Kodi Mudzalabadira ku Chikondi cha Yesu?
‘Chikondi cha Kristu chitikakamiza.’—2 AKORINTO 5:14.
1. Kodi tingachilongosole motani chikondi cha Yesu?
NDITHUDI, nchopambana chotani nanga chikondi cha Yesu! Tikalingalira mmene anavutikira kosaneneka pamene ankapereka dipo, limene kupyolera mwa ilo lokha titha kupeza moyo wosatha, kunena zowona mitima yathu isefukira ndi chiyamikiro kwa iye! Yehova Mulungu ndi Yesu iyemwini ndiwo anayamba kuchitapo kanthu. Ndiwo anayamba kutikonda, pamene tidali ochimwa. (Aroma 5:6-8; 1 Yohane 4:9-11) Kudziŵa ‘chikondi cha Kristu,’ analemba tero mtumwi Paulo, ‘kuposa mazindikiridwe.’ (Aefeso 3:19) Ndithudi, chikondi cha Yesu chimapambana luntha la chidziŵitso cha munthu. Chimaposa chirichonse chimene anthu anawonapo kapena kukhalapo nacho.
2. Kodi nchiyani chimene sichingamlepheretse Yesu kutikonda?
2 Polembera Akristu a ku Roma, Paulo anafunsa kuti: ‘Adzatisiyanitsa ndani ndi chikondi cha Kristu? Nsautso kodi, kapena kupsinjika mtima, kapena kuzunza, kapena njala, kapena usiŵa, kapena zowopsa kapena lupanga kodi?’ Palibe chirichonse cha zinthuzi chingalepheretse Yesu kutikonda. ‘Ndakopeka mtima,’ akupitiriza motero Paulo, ‘kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu ziripo, ngakhale zinthu zirinkhudza, ngakhale zimphamvu, ngakhale utali, ngakhale kuya, ngakhale cholengedwa china chirichonse, sichingadzakhoze kutisiyanitsa ife ndi chikondi cha Mulungu, chimene chiri mwa Kristu Yesu Ambuye wathu.’—Aroma 8:35-39.
3. Kodi nchiyani chokha chimene chingapangitse Yesu ndi Atate wake kutisiya?
3 Chikondi cha Yehova Mulungu ndi Yesu pa inu nchachikuludi motero. Pali chinthu chimodzi chokha chimene chingawaletse kukukondani, ndicho kukana kwanu kwadala chikondi chawo mwakukana kuchita zimene akupemphani. Panthaŵi ina mneneri wa Mulungu anauza Mfumu ya Yuda kuti: ‘Yehova ali nanu; mukakhala ndi iye, mukamfuna iye, mudzampeza; koma mukamsiya, adzakusiyani.’ (2 Mbiri 15:2) Kodi ndani wa ife amene akafuna konse kutaya mabwenzi abwino achifundo oterowo, Yehova Mulungu ndi Mwana wake, Yesu Kristu?
Kulabadira Kwabwino ku Chikondi cha Yesu
4, 5. (a) Kodi chikondi cha Yesu pa ife chiyenera kusonkhezera motani maunansi anthu ndi anthu anzathu? (b) Kodi ndaninso amene tiyenera kukonda chifukwa cha chikondi cha Yesu pa ife?
4 Kodi inu panokha mumakhudzidwa motani ndi chikondi chachikulucho cha Yesu pa inu? Kodi muyenera kukhala wotani? Eya, Yesu anasonyeza mmene chitsanzo chake cha chikondi chiyenera kuyambukirira unansi wathu ndi anthu anzathu. Atatumikira atumwi ake modzichepetsa mwakusambitsa mapazi awo, Yesu anati: ‘Ndakupatsani inu chitsanzo, kuti, monga ine ndakuchitirani inu, inunso muchite.’ Nawonjezera kuti: ‘Ndikupatsani inu lamulo latsopano, kuti mukondane wina ndi mnzake; monga ndakonda inu, kuti inunso mukondane wina ndi mnzake.’ (Yohane 13:15, 34) Ophunzira ake anadziŵa, ndipo anasonkhezeredwa kuyesayesa kuchita monga momwe iye anachitira. ‘Umo tizindikira chikondi,’ analemba tero mtumwi Yohane, ‘popeza iyeyu anapereka moyo wake chifukwa cha ife; ndipo ife tiyenera kupereka moyo wathu chifukwa cha abale.’—1 Yohane 3:16.
