“Israyeli wa Mulungu” ndi “Khamu Lalikulu”
“Ndinapenya, taonani, khamu lalikulu, loti palibe munthu anakhoza kuliŵerenga.”—CHIVUMBULUTSO 7:9.
1-3. (a) Kodi ndi ziyembekezo zaulemerero zakumwamba zotani zimene Akristu odzozedwa ali nazo? (b) Kodi Satana anayesa motani kuwononga mpingo wa m’zaka za zana loyamba? (c) Kodi nchiyani chimene chinachitika mu 1919 chimene chinasonyeza kuti zoyesayesa za Satana za kuipitsa mpingo wodzozedwa Wachikristu zinali zitalephera?
KUYAMBA kwa “Israyeli wa Mulungu” mu 33 C.E. kunali sitepe yaikulu pa kukwaniritsidwa kwa zifuno za Yehova. (Agalatiya 6:16) Ziŵalo zake zodzozedwa zili ndi chiyembekezo cha kukhala zolengedwa zauzimu zosafa ndi kulamulira ndi Kristu mu Ufumu wakumwamba wa Mulungu. (1 Akorinto 15:50, 53, 54) Pokhala m’malo otero iwo ali ndi mbali ya kutsogolera m’kuyeretsa dzina la Yehova ndi kuphwanya mutu wa Mdani wamkuluyo, Satana Mdyerekezi. (Genesis 3:15; Aroma 16:20) Mposadabwitsa kuti Satana anachita zonse zimene anakhoza kuti awononge mpingo umenewu watsopano, mwa kuuzunza ndi mwa kuyesa kuuipitsa!—2 Timoteo 2:18; Yuda 4; Chivumbulutso 2:10.
2 Pamene atumwi anali ndi moyo, Satana sanathe kuchita zimenezo. Komabe, pambuyo pa imfa yawo, mpatuko unawanda mosalamulirika. Potsirizira pake, pa kaonedwe kaumunthu, mpingo woyera Wachikristu umene unayambidwa ndi Yesu unakhala ngati waipitsidwa pamene Satana anadzetsa chipembedzo chonamizira cha mpatuko chimene lero chimadziŵika kukhala Dziko Lachikristu. (2 Atesalonika 2:3-8) Komabe, Chikristu choona chinapitiriza kukhalapo.—Mateyu 28:20.
3 Yesu, m’fanizo lake la tirigu ndi namsongole, ananeneratu kuti Akristu oona panthaŵi ina adzakulira pamodzi ndi “namsongole,” kapena Akristu onyenga; ndipo zimenezi zinachitika. Koma iye ananenanso kuti mkati mwa masiku otsiriza, “ana a Ufumu” adzaonekanso kukhala osiyana ndi “namsongole.” (Mateyu 13:36-43) Zimenezinso zinachitika. Mu 1919 Akristu enieni odzozedwa anatuluka mu ukapolo wa Babulo. Iwo anadziŵika mwaumulungu monga “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” ndipo molimbika anayamba kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu. (Mateyu 24:14, 45-47; Chivumbulutso 18:4) Unyinji wa iwowo anali Akunja; koma chifukwa chakuti anali ndi chikhulupiriro chonga cha Abrahamu, iwo analidi ‘mbadwa za Abrahamu.’ Anali ziŵalo za “Israyeli wa Mulungu.”—Agalatiya 3:7, 26-29.
“Khamu Lalikulu”
4. Kodi ndi gulu liti la Akristu limene linaonekera, makamaka m’ma 1930?
4 Choyamba, awo amene analabadira kulalikira kwa Akristu odzozedwa ameneŵa nawonso anakhala Aisrayeli auzimu, otsalira a 144,000, okhala ndi chiyembekezo cha kumwamba. (Chivumbulutso 12:17) Komabe, makamaka m’ma 1930, gulu linanso linayamba kuonekera. Anthu a gulu limeneli anadziŵika kukhala a “nkhosa zina” za fanizo la makola. (Yohane 10:16) Iwo anali ophunzira a Kristu okhala ndi chiyembekezo cha moyo wosatha pa dziko lapansi la paradaiso. Anali mbadwa zauzimu, titero kunena kwake, za Akristu odzozedwa. (Yesaya 59:21; 66:22; yerekezerani ndi 1 Akorinto 4:15, 16.) Iwo anazindikira mpingo Wachikristu wa odzozedwa kukhala kapolo wokhulupirika ndi wanzeru, ndipo mofanana ndi abale awo odzozedwa, anali ndi chikondi chakuya pa Yehova, chikhulupiriro mu nsembe ya Yesu, changu pa kutamanda Mulungu, ndi kulolera kuvutika chifukwa cha chilungamo.
