Yehova—Mulungu Wowona ndi Wamoyo
FARAO wa Igupto analankhula mwamwano ndi monyoza pamene anafunsa kuti: “Yehova ndani?” (Eksodo 5:2) Monga momwe nkhani yapitayo yasonyezera, mkhalidwe wamaganizo umenewo unadzetsa miliri ndi imfa pa Aigupto, kuphatizikapo manda a m’madzi kwa Farao ndi magulu ake ankhondo.
M’Igupto wakale, Yehova Mulungu anatsimikiziritsa ukulu wake pa milungu yonama. Koma pali zambiri zoziphunzira ponena za iye. Kodi umunthu wake uli ndi mikhalidwe ina yotani? Ndipo kodi iye amafunanji kwa ife?
Dzina ndi Kutchuka Kwake
Pamene anauza Farao wa Igupto zimene anatumidwa, Mose sananene kuti: ‘Ambuye wanena zakutizakuti.’ Farao ndi Aigupto ena analingalira milungu yawo yonamayo kukhala ambuye. Mose sanatero, iye anagwiritsira ntchito dzina laumulungu, Yehova. Iye mwiniyo analimva likutchulidwa kuchokera kumwamba pamene anali pa chitsamba choyaka moto m’dziko la Midyani. Cholembedwa chouziridwacho chimati:
“Ndipo Mulungu ananena ndi Mose, nati kwa iye, Ine ndine YEHOVA: . . . Ndamvanso kubuula kwa ana a Israyeli, amene Aaigupto awayesa akapolo; ndipo ndakumbukira chipangano changa. Chifukwa chake nena kwa ana a Israyeli, Ine ndine Yehova, ndipo ndidzakutulutsani pansi pa akatundu a Aaigupto, ndipo ndidzakulanditsani ku ukapolo wanu; ndipo ndidzakuombolani ndi dzanja lotambasuka, ndi maweruzo aakulu; ndipo ndidzalandira inu mukhale anthu anga, ndipo ndidzakhala Ine Mulungu wanu; ndipo mudzadziŵa kuti Ine ndine Yehova Mulungu wanu, wakutulutsa inu pansi pa akatundu a Aaigupto. Ndipo ndidzakuloŵetsani m’dziko [la Kanani] limene ndinakweza dzanja langa kunena za ilo, kuti ndilipereke kwa [makolo anu] Abrahamu, kwa Isake ndi kwa Yakobo; ndipo ndidzakupatsani ilo likhale lanulanu; Ine ndine Yehova.”—Eksodo 6:1-8.
Izozo nzimene Yehova anachita kumene. Anamasula Aisrayeli kuukapolo wa Aigupto ndi kuwatheketsa kutenga dziko la Kanani. Monga momwe analonjezera, Mulungu anatheketsa zonsezi. Ha, nzoyenerera chotani nanga! Dzina lake, lakuti Yehova, limatanthauza “Wochititsa Kukhalako.” Baibulo limatcha Yehova ndi maina aulemu onga “Mulungu,” “Ambuye Mfumu,” “Mlengi,” “Atate,” “Wamphamvuyonse,” ndi “Wam’mwambamwamba.” Komabe, dzina lakelo lakuti Yehova limamdziŵikitsa monga Mulungu wowona amene m’kupita kwanthaŵi amakwaniritsa zifuno zake zazikulu.—Yesaya 42:8.
Ngati tinati tiŵerenge Baibulo m’zinenero zake zoyambirira, tikanapeza dzina la Mulungu kwa nthaŵi zikwi zambiri. M’Chihebri limalembedwa ndi makonsonanti anayi Yod He Waw He (יהוה), otchedwa Tetragrammaton, oŵerengedwa kuchokera kulamanja kumka kulamanzere. Awo olankhula Chihebri anaikamo mavawelo otchulira, koma anthu lerolino samadziŵa bwino kuti anali otani. Pamene kuli kwakuti ena amayanja kalembedwe kakuti Yahweh, kalembedwe ka Yehova kali kofala ndipo kamadziŵikitsa Mlengi wathu bwino lomwe.
Kugwiritsira ntchito dzina la Yehova kumasiyanitsanso Mulungu ndi wotchedwayo “Ambuye wanga” pa Salmo 110:1, pamene matembenuzidwe ena amati: “AMBUYE [Chihebri, יהוה] ananena kwa Ambuye wanga, Khala padzanja lamanja langa, kufikira nditaika adani ako chopondapo mapazi ako.” (King James Version) Povomereza kupezeka kwa dzina la Mulungu palemba la Chihebri panopa, New World Translation imati: “Mawu a Yehova kwa Ambuye wanga ngakuti: ‘Khala kudzanja langa lamanja kufikira nditaika adani ako monga chopondapo mapazi ako.’” Mawu a Yehova Mulungu amenewo amanena mwaulosi za Yesu Kristu, amene wolembayo anamutcha “Ambuye wanga.”
