Banja Lachikristu Limachitira Zinthu Pamodzi
“Koma ndikudandaulirani inu, abale, . . . mumangike mu mtima womwewo ndi m’chiweruziro chomwecho.”—1 AKORINTO 1:10.
1. Kodi mkhalidwe wa umodzi wa m’mabanja ambiri ngwotani?
KODI banja lanu nlogwirizana? Kapena kodi aliyense amachita mwanjira yake yodziimira? Kodi mumachitira zinthu pamodzi? Kapena kodi mumakhala malo amodzi panthaŵi yofanana mwakamodzikamodzi? Liwulo “banja” limanena za nyumba yogwirizana.a Komabe, simabanja onse amene ali ogwirizana. Mlangizi wina wa ku Britain anafikira pakunena kuti: “Mmalo mwakukhala maziko a chitaganya chabwino, banja . . . lakhala magwero a kusakhutiritsidwa kwathu konse.” Kodi zimenezo nzowona m’banja lanu? Ngati ndichoncho, kodi liyenera kukhala lotero?
2. Kodi ndianthu ati a m’Baibulo amene anapereka umboni wochokera kubanja labwino?
2 Kugwirizana kapena kusagwirizana kwa banja kaŵirikaŵiri kumadalira pautsogoleri, kaya wa makolo aŵiri kapena kholo limodzi. M’nthaŵi za Baibulo, mabanja ogwirizana amene analambirira pamodzi analandira dalitso la Yehova. Zimenezi zinali choncho mu Israyeli wakale, kumene mwana wamkazi wa Yefita, Samsoni, ndi Samueli, aliyense m’njira yosiyana, anapereka umboni wakuti anachokera m’banja laumulungu. (Oweruza 11:30-40; 13:2-25; 1 Samueli 1:21-23; 2:18-21) M’nthaŵi zakale Zachikristu, Timoteo, tsamwali wa Paulo wokhulupirika pamaulendo ena a Paulo a umishonale, analeredwa ndi chidziŵitso cha Malemba Achihebri ndi agogo ake aakazi Loisi ndi amake, Yunike. Ha anadzakhala wophunzira ndi mmishonale wapadera chotani nanga!—Machitidwe 16:1, 2; 2 Timoteo 1:5; 3:14, 15; onaninso Machitidwe 21:8, 9.
Kodi Nchifukwa Ninji Kuchitira Zinthu Pamodzi?
3, 4. (a) Kodi ndimikhalidwe iti imene iyenera kuwonekera m’banja logwirizana? (b) Kodi banja lingakhale bwanji loposa nyumba wamba?
3 Kodi nchifukwa ninji kuli kopindulitsa kuti mabanja achitire zinthu pamodzi? Chifukwa chakuti kumamangirira kumvetsetsana ndi kulemekezana. Mmalo mwa kudzipatula ife eni kwa wina ndi mnzake, timakhala athithithi ndi kuchilikizana. Nkhani yaposachedwa ya m’magazini akuti Family Relations inasimba kuti: “Chithunzi chabwinopo chofotokoza mikhalidwe ina ya ‘mabanja olimba’ chaonekera. Mikhalidwe imeneyo ikuphatikizapo kudalirana ndi kuyamikirana, kumamatirana, kulankhulana kwabwino, luso la kuthetsa mavuto, ndi mkhalidwe wauzimu.”
4 Pamene mikhalidwe imeneyi ikhala m’banja, panyumba sipamakhalanso monga malo ongoimapo pogula petulo. Sipamangokhala panyumba wamba. Pamakhala malo okondeka amene amakopa ziŵalo za banja. Ali malo achisangalalo ndi chikondi, chifundo, ndi kumvetsetsa. (Miyambo 4:3, 4) Ndiwo chisa kumene umodzi wabanja umapezeka, osati ngaka ya namkalizi ya kuvutana ndi magaŵano. Koma kodi zimenezi zimachitidwa motani?
