayenera kukhala wolamulirika, wosakhala kapolo wa zizolowezi zoipa. Pamene ayang’anizana ndi ziyeso, Mulungu adzamthandiza kukhala wokhazikika ngati apemphera monga momwe adachitira wamasalmo kuti: “Masautso a mtima wanga akula: munditulutse m’zondipsinja.” (Salmo 25:17) Woyang’anira ayeneranso kupempherera mzimu wa Mulungu ndikusonyeza zipatso zake, kuphatikizapo kudziletsa. (Luka 11:13; Agalatiya 5:22, 23) Kulamulira malingaliro, mawu, ndi machitidwe kumakhozetsa mkulu kupeŵa kupambanitsa pamene akupereka chitsogozo chauzimu kumpingo.
17. Kodi nchiyani chimene chikuphatikizidwa m’kukhala wolama m’maganizo?
17 Wolama m’maganizo. (1 Timoteo 3:2, NW) Mkulu ayenera kukhala wolingalira, wochenjera, ndi wakhama. Mawu ake ndi zochita zake ziyenera kukhala ndicholinga ndi zanzeru. Kuganiza kwake kodzichepetsa, ndi kokhazikika kuli kozikidwa panzeru yaumulungu ndi paziphunzitso zabwino za Mawu a Mulungu, amene ayenera kukhala wophunzira wake wakhama.—Aroma 12:3; Tito 2:1.
18. Kodi kukhala wolongosoka kumafunikiritsa chiyani kwa mkulu?
18 Wolongosoka. (1 Timoteo 3:2) Liwu Lachigiriki logwiritsiridwa ntchito pano latembenuzidwa “kulinganizidwa bwino” pa 1 Timoteo 2:9. Chotero mkulu ayenera kukhala ndi njira yamoyo yodekha, yolinganizidwa bwino. Mwachitsanzo, iye ayenera kukhala wosunga nthaŵi. Mwachiwonekere, Akristu a m’zaka za zana loyamba sanachite makonzedwe a zolembedwa kukhala nkhani yaikulu, chotero mkulu lerolino satofunikira kukhala katswiri wa maakaunti kapena kalaliki. Atumiki otumikira angasamalire zinthu zofunikira m’zimenezi. Koma liwu Lachigiriki lotanthauza “kulongosoka” lingasonye kukudzisungira kwabwino, ndipo ndithudi mwamuna sakayeneretsedwa kukhala mkulu ngati ali wamwano kapena wosalongosoka.—1 Atesalonika 5:14; 2 Atesalonika 3:6-12; Tito 1:10.
19. Chifukwa chakuti ngwochereza, kodi mkulu amachitanji?
19 Wochereza alendo. (1 Timoteo 3:2; Tito 1:8) Mkulu ‘amakhala wochereza.’ (Aroma 12:13; Ahebri 13:2) Liwu Lachigiriki lotanthauza “kuchereza” m’lingaliro lenileni limatanthauza “wokonda alendo.” Chifukwa chake, mkulu wochereza amalonjera atsopano kumisonkhano Yachikristu, akumasonyeza chikondwerero chofananacho kwa osauka monga momwe amachitira kwa okhupuka mwakuthupi. Iye amakhala wochereza kwa oyendayenda kaamba ka zabwino Zachikristu ndi kumawalola kumuka ‘mumkhalidwe woyenerera kwa Mulungu.’ (3 Yohane 5-8) Ndithudi, mkulu amasonyeza kuchereza makamaka kwa okhulupirira anzake mogwirizana ndi zosoŵa zawo ndipo monga momwe mikhalidwe yake ingamlolere.—Yakobo 2:14-17.
