Phunzitsani Mwachikondi Ngati Yesu
“Palibe munthu analankhulapo ngati iyeyu n’kale lonse.”—YOH. 7:46.
1. Kodi anthu anakhudzidwa bwanji ndi kaphunzitsidwe ka Yesu?
N’ZOSACHITA kufunsa kuti anthu anasangalala kwambiri kumva Yesu akuphunzitsa. Baibulo limatithandiza kudziwa mmene mawu a Yesu anakhudzira anthu amene anamumva akulankhula. Mwachitsanzo, Luka analemba mu Uthenga Wabwino kuti anthu a mumzinda wakwawo kwa Yesu “anayamba . . . kudabwa ndi mawu ogwira mtima otuluka pakamwa pake.” Mateyo analemba kuti anthu amene anamvetsera ulaliki wa Yesu wapaphiri, “anazizwa ndi kaphunzitsidwe kake.” Nayenso Yohane analemba kuti alonda amene anatumidwa kuti akagwire Yesu anabwerera chimanjamanja n’kunena kuti: “Palibe munthu analankhulapo ngati iyeyu n’kale lonse.”—Luka 4:22; Mat. 7:28; Yoh. 7:46.
2. Kodi Yesu ankagwiritsa ntchito njira ziti pophunzitsa?
2 Alonda aja sanalakwitse. Yesu anali Mphunzitsi waluso kuposa onse amene anakhalako. Iye ankaphunzitsa momveka, ndi mawu osavuta kumva komanso motsatirika bwino, moti palibe akanamutsutsa. Iye ankagwiritsa ntchito mafanizo ndi mafunso mwaluso. Kaphunzitsidwe kake kanali kogwirizana ndi anthu amene ankalankhula nawo, kaya akhale apamwamba kapena otsika. Choonadi chimene iye ankaphunzitsa chinali chozama koma ankachifotokoza m’njira yosavuta kumva. Komatu si zokhazi zimene zinachititsa Yesu kukhala Mphunzitsi waluso.
Chikondi ndi Khalidwe Lofunika Kwambiri
3. Kodi kaphunzitsidwe ka Yesu kanali kosiyana bwanji ndi ka atsogoleri a chipembedzo a m’nthawi yake?
3 Pakati pa alembi ndi Afarisi payenera kuti panali anthu anzeru omwe ankadziwa bwino zinthu komanso amene anali ndi luso lophunzitsa. Komano n’chifukwa chiyani kaphunzitsidwe ka Yesu kanali kosiyana ndi ka anthu amenewa? Atsogoleri a chipembedzo a m’nthawi ya Yesu sankakonda anthu wamba. Iwo ankawanyoza ndipo ankangowaona ngati ‘anthu otembereredwa.’ (Yoh. 7:49) Koma Yesu anawamvera chisoni anthu wamba, chifukwa “anali okalikakalika ndi otayika ngati nkhosa zopanda m’busa.” (Mat. 9:36) Iye anali wachikondi, wachifundo komanso wokoma mtima. Chinanso n’chakuti atsogoleri a chipembedzo analibe chikondi chenicheni kwa Mulungu. (Yoh. 5:42) Koma Yesu ankakonda Atate wake ndipo ankasangalala kuchita chifuniro cha Atate wakewo. Atsogoleri a chipembedzo ankapotoza mawu a Mulungu n’cholinga choti akwaniritse zofuna zawo, koma Yesu ankakonda “mawu a Mulungu” ndipo ankawaphunzitsa, kuwafotokoza, kuwateteza komanso kuwatsatira. (Luka 11:28) Zoonadi, chikondi chinamulowerera kwambiri Khristu ndipo ankachisonyeza pophunzitsa, pochita zinthu zina ndi anthu komanso popereka malangizo.
4, 5. (a) N’chifukwa chiyani tifunika kuphunzitsa mwachikondi? (b) Pophunzitsa, n’chifukwa chiyani kudziwa zinthu komanso kukhala ndi luso kulinso kofunika?