5 Chikhalirechobe, tikhoza kuchiphonya chifuno cha moyo wa Yesu ndi uminisitala wake ngati chitsanzo chake chingotisonkhezera kukonda ena ndi kuthandiza anthu anzathu basi. Kodi chikondi cha Yesu sichiyenera kutipangitsa ifenso kumkonda iye makamaka kukonda Atate wake, amene adamphunzitsa zonse zimene iye adziŵa? Kodi mudzalabadira ku chikondi cha Kristu ndi kutumikira Atate wake mmene iye anachitira?—Aefeso 5:1, 2; 1 Petro 1:8, 9.
6. Kodi mtumwi Paulo anayambukiridwa motani ndi chikondi cha Yesu pa iye?
6 Talingalirani nkhani ya Saulo, yemwe pambuyo pake anadzatchedwa Paulo. Panthaŵi ina iye ankazunza Yesu, ‘kupumira pa akuphunzira . . . kuwopsa ndi kupha.’ (Machitidwe 9:1-5; Mateyu 25:37-40) Pamene Paulo anadzamdziŵadi Yesu, anayamikira kwambiri kaamba ka kukhululukidwa kwake kwakuti anali wofunitsitsa osati kuvutikira Yesu kokha komanso analinso wokonzekera kumfera iye. ‘Ndinapachikidwa ndi Kristu,’ analemba tero iye. ‘Ndili ndi moyo; wosatinso ine ayi . . . koma moyo umene ndili nawo tsopano m’thupi, ndili nawo m’chikhulupiriro cha Mwana wa Mulungu, amene anandikonda, nadzipereka yekha chifukwa cha ine.’—Agalatiya 2:20.
7. Kodi chikondi cha Yesu chiyenera kutisonkhezera kuchitanji?
7 Ha, chikondi cha Yesu pa ife chiyenera kukhala mphamvu yosonkhezera chotani nanga m’miyoyo yathu! ‘Chikondi cha Kristu chitikakamiza,’ nzimene Paulo analembera Akorinto, ‘kuti iwo akukhala ndi moyo asakhalenso ndi moyo kwa iwo okha, koma kwa iye amene adawafera iwo, nauka.’ (2 Akorinto 5:14, 15) Indedi, chiyamikiro chathu kwa Yesu kaamba ka kupereka moyo wake mmalo mwathu chiyenera kutisonkhezera kuchita chirichonse chimene atipempha. Iyi ndiyo njira yokha imene tingatsimikizirire kuti timamkondadi iye. ‘Ngati mukonda ine, sungani malamulo anga,’ anatero Yesu. ‘Iye wakukhala nawo malamulo anga, ndi kuwasunga, iyeyu ndiye wondikonda ine.’—Yohane 14:15, 21; yerekezerani ndi 1 Yohane 2:3-5.
8. Kodi chikondi cha Yesu chayambukira motani miyoyo ya ochita zoipa ambiri?
8 Pamene anaphunzira malamulo a Yesu, adama, achigololo, ogonana ofanana ziŵalo, mbala, zidakwa, ndi olanda a m’Korinto wakale analabadira ku chikondi cha Yesu mwakuleka machitachita amenewo. Paulo anawalembera kuti: “Munasambitsidwa, . . . munayesedwa olungama, m’dzina la Ambuye Yesu Kristu.” (1 Akorinto 6:9-11) Mofananamo, chikondi cha Yesu chasonkhezera ambiri lerolino kupanga masinthidwe aakulu m’miyoyo yawo. “Zipambano zenizeni za Chikristu zinawonekera m’kusintha anthu amene anatsatira ziphunzitso zake kukhala abwino,” analemba tero wolemba mbiri John Lord. “Tili nawo umboni wa miyoyo yawo yopanda liŵongo, makhalidwe awo opanda chitonzo, unzika wawo wabwino, ndi maubwino awo Achikristu.” Ha, ziphunzitso za Yesu zinali zosiyana chotani nanga!