Kuchitira Zinthu Pamodzi Paphunziro Labanja
5. Kodi timagwiritsira ntchito chiyani kotero kuti tiphunzire kulambira kowona?
5 Kulambira kowona kwa Yehova kumaphunziridwa mwakugwiritsira ntchito luso lathu la kulingalira, kapena ‘mphamvu za kulingalira.’ (Aroma 12:1, NW) Khalidwe lathu siliyenera kutsogozedwa ndi maganizo otengeka akanthaŵi mofanana ndi awo oyambitsidwa ndi maulaliki onyenga a magulu achipembedzo amene amalalikira zikhulupiriro zawo pa TV. Mmalomwake, timasonkhezeredwa ndi phunziro lathu lokhazikika ndi kusinkhasinkha pa Baibulo ndi mabuku a maphunziro a Baibulo ogaŵiridwa ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru.” (Mateyu 24:45) Zochita zathu Zachikristu zili zotulukapo za kupeza malingaliro a Kristu pamkhalidwe uliwonse kapena mayesero amene angabuke. M’mbali imeneyo, Yehova ndiye Mphunzitsi wathu Wamkulu.—Salmo 25:9; Yesaya 54:13; 1 Akorinto 2:16.
6. Kodi nchitsanzo chotani cha padziko lonse cha phunziro la banja chomwe tili nacho?
6 Phunziro la banja la Baibulo lili ndi mbali yofunika kumkhalidwe wauzimu wabanja Lachikristu lililonse. Kodi ndiliti pamene mumakhala ndi phunziro lanu labanja? Ngati lili losalinganizidwa kapena longochitidwa mwadzidzidzi, pamenepo nkosakayikitsa kuti phunziro la banjalo nlodumphadumpha, kapena silichitidwa konse. Kuchitira zinthu pamodzi m’phunziro la banja kumafunikira programu yokhazikitsidwa yanthaŵi zonse. Ndiyeno onse adziŵe kuti ndi tsiku liti ndi nthaŵi pamene akayembekezeredwa kupezekapo kuti asangalale ndi chakudya chauzimu chabanja. Ziŵalo zoposa 12,000 padziko lonse za banja la Beteli zimadziŵa kuti phunziro lawo labanja limakhalapo usiku pa Lolemba. Kumakhala kokhutiritsa chotani kwa antchito odzifunira a pa Beteli ameneŵa kukumbukira kuti onse adzagaŵana m’phunziro lofananalo pamene tsiku litha, kuzisumbu za Pacific ndi New Zealand, ndiyeno m’Australia, Japan, Taiwan, Hong Kong, kenako ku Asia, Afirika, ndi Ulaya, ndiyeno kumalizira ku America. Ngakhale kuti ali olekanitsidwa ndi mamailo zikwi zambiri ndi zilankhulidwe zambiri, phunziro la banja limeneli limasonkhezera ziŵalo zabanja la Beteli kudzimva kukhala zochitira zinthu pamodzi. Pamlingo waung’ono, mungakulitse lingaliro lofananalo m’phunziro lanu la banja.—1 Petro 2:17; 5:9.
7. Malinga nkunena kwa Petro, kodi mawu a chowonadi tiyenera kuwalingalira motani?
7 Mtumwi Petro amatilangiza kuti: “Lirani monga makanda alero mkaka woyenera, wopanda chinyengo, kuti mukakule nawo kufikira chipulumutso; ngati mwalaŵa kuti Ambuye ali wokoma mtima.” (1 Petro 2:2, 3) Nchithunzi chabwino chotani nanga chimene Petro akutikumbutsa ndi mawu amenewo! Iye anagwiritsira ntchito mneni Wachigiriki wakuti e·pi·po·theʹsa·te, amene, malinga nkunena kwa Linguistic Key to the Greek New Testament, amachokera kuliwu lotanthauza “kulakalaka, kukhumba, kufunitsitsa.” Limapereka lingaliro la chikhumbo chachikulu. Kodi munawona mmene nkhanda imafunira mwaphamphu nkhumbu ya amake ndi mmene mwana wakhanda amakhutiritsidwira pamene akuyamwa bele la amake? Tiyenera kukhala ndi chikhumbo chofananacho cha mawu a chowonadi. Katswiri Wachigiriki William Barclay anati: “Kwa Mkristu wowona, kuphunzira mawu a Mulungu sintchito yotopetsa koma nkokondweretsa, chifukwa amadziŵa kuti m’menemo mtima wake udzapeza chakudya chimene ukulakalaka.”
