Sali Ochita Malonda Nawo Mawu a Mulungu
“TINALI kugulitsa uminisitala wathu ndi ndalama.” Amenewo ndimawu a amene kale anali “minisitala wa pemphero pa telefoni” wofunsidwa mu lipoti lofufuza la alaliki a pa wailesi yakanema aku Amereka chakumapeto kwa 1991.
Programu imeneyi inasumika pa mautumiki amaulaliki atatu mu United States. Inaulula kuti anthu akufunkhidwa madola mamiliyoni makumi ambiri chaka chirichonse ndi atatu okha amenewa. “Ulaliki” wina unafotokozedwa kukhala “fakitale ya zopereka yopangidwa mwamachenjera.” Onsewa anaphatikizidwa m’zinyengo zambiri. Kodi zimenezi zikukudabwitsani?
Chipembedzo Chikufufuzidwa
Sikuchitira ulaliki pa televizeni kokha komanso ngakhale zipembedzo zoyanjidwa zikufufuzidwa mosamalitsa ndi maboma, magulu ena openda zizoloŵezi zotsutsana ndi lamulo, ndi anthu onse. M’zochitika zina, kuyenera kwa tchalitchi kwakukhala mwini katundu, zochita zandale zadziko zochirikizidwa ndi ndalama zachipembedzo, ndi moyo wamataya wa atsogoleri achipembedzo olandira ndalama zambiri zachititsa zikaikiro zakuyenerera kwake.
Kodi atsogoleri achipembedzo ena amayenerera motani malongosoledwe olemekezeka a uminisitala Wachikristu operekedwa ndi mtumwi Paulo pafupifupi zaka 2,000 zapitazo? Iye analemba kuti: ‘Sitichita malonda nawo mawu a Mulungu; koma monga mwa chowona mtima, koma monga mwa Mulungu pamaso pa Mulungu, tilankhula mwa Kristu.’ (2 Akorinto 2:17) Kodi ndani lerolino amene amayenerera malongosoledwe amenewa?
Kukuthandizani kupenda mikhalidweyo, tiyeni tipende mosamalitsa mmene uminisitala Wachikristu wa Paulo ndi anzake unachirikizidwira ndi ndalama. Kodi unali wosiyana motani ndi enawo a m’tsiku lake?
Alaliki Oyendayenda a M’zaka za Zana Loyamba
Monga mlaliki woyendayenda, Paulo sanali iye yekha. M’tsikulo ambiri anayendayenda kupititsa patsogolo malingaliro awo okhudza chipembedzo ndi nthanthi. Wolemba Baibulo Luka akulankhula za “Ayuda enanso oyendayenda, otulutsa ziŵanda.” (Machitidwe 19:13) Pamene Yesu Kristu anatsutsa Afarisi, anawonjezera kuti: “Chifukwa mupitapita kunyanja ndi kumtunda kuyesa munthu mmodzi mtembenuki.” (Mateyu 23:15) Yesu mwiniyo anali minisitala woyendayenda. Iye anaphunzitsa atumwi ake ndi ophunzira kumtsanzira mwakulalikira osati m’Yudeya ndi Samariya mokha koma “kufikira malekezero ake adziko.”—Machitidwe 1:8.
M’maulendo awo, otsatira a Yesu anakumana ndi alaliki osakhala Ayuda. M’Atene, Paulo anapikisana ndi anthanthi a Epikureya ndi a Stoiki. (Machitidwe 17:18) Muulamuliro wonsewo wa Roma, Asinikisi anakopa anthu mwa kulalikira mofuula. Atsatiri a Isis ndi Serapis anawonjezera chisonkhezero chawo pa akazi ndi akapolo mwa malonjezo akuti anthu onse akalingana m’chipembedzo ndi m’zamayanjano. Zikhulupiriro za madzoma amphamvu yakubala za kummawa zinali poyambira zipembedzo za chinsinsi zambiri za dziko la Girisi ndi Roma. Lonjezo lakutetezeredwa machimo ndi chikhumbo chakukhala ndi phande m’kudziŵa zinsinsi za umulungu zinakopa anthu kutsatira milungu yonama ya Demeter ndi Dionysus, ndi Cybele.