4 Nanga bwanji ifeyo? Popeza ndife otsatira a Khristu, tiyenera kumutsanzira tikakhala mu utumiki komanso pa moyo wathu. (1 Pet. 2:21) Motero, cholinga chathu sikungophunzitsa anthu Baibulo koma kuwasonyezanso makhalidwe a Yehova, makamaka chikondi chake. Kaya tikudziwa zambiri kapena zochepa, kaya tili ndi luso kwambiri kapena ayi, chikondi chimene timasonyeza n’chimene chingatithandize kuwafika pamtima anthu amene tikuwalalikira. Kuti tikhale ogwira mtima pa ntchito yopanga ophunzira, tiyenera kuphunzitsa mwachikondi ngati Yesu.
5 Kuti tikhale aphunzitsi ogwira mtima, tiyeneranso kudziwa zinthu zimene tikukaphunzitsa ndiponso kukhala ndi luso lophunzitsa zinthuzo. Yesu anathandiza ophunzira ake kudziwa zinthu ndiponso kukhala ndi luso la kuphunzitsa. Ndipo masiku ano, Yehova amagwiritsa ntchito gulu lake potithandiza kuti tikhale aphunzitsi ogwira mtima. (Werengani Yesaya 54:13; Luka 12:42.) Ngakhale zili choncho, tiyenera kuyesetsa kuti tiziphunzitsa ndi nzeru zathu zonse komanso ndi mtima wathu wonse. Tikamaphunzitsa zinthu molondola, mwaluso ndiponso mwachikondi, zotsatira zake zimakhala zosangalatsa. Ndiyeno kodi tingatani kuti tizisonyeza chikondi pophunzitsa? Kodi Yesu ndi ophunzira ake anachita bwanji zimenezi? Tiyeni tione.
Tiyenera Kukonda Yehova
6. Kodi timalankhula motani pofotokoza za munthu amene timam’konda?
6 Anthufe timamva bwino tikamalankhula za zinthu zimene timazikonda. Timalankhula mwamphamvu ndiponso mosangalala moti anthu amatha kuona kuti zikutisangalatsa. Izi zimachitika makamaka tikamalankhula za munthu amene timam’konda. Nthawi zambiri timalakalaka kuuza ena zinthu zokhudza munthuyo zimene ife tikudziwa. Timalankhula zabwino za iye, kumukweza ndiponso kumuikira kumbuyo. Timatero chifukwa chakuti timafuna kuti anthu akopeke naye ndiponso kuti akopeke ndi makhalidwe ake ngati mmene ifeyo timachitira.
7. Kodi chikondi cha Yesu kwa Mulungu chinamulimbikitsa kuchita chiyani?
7 Tiyenera kumudziwa bwino Yehova ndiponso kumukonda, tisanayambe kuthandiza ena kuti nawonso azimukonda. Ndipotu kulambira koona kumafuna kuti tizikonda Mulungu. (Mat. 22:36-38) Yesu anapereka chitsanzo chabwino kwambiri pa nkhani imeneyi. Iye ankakonda Yehova ndi mtima wake wonse ndi maganizo ake onse, ndi moyo wake wonse komanso ndi mphamvu zake zonse. Yesu ankawadziwa bwino kwambiri Atate wake wakumwamba chifukwa chakuti anakhala nawo kwa zaka mwina mabiliyoni ambiri. Kodi zotsatira zake zinali zotani? Yesu anati: “Ndimakonda Atate.” (Yoh. 14:31) Iye anasonyeza chikondi chimenechi mwa zolankhula ndi zochita zake. Chikondicho chinamulimbikitsa kuti nthawi zonse azichita zinthu zokondweretsa Mulungu. (Yoh. 8:29) Chinamulimbikitsanso kudzudzula atsogoleri a chipembedzo amene ankanena kuti amaimira Mulungu, koma anali onyenga. Chikondicho chinamulimbikitsanso kulankhula za Yehova komanso kuthandiza ena kuti adziwe ndi kukonda Mulungu.
8. Kodi chikondi cha ophunzira a Yesu kwa Mulungu chinawalimbikitsa kuchita chiyani?
8 Nawonso ophunzira a Yesu, ankakonda Yehova ndipo chikondi chimenechi chinawalimbikitsa kulalikira uthenga wabwino molimba mtima komanso mwachangu. Iwo anadzaza Yerusalemu yense ndi chiphunzitso chawo ngakhale kuti ankadziwa kuti atsogoleri a chipembedzo amene ankawatsutsa anali ndi mphamvu yochita chilichonse. Iwo sakanatha kusiya kulankhula zinthu zimene anaziona ndi kuzimva. (Mac. 4:20; 5:28) Ankadziwa kuti Yehova adzawathandiza ndi kuwadalitsa, ndipo anatero kumene. Ndipotu pasanathe zaka 30 kuchokera pamene Yesu anafa, mtumwi Paulo analemba kuti uthenga wabwino unali utalalikidwa “m’chilengedwe chonse cha pansi pa thambo.”—Akol. 1:23.