8. Kodi ndithayo lotani limene limayang’anizana ndi mutu wabanja pochititsa phunziro labanja?
8 Phunziro la banja limaika thayo lalikulu pamutu wabanja. Uyenera kutsimikizira kuti phunzirolo nlosangalatsa kwa aliyense ndi kuti onse akutengamo mbali. Ana sayenera kulingalira kuti phunzirolo kwenikweni nla achikulire. Kaphunzitsidwe kake nkamene kali kofunika kwambiri koposa kuchuluka kwa zimene mwakambitsirana. Pangitsani zophunziridwa m’Baibulo kukhala zenizeni. Kumene kuli koyenera, thandizani ana anu kuyerekezera malo ndi zinthu za ku Palestina kumene zinthu zokambiranazo zinachitikira. Onse ayenera kulimbikitsidwa kufufuza zinthu paokha ndi kuzigaŵana ndi banja. Mwanjirayi ananso ‘angakule pamaso pa Yehova.’—1 Samueli 2:20, 21.
Kuchitira Zinthu Pamodzi m’Kulalikira
9. Kodi ndimotani mmene ntchito yolalikira ingakhalire chokumana nacho chabwino cha banja lachimwemwe?
9 Yesu anati: “Ndipo uthenga wabwino uyenera uyambe kulalikidwa kwa anthu a mitundu yonse.” (Marko 13:10) Mawu amenewo amapereka ntchito kwa Mkristu aliyense wodera nkhaŵa—kulalikira, kugaŵana uthenga wabwino wa ulamuliro wa Ufumu wa Mulungu ndi ena. Kuchitira zimenezi pamodzi monga banja kungakhale chochitika cholimbikitsa ndi chosangalatsa. Amayi ndi atate amanyadira maulaliki a ana awo a uthenga wabwino. Banja lina la ana amuna atatu a zaka zapakati pa 15 ndi 21 akusimba kuti anali ndi chizoloŵezi cha kutsagana ndi ana awo muntchito yolalikira poyera Lachitatu lililonse pambuyo pa sukulu ndi m’maŵa Loŵeruka lililonse. Atatewo anati: “Timawaphunzitsa kanthu kena nthaŵi zonse. Ndipo timatsimikizira kuti chochitikacho chikhale chosangalatsa, cholimbikitsa.”
10. Kodi ndimotani mmene makolo angapindulitsire ana awo muutumiki?
10 Kugwirira ntchito pamodzi monga banja m’kulalikira ndi kuphunzitsa kungakhale ndi zotulukapo zabwino kwambiri. Nthaŵi zina anthu amalabadira kwambiri ulaliki wosavuta koma wowona mtima wa mwana. Pamenepo, Amayi kapena Atate amakhalapo kuti athandize ngati kuli kofunika. Makolo angatsimikizire kuti ana awo akulandira chiphunzitso chopita patsogolo ndipo motero nakhala atumiki ‘opanda chifukwa cha kuchita manyazi, olunjika nawo bwino mawu a Mulungu.’ Kulalikira pamodzi mwanjirayi kumapatsa makolo mpata wa kuwona mkhalidwe wamaganizo, kugwira mtima, ndi makhalidwe abwino a mwana wawo muutumiki. Mwakukhala ndi njira yochitira zinthu yokhazikika, iwo amaona kupita patsogolo kwa mwana ndi kupereka chiphunzitso ndi chilimbikitso chosalekeza kulimbitsa chikhulupiriro chake. Panthaŵi imodzimodziyo, anawo amaona kuti makolo awo ali zitsanzo zabwino muutumiki. M’nthaŵi zowawitsa ndi zachiwawa zino, kugwira ntchito pamodzi monga banja logwirizana ndi losamala kungapereke chitetezo china m’malo aupandu kwambiri.—2 Timoteo 2:15; Afilipi 3:16.