Kodi Ndalama Zogwiritsira Ntchito Zinapezedwa Motani?
Komabe, maulendo anali odya ndalama zambiri. Kuwonjezera pa kulipirira kusamuka, misonkho ya pamsewu, ndi kulipirira ngalawa, apaulendo anafunikira chakudya, malo ogona, nkhuni, zovala, ndi mankhwala. Alaliki, aphunzitsi, anthanthi, ndi okhulupirira zinsinsi anakhutiritsa zosoŵa zimenezi m’njira zazikulu zisanu. Iwo (1) anaphunzitsa molandira malipiro; (2) anachita ntchito zazing’onozing’ono ndi zaganyu; (3) anavomereza kuchereza ndi zopereka zodzifunira; (4) anazigwirizanitsa ndi anthu achuma, kaŵirikaŵiri aphunzitsi a sande sukulu; ndipo (5) anapempha. Kudzikonzekeretsa kumanidwa, wopemphapempha wina wotchuka Wachisiniki Diogenes anapempha ngakhale mafano opanda moyo kukhala chopereka.
Paulo anadziŵa alaliki ena amene anadzinenera kukhala aminisitala Achikristu koma, mofanana ndi anthanthi ena Achigiriki, anapalana ubwenzi ndi achuma nabera osauka. Iye anachenjeza mpingo m’Korinto, akumati: “Mulola . . . ngati wina alikwira inu, ngati wina alanda zanu.” (2 Akorinto 11:20) Yesu Kristu sanafunkhe chinthu chirichonse, ndiponso Paulo ndi antchito anzake sanatero. Koma alaliki aumbombo a ku Korinto anali “atumwi onyenga, ochita ochenjerera,” ndi aminisitala a Satana.—2 Akorinto 11:13-15.
Malangizo a Yesu kwa ophunzira ake anali kukaniza kuphunzitsa kaamba ka malipiro. “Munalandira kwaulere, patsani kwaulere,” iye analangiza motero. (Mateyu 10:8) Ngakhale kuti kupemphapempha kunali kofala, sikunali koyanjidwa m’masiku amenewo. M’limodzi la mafanizo ake, Yesu akusimba za mdindo wina kukhala akunena kuti, “Kupemphapempha kundichititsa manyazi.” (Luka 16:3) Chifukwa chake, m’malongosoledwe a Baibulo sitimapeza konse otsatira okhulupirika a Yesu kukhala akupempha ndalama kapena katundu. Iwo anatsatira lamulo la makhalidwe abwino lakuti: “Ngati munthu safuna kugwira ntchito, asadyenso.”—2 Atesalonika 3:10.
Yesu analimbikitsa ophunzira ake kusamalira zosoŵa zawo m’njira ziŵiri. Choyamba, iwo akakhoza, monga momwe Paulo ananenera, ‘kukhala ndi moyo mwauthenga wabwino.’ Motani? Mwakuvomereza kuchereza koperekedwa modzifunira. (1 Akorinto 9:14; Luka 10:7) Chachiŵiri, iwo akadzipezera okha zinthu zakuthupi.—Luka 22:36.
Njira Zimene Paulo Anagwiritsira Ntchito
Kodi ndimotani mmene Paulo anagwiritsirira ntchito malamulo amakhalidwe abwino otchulidwawo? Eya, ponena za ulendo waumishonale wachiŵiri wa mtumwiyo, Luka analemba kuti: “Tinachokera ku Trowa m’ngalawa, mmene tinalunjikitsa ku Samotrake, ndipo m’mawa mwake ku Neapoli; pochokera kumeneko tinafika ku Filipi, mudzi wa ku Makedoniya, waukulu wa m’dzikomo, wa miraga ya Roma; ndipo tidagona momwemo masiku ena.” Ulendo wonse, chakudya, ndi kulipirira malo ogona zinasamaliridwa ndi iwo eni.—Machitidwe 16:11, 12.
