Kodi Nchifukwa Ninji Mboni Zimapitirizabe Kufikira Anthu?
‘AWO, afikanso! Komatu anali pompano masabata angapo okha apitawo!’ Kodi zimenezo zimadza m’maganizo mwanu pamene mmodzi wa Mboni za Yehova akufikirani? Lerolino mamiliyoni ambiri amafikiridwa nthaŵi zonse ndi Mboni za Yehova. Inu mungafunse kuti, Kodi nchifukwa ninji amachita khama pamene akudziŵa kuti anthu ochuluka ali ndi chipembedzo chawo kapena ali osakondweretsedwa? Funso limenelo lifunikira yankho.
Thayo Pamaso pa Mulungu
Mboni za Yehova zaphunzira m’Malemba kuti chiyambire 1914, chaka chimene Nkhondo Yadziko I inayamba, zochitika zadziko zakhala zikukwaniritsa maulosi a Baibulo onena za mapeto a dongosolo ladziko limene lilipoli ndi ulamuliro umene ukudzawo wa Ufumu wa Mulungu padziko lapansili. Zaka pafupifupi zana limodzi za chiwawa, kukhetsa mwazi, ndi udani zikuonekera kukhala zitakankhira anthu kutali ndi chothetsera mavuto awo cha ndale koposa ndi kale lonse. Nkhondo ndi uchigaŵenga zimene zikuvutitsabe banja laumunthu zili umboni wakuti ulamuliro waumunthu walephera kusintha mitima, maganizo, ndi mkhalidwe wa anthu. Udani waukulu pa nkhani zimene zinachitika kale m’mbiri umaipitsabe maunansi pakati pa magulu a mitundu, mafuko, ndi zipembedzo. Zimenezo zili choncho m’madera otalikirana onga Afghanistan, India, Middle East, Northern Ireland, South Africa, ndi amene kale anali Yugoslavia. Nangano, kodi nchiyani chimene chili chothetsera mavuto chokha chokhalitsa?
Kodi Nchiyani Chimene Chimasonkhezera Mboni?
Mboni za Yehova zimazindikira kuti chothetsera mavuto cha Mulungu—ulamuliro wake wa Ufumu wolonjezedwa wochitidwa ndi Kristu Yesu—ndicho yankho lokha loyenera. Yesu anaphatikizadi pempho la ulamuliro wa Ufumu umenewo m’pemphero lake lachitsanzo kuti: “Chifukwa chake pempherani inu chomwechi: Atate wathu wa Kumwamba, Dzina lanu liyeretsedwe. Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano.” Mboni zimakhulupirira kuti pemphero limeneli limapemphadi kuloŵerera kwa Mulungu m’zochitika za mtundu wa anthu.—Mateyu 6:9, 10.
Chotero kodi nchifukwa ninji Mboni za Yehova zimaona kukhala kofunika kupita kunyumba ndi nyumba mosalekeza kukayesa kupereka uthenga umenewo? Chifukwa cha malamulo aŵiri amene Yesu anasonyeza akuti: “Uzikonda [Yehova, NW] Mulungu wako ndi mtima wako wonse, ndi moyo wako wonse, ndi nzeru zako zonse. Ili ndilo lamulo lalikulu ndi loyamba. Ndipo lachiŵiri lolingana nalo ndi ili, Uzikonda mnzako monga udzikonda iwe mwini.”—Mateyu 22:37-39.
Mboni zimafuna kukhala ndi dalitso la Mulungu, ndipo popeza kuti zimakonda anansi awo, zimafuna dalitso limodzimodzilo kukhala pa iwo. Motero, potsanzira chitsanzo cha Yesu, zimakakamizika ndi chikondi chopanda dyera kufikira anansi awo. Izo zimafuna kuwapatsa mwaŵi wa kudziŵa zimene “Mulungu [wachimwemwe, NW]” walonjeza mtundu womvera wa anthu padziko lapansi loyeretsedwa.—1 Timoteo 1:11; 2 Petro 3:13.
Mmishonale Wachikristu Paulo anakhulupirira malonjezo a Mulungu ndipo motero anatha kulemba kuti: “Paulo, kapolo wa Mulungu, ndi mtumwi wa Yesu Kristu, monga mwa chikhulupiriro cha osankhika a Mulungu, ndi chizindikiritso cha choonadi chili monga mwa chipembedzo, m’chiyembekezo cha moyo wosatha, umene Mulungu, wosanamayo, analonjeza zisanayambe nthaŵi zosayamba.” Inde, Mulungu, “wosanamayo,” “analonjeza” moyo wosatha kwa awo amene modzichepetsa amafuna kumdziŵa ndi kumtumikira.—Tito 1:1, 2; Zefaniya 2:3.
Kodi Mboni Zimalipidwa?
Panthaŵi ndi nthaŵi ena anena kuti Mboni zimalipidwa kaamba ka utumiki wawo. Zimenezo sizoona konse! Izo zimaona mwamphamvu mawu a Paulo ku mpingo wa ku Korinto akuti: “Sitikhala monga ambiriwo, akuchita malonda nawo mawu a Mulungu; koma monga mwa choona mtima, koma monga mwa Mulungu pamaso pa Mulungu, tilankhula mwa Kristu.”—2 Akorinto 2:17.
Atsogoleri azipembedzo ena amalalikira kuti apeze ndalama, kaya mwa malipiro a utumiki wachipembedzo kapena kuchirikiza magulu amalonda pa mautumiki awo a pa TV. Zipembedzo zambiri zili ndi atsogoleri achipembedzo olipidwa.