9. Kodi kumvetsera Yesu kumaphatikizapo chiyani?
9 Kunena zowona, palibe maphunziro amene munthu angachite lerolino oposa a moyo ndi uminisitala za Yesu Kristu. ‘Yang’anitsitsani dwii pa . . . Yesu,’ analangiza tero mtumwi Paulo. ‘Ndithudi, mlingalireni mosamalitsa [ameneyo].’ (Ahebri 12:2, 3, NW) Pakusandulika kwa Yesu, Mulungu iyemwini analamula ponena za Mwana wake kuti: “Mverani Iye.” (Mateyu 17:5) Ngakhale nditero, tiyenera kugogomezera kuti kumvetsera Yesu kumaphatikizapo zoposa kumva zimene amanena. Kumatanthauza kulabadira malangizo ake, inde, kumtsanzira mwakuchita zimene anachita m’njira imene anazichitira. Timalabadira ku chikondi cha Yesu mwakumtengera monga chitsanzo chathu, mwakutsatira mosamalitsa m’mapazi ake.
Zimene Yesu Amafuna Kuti Tichite
10. Kodi Yesu anaphunzitsa yani ntchito ndipo ndi chifuno chotani?
10 Ntchito ya Yesu yopatsidwa ndi Mulungu inali yakulalikira ponena za Ufumu wa Atate wake, ndipo anaphunzitsa otsatira ake kuchita ntchito yofananayo. “Tiyeni kwina,” iye anauza ophunzira ake oyamba, ‘kuti ndilalikire komwekonso; pakuti ndadzera ntchito imeneyo.’ (Marko 1:38; Luka 4:43) Pambuyo pake, atawaphunzitsa mofikapo atumwi 12, Yesu anawalangiza kuti: ‘Ndipo pamene mulikupita lalikani kuti, Ufumu wakumwamba wayandikira.’ (Mateyu 10:7) Miyezi ingapo pambuyo pake, apo nkuti ataphunzitsa kale ena 70, anawatumiza nawalamula kuti: ‘Munene nawo, Ufumu wa Mulungu wayandikira.’ (Luka 10:9) Nzowonekeratu kuti, Yesu anafuna ophunzira ake kukhala alaliki ndi aphunzitsi.
11. (a) Kodi ndimotani mmene ophunzira a Yesu akachitira ntchito zoposa zimene iye anachita? (b) Kodi nchiyani chinachitika kwa ophunzira pamene Yesu anaphedwa?
11 Yesu anapitiriza kuphunzitsa ophunzira ake ntchito imeneyi. Pamadzulo omalizira imfa yake isanachitike, anawalimbikitsa ndi mawu akuti: ‘Wokhulupirira ine, ntchito zimene ndichita ine adzazichitanso iyeyu; ndipo adzachita zoposa izi.’ (Yohane 14:12) Ntchito za otsatira ake zikaposa zake chifukwa chakuti muuminisitala wawo akafikira anthu ambiri kwambiri ndi kukwaniritsa malo aakulu koposa ndipo kwa nthaŵi yotalikirapo. Komabe, pamene Yesu anaphedwa, ophunzira ake anakhwetemuka ndi mantha. Anabisala ndipo sanapitirize kuchita ntchito imene anawaphunzitsa. Ena anabwereradi kuntchito yausodzi. Komabe, mwanjira yosaiŵalika, iye anagogomezera kwa asanu ndi aŵiri ameneŵa chimene anafuna kuti iwo achite, limodzinso ndi otsatira ake ena onse.
12. (a) Kodi nchozizwitsa chotani chimene Yesu anachita ku Nyanja ya Galileya? (b) Mwachiwonekere, kodi Yesu anatanthauzanji pamene anafunsa Petro ngati anamkonda Iye ‘kuposa izi’?
12 Yesu anavala thupi laumunthu ndi kuwonekera ku Nyanja ya Galileya. Atumwi asanu ndi aŵiriwo adaloŵa pamadzi ndi ngalaŵa koma analephera kugwira nsomba iliyonse usiku wonsewo. Yesu anafuula ali kugombe nati: ‘Ponyani khoka kumbali ya dzanja lamanja ya ngalawa, ndipo mudzapeza.’ Pamene khokalo mozizwitsa linadzala ndi nsomba moti nkutsala pang’ono kupanthuka, okwera m’ngalawamo anazindikira kuti anali Yesu pagomepo, ndipo anafulumiza kupita kumene iye ankawadikirira. Atawapatsa chakudya chofisula, Yesu, mwachiwonekere akupenya nsomba zochuluka zogwidwazo, anafunsa Petro kuti: ‘Simoni mwana wa Yona, kodi undikonda ine koposa [izi, NW]?’ (Yohane 21:1-15) Mosakaikira Yesu anatanthauza kuti, Kodi umakonda ntchito yausodzi kuposa ntchito yakulalikira imene ndakukonzekeratsani kuichita?