Potsirizira pake, mkazi wina dzina lake Lidiya anavomereza “zimene anazinena Paulo. Pamene anabatizidwa iye ndi apabanja pake anatidandaulira ife, kuti, ngati mwandiyesera ine wokhulupirika kwa Ambuye, muloŵe m’nyumba yanga, mugone m’menemo. Ndipo anatiumiriza ife.” (Machitidwe 16:13-15) Mwinamwake kwakukulukulu chifukwa cha kuchereza kwa Lidiya, Paulo anakhoza kulembera okhulupirira anzake m’Filipi kuti: “Ndiyamika Mulungu wanga pokumbukira inu ponse; nthaŵi zonse m’pembedzero langa lonse la kwa inu nonse ndichita pembedzerolo ndi kukondwera, chifukwa cha chiyanjano chanu chakuthandizira Uthenga Wabwino, kuyambira tsiku loyambalo, kufikira tsopano lino.”—Afilipi 1:3-5.
Luka akutchula zochitika zochuluka za anthu ochereza antchito Achikristu oyendayenda amenewa. (Machitidwe 16:33, 34; 17:7; 21:7, 8, 16; 28:2, 7, 10, 14) M’makalata ake ouziridwa, Paulo anavomereza ndipo anapereka zithokozo za kuchereza ndi mphatso zimene adalandira. (Aroma 16:23; 2 Akorinto 11:9; Agalatiya 4:13, 14; Afilipi 4:15-18) Komabe, iyemwini kapena atsamwali ake sanapereke lingaliro lakuti ayenera kupatsidwa mphatso kapena chichirikizo cha ndalama. Mboni za Yehova zinganene kuti kaimidwe kamaganizo kameneka kakuwonekabe pakati pa oyang’anira awo oyendayenda.
Wosadalira pa Kucherezedwa
Paulo sanali wodalira pa kucherezedwa. Iye anaphunzira ntchito imene inafunikira kugwira ntchito zolimba ndi maola ochuluka koma yopereka malipiro ochepa. Pamene mtumwiyo anafika m’Korinto monga mmishonale, “Anapeza Myuda wina dzina lake Akula, . . . ndi mkazi wake Priskila. . . . ndipo popeza anali wa ntchito imodzimodzi, anakhala nawo, ndipo iwowa anagwira ntchito; pakuti ntchito yawo inali yakusoka mahema.”—Machitidwe 18:1-3.
Pambuyo pake, m’Efeso, Paulo anali kugwirabe ntchito zolimba. (Yerekezerani ndi Machitidwe 20:34; 1 Akorinto 4:11, 12.) Iye angakhale atapeza maphunziro apadera a kusoka mahema a cilicium, mahema okakala, a ubweya wa mbuzi kuchokera kuchigawo cha tawuni lakwawo. Tingathe kuyerekezera Paulo atakhala pakampando, ataweramira pa benchi lake logwirirapo ntchito, kudula ndi kusoka kufikira mdima bii. Popeza kuti phokoso la mushopu logwirira ntchito linali lochepekera, kutheketsa kulankhula pogwira ntchito yakalavula gagayo kukhala kosavuta, Paulo angakhale anali ndi mpata wakuchitira umboni kwa mwinishopu, antchito ake, akapolo, odzagula, ndi mabwenzi.—Yerekezerani ndi 1 Atesalonika 2:9.
Mmishonale Paulo anakana kuchita nawo malonda uminisitala wake kapena mwanjira iriyonse kupereka lingaliro lakuti anali kuchirira pa Mawu a Mulungu. Iye anauza Atesalonika kuti: “Pakuti mudziŵa nokha mmene muyenera kutitsanza ifemo; pakuti sitinakhala dwachedwache mwa inu; kapena sitinadya mkate chabe pa dzanja la munthu ali yense, komatu m’chivuto ndi chipsinjo, tinagwira ntchito usiku ndi usana, kuti tingalemetse wina wa inu; sichifukwa tiribe ulamuliro, komatu kuti tidzipereke tokha tikhale kwa inu chitsanzo chanu, kuti mukatitsanze ife.”—2 Atesalonika 3:7-9.
