Phunzirani Mawu A Mulungu Mokhazikika Monga Banja
“Munthu sadzakhala ndi moyo ndi mkate wokha, koma ndi mawu onse akutuluka mkamwa mwa Mulungu.”—MATEYU 4:4.
1. Kodi Baibulo limanenanji za udindo wa mitu ya mabanja wophunzitsa ana awo njira za Yehova?
YEHOVA MULUNGU nthaŵi ndi nthaŵi anali kukumbutsa mitu ya mabanja za udindo wawo wophunzitsa ana awo. Malangizo oterowo ankakonzekeretsa anawo mmene anayenera kukhalira ndi moyo panthaŵiyo ndiponso ankawathandiza kukonzekera za moyo wa m’tsogolo. Mngelo amene anali kuimira Mulungu anafotokozera Abrahamu udindo wake wophunzitsa banja lake kotero kuti iwo “asunge njira ya Yehova.” (Genesis 18:19) Makolo achiisrayeli anauzidwa kuti azifotokozera ana awo mmene Mulungu anawalanditsira mu Igupto ndiponso mmene anawapatsira Chilamulo pa Phiri la Sinai, mu Horebe. (Eksodo 13:8, 9; Deuteronomo 4:9, 10; 11:18-21) Mitu ya mabanja yachikristu ikulimbikitsidwa kulera ana awo “m’maleredwe ndi chilangizo cha Ambuye.” (Aefeso 6:4) Ngakhale kuli kwakuti kholo limodzi lokha n’limene limatumikira Yehova, kholo limenelo liyenera kuyesetsa kuphunzitsa anawo njira za Yehova.—2 Timoteo 1:5; 3:14, 15.
2. Kodi phunziro labanja ndi lofunika ngati m’banjamo mulibe ana? Longosolani.
2 Izi sizitanthauza kuti mabanja amene ali ndi ana okha ndiwo ayenera kuphunzira Mawu a Mulungu. Pamene mwamuna ndi mkazi akhala ndi phunziro labanja ngakhale iwo alibe ana m’banjamo, zimasonyeza kuti amayamikira kwambiri zinthu zauzimu.—Aefeso 5:25, 26.
3. Kodi n’chifukwa chiyani kuchita phunziro labanja nthaŵi zonse kuli kofunika?
3 Kuti papezeke mapindu ochuluka, malangizo ayenera kuperekedwa nthaŵi ndi nthaŵi, mogwirizana ndi phunziro limene Yehova anaphunzitsa Aisrayeli m’chipululu lakuti: “Munthu sakhala wamoyo ndi mkate wokha, koma munthu akhala wamoyo ndi zonse zakutuluka mkamwa mwa Yehova.” (Deuteronomo 8:3) Malinga ndi mikhalidwe ya banjalo, mabanja ena angakonze zomaphunzira mlungu uliwonse; ena angamakhale ndi nthaŵi pang’ono tsiku lililonse yoti aphunzire. Zilizonse zimene mungasankhe kuchita, musangosiya kuti phunzirolo lizichitika mwangozi. ‘Wombolani nthaŵi’ yochita phunziro. Mtengo umene mumalipira pa nthaŵi yotereyi ndi njira yanzeru yosungira chuma. Miyoyo ya anthu a m’banja lanu ili pachiswe.—Aefeso 5:15-17, NW; Afilipi 3:16.
Zolinga Zofunika Kuzikumbukira
4, 5. (a) Kupyolera mwa Mose, kodi Yehova anauza makolo chiyani kukhala cholinga chofunika pophunzitsa ana awo? (b) Kodi zimenezi lerolino zikuphatikizapo chiyani?
4 Pamene muchititsa phunziro labanja, lidzakhala lopindulitsa kwambiri ngati muli ndi zolinga zenizeni. Talingalirakoni zochepa izi.