13. Kodi ndimotani mmene Yesu anagogomezerera mwamphamvu kwa ophunzira ake njira imene anayenera kulabadirira ku chikondi chake?
13 Petro anayankha kuti: ‘Inde, Ambuye; mudziŵa kuti ndikukondani inu.’ Yesu anayankha kuti: ‘Dyetsa ana ankhosa anga.’ Yesu anafunsanso kachiŵiri nati: ‘Simoni mwana wa Yona, ukonda ine kodi?’ Petro anayankhanso, ndipotu ndi chitsimikizo chokulirapo nati: ‘Inde, Ambuye; mudziŵa kuti ndikukondani inu.’ Yesu analamulanso nati: ‘Weta nkhosa zanga.’ Yesu anafunsa kachitatu nati: ‘Simoni mwana wa Yona, kodi undikonda ine?’ Tsopano Petro anamvadi chisoni. Masiku ochepa pasadakhale, adakana katatu konse kuti sadamdziŵe Yesu, chotero ayenera kukhala akulingalira kuti mwina Yesu akukaikira kukhulupirika kwake. Choncho, panthaŵi yachitatu, mothekera, Petro anayankha ndi mawu ochonderera kuti: ‘Ambuye, mudziŵa inu zonse, muzindikira kuti ndikukondani inu.’ Yesu anangoyankha kuti: ‘Dyetsa nkhosa zanga.’ (Yohane 21:15-17) Kodi pangakhale chikaikiro chirichonse ponena za chimene Yesu anafuna Petro ndi anzake kuchita? Ha, iye anagogomezera mwamphamvu kwa iwo chotani nanga—limodzinso ndi kwa alionse amene akakhala ophunzira ake lerolino—kuti ngati amkonda iye, adzakhala ndi phande m’ntchito yopanga ophunzira!
14. Pazochitika zina, kodi ndimotani mmene Yesu anasonyezera njira imene ophunzira ake ayenera kulabadirira ku chikondi chake?
14 Masiku angapo pambuyo pa kukambitsirana kwa pagombe kumeneko, Yesu anawonekera paphiri m’Galileya ndipo analangiza msonkhano wa otsatira achimwemwe okwanira pafupifupi 500 kuti: ‘Chifukwa chake mukani, phunzitsani anthu amitundu yonse, . . . kuwaphunzitsa, asunge zinthu zonse zimene ndinakulamulirani inu.’ (Mateyu 28:19, 20; 1 Akorinto 15:6) Tangolingalirani! Amuna, akazi, ndi ana onse analandira ntchito yofananayo. Chikhalirechobe, ali pafupi kukwera kumwamba, Yesu anauza ophunzira ake kuti: ‘Mudzakhala mboni zanga . . . kufikira malekezero ake a dziko.’ (Machitidwe 1:8) Pambuyo pachilangizo chonsechi, mposadabwitsa kuti, zaka zambiri pambuyo pake, Petro anati: ‘[Yesu] anatilamulira ife tilalikire kwa anthu, ndipo tichite umboni.’—Machitidwe 10:42.
15. Kodi palibe chikaikiro ponena za chiyani?
15 Palibe chikaikiro chirichonse ponena za mmene tiyenera kulabadirira ku chikondi cha Yesu. Monga momwe iye anauzira atumwi ake kuti: ‘Ngati musunga malamulo anga mudzakhala m’chikondi changa . . . Muli abwenzi anga inu, ngati muzichita zimene ndikulamulirani inu.’ (Yohane 15:10-14) Tsopano tifunse, Kodi inuyo mudzasonyeza chiyamikiro kaamba ka chikondi cha Yesu mwakumvera lamulo lake lakukhala ndi phande m’ntchito yopanga ophunzira? Ndithudi, ichi chingakhale chovuta kwa inu pazifukwa zosiyanasiyana. Koma chinalinso chovuta ngakhale kwa Yesu. Talingalirani masinthidwe amene iye anafunikira kuwapanga.