20. Kodi mkulu ayenera kuyeneretsedwa kuphunzitsa mwanjira zotani?
20 Woyeneretsedwa kuphunzitsa. (1 Timoteo 3:2, NW) Luso la mkulu monga mphunzitsi wauzimu silimachokera kunzeru za munthuyo zachibadwa kapena nzeru zakudziko. (1 Akorinto 2:1-5, 13) Amakhala nalo chifukwa chakukhala ‘wogwira zolimba mawu okhulupirika malinga ndi luso lake [kapena, njira] yakuphunzitsa, kuti akakhale wokhoza ponse paŵiri kuchenjeza mwachiphunzitso chimene chiri cholama ndi kudzudzula awo amene akutsutsa.’ (Tito 1:9; yerekezerani ndi Machitidwe 20:18-21, 26, 27.) Ayenera kukhala wokhoza ‘kulangiza mofatsa otsutsa.’ (2 Timoteo 2:23-26) Ngakhale ngati mkulu saali wokamba nkhani Zabaibulo wabwino koposa mumpingo, iye ayenera kukhala wophunzira Mawu a Mulungu wakhama kotero kuti ali waluso mokwanira kulangiza ndi kupatsa uphungu kwa okhulupirira, amenenso amaphunzira Baibulo. (2 Akorinto 11:6) Ayenera kukhala woyeneretsedwa kupereka “chiphunzitso cholamitsa” chimene chimathandiza mabanja ndi anthu alionse paokha kulondola moyo wopembedza Mulungu.—Tito 2:1-10.
21. (a) Kodi nchifukwa ninji kunganenedwe kuti mkulu saali woputa ena? (b) Kodi kukhala wolingalira kumatanthauzanji? (c) Kodi kusakhala wandewu kumatanthauzanji?
21 Osati woputa anzake, koma wolingalira, osati wandewu. (1 Timoteo 3:3, NW; Tito 1:7, NW) Pokhala wamtendere, mkulu samamenya ena ndi nkhonya yeniyeni kapena kuwapamantha ndi mawu mwakulankhula mawu onyoza kapena obaya mumtima. (Yerekezerani ndi 2 Akorinto 11:20.) (Ndemanga yapitayo yakuti “osati wakumwa waphokoso” imasonyeza kuti iye amapeŵa kugwiritsira ntchito molakwa moŵa umene kaŵirikaŵiri umatsogolera kukuchita ndewu.) Pokhala “wolingalira” (kapena, “wogonjera”), osati wolamula ndi wovuta kukondweretsa, iye samakuza nkhani zazing’ono. (1 Akorinto 9:12; Afilipi 4:5; 1 Petro 2:18) Popeza kuti mkulu saali wandewu, kapena wotetana, amapeŵa kulongolola ndipo saali “wokonda mkwiyo.”—Tito 3:2; Yakobo 1;19, 20.
22. Kodi nchiyani chimene chikusonyezedwa ndi chenicheni chakuti mkulu sayenera kukhala woumirira gwagwagwa?
22 Osati woumirira. (Tito 1:7, NW) M’lingaliro lenileni, ichi chimatanthauza “kusadzikondweretsa wekha.” (Yerekezerani ndi 2 Petro 2:10.) Mkulu sayenera kukhala woumirira gwagwagwa koma ayenera kukhala wodzichepetsa ponena za luso lake. Posalingalira kuti iye amachita zinthu bwinopo kuposa wina aliyense, modzichepetsa amagaŵana mathayo ndi ena ndipo amayamikira pochuluka aphungu.—Numeri 11:26-29; Miyambo 11:14; Aroma 12:3, 16.
23. (a) Kodi mungatanthauzire motani “wokonda ubwino”? (b) Kodi kukhala wolungama kumatanthauzanji?
