Khalani Oyamikira—Ufumu Waumesiya wa Yehova Ukulamulira
“Tikuyamikani, Yehova Mulungu, Wamphamvuyonse, . . . popeza mwadzitengera mphamvu yanu yaikulu ndikuyamba kulamulira monga mfumu.”—CHIBVUMBULUTSO 11:17, “NW.”
1. Kodi nchiyani chimene prezidenti wa Watch Tower Society ananena pambuyo paulendo wake wa ku Yuropu mu 1911?
KUCHIYAMBIYAMBI kwa 1911, prezidenti wa Watch Tower Society, C. T. Russell, anapereka mpambo wa nkhani za Baibulo m’mizinda yaikulu ya Yuropu. Pothirira ndemanga paulendowo, Russell analemba mawu otsatirawa mu The Watch Tower, ya May 15, 1911: “Tinazizwa kupeza umboni wambiri wa kupita patsogolo kulikonse . . . Aŵerengi athu amadziŵa kuti kwa zaka zambiri takhala tikuyembekezera Nyengo ino kutha ndi nthaŵi ya mavuto owopsya kwenikweni, ndipo tikuwayembekezera kuwulika balamanthu mofulumira pambuyo pa October, 1914, deti limene, malinga nkumvetsetsa kwathu Malemba, mpamene Nthaŵi za Akunja—kubwerekedwa kwa ulamuliro wadziko lapansi kwa Akunja—kudzatha; chotero, idzakhalanso nthaŵi pamene ufumu wa Mesiya udzafunikira kuyamba kulamulira kwake.” Kodi chiyembekezo chimenechi chinakwaniritsidwa?
2. Kodi mtendere unawonongedwa motani mu 1914, ndipo kodi panali zotulukapo zoipa zotani?
2 M’theka loyamba la chaka cha 1914, dziko lidawonekera kukhala lachisungiko ndi losakhudzidwa ndi nkhondo. Komatu mtendere unapasulidwa mwamsanga ndi kuphedwa kwa wolowa pa mpando wachifumu wa Austria kochitidwa ndi munthu wa ku Serbia pa June 28, 1914. Austria mogwirizana ndi Hungary mwamsanga analengeza nkhondo yolimbana ndi Serbia. Russia inagwirizana ndi Serbia, chotero Jeremani nayonso inalengeza nkhondo yolimbana ndi Russia pa August 1. Pambuyo pakenso Jeremani inalengeza nkhondo yotsutsana ndi Falansa pa August 3; Greti Briteni inatero molimbana ndi Jeremani pa August 4; Montenegro molimbana ndi Austria yogwirizana ndi Hungary pa August 7; Japan molimbana ndi Jeremani pa August 23; Austria yogwirizana ndi Hungary molimbana ndi Belgium pa August 28. Ambiri anakhulupirira kuti nkhondoyo ikatha posachedwa. Mmalo mwake, iyo inakula kukhala nkhondo yoipitsitsa m’mbiri yadziko panthaŵiyo, yokhala ndi maiko 19 ophatikizidwa m’kukhetsa mwazi kwankhaninkhani kwa mitundu yonse kumene kunapha miyoyo ya asilikali ndi anthu wamba oposa 13,000,000, ndi anthu olemazidwa ndi kuvulazidwa oposa 21,000,000.
3, 4. Kodi chinachitika nchiyani pamalikulu a Sosaite pa Lachisanu m’mawa, October 2, 1914?
3 Pa Lachisanu m’mawa, October 2, 1914, Russell analengeza kwa ogwira ntchito pa malikulu a Watch Tower Society mu Brooklyn, New York kuti: “Nthaŵi za Akunja zatha; mafumu awo akhalatu nayo nthaŵi yawo.” Ichi chinalandiridwa ndi kuomba m’manja kochititsa chidwi kwa banja la Beteli, “nyumba ya Mulungu.”