Tsatirani Chitsanzo cha Yesu
16. Kodi nchitsanzo chabwino koposa chotani chimene Yesu anapereka?
16 Mwana wa Mulungu wobadwa yekha anali ndi malo olemekezeka a ulemerero wakumwamba wopambana angelo onse. Anali wolemera kwabasi! Chikhalirechobe, anadzikhutula mofunitsitsa, kubadwa monga chiŵalo cha banja losauka, ndi kukulira mwa anthu omadwala ndi kufa. Anachita zimenezi chifukwa cha ife, monga momwe mtumwi Paulo anafotokozera kuti: ‘Pakuti mudziŵa chisomo cha Ambuye wathu Yesu Kristu, kuti, chifukwa cha inu anakhala wosauka, angakhale anali wolemera, kuti inu ndi kusauka kwake mukakhale olemera.’ (2 Akorinto 8:9; Afilipi 2:5-8) Ha, nchitsanzo chabwino chotani nanga! Inde, nchisonyezero chachikondi chotani nanga! Palibe amene anaperekapo zoposa zimenezo kapena kuvutika koposa kwake chifukwa cha ena. Ndipo palibe amene anatheketsapo ena kupeza chuma chopambana, inde, moyo wosatha wangwiro!
17. Kodi ndinjira yotani imene yaikidwa patsogolo pathu, ndipo kodi nchiyani chimene chidzakhala chotulukapo ngati tiitsatira?
17 Tikhoza kutsatira chitsanzo cha Yesu ndi kupindulitsa ena mofananamo. Mobwerezabwereza, Yesu anafulumiza anthu kukhala otsatira ake. (Marko 2:14; Luka 9:59; 18:22) Kwenikweni, Petro analemba kuti: ‘Pakuti kudzachita ichi mwaitanidwa; pakutinso Kristu anamva zoŵaŵa m’malo mwanu, nakusiirani chitsanzo kuti mukalondole mapazi ake.’ (1 Petro 2:21) Kodi mudzalabadira ku chikondi cha Kristu ngakhale ngati zingatanthauze kuvutika kotero kuti mutumikire Atate wake mmene iye anachitira? Ha, kachitidwe koteroko kangakhale kaphindu chotani nanga kwa ena! Ndithudi, mwakutsatira chitsanzo cha Yesu, mwakugwiritsira ntchito mokwanira ziphunzitso zimene anazilandira kwa Atate wake, ‘mudzadzipulumutsa inu eni ndi iwo akumva inu.’—1 Timoteo 4:16.
18. (a) Kodi nchitsanzo chotani chimene Yesu anapereka ponena za kaimidwe kake kulinga kwa anthu? (b) Kodi anthu analabadira motani ku umunthu wa Yesu?
18 Kuti tiwathandize bwino koposa anthu, tiyenera kumva mmene Yesu anamverera ponena za iwo. Mneneri wina anati ponena za iye: ‘Adzachitira nsoni wosauka ndi waumphaŵi.’ (Salmo 72:13) Otsatira ake anatha kuwona kuti Yesu ‘anagwidwa chifundo’ kwa amene analankhula nawo ndi kuti anafunitsitsadi kuwathandiza. (Marko 1:40-42; 10:21) ‘Powona makamuwo,’ limatero Baibulo, ‘anagwidwa m’mtima ndi chisoni chifukwa cha iwo, popeza anali okambululudwa ndi omwazikana, akunga nkhosa zopanda mbusa.’ (Mateyu 9:36) Ngakhale ochita machimo aakulu anachizindikira chikondi chake ndipo anakopeka naye. Chifukwa cha kukoma kwa mawu ake, ulemu wake, ndi kaphunzitsidwe kake, anthu anali omasuka kwa iye. Monga chotulukapo, ngakhale okhometsa msonkho odedwa ndi akazi achigololo anamfunafuna.—Mateyu 9:9-13; Luka 7:36-38; 19:1-10.
