Chivumbulutso Chimene Yohane Analandira
4 Zimenezi zitatha, ndinayangʼana kumwamba ndipo ndinaona khomo lotseguka. Mawu oyamba amene ndinamva akundilankhula anali ngati kulira kwa lipenga. Mawuwo anali akuti: “Kwera kumwamba kuno ndipo ndikuonetsa zinthu zimene zikuyenera kuchitika.” 2 Kenako nthawi yomweyo mzimu wa Mulungu unayamba kugwira ntchito mwa ine ndipo mpando wachifumu unaoneka uli pamalo ake kumwamba, wina atakhalapo.+ 3 Amene anakhala pampandoyo ankaoneka ngati mwala wa yasipi+ komanso mwala wa sadiyo.* Utawaleza wooneka ngati mwala wa emarodi unazungulira mpando wachifumuwo.+
4 Kuzungulira mpando wachifumuwo panalinso mipando yachifumu yokwana 24. Pamipando yachifumuyo, ndinaona patakhala akulu 24+ atavala zovala zoyera komanso zisoti zachifumu zagolide kumutu kwawo. 5 Kumpando wachifumuko kunkatuluka mphezi,+ mawu komanso mabingu.+ Panalinso nyale zamoto 7 zimene zinkayaka patsogolo pa mpando wachifumuwo. Nyalezo zikuimira mizimu 7 ya Mulungu.+ 6 Patsogolo pa mpando wachifumuwo, panali chinachake chooneka ngati nyanja ya galasi+ komanso ngati mwala wa kulusitalo.
Pakati pa mpando wachifumuwo ndiponso kuzungulira mpandowo, panali angelo 4+ amene anali ndi maso ambirimbiri, kutsogolo ndi kumbuyo komwe. 7 Mngelo woyamba ankaoneka ngati mkango.+ Mngelo wachiwiri ankaoneka ngati mwana wa ngʼombe wamphongo.+ Mngelo wachitatu+ anali ndi nkhope yooneka ngati ya munthu ndipo mngelo wa 4+ ankaoneka ngati chiwombankhanga chimene chikuuluka.+ 8 Aliyense wa angelo 4 amenewa anali ndi mapiko 6 ndipo mapikowo anali ndi maso paliponse.+ Angelo amenewa sankapuma masana ndi usiku, ankangokhalira kunena kuti: “Woyera, woyera, woyera ndi Yehova*+ Mulungu, Wamphamvuyonse, amene analipo, amene alipo ndi amene akubwera.”+
9 Nthawi zonse angelowo akamapereka ulemerero ndi ulemu ndiponso akamayamikira Mulungu amene wakhala pampando wachifumuyo, Amene adzakhale ndi moyo kwamuyaya,+ 10 akulu 24 aja+ ankagwada nʼkuwerama pamaso pa Amene wakhala pampando wachifumuyo, nʼkulambira Amene adzakhale ndi moyo kwamuyayayo. Iwo ankaponya pansi zisoti zawo zachifumu pamaso pa mpando wachifumuwo nʼkunena kuti: 11 “Ndinu woyenera, inu Yehova* Mulungu wathu kulandira ulemerero,+ ulemu+ ndi mphamvu+ chifukwa munalenga zinthu zonse+ ndipo mwa kufuna kwanu, zinakhalapo ndipo zinalengedwa.”