9. Kodi tingakulitse bwanji chikondi chathu kwa Mulungu?
9 Ngati tikufuna kuti tikhale aphunzitsi ogwira mtima, nafenso tiyenera kupitiriza kukulitsa chikondi chathu kwa Mulungu. Kodi tingachite bwanji zimenezi? Tingachite zimenezi mwa kulankhulana ndi Mulungu m’pemphero pafupipafupi. Tingakulitsenso chikondi chathu kwa Mulungu mwa kuphunzira Mawu ake, kuwerenga mabuku ofotokoza Baibulo ndiponso kupezeka pamisonkhano. Tikamapitiriza kuphunzira za Mulungu, chikondi chathu chimakula kwambiri mumtima mwathu. Ndiyeno tikamasonyeza kuti timakonda Mulungu mwa zolankhula ndi zochita zathu, anthu adzaona ndipo angayambenso kukonda Yehova.—Werengani Salmo 104:33, 34.
Tiyenera Kukonda Zimene Timaphunzitsa
10. Kodi mphunzitsi wabwino amatani?
10 Mphunzitsi wabwino ndi amene amakonda zimene amaphunzitsazo. Iye amakhulupirira kuti zimene akuphunzitsazo n’zoona, n’zofunika komanso n’zaphindu. Ngati mphunzitsi amakonda zimene amaphunzitsa, zimaonekera m’kaphunzitsidwe kake ndipo amatha kuwafika pa mtima ophunzira ake. Koma ngati mphunzitsi sakonda kwenikweni zimene amaphunzitsa, angayembekezere bwanji ophunzira ake kuona phindu la zinthuzo? Motero, dziwani kuti chitsanzo chanu n’chofunika kwambiri pophunzitsa Mawu a Mulungu. Yesu ananena kuti: “Aliyense amene waphunzitsidwa bwino adzafanana ndi mphunzitsi wake.”—Luka 6:40.
11. N’chifukwa chiyani Yesu ankakonda zimene ankaphunzitsa?
11 Yesu ankakonda zimene ankaphunzitsa. Iye ankadziwa kuti “mawu a Mulungu,” omwe ndi “mawu amoyo wosatha” ndiponso choonadi chonena za Atate wake wakumwamba, ndi amtengo wapatali ndipo anafunika kuuza ena. (Yoh. 3:34; 6:68) Mofanana ndi muuni wowala kwambiri, choonadi chimene Yesu ankaphunzitsa chinkaunika zinthu zoipa zofunika kuzipewa komanso zinthu zabwino zofunika kuzitsatira. Choonadi chimene Yesu ankaphunzitsa chinapatsa chiyembekezo ndipo chinalimbikitsa anthu odzichepetsa amene ankanamizidwa ndi atsogoleri a chipembedzo komanso kuponderezedwa ndi Mdyerekezi. (Mac. 10:38) Yesu anasonyeza kuti ankakonda choonadi mwa zimene ankaphunzitsa komanso zochita zake zonse.
12. Kodi mtumwi Paulo ankauona bwanji uthenga wabwino?
12 Nawonso ophunzira a Yesu ankakonda kwambiri choonadi chonena za Yehova ndi Khristu, moti anthu owatsutsa analephera kuwaletsa kulalikira. Paulo analembera Akhristu a ku Roma kuti: “Ndikufunitsitsa kudzalengeza uthenga wabwino . . . Pakuti sindichita nawo manyazi uthenga wabwino. Kunena zoona, uthengawo ndiwo mphamvu ya chipulumutso imene Mulungu amaipereka kwa aliyense amene ali ndi chikhulupiriro.” (Aroma 1:15, 16) Paulo ankaona kuti kulalikira choonadi ndi mwayi wamtengo wapatali. Iye analemba kuti: “Ndinapatsidwa kukoma mtima kumeneku kuti ndilengeze kwa mitundu uthenga wabwino wonena za chuma chopanda polekezera cha Khristu.” (Aef. 3:8) Apa aliyense atha kuona kuti Paulo ankalalikira motsimikiza za Yehova ndi zolinga zake.