19. Kodi ndimotani mmene Paulo anatsanzirira Yesu, ndipo nchiyani chidzakhala chotulukapo ngati tichita mofananamo?
19 Ophunzira a Yesu a m’zaka za zana loyamba anatengera chitsanzo chake. Paulo analembera ena a iwo amene anawatumikira kuti: ‘Komatu, tinakhala ofatsa pakati pa inu, monga mmene mlezi afukata ana ake a iye yekha . . . Monga atate achitira ana ake a iye yekha, ndi kukudandaulirani, ndi kukusangalatsani ndi kuchita umboni.’ (1 Atesalonika 2:7-11) Kodi muli nayo nkhaŵa yeniyeni yofananayo kulinga kwa anthu a m’gawo lanu imene makolo achikondi amakhala nayo kwa ana awo okondedwa? Kusonyeza nkhaŵa yoteroyo m’mawu anu, pankhope panu, ndi m’machitidwe anu kudzapangitsa uthenga wa Ufumu kukhala wokopa kwa onga nkhosa.
20, 21. Kodi nzochitika zamakono zotani za anthu omwe anatsatira chitsanzo cha Yesu chachikondi?
20 Patsiku lina lozizira mu Spanya, Mboni ziŵiri zinapeza mkazi wokalamba woyenda ndi ndondo amene nyumba yake inazizira kwambiri chifukwa chakuti nkhuni zidamthera. Iye ankayembekezera mwana wake wamwamuna kubwera kuchokera kuntchito kuti adzaŵazirepo zina. Mbonizo zinaŵaza nkhuni, ndi kusiyanso magazini kuti adziŵerenga. Pamene mwanayo anabwera, anakondwa kwambiri kaamba ka nkhaŵa yachikondi ya Mbonizo kwa amayi ŵake kwakuti anaŵerenga magaziniwo, anayamba kuphunzira Baibulo, nabatizidwa, ndipo mwamsanga analoŵa utumiki waupainiya.
21 Mu Australia mwamuna wina ndi mkazi wake anauza Mboni zowachezera kuti analibe ndalama zodyetsera banja lawo. Mboni ziŵiri zokwatiranazo zinapita nizikagula zakudya, kuphatikizapo masiwiti a ana. Makolowo anagwa m’misozi ndi kulira, nati anali osoŵeratu chochita kwakuti analingalira zakudzipha. Onse aŵiri anayamba kuphunzira Baibulo, ndipo mkazi anabatizidwa posachedwapa. Mkazi wina mu United States yemwe anazilingalira moipa Mboni za Yehova anasimba motere pambuyo pokumana ndi imodzi: “Sindikukumbukira kwenikweni zimene tinakambitsirana, koma chimene ndikukumbukira ndichifundo chake kwa ine, ndi mmene analiri wokoma mtima ndi wodzichepetsa. Ndinakopekadi ndi umunthu wake. Ndiukhumbirabe mkhalidwe wake waubwenzi ngakhale ndi lerolomwe.”
22. Pokhala kuti taupenda moyo wa Yesu, kodi tinganenenji motsimikiza ponena za iye?
22 Ngati tilabadira ku chikondi cha Yesu mwakuchita ntchito imene anaichita m’njira imene anaichitiramo, tingasangalale ndi madalitso odabwitsa zedi! Ukulu wa Yesu ngowonekeratu ndi wochititsa chidwi. Timasonkhezeredwa kubwereza mawu a bwanamkubwa Wachiroma Pontiyo Pilato kuti: ‘Tawonani munthuyo!’ Inde, ‘Munthuyo,’ munthu wamkulu woposa onse amene anakhalako.—Yohane 19:5.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi chikondi cha Yesu nchachikulu motani?
◻ Kodi chikondi cha Yesu chiyenera kutisonkhezera kukonda yani, ndipo kodi chiyenera kutisonkhezera kuchitanji?
◻ Kodi ndintchito yotani imene Yesu amafuna kuti tichite?
◻ Kodi ndimotani mmene Yesu analiri wolemera, ndipo nchifukwa ninji anakhala wosauka?
◻ Kodi tiyenera kumtsanzira motani Yesu m’njira imene anatumikirira anthu?
[Chithunzi patsamba 15]
Yesu anapereka chitsanzo chakusonyeza chikondi
[Chithunzi patsamba 17]
Yesu anachitira fanizo mwamphamvu mmene ophunzira ake ayenera kusonyezera chikondi kwa iye