Kalata Yopita kwa Tito
1 Ine Paulo, kapolo wa Mulungu ndi mtumwi wa Yesu Khristu, ndili ndi chikhulupiriro chogwirizana ndi cha anthu osankhidwa ndi Mulungu. Komanso ndikudziwa molondola choonadi chokhudza kudzipereka kwathu kwa Mulungu. 2 Zinthu zimenezi timakhala nazo chifukwa cha chiyembekezo cha moyo wosatha,+ chimene Mulungu amene sanganame+ analonjeza kalekale. 3 Koma pa nthawi yake, anachititsa kuti mawu ake adziwike kudzera mu ntchito yolalikira imene ndinapatsidwa+ mogwirizana ndi lamulo la Mpulumutsi wathu, Mulungu. 4 Ndikukulembera iwe Tito, mwana wanga weniweni amene uli ndi chikhulupiriro chofanana ndi changa:
Kukoma mtima kwakukulu ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate wathu ndi Khristu Yesu Mpulumutsi wathu, zikhale nawe.
5 Ndinakusiya ku Kerete kuti ukonze zinthu zolakwika komanso uike akulu mumzinda uliwonse, mogwirizana ndi malangizo amene ndinakupatsa. 6 Mkulu ayenera kukhala wopanda chifukwa chomunenezera, mwamuna wa mkazi mmodzi, wa ana okhulupirira ndiponso osanenezedwa kuti ndi amakhalidwe oipa kapena osalamulirika.+ 7 Popeza ndi mtumiki* wa Mulungu, woyangʼanira ayenera kukhala wopanda chifukwa chomunenezera. Asakhale womva zake zokha,+ wa mtima wapachala,+ womwa mowa mwauchidakwa, wankhanza* kapena wokonda kupeza phindu mwachinyengo. 8 Koma akhale wochereza alendo,+ wokonda zabwino, woganiza bwino,+ wolungama, wokhulupirika+ komanso wodziletsa.+ 9 Akhalenso wogwira mwamphamvu mawu okhulupirika pamene akuphunzitsa mwaluso,+ kuti athe kulimbikitsa anthu ndi mfundo zolondola+ ndiponso kudzudzula+ otsutsa.
10 Chifukwa pali anthu ambiri osalamulirika, olankhula zosathandiza ndiponso opusitsa ena, ndipo pakati pa anthu amenewa palinso amene akulimbikitsabe mdulidwe.+ 11 Anthu amenewa ndi ofunika kuwatseka pakamwa, chifukwa pofuna kupeza phindu mwachinyengo, akuwonongabe mabanja pophunzitsa zinthu zimene sayenera kuphunzitsa. 12 Mmodzi wa iwo, amenenso ndi mneneri wawo, ananena kuti: “Akerete ndi anthu abodza nthawi zonse, zilombo zolusa zakutchire ndiponso alesi osusuka.”
13 Umboni umenewu ndi woona. Chifukwa cha zimenezi, pitiriza kuwadzudzula mwamphamvu kuti akhale ndi chikhulupiriro cholimba. 14 Asamamvetsere nthano zachiyuda ndiponso kutsatira malamulo a anthu amene asiya choonadi. 15 Zinthu zonse nʼzoyera kwa anthu oyera.+ Koma kwa anthu oipitsidwa ndi opanda chikhulupiriro kulibe choyera, chifukwa maganizo awo ndi chikumbumtima chawo nʼzoipitsidwa.+ 16 Amanena poyera kuti amadziwa Mulungu, koma amamukana ndi zochita zawo+ chifukwa ndi onyansa, osamvera ndiponso osayenerera ntchito iliyonse yabwino.