5. Kodi ndimotani mmene malo a nkhosa zina azindikiridwira bwino pang’onopang’ono?
5 Poyamba malo a nkhosa zina zimenezi sanazindikiridwe bwino, koma pamene nthaŵi inali kupita, zinthu zinayamba kuzindikiridwa bwino. Mu 1932 Akristu odzozedwa analimbikitsidwa kufulumiza nkhosa zina kukhala ndi phande mu ntchito yolalikira—kanthu kena kamene a nkhosa zina ambiri anali atayamba kale kuchita. Mu 1934 nkhosa zina zinalimbikitsidwa kudzipereka mu ubatizo wa m’madzi. Mu 1935 iwo anadziŵika kukhala “khamu lalikulu” la m’Chivumbulutso chaputala 7. Mu 1938 iwo anaitanidwa pa Chikumbutso cha imfa ya Yesu Kristu monga openyerera. Mu 1950 amuna okula msinkhu mwa iwo anazindikiridwa kukhala ena a “akalonga” amene ali monga “pobisalira mphepo, ndi pousira chimphepo.” (Salmo 45:16; Yesaya 32:1, 2) Mu 1953, gulu la Mulungu la pa dziko lapansi—limene mbali yake yokulirapo inali yopangidwa ndi nkhosa zina panthaŵiyo—linalingaliridwa kukhala chithima cha chitaganya cha pa dziko lapansi chimene chidzakhalako m’dziko latsopano. Mu 1985 kunazindikiridwa kuti pa maziko a nsembe ya dipo ya Yesu, nkhosa zina zimayesedwa zolungama monga mabwenzi a Mulungu ndi chiyembekezo cha kupulumuka Armagedo.
6. Kodi ndi unansi wotani umene uli pakati pa odzozedwa ndi a nkhosa zina lerolino, zikumadzutsa mafunso ati?
6 Pofika nthaŵi ino, m’mbali yotsalayi ya “masiku otsiriza,” unyinji waukulu wa 144,000 wamwalira ndi kulandira mfupo yawo yakumwamba. (2 Timoteo 3:1; Chivumbulutso 6:9-11; 14:13) Akristu okhala ndi chiyembekezo cha pa dziko lapansi tsopano amachita ntchito yambiri yolalikira uthenga wabwino, ndipo kuchirikiza abale odzozedwa a Yesu pa zimenezi amakuyesa mwaŵi. (Mateyu 25:40) Komabe, odzozedwa ameneŵa ali kapolo wokhulupirika ndi wanzeru amene kupyolera mwa iye chakudya chauzimu chimaperekedwa m’masiku ano otsiriza. Kodi mkhalidwe udzakhala wotani kwa nkhosa zina pamene odzozedwa onse alandira mfupo yawo yakumwamba? Kodi ndi makonzedwe otani tsopano amene adzapangidwa kaamba ka nkhosa zina? Kupenda mwachidule Israyeli wakale kudzatithandiza kuyankha mafunso amenewo.
“Ufumu wa Ansembe” Weniweni
7, 8. Kodi Israyeli wakale pansi pa pangano la Chilamulo anali ufumu wa ansembe ndi mtundu wopatulika kufikira pati?
7 Pamene Yehova anasankha Israyeli kukhala mtundu wake wapadera, anapangana nawo pangano, akumati: “Ngati mudzamvera mawu anga ndithu, ndi kusunga chipangano changa, ndidzakuyesani chuma changa chapadera koposa mitundu yonse ya anthu; pakuti dziko lonse lapansi ndi langa; ndipo ndidzakuyesani ufumu wanga wa ansembe, ndi mtundu wopatulika.” (Eksodo 19:5, 6) Israyeli anali mtundu wapadera wa Yehova pa maziko a pangano la Chilamulo. Komabe, kodi ndimotani mmene lonjezo lophatikizapo ufumu wa ansembe ndi mtundu wopatulika likanakwaniritsidwira?