Atsanziri a m’Zaka za Zana la Makumi Aŵiri
Kufikira lerolino, Mboni za Yehova zimatsatira chitsanzo chabwino kwambiricho cha Paulo. Akulu ndi atumiki otumikira samalandira ndalama kapena ngakhale malipiro alionse ku mipingo imene amatumikira. Mmalo mwake iwo amapezera zofunika za mabanja awo mofanana ndi munthu wina aliyense, unyinji wawo mwakuloŵa ntchito yolembedwa. Aminisitala apainiya a nthaŵi yonse nawonso amadzipezera zosoŵa, ambiri amagwira ntchito zongowatheketsa kupeza zofunika zazikulu. Chaka chirichonse Mboni zimayenda maulendo odzilipirira kukalalikira kumalo akutali osafikidwa kaŵirikaŵiri ndi mbiri yabwino. Ngati mabanja a m’malowo awaitanira kukadya nawo chakudya kapena kuwapatsa malo ogona, amayamikira zimenezi koma samaluluza kuchereza kotero.
Kulalikira konse ndi kuphunzitsa kochitidwa ndi Mboni za Yehova nkodzifunira, ndipo sizimalipiritsa konse uminisitala wawo. Komabe, zopereka zochepa ku ntchito yawo yolalikira yapadziko lonse lapansi zimalandiridwa ndi kutumizidwa ku Watch Tower Society kaamba ka chifuno chimenechi. (Mateyu 24:14) Uminisitala wa Mboni sumaphatikizapo malonda mwanjira iriyonse. Mofanana ndi Paulo aliyense wa iwo angathe kunena mowona mtima kuti: “Ndinalalikira kwa inu Uthenga Wabwino wa Mulungu mwaufulu.” (2 Akorinto 11:7) Mboni za Yehova siziri “akuchita malonda nawo mawu a Mulungu.”
[Bokosi patsamba 27]
MMENE ENA AMAPATSIRA ZOPEREKA KU NTCHITO YOLALIKIRA UFUMU
◻ Zopereka Za Ntchito Yapadziko LONSE: Ambiri amaika pambali kapena kulinganiza ndalama imene amaika m’mabokosi azopereka olembedwa: “Zopereka za Ntchito Yapadziko Lonse ya Sosaite—Mateyu 24:14.” Mwezi uliwonse mpingo umatimiza ndalamazo kaya ku malikulu a dziko lonse ku Brooklyn, New York, kapena ku ofesi yanthambi yapafupi.
◻ MPHATSO: Zopereka zodzifunira za ndalama zingatumizidwe mwachindunji ku Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, 25 Columbia Heights, Brooklyn, New York 11201, kapena ku ofesi ya Sosaite ya nthambi yakwanuko. Zokometsera kapena zinthu zina zamtengo wapatali zingaperekedwenso. Kalata yachidule yofotokoza kuti zimenezo zaperekedwa monga mphatso iyenera kutsagana ndi zoperekazo.
◻ KAKONZEDWE KA CHOPEREKA CHODALIRA PA MKHALIDWE: Ndalama zingaperekedwe ku Watch Tower Society kuikiziridwa kufikira imfa ya woperekayo, limodzi ndi kuthekera kwakuti ngati munthuyo angazifune, zidzabwezeredwa kwa woperekayo.
◻ INSHUWALANSI: Watch Tower Society ingatchulidwe monga wopindula mu inshuwalansi kapena m’kakonzedwe ka penshoni. Sosaite iyenera kuuzidwa za kakonzedwe kalikonse kotero.
◻ MAAKAUNTI A BANKI: Maakaunti a banki, zikalata zoikizira ndalama, kapena maakaunti a aliyense payekha wopuma ntchito angalembedwe moikizira ku Watch Tower Society kapena kulembedwa kuti wolipiridwa pambuyo pa imfa akhale Watch Tower Society, mogwirizana ndi malamulo a mabanki amomwemo. Sosaite iyenera kuuzidwa za makonzedwe aliwonse.
