Idzani ku Msonkhano Wachigawo wa “Mantha Aumulungu”
ATUMIKI a Yehova m’nthaŵi zakale analamulidwa ndi Chilamulo cha Mose kusonkhana pamodzi katatu pachaka kaamba ka mapwando ena. Zimenezi zinali zochitika zachisangalalo ndi zolimbikitsa mwauzimu.—Deuteronomo 16:16.
M’nthaŵi zamakono atumiki a Yehova amasonkhananso pamodzi katatu pachaka: kaamba ka tsiku la msonkhano wapadera, msonkhano wadera wa masiku aŵiri, ndi msonkhano wachigawo wa masiku atatu kapena anayi. Mu chaka chautumiki cha 1994, Mboni za Yehova zidzasonkhana pamodzi kaamba ka Msonkhano Wachigawo wa “Mantha Aumulungu.”
Mawu a Mulungu samasiya chikayikiro chilichonse ponena za kufunika kwa mantha aumulungu. Mantha a mtundu umenewo akutchulidwa mmenemo kwa nthaŵi pafupifupi 200. Mantha aumulungu ali chitetezo, monga momwe tingaonere pa Miyambo 16:6 kuti: “Apatuka pa zoipa powopa Yehova.” Eya, tikuuzidwa pa Salmo 111:10 kuti mantha aumulungu ndiwo chiyambi chenicheni cha nzeru!
Tinganene kuti pali mbali ziŵiri za mantha aumulungu. Choyamba, mantha oterowo amachititsidwa ndi chikondi. Timawopa kusakondweretsa Mulungu chifukwa cha chikondi chathu chachikulu kwa iye. (Miyambo 27:11) Ndiyenonso, kukhala kwathu ndi nzeru kudzatipatsa manthu aumulungu, popeza timadziŵa kuti Mulungu alinso “moto wonyeketsa” kwa onse ochita zoipa.—Ahebri 12:29.
Pamsonkhano wathu Wachigawo wa “Mantha Aumulungu,” tidzalandira malangizo ochuluka ndi chilimbikitso kuti tikule m’mantha aumulungu. Chiphunzitso choterocho chidzaperekedwa mwa nkhani, zitsanzo, ndi drama, limodzinso ndi kusimba zokumana nazo.
Monga momwe Aisrayeli akale analamulidwira kusafika kumisonkhano chimanjamanja, ifenso tifuna kuchita chopereka cha mbali yathu ku chisangalalo ndi chipambano cha misonkhano yathu. (Deuteronomo 16:17) Tingachite zimenezi mwa kusonyeza ulemu kaamba ka gome la Yehova. Motani? Mwa kufika mwamsanga, mwa kumvetsera motchera khutu zimene zikukambidwa paplatifomu, mwa kutengamo mbali ndi mtima wonse m’kuimba nyimbo. Sitidzakhala tikumadziloŵetsa m’kukambitsirana nkhani kapena kuyendayenda mkati mwa maprogramu. Tidzafunanso kupatsa chopereka kumlingo umene tingakhoze mwa kudzipereka m’ntchito zotumikira. Makonzedwe a msonkhano amaphatikizapo madipatimenti ambiri, ndipo onsewo amafuna antchito. Tidzafunanso kupatsa zopereka za ndalama malinga ndi mmene Yehova watidalitsira.
Tikulimbikitsa mtumiki wa Yehova aliyense kupanga makonzedwe tsopano kuti akakhalepo pamasiku onse atatu a Msonkhano Wachigawo wa “Mantha Aumulungu,” kuyambira ndi nyimbo yotsegulira pa tsiku loyamba mmaŵa mpaka papemphero lomalizira pa tsiku lotsiriza masana.