Zimene Ufumu wa Mulungu Ungatanthauze kwa Inu
YESU KRISTU anaphunzitsa otsatira ake kupemphera kuti: “Ufumu wanu udze.” (Mateyu 6:10) Ha, mawu amenewo anenedwa mobwerezabwereza chotani nanga kwa Mulungu ndi anthu odzitcha otsatira a Yesu!
Komabe, Yesu anachita zambiri kuposa kungophunzitsa ophunzira ake kupempherera Ufumu wa Mulungu. Iye anapanga Ufumuwo kukhala nkhani yaikulu ya ntchito yake yolalikira. Kwenikweni, Encyclopædia Britannica imanena kuti Ufumu wa Mulungu “kaŵirikaŵiri umalingaliridwa kukhala mutu waukulu wa chiphunzitso cha Yesu.”
Pamene otsatira a Kristu apempherera Ufumu, kodi amapempherera chiyani? Kodi Ufumu wa Mulungu ungatanthauzenji kwa iwo ndi kwa inu? Ndipo kodi Yesu anaulingalira motani?
Lingaliro la Yesu la Ufumuwo
Kaŵirikaŵiri Yesu anadzitcha “Mwana wa munthu.” (Mateyu 10:23; 11:19; 16:28; 20:18, 28) Izi zikutikumbutsa za kunena kwa mneneri Danieli za “mwana wa munthu.” Ponena za chochitika chakumwamba chamtsogolo, Danieli anati: ‘Ndinawona m’masomphenya a usiku, tawonani, anadza ndi mitambo ya kumwamba wina ngati mwana wa munthu, nafika kwa Nkhalamba ya kale lomwe; ndipo anamyandikizitsa pamaso pake. Ndipo anampatsa ulamuliro, ndi ulemerero, ndi ufumu, kuti anthu onse, ndi mitundu yonse ya anthu, ndi a manenedwe onse, amtumikire.’—Danieli 7:13, 14.
Polankhula za nthaŵi imene akalandira ulamuliro umenewu, Yesu anauza atumwi ake kuti: ‘Pamene Mwana wa munthu adzakhala pa chimpando cha ulemerero wake, inunso, mudzakhala pa mipando khumi ndi iŵiri.’ Yesu anatinso: ‘Pamene Mwana wa munthu adzadza mu ulemerero wake, . . . adzasonkhanidwa pamaso pake anthu a mitundu yonse; ndipo iye adzalekanitsa iwo wina ndi mnzake, monga mbusa alekanitsa nkhosa ndi mbuzi. . . . Ameneŵa [osalungama] adzachoka kumka ku chilango cha nthaŵi zonse; koma olungama ku moyo wa nthaŵi zonse.’—Mateyu 19:28; 25:31, 32, 46.
Ulosi wotchula mipando ndi mitundu yonse umenewu umasonyeza kuti Ufumuwo uli boma limene Yesu ndi otsatira ake ena adzalamulira anthu. Boma limenelo lidzakhala ndi mphamvu yakulikha osalungama mu imfa. Komabe, mu ulamuliro wa Ufumu, olungama adzalandira mphatso ya Mulungu ya moyo wamuyaya.
Pamenepo, kuli kowonekera kuti Ufumu wa Mulungu uli boma lakumwamba lokhazikitsidwa mwaumulungu. Ufumuwo suli tchalitchi, ndipo Malemba samapereka maziko a kuulingalira kukhala wakudziko. Ndiponso, boma loperekedwa ndi Mulungu silingakhale chinachake chongokhala mumtima mwa munthu. Popeza kuti Ufumu wa Mulungu uli boma, suli chinachake chimene chimadza m’mitima mwathu titalandira Chikristu. Koma nchifukwa ninji ena amalingalira kuti Ufumuwo uli mkhalidwe woyambukira mtima?
Kodi Ufumuwo Uli Mkati Mwathu?
Ena amalingalira kuti Ufumuwo uli mumtima mwathu chifukwa cha njira imene Luka 17:21 wamasuliridwira ndi otembenuza Baibulo ena. Malinga ndi New International Version, pamenepo Yesu anati: “Ufumu wa Mulungu uli mkati mwanu.”
Ponena za zimenezi The Interpreter’s Dictionary of the Bible imalongosola kuti: “Ngakhale kuti kaŵirikaŵiri kumatchulidwa monga chitsanzo cha ‘chikhulupiriro’ kapena ‘malingaliro’ a Yesu, kumasulira kumeneku kwakukulukulu kumayedzamira pa matembenuzidwe akale, akuti ‘mkati mwanu,’ . . . omwe anamvedwa molakwa m’lingaliro lamakono la liwu lakuti ‘inu’ loimira munthu mmodzi; ‘inu’ ameneyo . . . akuloza kwa anthu ambiri (Yesu akulankhula ndi Afarisi—vesi 20) . . . Nthanthi yakuti ufumu wa Mulungu uli mkhalidwe wamkati wa maganizo, kapena chipulumutso cha munthu mwini, ili yosemphana ndi mawu apatsogolo ndi pambuyo pa vesili, ndiponso ili yosemphana ndi lingaliro loperekedwa mu C[hipangano] C[hatsopano] chonse.”