4 Kodi nkulungamitsika kotani kumene C. T. Russell ndi anzake anali nako kokhalira achimwemwe chotero m’mawa mwa October m’menemo? Kodi mawu akutiwo “Nthaŵi za Akunja” anachokera kuti? Kodi ndiumboni wotani umene ulipo wakuti Nthaŵi za Akunja zinatha mu October 1914? Ndipo kodi chimenechi chiyenera kukuyambukirani motani?
Yerusalemu ndi Nthaŵi za Akunja
5. Kodi mawu akuti “Nthaŵi za Akunja” anayambira kuti?
5 Mawu akutiwo “Nthaŵi za Akunja,” kapena “nthaŵi zoikika za amitundu,” amachokera muulosi waukulu wa Yesu wonena za kuwonongedwa kwa Yerusalemu. (Luka 21:5-36, King James Version) Masiku aŵiri Yesu asanaupereke, anadzionetsera yekha kwa nzika za Yerusalemu monga Mesiya wawo. Pamene anakwera pa buru modzichepetsa nalowa mumzinda, makamu a Ayuda anafuula mwachipambano, monga mmene Zekariya 9:9 ananeneratu. “Wolemekezeka Mfumuyo ikudza m’dzina la [Yehova, NW],” iwo anafuula tero.—Luka 19:28-40.
6, 7. Kodi ndi liwongo lamwazi loipa lotani limene anthu a ku Yudeya a m’zaka za zana loyamba anadzibweretsera, ndipo ndi zotulukapo zotani?
6 Koma Yesu anadziŵa kuti lingaliro la khamu la anthulo likasokeretsedwa posachedwa natsutsana naye chifukwa cha chidani chakupha chosonyezedwa ndi atsogoleri achipembedzo a mu Yerusalemu mosonkhezeredwa ndi atate wawo, Mdyerekezi. (Genesis 3:15; Yohane 8:44) Mosataya nthaŵi pambuyo pake, pa Nisan 14, khamu la Ayuda linaphokosera mwaukali kufuna kuti Yesu aphedwe. ‘Mwazi wake uli pa ife ndi pa ana athu,’ iwo anafuula tero kwa kazembe wa Roma wozengerezayo. (Mateyu 27:24, 25) Mmalo mwa kumuvomereza Yesu kukhala Mfumu Yaumesiya, akulu a ansembe analengeza kuti: “Tiribe Mfumu koma Kaisara.” (Yohane 19:15) Pambuyo pake Mesiya weniweniyo anakhomeredwa pamtengo wozunzirapo kuti afe, pokhala atazengedwa mlandu mwachinyengo kukhala wogalukira Roma ndi wochitira mwano Mulungu wa Ayuda.—Marko 14:61-64; Luka 23:2; Yohane 18:36; 19:7.
7 Mkwiyo wa Mulungu udali wotsimikizira kudza pa nzika za Yudeya chifukwa cha liwongo lawo loipa lamwazi. Yerusalemu, ndi kachisi yake yaikuluyo, sakatchedwanso ‘mzinda wa Mfumu yaikulu,’ Yehova. (Mateyu 5:35; Luka 13:33-35) Masiku angapo Yesu asanafe, ophunzira ake anathirira ndemanga zokhumbira nyumba ya kachisi ya mzindawo. Powayankha, Yesu analosera kuti: ‘Zinthu izi muziona, adzafika masiku, pamenepo sudzasiyidwa pano mwala pa mwala unzake, umene sudzagwetsedwa.’—Luka 21:5, 6.
8. Pamene Yesu anapereka ‘chizindikiro’ cha zochitika zotsogolera ku kuwonongedwa kwa Yerusalemu, kodi nchiyaninso chinaphatikizidwa?