11. Kodi nchiyani chimene chingazimiriritse changu cha mwana cha chowonadi?
11 Ana amazindikira mosavuta kusaona mtima kwa achikulire. Ngati makolo sasonyeza chikondi chenicheni cha chowonadi ndi utumiki wa kunyumba ndi nyumba, ana sangakhale konse achangu. Motero, kholo lathanzi labwino limene utumiki wake wakumunda uli wa kuchititsa ana phunziro la Baibulo chabe mlungu ndi mlungu lingakhale ndi zotulukapo zoipa pamene anawo akula.—Miyambo 22:6; Aefeso 6:4.
12. Kodi ndimotani mmene mabanja ena angapezere dalitso lapadera lochokera kwa Yehova?
12 Ubwino wa kukhala ‘womangika mu mtima womwewo’ ndiwo wakuti mwinamwake banja lingagwirizane kotero kuti chiŵalo chimodzi chokha chitumikire monga mtumiki wanthaŵi yonse wochita upainiya mumpingo. Mabanja ambiri kuzungulira dziko lonse amachita zimenezi, ndipo onse amalandira dalitso m’zokumana nazo ndi kugwira mtima kowonjezereka kwa chiŵalo chawo chochita upainiya.—2 Akorinto 13:11; Afilipi 2:1-4.
Kuchitira Zinthu Pamodzi Pothetsa Mavuto
13, 14. (a) Kodi ndimikhalidwe iti imene ingayambukire mgwirizano wa banja? (b) Kodi mavuto a banja angapewedwe motani?
13 M’nthaŵi zovuta zino za “chipsinjo” ndi “upandu,” tonsefe timatsenderezeka. (2 Timoteo 3:1, Revised Standard Version; Phillips) Kuntchito, kusukulu, kulikonse kumene timakhala kuli mavuto, ndipo ngakhale m’nyumba mwenimwenimo. Ena amadwala matenda kapena mavuto amalingaliro osatha, amene nthaŵi zina amachititsa mavuto ndi kusamvetsetsana m’banja. Kodi mikhalidwe yoteroyo ingasamaliridwe motani? Mwakusalankhulana kodi? Mwakudzipatula kodi ngakhale kuti mumakhala m’nyumba imodzi? Ayi. Mmalomwake, tifunikira kunena nkhaŵa zathu ndi kupempha chithandizo. Ndipo nkuti kuli malo abwino a zimenezi koposa m’banja lachikondi?—1 Akorinto 16:14; 1 Petro 4:8.
14 Monga mmene dokotala aliyense amadziŵira, kupeŵa matenda kuli bwino kuposa kuchiritsa. Nzofanana ndi mavuto a banja. Kukambitsirana momasuka ndi mosabisa mawu kaŵirikaŵiri kungapeŵetse mavuto pakukhala aakulu. Ngakhale ngati mavuto aakulu abuka, angasamaliridwe ndipo ngakhale kuthetsedwa ngati banja likambitsirana pamodzi malamulo a Baibulo ophatikizidwa. Kaŵirikaŵiri kusagwirizana kungasinthidwe kukhala unansi wabwino mwakugwiritsira ntchito mawu a Paulo pa Akolose 3:12-14 akuti: “Valani, . . . mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima; kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; . . . Khalani nacho chikondano, ndicho chomangira cha mtima wamphumphu.”
Kuchitira Zinthu Pamodzi Posanguluka
15, 16. (a) Kodi ndimkhalidwe uti umene uyenera kusiyanitsa mabanja Achikristu? (b) Kodi zipembedzo zina zatulutsa anthu otani, ndipo chifukwa ninji?