8 Israyeli, pamene anali wokhulupirika, anavomereza ulamuliro wa Yehova ndi kumlandira kukhala Mfumu yawo. (Yesaya 33:22) Motero, iwo anali ufumu. Koma, monga momwe kunasonyezedwera pambuyo pake, lonjezo lonena za “ufumu” likatanthauzadi zochuluka kuposa zimenezo. Ndiponso, pamene anamvera Chilamulo cha Yehova, anali oyera, olekana ndi mitundu yowazinga. Anali mtundu wopatulika. (Deuteronomo 7:5, 6) Kodi iwo anali ufumu wa ansembe? Chabwino, mu Israyeli fuko la Levi linapatulidwa kaamba ka utumiki wa pakachisi, ndipo mu fukolo munali kagulu ka ansembe Achilevi. Pamene Chilamulo cha Mose chinakhazikitsidwa, amuna Achilevi anatengedwa mosinthanitsana ndi mwana wachisamba aliyense wa m’banja losakhala la Alevi.a (Eksodo 22:29; Numeri 3:11-16, 40-51) Motero, banja lililonse mu Israyeli linali ndi oliimira, titero kunena kwake, mu utumiki wa pakachisi. Mwanjira imeneyo mtunduwo unakhala wa ansembe. Chikhalirechobe, uwo unaimira Yehova pamaso pa mitundu ina. Mlendo aliyense amene anafuna kulambira Mulungu woona anafunikira kuchita motero mogwirizana ndi Israyeli.—2 Mbiri 6:32, 33; Yesaya 60:10.
9. Kodi nchiyani chimene chinachititsa Yehova kukana ufumu wakumpoto wa Israyeli ‘kusakhala wansembe wake’?
9 Solomo atamwalira, anthu a Mulunguwo anagaŵanika kukhala mtundu wakumpoto wa Israyeli wolamuliridwa ndi Mfumu Yerobiamu ndi mtundu wakummwera wa Yuda wolamuliridwa ndi Mfumu Rehabiamu. Kachisi, phata la kulambira koyera, anali m’dera la Yuda, Yerobiamu anakhazikitsa mtundu wa kulambira kosaloledwa mwa kupanga mafano a ana a ng’ombe m’dera la dziko lake. Ndiponso, “[a]namanga nyumba za m’misanje, nalonga anthu achabe akhale ansembe, osati ana a Levi ayi.” (1 Mafumu 12:31) Mtundu wakumpoto unaloŵerera kwambiri m’kulambira konyenga pamene Mfumu Ahabu analola mkazi wake wachikunja, Yezebeli, kukhazikitsa kulambira Baala m’dzikolo. Potsirizira pake, Yehova analengeza za chiweruzo pa ufumu wopandukawo. Kupyolera mwa Hoseya, iye anati: “Anthu anga awonongeka chifukwa cha kusadziŵa; popeza unakana kudziŵa, inenso ndikukaniza, kuti usakhale wansembe wanga.” (Hoseya 4:6) Posapita nthaŵi, Asuri anawononga ufumu wakumpoto wa Israyeli.
10. Kodi ndimotani mmene ufumu wakummwera wa Yuda, pamene unali wokhulupirika, unaimira Yehova pamaso pa amitundu?
10 Bwanji nanga za mtundu wakummwerawo, Yuda? M’masiku a Hezekiya, Yehova kupyolera mwa Yesaya anati kwa iwo: “Inu ndinu mboni zanga, . . . ndi mtumiki wanga, amene ndakusankha; . . . anthu amene ndinadzilengera ndekha, kuti aonetse matamando anga.” (Yesaya 43:10, 21; 44:21) Pamene unali wokhulupirika, ufumu wakummwera unachita ntchito yolengeza ku mitundu ina za ulemerero wa Yehova ndi kukopa anthu owongoka mtima kudzamlambira pakachisi wake ndi kutumikiridwa ndi unsembe walamulo wa Alevi.