◻ CHUMA NDI MAPANGANO: Chuma ndi mapangano zingapatsidwe monga chopereka ku Watch Tower Society kaya monga mphatso yachindunji kapena mwakakonzedwe kamene ndalama zolandiridwa zikupitirizabe kulipiridwa kwa woperekayo.
◻ CHUMA MUMPANGIDWE WA NYUMBA KAPENA MINDA: Chuma mumpangidwe wa nyumba kapena minda chokhoza kugulitsidwa chingaperekedwe ku Watch Tower Society kaya mwa kuchipereka monga mphatso yachindunji kapena mwakusungidwa kwa chumacho ndi mwini wake amene angapitirizebe kukhala nacho kufikira imfa yake. Munthuyo ayenera kuuza Sosaite asanailoŵetse m’pangano la chuma chirichonse chotero.
◻ ZIKALATA ZOGAŴA CHUMA CHA MASIYE NDI MAPANGANO OIKIZIRA CHUMA: Chuma kapena ndalama zingakhale choloŵa ku Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania kudzera mwa pangano la amene adzatenga chuma chamasiye lovomerezedwa mwa lamulo, kapena Sosaite ingatchulidwe kukhala yodzapindula ndi pangano loikizira chuma. Pangano loikizira chuma lopindulitsa gulu lachipembedzo lingagaŵire mapindu ena amsonkho. Kope la chikalata chogaŵa chuma cha masiye kapena pangano loyikizira chuma liyenera kutumizidwa ku Sosaite.
Kuti mupeze chidziŵitso chowonjezereka pankhani zotere, lemberani ku Treasurer’s Office, Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, Box 33459, Lusaka 10101, kapena ku ofesi ya Sosaite ya nthambi yakwanuko.
[Bokosi patsamba 29]
ANAFUNA KUTHANDIZA
TIFFANY wazaka khumi ndi chimodzi zakubadwa ali msungwana wasukulu ku Baton Rouge, Louisiana, U.S.A. Posachedwapa, Mboni yachichepere ya Yehova imeneyi inalemba chimangirizo pa mutu wakuti “Maphunziro mu Amereka.” Monga chotulukapo, makolo ake amene ndi Mboni analandira kalata iyi kuchokera kwa hedimasitala:
“Mkati mwa mlungu Wamaphunziro a Amereka, chimangirizo chimodzi chopambana zonse m’kalasi lirilonse chimaŵerengedwa pa intakomu. Ndinali wosangalala kugwiritsira ntchito chimangirizo cha Tiffany mmawa uno. Iye alidi dona wachichepere wapadera. Iye ngwokhazikika maganizo, wachidaliro, waluso, ndi wachisomo. Sikaŵirikaŵiri kuti ndawona mwana wa giredi lachisanu ndi chimodzi wokhala ndi mikhalidwe yabwino yambiri imeneyi. Tiffany ngwachithandizo ku sukulu yathu.”
Tiffany anaposa onse mumpikisano wa chimangirizo umenewu. Pambuyo pake analembera Watch Tower Society kuti: “Mwinamwake ndinapambana mpikisanowo kokha chifukwa cha bukhu la Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza. . . .Ndinagwiritsira ntchito mitu yonena za maphunziro. . . . Zikomo kwambiri pakufalitsa bukhu lothandiza ndi losonkhezera maganizo limeneli. Chimangirizo changa chopambanacho chinandipatitsa mphotho ya 7 dola. Ndikutumiza 7 dola imeneyi ndi ina 13 dola, pamodzi 20 dola monga chopereka ku ntchito yolalikira yapadziko lonse lapansi. . . . Ndikakula, ndikuyembekezeranso kudzipereka ku utumiki wa pa Beteli.”
[Chithunzi patsamba 26]
Nthaŵi zina, Paulo anachirikiza moyo wake mwakusoka mahema