8 Atazizwitsidwa ophunzira a Yesu anamfunsa iye nati: ‘Mphunzitsi, nanga zinthu izi zidzaoneka liti? Ndipo chizindikiro nchiyani pamene izi ziti zichitike?’ (Luka 21:7) Powayankha Yesu ananeneratu molongosoka zochitika zimene zinatsogolera kuwonongedwa kwa Yerusalemu, ndipo iye anawonjezera mawu apadera awa: “Akunjawo adzapondereza Yerusalemu, kufikira nthaŵi za Akunja zitakwanira.” (Luka 21:8-24, KJ) Chotero Yesu anasonya ku chinthu chinachake kutsogolo choposa chiwonongeko cha Yerusalemu—chomwe chinafunikira kuyembekezera “kufikira nthaŵi za Akunja zitakwanira.” Ponena za ‘chizindikiro,’ Yesu anati: ‘Pakuwona zinthu izi zirikuchitika, zindikirani kuti Ufumu wa Mulungu uli pafupi.’ (Luka 21:31) Chotero, chizindikirocho chinafunikira kukwaniritsidwa kaŵiri. Kukwaniritsidwa koyamba, kapena kwapang’ono, kukasonyeza kuti ‘chipululutso cha Yerusalemu chayandikira.’ (Luka 21:20) Kukwaniritsidwa kwachiŵiri, ndipo kwakukulu, kukachitika Nthaŵi za Akunja zitatha, ndipo kukasonyeza kuti “ufumu wa Mulungu uli pafupi.”—Yerekezerani ndi Mateyu 24:3.
Yerusalemu wa Padziko Lapansi Alowedwa Mmalo ndi Mzinda Waukulu
9. Kodi ndiliti pamene Yerusalemu wa padziko lapansi anataikiridwa malo ake oyanjika, ndipo kodi iye walowedwa mmalo ndi chiyani?
9 Mwa kunena kuti “Yerusalemu adzaponderezedwa ndi amitundu, kufikira nthaŵi zoikidwiratu za amitundu zitakwanira,” (NW) kodi Yesu anali kupereka lingaliro lakuti mzinda wa padziko lapansiwo ukabwezeretsedwa pambuyo pake kuchiyanjo cha Mulungu? Ayi. Pambuyo pa kuphedwa kwa Mwana wokondedwa wa Mulungu, Yerusalemu wapadziko lapansi anataikidwiratu malo ake apaderawa ndipotu walowedwa mmalo ndi “mzinda wa Mulungu wamoyo, Yerusalemu wakumwamba” waukulu zedi.—Ahebri 12:22, NW; Mateyu 23:37, 38; 27:50, 51.
10. Kodi chikutanthauzidwa nchiyani ndi mawu akuti “Yerusalemu wakumwamba”?
10 Mawu akutiwo “Yerusalemu wakumwamba” agwiritsiridwa ntchito m’Baibulo kufotokoza Ufumu wakumwamba wosakhoza kuwonongedwa komwe kwaitanidwira Akristu odzozedwa.a (Ahebri 11:10; 12:22, 28) Pamene mtumwi Paulo analemba mawuwa, mzinda wa padziko lapansi ndi kachisi wake udali udakakhumbiridwabe ndi Ayuda. Motero, Paulo anawakumbutsa Akristu Achihebri kuti “pakuti pano tiribe [mzinda, NW] wokhalitsa, komatu tifunafuna ulinkudzawo.”—Ahebri 13:14.
Chifukwa Chimene Ukutchedwera Yerusalemu Wakumwamba
11. Kufikira pamene Yerusalemu wa padziko lapansi anataikiridwa chiyanjo chake, kodi iye ankaimiranji?
11 Yerusalemu udali mzinda waukulu wa mtundu wa Israyeli kwanthaŵi yaitali, amene mafumu ake adanenedwa kuti ankakhala ‘pa mpando wachifumu wa Yehova.’ (1 Mbiri 29:23) Ndiponso, Yehova anapanga pangano ndi Davide kuti ufumuwo ukakhalabe m’banja lake kosatha. Monga mmene zikukhalira ndi malikulu amakono, monga ngati Washington, Moscow, Canberra, ndi Pretoria, akugwiritsiridwa ntchito kuzindikiritsa maboma awo osiyanasiyana, m’momwemonse kuti Yerusalemu akugwiritsiridwa ntchito m’Baibulo kuimira ufumu wa Davide.—2 Samueli 7:16; Luka 1:32.