13. Kodi n’chifukwa chiyani timakonda kwambiri uthenga wabwino?
13 Uthenga wabwino wopezeka m’Mawu a Mulungu umatithandiza kudziwa Mlengi komanso kukhala naye pa ubwenzi wolimba. Umatithandizanso kupeza mayankho a mafunso ofunika kwambiri pa moyo wathu. Ulinso ndi mphamvu yotithandiza kusintha moyo wathu, kukhala ndi chiyembekezo komanso kukhala olimba pa nthawi ya mavuto. Kuwonjezera pamenepa, umatithandiza kukhala ndi moyo waphindu umene sudzatha. Palibe chinthu chofunika kwambiri komanso chamtengo wapatali kuposa kudziwa uthenga wabwino. Uthengawu ndi mphatso yamtengo wapatali kwambiri imene tapatsidwa ndipo umatipatsa chimwemwe chosaneneka. Timasangalalanso kwambiri ndi mphatso imeneyi tikamauza ena.—Mac. 20:35.
14. Kodi tingalimbitse bwanji chikondi chathu cha zimene timaphunzitsa?
14 Kodi mungatani kuti muzilimbitsa chikondi chanu cha uthenga wabwino. Powerenga Mawu a Mulungu, muyenera kumaima kaye pang’ono n’kuganizira mozama zimene mukuwerengazo. Mwachitsanzo, muzidziyerekezera inuyo muli limodzi ndi Yesu mu utumiki wake padziko lapansi, kapena mukutsagana ndi mtumwi Paulo pa maulendo ake. Muzidziyerekezeranso mutalowa m’dziko latsopano n’kumaganizira mmene moyo udzasinthire. Ganizirani madalitso amene mwapeza chifukwa chomvera uthenga wabwino. Ngati chikondi chanu cha uthenga wabwino chili cholimba, anthu amene mumaphunzira nawo adzatha kuona zimenezo. N’chifukwa chake tiyenera kusinkhasinkha mozama zinthu zimene taphunzira ndi kusamalanso zimene timaphunzitsa.—Werengani 1 Timoteyo 4:15, 16.
Tizikonda Anthu
15. N’chifukwa chiyani mphunzitsi ayenera kukonda ophunzira ake?
15 Mphunzitsi wabwino amachititsa kuti ophunzira azikhala omasuka n’cholinga choti azisangalala kufotokoza bwinobwino maganizo awo pa zimene akuphunzirazo. Iye amaphunzitsa anthu chifukwa choti amawakonda kwambiri. Amasintha njira zophunzitsira kuti zigwirizane ndi nzeru za ophunzirawo komanso mavuto amene ali nawo. Iye amadziwa zimene ophunzirawo angathe ndi zimene sangathe kuchita komanso mmene zinthu zilili pa moyo wawo. Aphunzitsi akakhala ndi chikondi choterechi, ophunzira amaona ndipo maphunziro amasangalatsa.
16. Kodi Yesu anasonyeza bwanji kuti amakonda anthu?
16 Yesu anasonyeza chikondi choterechi. Njira yaikulu kwambiri imene anasonyezera chikondi chimenechi ndiyo kupereka moyo wake n’cholinga choti anthu apulumutsidwe. (Yoh. 15:13) Mu utumiki wake, Yesu anali wakhama pothandiza anthu mwakuthupi ndiponso makamaka mwauzimu. Iye sanali kuyembekezera kuti anthu abwere koma ankayenda pansi maulendo ataliatali kukawalalikira uthenga wabwino. (Mat. 4:23-25; Luka 8:1) Iye anali woleza mtima komanso womvetsa zinthu. Ophunzira ake akalakwitsa zinazake, iye ankawathandiza mwachikondi. (Maliko 9:33-37) Iye ankawalimbikitsa powasonyeza kuti akuwadalira kuti iwo adzakhala alaliki ogwira mtima a uthenga wabwino. Sipanakhalepo mphunzitsi wachikondi ngati Yesu. Chikondi chimene ankasonyeza kwa ophunzira ake chinachititsa kuti nawonso azimukonda komanso kuti azisunga malamulo ake.—Werengani Yohane 14:15.