15 Yehova ndi Mulungu wachimwemwe, ndipo chowonadi ndiuthenga wachimwemwe—chiyembekezo chimodzi cha mtundu wa anthu. Ndiponso, chimodzi cha zipatso za mzimu ndichimwemwe. Chimwemwe chimenechi nchosiyana kotheratu ndi chisangalalo chakanthaŵi cha wamaseŵera amene amapambana mumpikisano wa maseŵera. Chili chikhutiro chotsitsimula chamkati chimene chimasefukira mumtima monga chotulukapo cha kukulitsa unansi wathithithi ndi Yehova. Chili chimwemwe chozikidwa pamikhalidwe yauzimu ndi maunansi omangirira.—Agalatiya 5:22; 1 Timoteo 1:11.
16 Chifukwa chake, monga Mboni Zachikristu za Yehova, tilibe chifukwa chokhalira ndwii kapena osaseka. Zipembedzo zina zimakhala ndi anthu otero chifukwa chakuti mtundu wa chikhulupiriro chawo umagogomezera zinthu zosakondweretsa. Ziphunzitso zawo zimachititsa mtundu wa kulambira kopanda chisangalalo, kumene sikuli kwa m’Baibulo ndi kosoŵa uchikatikati. Samakhala ndi mabanja achimwemwe otumikira Mulungu. Yesu anawona kufunikira kwa kusanguluka ndi kupumula. Mwachitsanzo, pachochitika china, anapempha ophunzira ake kupita ‘padera ku malo achipululu, kukapuma kamphindi.’—Marko 6:30-32; Salmo 126:1-3; Yeremiya 30:18, 19.
17, 18. Kodi mabanja Achikristu angapumule m’njira zoyenerera zotani?
17 Mofananamo mabanja amafunikira nthaŵi yosanguluka. Kholo lina linanena za ana ake kuti: “Timasangalalira limodzi—kumka kugombe, kuseŵera mpira m’paki, kupanga ulendo wokayenda kumapiri. Mwakamodzimodzi, timathera tsiku lathunthu pamodzi muutumiki monga mmene apainiya amachitira; ndiyeno timasangalala ndi chakudya chapadera, ndipo mwina ngakhale kupatsana mphatso.”
18 Malingaliro ena amene makolo angalingalire angakhale a ulendo wabanja wopita kumalo osungira zinyama, kumapaki okongola, ku myuziyamu, ndi malo ena osangalatsa. Kuyenda m’thengo, kukawona mbalame, ndi kulima zili ntchito zina zimene mungachitire pamodzi mosangalala. Makolo angalimbikitsenso ana awo kuphunzira kuseŵera ziwiya zoimbira kapena kuchita ntchito yokondedwa. Ndithudi, makolo achikatikati akapeza nthaŵi ya kuseŵera ndi ana awo. Ngati mabanja aseŵerera pamodzi, mosakayikira adzakhala oyandikana kwambiri!
19. Kodi ndichikhoterero chamakono chotani chimene chingawononge banja?
19 Chikhoterero chamakono nchakuti achichepere amafuna kulekana ndi banja ndi kuchita zinthu zawo ngati ili nthaŵi yopuma. Pamene kuli kwakuti palibe cholakwika ndi munthu wachichepere kuchita ntchito yokondedwa kapena kucheza, sikukhala kwanzeru kulola zikondwerero zotero kutilekanitsa mwachikhalire ndi banja lonse. Mmalo mwake, tikufuna kugwiritsira ntchito lamulo lamakhalidwe limene Paulo ananena lakuti: “Munthu yense asapenyerere zake za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzake.”—Afilipi 2:4.