Yehova anatchuka mbiri m’tsiku la Farao. Kupyolera mwa Mose, Mulungu anauza wolamulira wouma mtima uja kuti: “Pakuti nthaŵi ino ndidzatuma miliri yanga yonse pamtima pako, ndi pa anayamata ako, ndi pa anthu ako; kuti udziŵe kuti palibe wina wonga ine pa dziko lonse lapansi. Pakuti ndatambasula dzanja langa tsopano, kuti ndikupande iwe ndi anthu ako ndi mliri, ndi kuti uwonongeke pa dziko lapansi. Koma ndithu chifukwa chake ndakuimika kuti ndikuwonetse mphamvu yanga, ndi kuti alalikire dzina langa pa dziko lonse lapansi.”—Eksodo 9:14-16.
Ponena za ulendo wa Israyeli wochoka ku Igupto ndi kugonjetsa kwawo mafumu ena Achikanani, mkazi wina Rahabi wa m’Yeriko anauza azondi aŵiri Achihebri kuti: “Ndidziŵa kuti Yehova wakupatsani dzikoli [inu Aisrayeli], ndi kuti kuopsa kwanu kwatigwera, ndi kuti okhala m’dziko onse asungunuka pamaso panu. Popeza tidamva kuti Yehova anaphwetsa madzi a m’Nyanja Yofiira pamaso panu, muja mudatuluka m’Aigupto; ndi chija munachitira mafumu aŵiri a Aamori okhala tsidya la Yordano, ndiwo Sihoni ndi Ogi, amene mudawawononga konse. Ndipo titamva ichi mitima yathu inasungunuka; analibenso mtima ndi mmodzi yense, chifukwa cha inu; pakuti Yehova Mulungu wanu, ndiye Mulungu wa m’mwamba umo, ndi pa dziko lapansi.” (Yoswa 2:9-11) Inde, kutchuka kwa Yehova kunafalikira.
Yehova ndi Mikhalidwe Yake
Wamasalmo anatchula chikhumbo chake cha mtima wonse ichi: “Kuti adziŵe kuti inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, Ndinu Wam’mwambamwamba pa dziko lonse lapansi.” (Salmo 83:18) Popeza kuti uchifumu wa Yehova ngwaponseponse m’chilengedwe chonse, otsatira ozunzidwa a Yesu anakhoza kupemphera kuti: “Mfumu, Inu ndinu wolenga thambo la kumwamba ndi dziko, ndi nyanja, ndi zonse zili mmenemo.” (Machitidwe 4:24) Ndipo nkotonthoza chotani nanga kudziŵa kuti Yehova ali “Wakumva pemphero”!—Salmo 65:2.
Mkhalidwe waukulu wa Yehova ndiwo chikondi. Ndithudi, “Mulungu ndiye chikondi”—chitsanzo chenicheni cha mkhalidwe umenewu. (1 Yohane 4:8) Ndiponso, “kwa iye kuli nzeru ndi mphamvu.” Yehova ali wa nzeru zonse ndi wa mphamvu zonse, komatu samagwiritsira ntchito mphamvu zake mwanjira yolakwa. (Yobu 12:13; 37:23) Tikhoza kukhalanso otsimikiza kuti Yehova adzachita nafe mwachilungamo nthaŵi zonse, popeza kuti “chilungamo ndi chiweruzo ndizo zolimbitsa mpando wachifumu wake.” (Salmo 97:2) Ngati tilakwa koma tilapa, tingapeze chitonthozo mwakudziŵa kuti Yehova ali “Mulungu wachifundo ndi wachisomo, wolekereza, ndi wa ukoma mtima wochuluka, ndi wachowonadi.” (Eksodo 34:6) Chotero mposadabwitsa kuti tikhoza kupeza chimwemwe m’kutumikira Yehova!—Salmo 100:1-5.
Mfumu Yakumwamba Yosayerekezereka
Mwana wa Yehova, Yesu Kristu, anati: “Mulungu ndiye Mzimu.” (Yohane 4:24) Chifukwa chake, nkosatheka kumuwona Yehova ndi maso aumunthu. Ndipotu, Yehova anauza Mose kuti: “Sungathe kuona nkhope yanga; pakuti palibe munthu adzandiona ine ndi kukhala ndi moyo.” (Eksodo 33:20) Mfumu yakumwamba imeneyi njaulemerero kwambiri kwakuti anthu sangathe kuwonana nayo nakhalabe ndi moyo.