12. Kodi mawu akutiwo “Nthaŵi za Akunja” ayenera kugwiritsiridwa motani?
12 Ufumu wa Davide unali ndi miraga yochepa, udafutukulidwira kumalire opatsidwa ndi Mulungu okha kwa Israyeli wakale. Chotero Yerusalemu wa padziko lapansi adali chithunzi chokha cha Ufumu Waumesiya weniweni womwe ukalamulira kuchokera kumwamba ndi kukhala nalo dziko lonse lapansi monga miraga yake. (Salmo 2:2, 7, 8; Danieli 7:13, 14; 2 Timoteo 4:18) Chotero, bukhu lakuti The Time Is At Hand, lofalitsidwa ndi Watch Tower Society mu 1889, mosabisa linanena kuti: “Mawu akuti ‘Nthaŵi za Akunja’ anagwiritsiridwa ntchito ndi Ambuye wathu kutanthauza mbiri yochitika panyengo ija yokhala pakati pa kuchotsedwa kwa Ufumu wenieni wa Mulungu, Ufumu wa Israyeli (Ezek. 21:25-27), ndi kuyambika ndi kukhazikitsidwa kwa unzake wa uwu, Ufumu woona wa Mulungu.”
Nthaŵi za Akunja—Kodi Nzautali Wotani?
13. Kodi Nthaŵi za Akunja zinayamba liti, ndipo kodi mukuyankhiranji tero?
13 Ufumu weniweni wa Mulungu unagwetsedwa ndi mfumu Nebukadinezara ya ku Babulo mu 607 B.C.E. Pamwezi wa chisanu ndi chiŵiri Wachiyuda, pafupifupi chapakati pa October, dzikolo lidali bwinja.b (2 Mafumu 25:8, 9, 22, 25, 26) Kutsimikizira kuti ichi chidachitika ndi chilolezo chaumulungu, Yehova Mulungu anampatsa loto Nebukadinezara. Ilo lidali la mtengo umene unalikhidwa ndikuloledwa kuphukanso pambuyo pa nyengo ya “nthawi zisanu ndi ziwiri.” Lotoli kukwaniritsidwa kwake koyamba kudali pamene Nebukadinezara anabwezeretsedwa ku mpando wake wachifumu pambuyo pa nyengo yochepa ya kukhala wopenga.—Danieli 4:10-17, 28-36.
14. Kodi ndiiti imene inali mfundo yaikulu ya loto la Nebukadinezara?
14 Komabe, mutu wa loto la Nebukadinezara unasonyeza kuti kukwaniritsidwa kwake kwakukulu kunaphatikizapo ufumu weniweni wa Mulungu, umene mfumu Yakunjayi inaloledwa ‘kuwulikha.’ Lotolo linamalizidwa ndi ndemanga yodzala ndi chifuno iyi: “Kuti amoyo adziwe kuti Wam’mwambamwamba alamulira m’ufumu wa anthu, naupereka kwa ali yense Iye afuna, nauutsira [wodzichepetsa mwa, NW] anthu.”—Danieli 4:17.
15. Kodi ndimotani mmene Yesu Kristu anayenerera kukhala “wodzichepetsa mwa anthu”? (Mateyu 11:29, NW)
15 Ndimunthu mmodzi yekha amene anadzayenerera m’mbali zonse kutchedwa “wodzichepetsa mwa anthu.” Mwana wobadwa yekha wa Mulungu anadzitsimikizira yekha kukhala munthuyu mwa kuusiya ulemerero wake wakumwamba mofunitsitsa nabadwa monga munthu, monga Yesu, amene anavutika ndi imfa yonyozeka ndi yankhanza kwenikweni pamanja a Satana. (Afilipi 2:3, 5-11) Pambuyo pa kuukitsidwa kwake ndikubwerera kuulemerero wakumwamba, Yesu adafunikira kuyembekezera kufikira nyengo ya nthaŵi zisanu ndi ziŵiri za kulamulira kwa Akunja zitatha asanaikidwe pampando wachifumu monga Mfumu Yaumesiya ya anthu.—Ahebri 10:12, 13.