Alendo mu Israyeli
11, 12. Tchulani anthu ena amene anali alendo omwe anatumikira Yehova pamodzi ndi Israyeli.
11 Ponena za alendo amene analabadira umboni wa mtunduwo, panapangidwa makonzedwe awo m’Chilamulo choperekedwa kupyolera mwa Mose—amene mkazi wake, Zipora, anali Mmidyani. “Anthu ambiri [osakanizika, NW]” osakhala Aisrayeli anachoka ku Igupto ndi Israyeli ndipo analipo pamene Chilamulo chinaperekedwa. (Eksodo 2:16-22; 12:38; Numeri 11:4) Rahabi ndi banja lake anapulumutsidwa mu Yeriko ndipo pambuyo pake anavomerezedwa kukhala mumpingo Wachiyuda. (Yoswa 6:23-25) Posapita nthaŵi, Agibeoni anachita pangano la mtendere ndi Israyeli ndipo anapatsidwa ntchito yokhudza za chihema.—Yoswa 9:3-27; onaninso 1 Mafumu 8:41-43; Estere 8:17.
12 Potsirizira pake, alendo anatumikira m’malo apamwamba. Uriya Mhiti, mwamuna wake wa Beteseba, anaŵerengedwa pakati pa “amphamvuwo” a Davide, monga momwe zinalili kwa Zeleki Mwamoni. (1 Mbiri 11:26, 39, 41; 2 Samueli 11:3, 4) Ebedi-Meleki, Mkusi, anatumikira m’nyumba yachifumu ndipo anali wovomerezedwa kulankhula ndi mfumu. (Yeremiya 38:7-9) Israyeli atabwerako ku ukapolo wa ku Babulo, Anetini osakhala Aisrayeli anapatsidwa thayo lowonjezereka la kuthandiza ansembe. (Ezara 7:24) Popeza kuti ambiri a alendo okhulupirika ameneŵa, kapena nzika zachilendo, amaonedwa kukhala akuchitira chithunzi khamu lalikulu lerolino, mkhalidwe wawo ngwofunika kwambiri kuti tiudziŵe.
13, 14. (a) Kodi otembenuka mu Israyeli anali ndi mwaŵi ndiponso ndi mathayo otani? (b) Kodi ndimotani mmene Aisrayeli anayenera kuonera otembenuka okhulupirika?
13 Anthu ameneŵa anali otembenuka, olambira Yehova odzipatulira pansi pa Chilamulo cha Mose amene pamodzi ndi Aisrayeli anali olekana ndi mitundu ina. (Levitiko 24:22) Anapereka nsembe, anapeŵa kulambira konyenga, ndipo anasala mwazi, monga momwe Aisrayeli anachitira. (Levitiko 17:10-14; 20:2) Anathandiza kumanga kachisi wa Solomo ndipo anagwirizana nawo pa kubwezeretsa kulambira koona motsogoleredwa ndi Mfumu Asa ndi Mfumu Hezekiya. (1 Mbiri 22:2; 2 Mbiri 15:8-14; 30:25) Pamene Petro anagwiritsira ntchito mfungulo yoyamba ya Ufumu pa Pentekoste wa 33 C.E., mawu ake anamvedwa ndi “Ayuda, ndiponso [osakhala Ayuda] opinduka.” Mwinamwake, ena a zikwi zitatu amene anabatizidwa patsikulo anali otembenuka. (Machitidwe 2:10, 41) Posapita nthaŵi, Mwaitiyopiya wina wotembenuka anabatizidwa ndi Filipo—Petro asanagwiritsire ntchito mfungulo yotsiriza ya Ufumu kwa Korneliyo ndi banja lake. (Mateyu 16:19; Machitidwe 8:26-40; 10:30-48) Mwachionekere, otembenukawo sanaonedwe monga ngati Amitundu.