23 Wokonda ubwino; wolungama. (Tito 1:8, NW) Kuti munthu ayeneretsedwe kukhala mkulu, ayenera kukonda ubwino ndi kukhala wolungama. Wokonda ubwino amakonda chimene chiri chabwino m’maso mwa Yehova, amachita ntchito zachifndo ndi zothandiza, ndipo amasonyeza chiyamikiro kaamba ka ubwino wa ena. (Luka 6:35; yerekezerani ndi Machitidwe 9:36, 39; 1 Timoteo 5:9, 10.) Kukhala wolungama kumatanthauza kugwirizana ndi malamulo a Mulungu ndi miyezo yake. Pakati pa zinthu zina, mwamuna woteroyo ngwopanda tsankhu ndipo amasumika maganizo pazinthu zolungama, zoyera, ndi zabwino. (Luka 1:6; Afilipi 4:8, 9; Yakobo 2:1-9) Popeza kuti ubwino umasiyana ndi chilungamo mchakuti umapitirira zimene chilungamo chimafunikira, wokonda ubwino amachitira ena zowonjezereka koposa zimene afunikira kuwachitira.—Mateyu 20:4, 13-15; Aroma 5:7.
24. Kodi kukhala wokhulupirika kumafunikiritsa chiyani?
24 Wokhulupirika. (Tito 1:8, NW) Mwamuna woyeneretsedwa kukhala mkulu amasunga kudzipereka kosasweka kwa Mulungu ndipo amamamatira kulamulo lake, mosasamala kanthu za mmene umphumphu wake wayesedwera. Iye amachita zimene Yehova amamyembekezera, ndipo izi zimaphatikizapo kutumikira monga wolengeza Ufumu wokhulupirika.—Mateyu 24:14; Luka 1:74, 75; Machitidwe 5:29; 1 Atesalonika 2:10.
Kuzifikira Ziyeneretsozo
25. Kodi ziyeneretso zimene zangokambitsiridwa kumene nzofunika kwa ayani, ndipo kodi ziyeneretso zoterozo zingafikiridwe motani?
25 Ziyeneretso zambiri zimene tangokambitsirana kumene zimaphatikizapo zinthu zoyembekezeredwa kwa Mboni ya Yehova iriyonse ndipo ziri zofikirika kupyolera mwa dalitso la Mulungu pa phunziro la munthu aliyense, kuyesayesa, mayanjano abwino, ndi pemphero. Anthu ena angakhale ochita bwino kwambiri m’ziyeneretso zina kuposa m’zina. Koma kumlingo woyenera, atumiki otumikira ndi akulu ayenera kuzifikira ziyeneretso zonse kaamba ka mwaŵi wawo wapadera.
26. Kodi nchifukwa ninji amuna Achikristu amadzipereka ku mathayo ampingo?
26 Mboni za Yehova zonse ziyenera kufuna kuchita chirichonse chothekera muutumiki wa Mulungu. Mzimu umenewu umasonkhezera amuna Achikristu kudzipereka okha ku mathayo ampingo. Kodi ndinu mwamuna wodzipereka, wobatizidwa? Ngati ndichoncho, kalimirani ndipo pangani kuyesayesa kulikonse kuti muyeneretsedwe kutumikira!
[Mawu a M’munsi]
a Wonaninso Nsanja ya Olonda, September 1, 1983, tsamba 30, pansi pamutu waung’ono wakuti “Chisudzulo Chamalemba.”
Kodi Mukayankha Motani?
◻ Kodi nchifukwa ninji tsopano pali kufunika kwakukulu kwa amuna obatizidwa kulandira mathayo ampingo?
◻ Kodi nziyeneretso zina ziti zimene ziyenera kufikiridwa ndi atumiki otumikira?
◻ Kodi nziyeneretso zina ziti zimene akulu ayenera kuzifikira?
◻ Kodi nchifukwa ninji mkulu ayenera kudziŵa kutsogoza bwino nyumba yake?
◻ Kodi nchiyani chimene chimasonkhezera amuna Achikristu kudzipereka ku ntchito zampingo?
[Chithunzi pamasamba 24, 25]
Akulu ndi atumiki otumikira ayenera kutsogoza mabanja awo mogwirizana ndi malamulo a makhalidwe abwino Abaibulo