16. Kodi ndimotani mmene bukhu la Chibvumbulutso likuthandizira Akristu kupenda pamene nthaŵi zisanu ndi ziŵiri zinatha?
16 Koma kodi Mboni za Yehova zinauzindikira motani utali wa nthaŵi zisanu ndi ziŵiriwu? Baibulo limavumbula kuti “nthawi, ndi zinthawi, ndi nusu la nthawi,” kapena nthaŵi zitatu ndi nusu, ziri ndi chiwonkhetso cha masiku 1,260. (Chibvumbulutso 12:6, 14) Chotero, chiŵerengerochi chitawonkhetsedwa kaŵiri, kapena nthaŵi zisanu ndi ziŵiri, chikafikira kuchiwonkhetso cha masiku 2,520. Pamaziko a chitsogozo chaulosi a ‘kuliyesa tsiku limodzi ngati chaka chimodzi,’ nthaŵi zisanu ndi ziŵirizi zikafikira chiwonkhetso cha zaka 2,520. (Numeri 14:34; Ezekieli 4:6) Mwa kutsatira kupendaku, Nthaŵi za Akunja, zimene zinayambira mu October 607 B.C.E., zinadzatha pambuyo pa zaka 2,520 mu October 1914.
17. Kodi nchilengezo chosangalatsa chotani chimene chidali pafupi kupangidwa mu 1914?
17 Mu October 1914, Yehova Mulungu anaika Mwana wake wokondedwa, Ambuye Yesu Kristu, pampando wachifumu mu Ufumu wakumwamba. Pomalizira, masomphenya a Chibvumbulutso a mtumwi Yohane Wachikristu anayamba kukwaniritsidwa, ndipo chilengezo chikapangidwa chakuti: ‘Ufumu wa dziko lapansi wayamba kukhala wa Ambuye wathu [Yehova], ndi wa Kristu wake; ndipo [Yehova] adzachita ufumu kufikira nthawi za nthawi.’ (Chibvumbulutso 1:10; 4:1; 11:15) Ndi mbiri yaulemerero chotani nanga imeneyi ndipo nchodzetsa chimwemwe chotani nanga kumbali ya olowa nyumba onse ndi nzika za Ufumuwo!—Chibvumbulutso 11:17.
18. Kodi nchifukwa ninji mikhalidwe yachisoni yakantha anthu chiyambire 1914?
18 Zowonadi, kwa anthu ambiri, sipanakhalepo chimwemwe chochuluka padziko lapansi chiyambire 1914. Koma mkhalidwe watsoka padziko lapansili ndiwo chitsimikiziro chakuti kulamulira kwa Satana kuli pafupi kutha. Kodi tadziŵa bwanji? Bukhu la Chibvumbulutso linasonyeza kuti kukhazikitsidwa kwa Ufumu wa Mulungu kukatulukapo nkhondo m’mwamba. Satana ndi ziŵanda zake adafunikira kutulutsidwa kumwamba ndikuponyedwera kufupi ndi dziko lathu lapansi. Pambuyo powona kulakikaku m’masomphenya aulosi, Yohane anamva mawu ofuula akumati: ‘Kondwerani, miyamba inu, ndi inu akukhala momwemo. Tsoka mtunda ndi nyanja, chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo udani waukulu, podziwa kuti kamtsalira kanthawi.’—Chibvumbulutso 12:1-12.
19. Kodi nchifukwa ninji Akristu owona ali oyamikira kwenikweni kukhalapo ndi moyo m’nthaŵi ino?
19 Mikhalidwe yadziko yomaipaipabe chiyambire 1914 ili chitsimikiziro chakuti masomphenya a Yohane akwaniritsidwa ndikuti mapeto a anthu onse amene amakana kugonjera ku ufumu wa Mulungu akuyandikira pafupi moipa. (Luka 21:10, 11, 25-32) Nkosangalatsa chotani nanga kukhala ndi moyo m’nthaŵi yodabwitsayi pamene Yehova Mulungu, Wamphamvuyonse, adzathetsa nkhani yaikulu ya ufumu wake padziko lapansi! Kenaka, dziko lapansi lidzasinthidwa kukhala paradaiso wokongola, ndipo anthu olungama opulumuka adzakwezedwa kukhala angwiro. Ngakhale akufa adzaukitsidwa ndikupatsidwa mwaŵi wa kuyenerera kaamba ka moyo wosatha.—Chibvumbulutso 20:1-3, 12, 13; 21:3-5.
