Idzani ku Msonkhano Wachigawo wa “Atamandi Achimwemwe”
HA, ndi mutu wabwino chotani nanga umene wasankhidwa wa misonkhano yachigawo ya 1995: “Atamandi Achimwemwe”! Umu ndi mmenedi Mboni za Yehova zilili. Atamandi ayani? Si a Yehova Mulungu!
Yehova alibe wofanana naye, ali wosayerekezereka, wapadera m’njira zambiri. Iye ali mwini mphamvu, mwini nzeru, wangwiro m’chilugamo, ndi chitsanzo changwiro cha chikondi. Ali woyenera kulambiridwa ndi kutamandidwa kuposa wina aliyense.
Ndithudi, ife timafuna kukhala atamandi ake achimwemwe! Kuti atithandize kukhala otero, Bungwe Lolamulira la Mboni za Yehova lakonza programu yabwino ya masiku atatu, kuyambira m’chisanu cha 1995. Masiku atatu ameneŵa adzakhaladi achisangalalo, ndipo Mboni iliyonse ya Yehova idzayenera kuchita zonse zomwe ingathe kuti ikakhalepo kuyambira pa nyimbo yoyamba pa Lachisanu mmaŵa mpaka pa nyimbo yomaliza ndi pemphero pa Sande madzulo.