5 Paphunziro lililonse, yesetsani kukulitsa chikondi pa Yehova Mulungu. Pamene Aisrayeli anasonkhana m’zigwa za Moabu, asanaloŵe m’Dziko Lolonjezedwa, Mose anawachititsa kulingalira za chimene Yesu Kristu kenako anadzatcha kuti “lamulo lalikulu . . . la m’chilamulo.” Kodi linali chiyani? “Muzikonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, ndi mphamvu yanu yonse.” (Mateyu 22:36, 37; Deuteronomo 6:5) Mose analimbikitsa Aisrayeli kuika zimenezi m’mitima mwawo ndi kuphunzitsa ana awo. Zimenezi zinafuna kubwereza, kupeza zifukwa zokondera Yehova, kuthetsa malingaliro ndi makhalidwe amene angapinge kusonyeza chikondi chimenecho, ndiponso kumaonetsa kuti amakonda Yehova m’miyoyo yawo. Kodi ana athunso amafunika malangizo ofananawo? Inde! Ndipo iwonso afunika kuthandizidwa ‘kudula mitima yawo,’ ndiko kuti, kuchotsa chilichonse chimene chingajejemetse chikondi chawo kwa Mulungu. (Deuteronomo 10:12, 16; Yeremiya 4:4) Mwa zinthu zojejemetsa zimenezo pangakhale chilakolako cha zinthu za dziko lapansi ndi kufuna mipata yoloŵerera mu zochita zake. (1 Yohane 2:15, 16) Chikondi chathu pa Yehova chiyenera kukhala chosonyeza ntchito, choonekeratu, chotisonkhezera kuchita zinthu zokondweretsa Atate wathu wakumwamba. (1 Yohane 5:3) Kuti phunziro lathu labanja likhale ndi mapindu okhalitsa, phunziro lililonse liyenera kuchititsidwa m’njira imene idzalimbitsa chikondi chimenechi.
6. (a) Kodi chofunika ndi chiyani kuti tipereke chidziŵitso cholongosoka? (b) Kodi Malemba amagogomezera motani kufunika kwa chidziŵitso cholongosoka?
6 Perekani chidziŵitso cholongosoka cha zimene Mulungu amafuna. Kodi zimenezi zimaphatikizaponji? Zimaphatikizapo zambiri zoposa kungodziŵa chabe kuŵerenga yankho m’magazini kapena m’buku. Kaŵirikaŵiri zimafuna kukambirana kuti mutsimikize kuti mawu ofunika ndi mfundo zikuluzikulu zamvetsetsedwa bwino. Chidziŵitso cholongosoka ndi mbali yofunika kwambiri povala umunthu watsopano, pokumbukira zinthu zofunikadi kwambiri pamene tikulimbana ndi mavuto m’moyo, ndiponso, pochita zimene zimakondweretsadi Mulungu.—Afilipi 1:9-11; Akolose 1:9, 10; 3:10.
7. (a) Kodi ndi kugwiritsa ntchito mafunso ati kumene kungathandize banja kugwiritsa ntchito nkhani imene laphunzira? (b) Kodi Malemba amagogomezera motani phindu la cholinga chimenechi?
7 Athandizeni kugwiritsa ntchito zimene akuphunzira. Ndi cholinga chimenechi m’maganizo, paphunziro lililonse labanja, funsani kuti: ‘Kodi nkhani imeneyi iyenera kukhudza miyoyo yathu motani? Kodi pakufunika kuti tisinthe zimene tikuchita tsopano? Kodi n’chifukwa chiyani tiyenera kufuna kusintha?’ (Miyambo 2:10-15; 9:10; Yesaya 48:17, 18) Kulingalira mokwanira mmene tingagwiritsire ntchito zinthu zimene tikuphunzira kungakhale mbali yofunika kwambiri pa kukula kwauzimu kwa anthu a m’banja.
Gwiritsani Ntchito Mwanzeru Zida Zophunzitsira
8. Kodi kagulu ka kapolo kapereka zida zotani zophunzirira Baibulo?
8 “Kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” wapereka zida zochuluka zimene zingagwiritsidwe ntchito pophunzira. Magazini ya Nsanja ya Olonda, yogwiritsidwa ntchito pamodzi ndi Baibulo, ikupezeka m’zinenero 131. Pali mabuku ophunzirira Baibulo m’zinenero 153, mabolosha m’zinenero 284, makaseti omvetsera m’zinenero 61, mavidiyokaseti m’zinenero 41, ngakhalenso pologalamu yapakompyuta yochitira kafukufuku m’Baibulo m’zinenero 9!—Mateyu 24:45-47.
9. Kodi uphungu umene uli m’malemba amene asonyezedwa m’ndime ino tingaugwiritse ntchito motani pamene tikuchita phunziro labanja la Nsanja ya Olonda?