Kufunikira Kuwongolera Kwamakono
20. (a) Kodi ndani amene anatsimikizira kukhala atumiki owona ovomerezedwa ndi Yehova padziko lapansi 1914 isanadze? (b) Kodi ndi kuwongolera kotani kumene Akristu okhulupirika odzozedwa anali ofunitsitsa kupanga?
20 Kwa zaka 38 isanadze 1914, Ophunzira Baibulo, monga mmene Mboni za Yehova zinkatchedwera nthaŵiyo, anasonya ku deti limenelo kukhala chaka chimene Nthaŵi za Akunja zikatha.c Ndichitsimikiziro chotani nanga chakuti iwo adali atumiki owona a Yehova! Komabe, mofanana ndi atumiki a Mulungu a m’zaka za zana loyamba, iwo adali nazonso ziyembekezo zolakwika. Mwachitsanzo, iwo anayembekezera kuti Akristu odzozedwa m’chiŵerengero chokwanira akadzutsidwira kumwamba itafika October 1914. Iwo anaganizanso kuti nkhondo imene inayambira mu 1914 ikatsogolera mwachindunji mpaka kukafika kumapeto a dziko la Satana.
21. Kodi ndi kulangidwa kotani kumene Akristu owona anakumana nako m’Nkhondo Yadziko ya I?
21 Komabe, m’kupita kwanthaŵi, Akristu odzozedwa anazindikira kuti padali ntchito yambiri yoti iwo aichite padziko lapansi. Chifukwa cha kulimbikira kwawo kuchitira umboni kwapoyera m’nthaŵi ya Nkhondo Yadziko ya I, iwo anakumana ndi chizunzo chokakala kuchokera kwa akuluakulu a ndale zadziko, osonkhezeredwa ndi atsogoleri a chipembedzo a Chikristu Chadziko. (Salmo 2:1-6) Ntchito ya Akristu owona inakanthidwa ndi nkhonya yamphamvu pa June 21, 1918, pamene akuluakulu otsogolera a Watch Tower Society mu United States anazengedwa mlandu wonyenga ndikuweruzidwa kukhala m’ndende kwa zaka 20.
22, 23. (a) Kodi Akristu okhulupirika odzozedwa achitanji chiyambire 1919, ndipo ndikukwaniritsidwa kotani kwa mbali ziŵiri? (b) Kodi mnzake wa Yerusalemu wosakhulupirika ndiuti?
22 Nkhondo Yadziko ya I inatha mwadzidzidzi mu November 1918. Kenaka, pa March 25, 1919, akuluakulu a Watch Tower Society anatulutsidwa m’ndende. Iwo anamasulidwiratu pambuyo pake. Nyengo ya mtendere yosayembekezeredwa inawatsegukira Akristu okhulupirika odzozedwawa, yofanana ndi mwaŵi umene unawonekera wokha kwa ophunzira oyambirira a Kristu pambuyo pa kupatsidwa kwawo mphamvu ndi mzimu woyera mu 33 C.E.—Machitidwe 2:17-21, 41.