14 Komabe, malo a otembenuka m’dzikolo sanali ofanana ndi aja a mbadwa Zachiisrayeli. Otembenukawo sanatumikire monga ansembe, ndipo ana awo achisamba sanaimiridwe ndi ansembe a Alevi.b Ndipo otembenukawo analibe dziko la choloŵa mu Israyeli. Chikhalirechobe, Aisrayeli analamulidwa kukhala olingalira za otembenuka okhulupirikawo ndi kuwaona monga abale.—Levitiko 19:33, 34.
Mtundu Wauzimu
15. Kodi nchiyani chimene chinachitika pamene Israyeli wakuthupi anakana kulandira Mesiya?
15 Chilamulo chinalinganizidwira kuchititsa Israyeli kukhala woyera, wolekana ndi mitundu yomuzinga. Komanso chinali ndi chifuno china. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Chilamulo chidakhala namkungwi wathu wakutifikitsa kwa Kristu, kuti tikayesedwe olungama ndi chikhulupiriro.” (Agalatiya 3:24) Mwachisoni, Aisrayeli ochuluka sanafikitsidwe kwa Kristu ndi Chilamulocho. (Mateyu 23:15; Yohane 1:11) Chotero Yehova Mulungu anakana mtunduwo ndi kuchititsa “Israyeli wa Mulungu” kubadwa. Ndiponso, iye anapereka chiitano kwa osakhala Ayuda cha kudzakhala nzika zenizeni mu Israyeli ameneyu watsopano. (Agalatiya 3:28; 6:16) Kukwaniritsidwa bwino kwambiri ndi komalizira kwa lonjezo la Yehova la pa Eksodo 19:5, 6 lonena za ufumu wa ansembe kunachitidwa pa mtundu umenewu. Motani?
16, 17. Kodi Akristu odzozedwa okhala pa dziko lapansi ali “achifumu” m’lingaliro lotani? ali “ansembe” m’lingaliro lotani?
16 Petro anagwira mawu Eksodo 19:6 pamene analembera Akristu odzozedwa a m’tsiku lake kuti: “Inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake.” (1 Petro 2:9) Kodi zimenezi zikutanthauzanji? Kodi Akristu odzozedwa amene ali pa dziko lapansi ndi mafumu? Ayi, uchifumu wawo ukali mtsogolobe. (1 Akorinto 4:8) Komabe, iwo ali “achifumu” m’lingaliro lakuti ali osankhidwa kukhala m’malo achifumu mtsogolo. Ngakhale tsopano lino iwo ali mtundu umene uli pansi pa mfumu, Yesu, yoikidwa ndi Mfumu Yaikulu, Yehova Mulungu. Paulo analemba kuti: “[Yehova] anatilanditsa ife ku ulamuliro wa mdima, natisunthitsa kutiloŵetsa [mu] ufumu wa Mwana wa chikondi chake.”—Akolose 1:13.
17 Kodi Akristu odzozedwa okhala pa dziko lapansi ali ansembe? Inde, m’lingaliro lina. Monga mpingo, iwo amachita ntchito yeniyeni yaunsembe. Petro analongosola zimenezi pamene anati: “Inunso . . . mumangidwa nyumba ya uzimu, kuti mukhale ansembe oyera mtima.” (1 Petro 2:5; 1 Akorinto 3:16) Lerolino, otsalira a Akristu odzozedwa onse pamodzi ndiwo “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” ngalande yoperekeramo chakudya chauzimu. (Mateyu 24:45-47) Monga momwe zinalili kwa Israyeli wakale, aliyense amene akufuna kulambira Yehova ayenera kuchita choncho mogwirizana ndi Akristu odzozedwa ameneŵa.
18. Monga ansembe, kodi mpingo wodzozedwa Wachikristu pa dziko lapansi uli ndi thayo liti lalikulu?
18 Ndiponso, Akristu odzozedwawo analanda Israyeli mwaŵi wa kuchitira umboni za ukulu wa Yehova pakati pa mitundu. Mawu a m’nkhaniyo amasonyeza kuti pamene Petro anatcha Akristu odzozedwa kuti ansembe achifumu, anali kulingalira za ntchito yolalikira. Indedi, iye anagwirizanitsa lonjezo la Yehova la pa Eksodo 19:6 ndi mawu Ake kwa Israyeli pa Yesaya 43:21 kukhala mawu amodzi ogwidwa pamene anati: “Inu ndinu . . . ansembe achifumu, . . . kotero kuti mukalalikire zoposazo za iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, muloŵe kuunika kwake kodabwitsa.” (1 Petro 2:9) Mogwirizana ndi zimenezi, Paulo ananena za kulalikira kwa zoposa za Yehova kukhala nsembe ya pakachisi. Iye analemba kuti: “Mwa [Yesu] tipereke chiperekere nsembe yakuyamika Mulungu, ndiyo chipatso cha milomo yovomereza dzina lake.”—Ahebri 13:15.