Mawu a m’tsinde pa Luka 17:21 mu New International Version amasonyeza kuti mawu a Yesu angamasuliridwe motere: “Ufumu wa Mulungu uli pakati panu.” Matembenuzidwe a Mabaibulo ena amati: “Ufumu wa Mulungu uli pakati panu” kapena “uli mwa inu.” (The New English Bible; The Jerusalem Bible; Revised Standard Version) Malinga ndi New World Translation of the Holy Scriptures, Yesu anati: “Ufumu wa Mulungu uli pakati pa inu.” Yesu sanatanthauze kuti Ufumuwo unali m’mitima ya Afarisi onyada omwe anali kulankhula nawo. Mmalomwake, monga Mesiya woyembekezeredwa kwa nthaŵi yaitali ndi Wosankhidwa kukhala Mfumu, Yesu anali pakati pawo penipenipo. Koma nthaŵi yakutiyakuti ikapitapo Ufumu wa Mulungu usanadze.
Pamene Ukadza
Otsatira a Yesu Kristu okwanira chiŵerengero chakutichakuti asankhidwa kukhala olamulira anzake mu Ufumu Waumesiya wakumwamba. Mofanana ndi Yesu, iwo amafa okhulupirika kwa Mulungu ndipo amaukitsidwira ku moyo wauzimu kumwamba. (1 Petro 3:18) Pokhala ochepa m’chiŵerengero, iwo adzakhala mafumu ndi ansembe 144,000 ogulidwa mwa anthu. (Chivumbulutso 14:1-4; 20:6) Olamulira anzake a Yesu amaphatikizapo atumwi ake okhulupirika.—Luka 12:32.
Polankhula kwa otsatira ake pachochitika china, Yesu analonjeza kuti: ‘Alipo ena a iwo aima pano sadzalaŵa ndithu imfa, kufikira adzawona Mwana wa munthu atadza mu ufumu wake.’ (Mateyu 16:28) Mosangalatsa, vesi lotsatira limasonyeza kuti lonjezo la Yesu linakwaniritsidwa masiku oŵerengeka pambuyo pake. Panthaŵiyo anatenga ophunzira ake atatu kumka kuphiri kumene anasandulika pamaso pawo, ndipo iwo anamuwona m’masomphenya ali muulemerero wa Ufumu. (Mateyu 17:1-9) Koma Ufumuwo sunakhazikitsidwe panthaŵiyo. Kodi zimenezo zikachitika liti?
Limodzi la mafanizo a Yesu limasonyeza kuti sakaikidwa panthaŵi yomweyo monga Mfumu Yaumesiya. Pa Luka 19:11-15, timaŵerenga kuti: “Iye anawonjeza . . . fanizo, chifukwa anali iye pafupi pa Yerusalemu, ndipo iwo anayesa kuti ufumu wa Mulungu ukuti uwonekere pomwepo. Pamenepo anati, Munthu wa fuko lomveka ananka ku dziko lakutali, kudzilandirira yekha ufumu, ndi kubwerako. Ndipo anaitana akapolo ake khumi, nawapatsa iwo ndalama khumi, nati kwa iwo, Chita nazoni malonda kufikira ndibweranso. . . . Ndipo kunali, pakubwera iye, atalandira ufumuwo, anati aitanidwe kwa iye akapolo aja, amene adawapatsa ndalamazo, kuti adziŵe umo anapindulira pochita malonda.”
M’masiku amenewo kunkatenga nthaŵi yaitali kuti munthu ayende kuchoka ku Israyeli kupita ku Roma, kudikirira mumzindawo kufikira atalandira ufumu, ndi kubwerera kumudzi kwawo monga mfumu. Yesu anali ‘munthu wa fuko lomveka.’ Iye akalandira mphamvu monga Mfumu kwa Atate wake kumwamba koma sakaikidwa panthaŵi yomweyo monga Mfumu Yaumesiya. Otsatira ake akachita malonda mwakuchita ntchito yolengeza mbiri yabwino ya Ufumu kwa nthaŵi yaitali iye asanabwerere monga Mfumu.
Mmene Ufumuwo Umadzera
Kodi okonda Mulungu amapemphanji pamene apempherera kuti Ufumu wake udze? Iwo kwenikweni amapempha kuti Ufumu wakumwamba uchitepo kanthu mwakuwononga madongosolo aboma opangidwa ndi anthu amene alephera kukwaniritsa lonjezo lawo lakubweretsa mtendere weniweni ndi chipambano. Posonya ku chochitika chimenechi, mneneri Danieli analemba kuti: ‘Masiku a mafumu aja Mulungu wa kumwamba adzaika ufumu woti sudzawonongeka ku nthaŵi zonse, ndi ulamuliro wake sudzasiidwira mtundu wina wa anthu, koma udzaphwanya ndi kutha maufumu awo onse, nudzakhala chikhalire.’ (Danieli 2:44) Kodi zimenezi zidzachitika liti?