Mosiyana ndi zimenezo, Mboni zilibe atsogoleri achipembedzo olipidwa, ndipo kaŵirikaŵiri mabuku awo ofokotoza Baibulo amagaŵiridwa popanda ndalama kwa ofunafuna choonadi oona mtima, ngakhale kuti ambiri a ameneŵa amasonkhezereka kupereka zopereka zodzifunira. Zimenezi zimagwiritsiridwa ntchito kulipirira ntchito yolalikira imeneyi yapadziko lonse. Mogwirizana ndi uphungu wa Yesu wakuti: “Munalandira kwaulere, patsani kwaulere,” Mbonizo zimagwiritsira ntchito chuma chawo, kuphatikizapo nthaŵi ndi nyonga, m’kuthera mamiliyoni a maola muutumiki wa Mulungu chaka chilichonse. Motero, zimaphunzitsa anthu okondwerera kunyumba ndi nyumba ndi mwanjira ya maphunziro a Baibulo apanyumba.—Mateyu 10:8; 28:19, 20; Machitidwe 20:19, 20.
Umboni umasonyeza kuti Mboni za Yehova, iliyonse payokha ilibe cholinga cha kudzipezera ndalama, za mpingo wawo, kapena za Watch Tower Society. Palibe amene amalandira malipiro chifukwa cha kupita kunyumba ndi nyumba. Pamenepo kodi ndimotani mmene ntchitoyo imalipiridwira? Mwa zopereka zodzifunira zochokera kwa anthu oyamikira padziko lonse. Palibe konse kusonkhedwa kwa ndalama kumene kumachitidwa.
Chiyambukiro cha Umboni Wawo
Kodi utumiki wa kunyumba ndi nyumba ndi ulaliki wamwamwaŵi wa Mbonizo uli ndi chiyambukiro pa anthu? Umboni woperekedwa ndi zoulutsira nkhani umayankha mwamphamvu funso limenelo. Mboni za Yehova zatchulidwa mkati mwa maprogramu a TV ndi m’mafilimu pamene munthu wina asonyezedwa akugogoda pakhomo. Zithunzithunzi zoseketsa zatchula za Mboni. Ntchito yawo yachangu njodziŵika kwambiri kwakuti ojambula zithunzithunzi zoseketsa padziko lonse aphatikizamo mawu onena za Mboni za Yehova. Zimenezi zingaonekere kukhala zonyodola, koma kaŵirikaŵiri zimazikidwa pa choonadi chofunika kwambiri—chakuti Mboni zimadziŵika chifukwa cha khama lawo la kulalikira kunyumba ndi nyumba.—Machitidwe 20:20.
Chithunzithunzi china choseketsa chaposachedwapa chinasonyeza munthu akukwera phiri kukaonana ndi “guru.” Iye anati: “Ndiuzeni za zinthu zodabwitsa zimene zidzadza!” Kodi “guru” ameneyo anayankha motani? “Tione kaye . . . Padzakhala njala, miliri, ndi zivomezi. Dzuŵa lidzasanduka mdima, ndipo mwezi udzasanduka mwazi.” Wofunsayo anati: “Nangano mbiri yabwino njotani?” Funso limene “guru” analiyankha kuti: “Mulungu adzapukuta misozi yonse . . . ndipo sipadzakhalanso imfa kapena chisoni kapena choŵaŵitsa!” Mlendoyo anafunsa kuti: “Kodi mumadziŵa bwanji zinthu zoterozo?” Yankho lake? “Palibe munthu amene angazembe Mboni za Yehova!” Ndipo zimenezo ziyenera kukhala zinalinso choncho kwa wojambula zithunzithunzi zoseketsa mwiniyo!
Mfundo yofunika ya zithunzithunzi zimenezi ndi zina zofanana nazo njakuti zimavumbula osati kusalekeza kwa maulendo a Mboni kokha komanso kusasintha kwa uthenga wawo. M’mawu ochepa okha, wojambulayo anapereka mbali yaikulu ya umboni wawo wa kunyumba ndi nyumba ndi kugwira mawu malemba.—Yerekezerani ndi Mateyu 24:7, 29; Chivumbulutso 21:3, 4.
Chenicheni chakuti anthu ochuluka amakana uthengawo sichimalefula Mboni kapena kuziralitsa changu chawo. Mtumwi Petro anachenjeza kuti: “Masiku otsiriza adzafika onyoza ndi kuchita zonyoza, oyenda monga mwa zilakolako za iwo eni, ndi kunena, Lili kuti lonjezano la kudza kwake? pakuti kuyambira kuja makolo adamwalira zonse zikhala monga chiyambire chilengedwe.” Mosasamala kanthu za zimenezi, posonkhezeredwa ndi chikondi, Mboni zimapitirizabe kufikira anansi awo ndipo zidzatero kufikira pamene Mulungu abweretsa mapeto a dongosolo loipa lilipoli.—2 Petro 3:3, 4.
Yesu ananena kuti m’masiku otsiriza, mbiri yabwino ikayenera kulalikidwa choyamba. Kuti mupende mowonjezereka ponena za chifukwa chake ndi mmene kukuchitidwira, onani nkhani ziŵiri zotsatira.—Marko 13:10.
[Zithunzi patsamba 9]
Mboni za Yehova zilibe kagulu ka atsogoleri achipembedzo kolipidwa—zonse zili atumiki odzifunira