20. Kodi ndimotani mmene misonkhano yadera ndi yachigawo ingakhalire nthaŵi yosangalatsa?
20 Nkosangalatsa chotani nanga kwa tonsefe kuwona mabanja akukhalira pamodzi pamisonkhano yachigawo ndi yadera! Mwanjira imeneyo ana achikulire kaŵirikaŵiri angathandize ana aang’ono. Kakonzedwe koteroko kangapeŵetsenso chizoloŵezi cha achichepere ena cha kukhala m’timagulu kumbuyo ndi kusamvetsera chilichonse paprogramu yamsonkhano. Ngakhale panthaŵi ya kupita ndi kuchokera kumsonkhano ingakhale yosangalatsa pamene banja lifunsidwa njira imene liyenera kudzera, malo amene angawone pamene akuyenda ulendowo, ndi kumene akakhala. Tangoyerekezerani kuti inali nthaŵi yosangalatsa chotani m’tsiku la Yesu kwa mabanja kuyendera limodzi kumka ku Yerusalemu!—Luka 2:41, 42.
Madalitso Akuchitira Zinthu Pamodzi
21. (a) Kodi tingayesetse motani kuti tipambane muukwati? (b) Kodi malingaliro anayi abwino a ukwati wokhalitsa ndiati?
21 Nkovuta kukhala ndi maukwati achipambano ndi mabanja ogwirizana, ndipo samangokhalako mwangozi. Ena amakupeza kukhala kosavuta ‘kusiya kuyesayesa kulikonse,’ akumathetsa ukwati m’chisudzulo, ndi kuyesa kuyambiranso. Komabe, kaŵirikaŵiri mavuto amodzimodziwo amabukanso muukwati wachiŵiri ngakhale wachitatu. Yankho labwinopo ndi Lachikristu lakuti: Yesetsani kupambana mwakugwiritsira ntchito malamulo a mkhalidwe a Baibulo a chikondi ndi kulemekezana. Mabanja ogwirizana amadalira pamzimu wa kuvomereza zolakwa zawo, wopanda dyera. Phungu wina wa ukwati anapereka njira yosavuta kupangitsa ukwati kukhala wokhalitsa. Iye analemba kuti: “Njira zinayi zazikulu zopezeka m’maukwati onse abwino ndizo kufunitsitsa kumvetsera, kukhoza kupepesa, kukhoza kupereka chichilikizo cha malingaliro chosalekeza, ndi chikhumbo cha kusonyeza chikondi.” Ndithudi njira zimenezo zingathandize kupangitsa ukwati kukhala wokhalitsa chifukwa zili zozikidwa pamalamulo a mkhalidwe anzeru a Baibulo.—1 Akorinto 13:1-8; Aefeso 5:33; Yakobo 1:19.
22. Kodi pali mapindu otani akukhala ndi banja logwirizana?
22 Ngati titsatira uphungu wa Baibulo, tidzakhala ndi maziko olimba a banja logwirizana, ndipo mabanja ogwirizana ali maziko a mpingo wogwirizana ndi wolimba mwauzimu. Motero, tidzalandira madalitso ochuluka kuchokera kwa Yehova pamene tipitirizabe kumtamanda mogwirizana.
[Mawu a M’munsi]
a Liwu Lachingelezi lakuti “family [banja] limachokera ku la Chilatin lakuti familia, poyambilira limaloza kwa atumiki ndi akapolo a nyumba yaikulu, ndiyeno nyumbayo yokhala ndi mbuye, mbuye wachikazi, ana—ndi antchito.”—Origins—A Short Etymological Dictionary of Modern English, lolembedwa ndi Eric Partridge.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi nchifukwa ninji kuli kopindulitsa kuti mabanja achitire zinthu pamodzi?
◻ Kodi nchifukwa ninji phunziro la banja la Baibulo lokhazikika lili lofunika?
◻ Kodi nchifukwa ninji kuli bwino kwa makolo kupita muutumiki wakumunda limodzi ndi ana awo?
◻ Kodi nchifukwa ninji kumathandiza kukambitsirana mavuto mkati mwa banja?
◻ Kodi nchifukwa ninji mabanja Achikristu sayenera kukhala ongoti ndwii ndi osasangalala?
[Chithunzi patsamba 17]
Kodi banja lanu limadyera chakudya limodzi kamodzi patsiku?
[Chithunzi patsamba 18]
Maulendo okasangalala a banja ayenera kukhala otsitsimula ndi osangalatsa