9 Mabanja ambiri amagwiritsa ntchito nthaŵi ya phunziro labanja kukonzekera Phunziro la Nsanja ya Olonda lampingo. Zimenezitu ndi zothandiza kwambiri! Nsanja ya Olonda imakhala ndi chakudya chauzimu chofunika kwambiri chimene chimaperekedwa kuti chilimbikitse anthu a Yehova padziko lonse. Pamene muphunzira Nsanja ya Olonda monga banja, chitani zambiri kuposa pa kuŵerenga ndime ndi kuyankha mafunso osindikizidwa. Funitsitsani kuti mumvetsetse. Khalani ndi nthaŵi yokwanira yoŵerenga malemba amene asonyezedwa koma osagwidwa mawu. Funsani a m’banjamo kuti afotokoze mmene malembawo akugwirizanira ndi zimene zikutchulidwa m’ndime imene mukukambiranayo. Pangitsani mitima kuloŵetsedwamo.—Miyambo 4:7, 23; Machitidwe 17:11.
10. Kodi ndi chiyani chimene chingachitike kuti ana aloŵetsedwe m’phunziro ndi kuti nthaŵiyo ikhale yosangalatsa kwa iwo?
10 Ngati m’banja lanu muli ana, kodi mungachitenji kuti mupangitse phunziro lanu kukhala osati chabe chizoloŵezi cha banjalo koma nthaŵi yomangirirana, yokondweretsa, ndiponso yosangalatsa? Yesetsani kuchititsa aliyense kuloŵetsedwamo m’njira yoyenera kotero kuti malingaliro akhalebe ali pa nkhani imene mukuphunzirayo. Pamene kuli kotheka, konzani kuti mwana aliyense akhale ndi Baibulo lakelake ndiponso magazini yophunziridwa. Potsatira chikondi chimene Yesu anasonyeza, kholo lingakhale moyandikana kwambiri ndi mwana wamng’ono, mwina lingayangate mwanayo. (Yerekezerani ndi Marko 10:13-16.) Mutu wabanja angauze mwana wamng’ono kuti alongosole chithunzi chimene chili pankhani yomwe ikuphunziridwayo. Mwana wokulirapo angauzidwiretu kuti adzaŵerenge lemba lina. Mwana wamkulu angauzidwe kutchula mbali zimene nkhani yophunziridwayo ingagwiritsidwe ntchito.
11. Kodi ndi zida zophunzitsira zina ziti zimene zaperekedwa, ndipo kumene zimenezi zimapezeka, kodi zingagwiritsidwe ntchito mopindulitsa motani pa phunziro labanja?
11 Ngakhale kuti mungakhale mukukambirana nkhani ya mu Nsanja ya Olonda, musaiwale zida zina zophunzirira zimene zimapezeka m’zinenero zambiri. Ngati pakufunika kudziŵa za zonse zimene zinachitika panthaŵiyo kapena pakufunika kulongosola mawu ena a m’Baibulo, Insight on the Scriptures ingakuthandizeni. Mafunso ena angayankhidwe mwa kugwiritsa ntchito Watch Tower Publications Index kapena pologalamu yapakompyuta yochitira kafukufuku imene Sosaite imapereka. Kuphunzira kugwiritsa ntchito zida zimenezi, ngati zilipo m’chinenero chanu, kungakhale mbali yofunika kwambiri ya phunziro labanja. Pokhala ndi cholinga chodzutsa chidwi cha ana, mungapatulenso nthaŵi ina ya phunziro lanulo kuti muonere mbali ina ya imodzi mwa mavidiyo ophunzitsa a Sosaite kapena kumvetsera kambali kena ka seŵero la pakaseti ndiyeno ndi kuzikambirana. Kugwiritsa ntchito bwino zida zophunzirira zimenezi kungathandize kupangitsa phunziro lanu labanja kukhala losangalatsa ndi lopindulitsa kwa banja lonse.
Sinthani Mogwirizana ndi Zofunika pa Banja Lanu
12. Kodi phunziro labanja lingathandize motani pochita ndi nkhani zofunika kwambiri pa banja?
12 Kungakhale kuti banja lanu nthaŵi zambiri limaphunzira nkhani ya mu Nsanja ya Olonda yophunziridwa mlungu umenewo. Komano onetsetsani zimene zikuchitika m’banja lanu. Ngati amayi sagwira ntchito yolembedwa, akhoza kumacheza ndi anawo tsiku lililonse pamene abwerako kusukulu. Zochitika zina angazithetse panthaŵiyo; zina zingafune chisamaliro chowonjezeka. Pakakhala nkhani zofunika kwambiri pa banjapo, musazinyalanyaze. (Miyambo 27:12) Zimenezi zingakhale osati kokha mavuto a kusukulu komanso zochitika zina. Sankhani nkhani yoyenerera, ndipo mudziŵitsiretu banja lonse zimene mudzaphunzira.