Ngakhale kuti Yehova ngwosawoneka kwa ife, pali maumboni ochuluka osonyeza kuti iye aliko monga Mulungu Wamphamvuyonse. Ndithudi, “pakuti chilengedwere dziko lapansi zaoneka bwino zosaoneka zake ndizo mphamvu yake yosatha ndi umulungu wake.” (Aroma 1:20) Dziko lapansi—limodzi ndi udzu wake, mitengo, zipatso, zamasamba, ndi maluŵa—zimapereka umboni wa Umulungu wa Yehova. Mosiyana ndi milungu ya mafano yopanda pake, Yehova amapereka mvula ndi nyengo zobalitsa zipatso. (Machitidwe 14:16, 17) Penyani nyenyezi kumwamba usiku. Ndiumboni waukulu chotani nanga wa Umulungu wa Yehova ndi luso la kulinganiza!
Yehova walinganizanso zolengedwa zauzimu zoyera zaluntha kumwamba. Monga gulu logwirizana, iwo amachita chifuniro cha Mulungu, monga momwe wamasalmo akunenera kuti: “Lemekezani Yehova, inu angelo ake; a mphamvu zolimba, akuchita mawu ake, akumvera liwu la mawu ake. Lemekezani Yehova, inu makamu ake onse; inu atumiki ake akuchita chomkondweretsa iye.” (Salmo 103:20, 21) Yehova walinganizanso anthu ake padziko lapansi. Mtundu wa Israyeli unali wolinganizidwa bwino, analinso otero otsatira oyambirira a Mwana wa Mulungu. Mofananamo lerolino, Yehova ali ndi gulu la padziko lonse la Mboni zachangu, zikumalalikira mbiri yabwino yakuti Ufumu wake wayandikira.—Mateyu 24:14.
Yehova Ndiye Mulungu Wowona ndi Wamoyo
Umulungu wa Yehova wasonyezedwa m’njira zambiri! Iye ananyazitsa milungu yonama ya Igupto ndipo analoŵetsa Aisrayeli mwachisungiko m’Dziko Lolonjezedwa. Chilengedwe chikupereka umboni wochuluka wa Umulungu wa Yehova. Ndipo palibiretu kufanana kulikonse pakati pa iye ndi milungu ya mafano yopanda pake ya zipembedzo zonyenga.
Mneneri Yeremiya anasonyeza kusiyana kwakukulu pakati pa Yehova, Mulungu wamoyoyo, ndi mafano opanda moyo opangidwa ndi anthu. Kusiyana kumeneko kumafotokozedwa bwino lomwe m’chaputala 10 cha Yeremiya. Mwa zinthu zina, Yeremiya analemba kuti: “Yehova ndiye Mulungu wowona; ndiye Mulungu wamoyo, mfumu yamuyaya.” (Yeremiya 10:10) Mulungu wamoyo ndi wowona, Yehova, analenga zinthu zonse. Iye anamasula Aisrayeli kuukapolo wozunza m’Igupto. Palibe chosatheka kwa iye.
Yehova, “Mfumu yosatha,” adzayankha pemphero lakuti: “Atate wathu wa Kumwamba, dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga kumwamba chomwecho pansi pano.” (1 Timoteo 1:17; Mateyu 6:9, 10) Ufumu Waumesiya wakumwamba, wokhala kale m’manja mwa Yesu Kristu, posachedwapa udzakantha ndi kuwononga adani a Yehova onse. (Danieli 7:13, 14) Ufumu umenewo udzabweretsanso dziko latsopano la madalitso osatha kwa mtundu wa anthu omvera.—2 Petro 3:13.
Padakali zambiri zoziphunzira ponena za Yehova ndi zifuno zake. Bwanji osachipanga kukhala cholinga chanu chotsimikizirika kupeza chidziŵitso choterocho ndi kuchita mogwirizana nacho? Mukatero, mudzakhala ndi mwaŵi wakupeza moyo wosatha m’paradaiso wa padziko lapansi muulamuliro wa Ufumuwo. Mudzakhalapo ndi moyo pamene chisoni, choŵaŵitsa, ndipo ngakhale imfa yeniyeniyo zidzachoka ndi pamenenso chidziŵitso cha Yehova chidzadzaza dziko lapansi. (Yesaya 11:9; Chivumbulutso 21:1-4) Umenewo ungakhale moyo wanu wamtsogolo ngati mufunafuna, kupeza, ndi kuchita mogwirizana ndi mayankho ozikidwa pa Baibulo a funso lakuti, kodi “Yehova ndani?”
[Mawu a Chithunzi patsamba 7]
Pictorial Archive (Near Eastern History) Est.