17. Kodi ophunzira a Yesu anasonyeza bwanji kuti ankakonda anthu?
17 Mofanana ndi Yesu, ophunzira ake ankakonda kwambiri anthu amene ankawalalikira. Iwo anapirira pozunzidwa komanso analolera kuika moyo wawo pachiswe, n’cholinga choti alalikire uthenga wabwino ndipo zotsatira zake zinali zabwino. Ndithudi, ophunzirawo ankakondadi anthu amene anawathandiza mwauzimu. Mawu amene mtumwi Paulo analemba akusonyezanso kuti iye ankakonda kwambiri anthu. Iye anati: “M’malo mwake, tinakhala odekha pakati panu monga mmene mayi woyamwitsa amasamalira ana akeake. Choncho, pokhala ndi chikondi chachikulu kwa inu, tinali okonzeka kukupatsani uthenga wabwino wa Mulungu. Osati uthenga wokha ayi, komanso miyoyo ya ife eni, chifukwa munakhala okondedwa kwa ife.”—1 Ates. 2:7, 8.
18, 19. (a) N’chifukwa chiyani timalolera kugwiritsa ntchito zinthu zathu pa ntchito yolalikira? (b) Perekani chitsanzo chosonyeza kuti anthu amaona chikondi chimene timasonyeza.
18 Masiku ano, Mboni za Yehova zimakhala balalabalala padziko lonse kufufuza anthu amene akufuna kudziwa Mulungu komanso kumutumikira. Ndipotu zaka 17 zapitazi, takhala tikulalikira ndi kupanga ophunzira kwa maola oposa 1 biliyoni chaka chilichonse ndipo ntchitoyi ikupitirirabe. Timachita zimenezi mwakufuna kwathu, ngakhale kuti ntchitoyi imafuna nthawi, mphamvu komanso chuma chathu. Mofanana ndi Yesu, timadziwa kuti cholinga cha Atate wathu wakumwamba ndi choti anthu onse adziwe zinthu zimene zingawathandize kupeza moyo wosatha. (Yoh. 17:3; 1 Tim. 2:3, 4) Chikondi n’chimene chimatilimbikitsa kuthandiza anthu amtima wabwino kuti adziwe Yehova n’kuyamba kumukonda ngati mmene ife timam’kondera.
19 Anthu amaona chikondi chimene timasonyeza. Mwachitsanzo, mpainiya wina ku United States amalemba makalata otonthoza anthu amene aferedwa. Bambo wina anayankha kalata ya mlongoyu ndi mawu akuti: “Poyamba, ndinadabwa kwambiri kuti munthu wosandidziwa analemba kalata yondilimbikitsa pa nthawi yovuta kwambiri imeneyi. Ndazindikira kuti mumakonda kwambiri anthu komanso Mulungu amene amatsogolera anthu pa njira ya ku moyo.”
20. N’chifukwa chiyani kuphunzitsa mwachikondi kuli kofunika?
20 Munthu wina ananena kuti mukaphatikiza chikondi ndi luso pogwira ntchito, ntchitoyo imakhala yosiririka. Tikamaphunzitsa anthu, timayesetsa kuwathandiza kuti amudziwe bwino Yehova komanso kuti azimukonda ndi mtima wawo wonse. Inde, kuti tikhale aphunzitsi ogwira mtima, tiyenera kukonda Mulungu, kukonda choonadi komanso kukonda anthu. Tikamayesetsa kukhala ndi chikondi choterechi mu utumiki, timapeza chisangalalo chimene chimabwera chifukwa chopatsa, ndiponso timakhala pa mtendere chifukwa chodziwa kuti tikutsanzira Yesu komanso tikusangalatsa Yehova.
Kodi Mungayankhe Bwanji?
• Pamene tikuphunzitsa anthu uthenga wabwino, n’chifukwa chiyani tifunika . . .
kukonda Mulungu?
kukonda zimene timaphunzitsa?
kukonda anthu amene timawaphunzitsa?
[Chithunzi patsamba 15]
Kodi n’chifukwa chiyani kaphunzitsidwe ka Yesu kanali kosiyana ndi ka alembi ndi ka Afarisi?
[Chithunzi patsamba 18]
Mphunzitsi wabwino amafunika kudziwa zinthu molondola, luso ndiponso makamaka chikondi