13. Kodi ndi chifukwa chiyani kungakhale kothandiza kuti banja likambirane mmene lingapiririre umphaŵi?
13 Mwachitsanzo, mbali yaikulu ya dziko lapansi ili paumphaŵi wadzaoneni; motero m’madera ambiri kungakhale kofunika kukambirana mmene mungapiririre vutoli. Kodi phunziro labanja lokhudza mikhalidwe imene ikuchitikadi pamoyo ndiponso mapulinsipulo a Baibulo lingakhale lothandiza ku banja lanu?—Miyambo 21:5; Mlaliki 9:11; Ahebri 13:5, 6, 18.
14. Kodi ndi mikhalidwe iti imene ingapangitse kukambirana kwa banja mmene Yehova amaonera chiwawa, nkhondo, ndi uchete wachikristu kukhala kwapanthaŵi yake?
14 Nkhani ina yofunika kukambirana ndiyo chiwawa. Tonsefe tifunika kukhomereza zolimba m’maganizo ndi m’mitima mwathu mmene Yehova amaionera nkhaniyi. (Genesis 6:13; Salmo 11:5) Phunziro labanja la nkhani imeneyi ingakhale nthaŵi yabwino yokambirana mmene ana angachitire ndi ana a ndewu kusukulu, kaya kuti iwo aphunzire maluso omenyera, ndiponso mmene angasankhire zosangulutsa zoyenera. Mikangano yachiwawa ili ponseponse; pafupifupi m’dziko lililonse muli mwina nkhondo yapachiŵeniŵeni, mkangano wa zandale kapena wautundu, kapena muli nkhondo za magulu achifwamba. Motero, banja lanu lingafunike kukambirana mmene lingakhalirebe ndi khalidwe lachikristu pakati pa magulu odana.—Yesaya 2:2-4; Yohane 17:16.
15. Kodi malangizo onena za kugonana ndi ukwati ayenera kuperekedwa motani kwa ana?
15 Pamene ana akukula, amafunika kulangizidwa za kugonana ndi ukwati, mogwirizana ndi msinkhu wawo. Pa chikhalidwe cha anthu ena makolo ochuluka sakamba ndi ana awo nkhani za kugonana. Popeza kuti sanalangizidwe, ana angauzidwe zolakwika ndi achinyamata ena, ndipo zotsatira zake zingakhale zoipa kwambiri. Kodi sikungakhale bwino kutsanzira Yehova, amene amapereka uphungu wachindunji komanso wabwino pankhaniyi m’Baibulo? Uphungu waumulungu udzathandiza ana athu kumadzilemekeza nthaŵi zonse ndi kumapatsa ulemu anthu osiyana nawo ziwalo. (Miyambo 5:18-20; Akolose 3:5; 1 Atesalonika 4:3-8) Ngakhale kuti nkhani zimenezi munazikambapo kale, musazengereze kuzikambanso. Popeza kuti pakubuka mikhalidwe yatsopano, kubwereza ndi kofunika.
16. (a) M’mabanja ambiri, kodi phunziro labanja limachitika liti? (b) Kodi mwathetsa bwanji mavuto kuti mukhale ndi phunziro labanja lokhazikika?
16 Kodi phunziro labanja lingachitidwe liti? Potsatira mabanja a Beteli padziko lonse lapansi, mabanja ambiri amakhala ndi phunziro lawo labanja Lolemba madzulo. M’mabanja ena ndi zosiyana. Ku Argentina banja lina la anthu 11, momwe munali ana 9, nthaŵi zonse linali kudzuka 5 koloko mmaŵa uliwonse kuti lipange phunziro labanja. Kunali kosatheka kupeza nthaŵi ina chifukwa chosiyana ntchito zimene anali kugwira. Zinali zovuta, koma zinakhomereza kufunika kwa phunziro labanja m’maganizo ndi m’mitima mwa ana. Ku Philippines mkulu wina anali kuchita phunziro labanja mokhazikika ndi mkazi wake ndi ana awo atatu pamene anali kukula. Mkati mwa mlungu makolowo analinso kuphunzira ndi mwana aliyense payekha kuti aliyense apange choonadi kukhala chakechake. Ku United States, mlongo wina amene mwamuna wake si wa Mboni mmaŵa uliwonse amaperekeza ana ake kukakwera basi ya kusukulu kwawo. Pamene akuyembekeza basiyo, amatha mphindi pafupifupi khumi akuŵerenga ndi kukambirana nkhani yophunzira yoyenerera ya Malemba, ndiyeno amayiwo amapereka pemphero lalifupi anawo asanakwere basiyo. Ku Democratic Republic of Congo, mkazi wina amene mwamuna wake wosakhulupirira anachoka panyumbapo amafunika kuyesetsa kuti aphunzire chifukwa sanaphunzire kwenikweni kusukulu. Mwana wake wamwamuna wamkulu amamuthandiza mwa kumabwera mlungu uliwonse kudzachititsa phunziro limene pamakhala amayi akewo ndi azibale ake ang’onoang’ono. Amayiwo amapereka chitsanzo chabwino mwa kukonzekera mwakhama. Kodi pali mkhalidwe wina umene umapangitsa kukhala kovuta kuti m’banja lanu muzikhala ndi phunziro labanja mokhazikika? Musasiye. Funani madalitso a Yehova moona mtima pa kuyesayesa kwanu kuti mukhale ndi phunziro la Baibulo lokhazikika.—Marko 11:23, 24.