23 Chiyambire 1919, Akristu okhulupirika odzozedwa monga gulu amvera mwachangu lamulo lophatikizidwa m’mawu a Yesu pa Mateyu 24:14, (NW) akuti: “Mbiri yabwino imeneyi ya ufumu idzalalikidwa m’dziko lonse lokhalidwa ndi anthu kaamba ka umboni kwa mitundu yonse; ndipo pomwepo mapeto adzafika.” Monga chotulukapo, pafupifupi mamiliyoni anayi a “nkhosa zina” za Kristu adzipereka kutumikira Yehova mogwirizana ndi otsalira odzozedwa. (Yohane 10:16) Chikristu Chadziko, mosonkhezeredwa ndi atsogoleri ake achipembedzo, chikupitirizabe kukana uthenga Waufumu. Kusankhapo kwake machenjera andale zadziko aanthu ndi kuzunza kwake Mboni za Yehova kumafanana ndi kuchitiridwa moipa kwa Kristu pamanja a nzika za Yudeya wa m’zaka za zana loyamba. Mongadi mmene Yehova anaperekera chiweruzo pa Yerusalemu, iye adzateronso kwa Yerusalemu mnzake wosakhulupirika, wotchedwa, Chikristu Chadziko. Ndipo monga mmene mbadwo umene unamva uthenga wa chiweruzo wa Kristu unakhalapobe ndi moyo kuwona chiwonongeko chimene iye anachineneratucho, choteronso mbadwo wamakono womwe udalipo mu 1914 ‘sudzatha kuchoka’ ‘chisautso chachikulu’ chonenedweratucho chisanadze.—Mateyu 24:21, 22, 34.
24. Kuti tipulumuke kulowa m’dziko latsopano la Mulungu, kodi tiyenera kuchitanji?
24 Kodi tiyenera kuchitanji kuti tipulumuke chisautso chachikulu ndikukhalapobe ndi moyo kulowa m’dziko latsopano la Mulungu? Mosasamala kanthu za ziyembekezo zolakwika zimene aliyense wa ife angakhale adali nazo, tiyenera kupewa kugwera mtulo ponena za mathayo athu Achikristu. (Habakuku 2:3; 1 Atesalonika 5:1-6) Awo okhoza kukumbukira zochitika chiyambire 1914 akucheperacheperabe. Chotero, tiyenera kukhala ogalamuka; palibetu nthaŵi yoti tiwononge. (Mateyu 24:42) Onse amene akufuna kupulumuka mapeto a dziko loipa la Satana ayenera kuchitapo kanthu tsopano m’njira imene imamvana ndi mawu ouziridwa awa: “Tikuyamikani, Yehova Mulungu, Wamphamvuyonse, . . . popeza mwadzitengera mphamvu yanu yaikulu ndikuyamba kulamulira monga mfumu.”—Chibvumbulutso 11:17, NW.
[Mawu a M’munsi]
a Onani Nsanja ya Olonda ya September 1, 1983, tsamba 21.
b Kaamba ka chidziŵitso chowonjezereka chonena za chifukwa chimene ichi chimazindikiritsa kuyambika kwa Nthaŵi za Akunja, onani bukhu la “Let Your Kingdom Come,” mutu 14, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
c C. T. Russell analemba nkhani yokhala ndi mutu wakuti: “Nthaŵi za Akunja: Kodi Zidzatha Liti?,” imene inafalitsidwa m’magazine otchedwa Bible Examiner, October 1876. Patsamba 27, nkhaniyo inati: “Nthaŵi zisanu ndi ziŵiri zidzatha mu A.D. 1914.”
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi Yerusalemu wakale anaimiranji, koma kodi anataikiridwa motani malo ake olemekezedwa?
◻ Kodi ndiliti pamene Nthaŵi za Akunja zinayamba ndi kutha, ndipo ndi chotulukapo chonenedweratu chotani?
◻ Kodi nchiyani chimene chiwonongeko cha Yerusalemu wosakhulupirika chinachitira chithunzi?
◻ Kodi tikudziwa bwanji kuti chisautso chachikulu chiri pafupi, ndipo kodi tiyenera kuchitanji kuti tipulumuke?
[Chithunzi patsamba 16]
Yerusalemu ndi kachisi wake anataikiridwa malo ake olemekezeka, koma Mulungu anapitirizabe kudalitsa Mwana wake, Mesiya, ndikulankhuladi naye mwachindunji kuchokera kumwamba