Yesu ananeneratu kuti zimenezi zikachitika mkati mwa mbadwo wa amene akawona zochitika zachilendo m’mbiri ya anthu. Ponena za “kukhalapo” kwake, Yesu anapereka ‘chizindikiro’ chachiungwe chophatikizapo zochitika zonga nkhondo yosalingana ndi ina yonse, zivomezi, njala, miliri—inde, ndi kulalikidwa kwa padziko lonse kwa mbiri yabwino ya Ufumu wa Mulungu.—Mateyu, mitu 24, 25; Marko, mutu 13; Luka, mutu 21.
Ulosi wa Yesu umaphatikizapo zinthu zomwe zikuchitika tsopano lino—m’zaka zathu za zana la 20. Chifukwa chake, sipadzapita nthaŵi yaitali kuti Ufumu wa Mulungu ubweretse madalitso aakulu kwa anthu. Inuyo mungakhale pakati pa awo amene adzasangalala ndi mapindu a ulamuliro wa Ufumu. Koma kodi Ufumu wa Mulungu ungatanthauzenji kwa inu ndi okondedwa anu?
Madalitso a Ulamuliro wa Ufumu
Chimwemwe chidzafalikira padziko lonse lapansi. Pansi pa ‘miyamba yatsopano’—Ufumu wakumwamba—padzakhala “dziko latsopano,” chitaganya cha padziko lonse cha nzika zomvera za Ufumuwo. ‘Mulungu yekha adzakhala nawo,’ analemba motero mtumwi Yohane. ‘Ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo.’ Panthaŵiyo sipadzakhalanso chifukwa chodandaulira koma chimwemwe chokha, popeza kuti ‘sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa.’—Chivumbulutso 21:1-4.
Sipadzakhalanso imfa. Chochititsa chisoni chachikulu chimenechi sichidzatilandanso mabwenzi ndi okondedwa athu. “Mdani wotsiriza amene adzathedwa ndiye imfa.” (1 Akorinto 15:26) Padzakhala chisangalalo chotani nanga pamene maliro adzaloŵedwa m’malo ndi kuukitsidwa kwa okhala m’chikumbukiro cha Mulungu!—Yohane 5:28, 29.
Thanzi labwino lidzaloŵa m’malo matenda ndi ukalamba. Makama a m’chipatala sadzadzazanso ndi anthu ovutika ndi matenda akuthupi ndi amaganizo. Sing’anga Wamkulu, Yesu Kristu, adzagwiritsira ntchito mtengo wa nsembe yake yadipo ‘kuchiritsa nawo amitundu.’ (Chivumbulutso 22:1, 2; Mateyu 20:28; 1 Yohane 2:1, 2) Kuchiritsa kumene anakuchita pamene anali padziko lapansi kunali chitsanzo chokha cha zimene adzachita mu Ufumu.—Yerekezerani ndi Yesaya 33:24; Mateyu 14:14.
Chakudya chidzakhala chochuluka. Monga momwe wamasalmo ananenera, ‘m’dzikomo mudzakhala dzinthu dzochuluka pamwamba pa mapiri.’ (Salmo 72:16) Pa chimenechi, ulosi wa Yesaya ukuwonjezera kuti: ‘Ndipo m’phiri limeneli Yehova wa makamu adzakonzera anthu ake onse phwando la zinthu zonona, phwando la vinyo wa pamitsokwe, la zinthu zonona za mafuta okhaokha, la vinyo wansenga wokuntha bwino.’ (Yesaya 25:6) Ndithudi, njala sidzakantha nzika za dziko lapansi mu ulamuliro wa Ufumu.
Dziko lonse lapansi lidzakhala paradaiso. Pamenepo lidzakwaniritsidwa lonjezo la Yesu kwa wochita zoipa wolapa lakuti: “Udzakhala nane m’Paradaiso.” (Luka 23:43, NW) Nanunso mungasangalale ndi moyo wamuyaya padziko lapansili, dziko lapansi lochotseredwa kuipa ndi kusandulizidwa kukhala mbulunga yosangalatsa, yonga paki.—Yohane 17:3.
Ziyembekezo zosangalatsa zimenezi zikuperekedwa kwa anthu onse omvera. Mawu ouziridwa a Yehova, Baibulo, amapereka zitsimikizo zimenezi. Ndipo zonsezi nzimene Ufumu wa Mulungu ungatanthauze kwa inu.
[Chithunzi patsamba 7]
Kodi mumakhulupirira zimene Yesu ananena ponena za Ufumu wa Mulungu?