Mapindu a Kuchita Khama
17. (a) Kuti mukhale ndi phunziro labanja lokhazikika, kodi chimafunika ndi chiyani? (b) Ndi chochitika chiti chimene chikusonyeza kufunika kwakuti banja lizilangizidwa njira za Yehova nthaŵi zonse?
17 Kulinganiza zinthu ndi kofunika. Kuchita khama ndi kofunikanso. Koma mapindu amene amapezeka m’phunziro labanja lokhazikika alidi oyenera zimenezo. (Miyambo 22:6; 3 Yohane 4) Ku Germany, Franz ndi Hilda, anali ndi banja la ana 11. Patatha zaka zochuluka, mwana wawo wamkazi Magdalena anati: “Masiku ano chimene ndimaona kuti chinali chofunika koposa ndi chakuti panalibe tsiku ndi limodzi lomwe limene sitinalandirepo malangizo auzimu.” Pamene mzimu wautundu unakula kwambiri mu ulamuliro wa Adolf Hitler, atate ake a Magdalena anagwiritsa ntchito Baibulo kukonzekeretsa banja lawo pa ziyeso zimene anaona kuti zinali kubwera. M’kupita kwa nthaŵi, ana ang’onoang’ono a m’banjalo anagwidwa ndi kupita nawo kusukulu yosintha khalidwe la akaidi; ena a m’banjamo anamangidwa ndi kukawaika m’ndende ndi m’misasa yachibalo. Ena anaphedwa. Chikhulupiriro cha onsewo chinalimbabe—osati kokha panthaŵi imeneyo ya kuzunzidwa mwakhanza, komanso, kwa amene anapulumuka, m’zaka zimene zinatsatira.
18. Kodi zoyesayesa za makolo opanda mnzawo wamuukwati zafupidwa motani?
18 Makolo ambiri amene alibe mnzawo wamuukwati, komanso amene amasiyana zikhulupiriro ndi mnzawo wamuukwati, nawonso apereka malango a m’Baibulo mokhazikika kwa ana awo. Ku India, mayi wina, wamasiye, anayesetsa kukhomereza kukonda Yehova mwa ana ake aŵiri. Komabe, anakhumudwa kwambiri pamene mwana wake wamwamuna anasiya kuyanjana ndi anthu a Yehova. Iye anapempha Yehova kuti amukhululukire zolakwa zilizonse zimene anachita pophunzitsa mwana wakeyo. Komatu mwanayo sanaiwaliretu zimene anaphunzira. Patatha zaka zoposa khumi, anabwerera napita patsogolo kwambiri mwauzimu, ndipo anadzakhala mkulu mumpingo. Tsopano iye ndi mkazi wake akutumikira monga atumiki anthaŵi zonse achipainiya. Makolo amene alabadira uphungu wa Yehova ndi gulu lake wopereka malango a m’Baibulo nthaŵi zonse m’banja lawo alidi oyamikira kwambiri! Kodi inu m’banja lanu mukugwiritsa ntchito uphungu umenewo?
Kodi Mungalongosole?
◻ Kodi ndi chifukwa chiyani phunziro labanja lokhazikika lili lofunika?
◻ Kodi zolinga zathu ziyenera kukhala zotani paphunziro labanja lililonse?
◻ Kodi tapatsidwa zida zophunzirira zotani?
◻ Kodi tingasinthe motani phunziro kuti ligwirizane ndi zofunika pabanjapo?
[Chithunzi patsamba 15]
Zolinga zenizeni zidzalimbikitsa phunziro lanu labanja