Kukwaniritsidwa Kwake kwa Kumwamba
19. Kodi nkuti kumene kuli kukwaniritsidwa kwakukulu ndi kotsiriza kwa lonjezo lakuti Israyeli adzakhala ufumu wa ansembe?
19 Komabe, Eksodo 19:5, 6 potsirizira pake adzakhala ndi kukwaniritsidwa kokulirapo kwaulemerero. M’buku la Chivumbulutso, mtumwi Yohane akumva zamoyo zakumwamba zikumagwiritsira ntchito lemba limeneli pamene zikutamanda Yesu woukitsidwayo: “Mwaphedwa, ndipo mwagulira Mulungu ndi mwazi wanu anthu a mafuko onse, ndi manenedwe onse, ndi mitundu yonse, ndipo mudawayesa iwo ufumu ndi ansembe kwa Mulungu wathu; ndipo achita ufumu padziko.” (Chivumbulutso 5:9, 10) Pamenepo, m’lingaliro lake lotsiriza, ansembe achifumuwo ndiwo Ufumu wa Mulungu wakumwamba, boma lolamulira limene Yesu anatiphunzitsa kulipempherera. (Luka 11:2) Akristu odzozedwa onse a 144,000 amene amapirira mokhulupirika kufikira mapeto adzakhala ndi mbali m’kakonzedwe ka Ufumu umenewo. (Chivumbulutso 20:4, 6) Ha, ndi kukwaniritsidwa kwabwino chotani nanga kumeneko kwa lonjezo lonenedwa kalekale limenelo kupyolera mwa Mose!
20. Kodi ndi funso lotani limene liyenera kuyankhidwa?
20 Kodi zonsezi zili nchiyani pa mkhalidwe wa khamu lalikulu ndi mtsogolo mwawo pamene odzozedwa onse alandira choloŵa chawo chabwino kwambiricho? Zimenezi zidzazindikiridwa bwino m’nkhani yotsiriza ya mpambo uno.
[Mawu a M’munsi]
a Pamene unsembe wa Israyeli unakhazikitsidwa, ana aamuna achisamba a mafuko a Israyeli osakhala a Alevi ndi amuna Achilevi anaŵerengedwa. Panali ana achisamba 273 owonjezereka kuposa amuna Achilevi. Motero, Yehova analamula kuti masekeli asanu pa munthu aliyense wa 273 amenewo aperekedwe monga dipo la kuchulukitsitsako.
b Khamu lalikulu losakanizikalo la osakhala Aisrayeli linalipo pamene Chilamulo chinaperekedwa mu 1513 B.C.E., koma ana awo achisamba sanaphatikizidwe pamene Alevi anatengedwa monga chosinthanitsa ndi ana achisamba a Israyeli. (Onani ndime 8.) Motero, Alevi sanatengedwe mosinthanitsa ndi ana achisamba a osakhala Aisrayeli ameneŵa.
Kodi Mungalongosole?
◻ Kodi ndimotani mmene malo a nkhosa zina azindikiridwira bwino pang’onopang’ono?
◻ Kodi nchifukwa ninji Yehova anakana ufumu wakumpoto wa Israyeli kutumikira monga wansembe wake?
◻ Kodi Yuda anali ndi malo otani pamaso pa mitundu ina pamene anali wokhulupirika?
◻ Kodi malo a otembenuka okhulupirika anali otani mu Israyeli?
◻ Kodi mpingo wodzozedwa umatumikira motani monga ufumu wa ansembe?
[Chithunzi patsamba 16]
Monga ansembe achifumu, Akristu odzozedwa amalengeza za ulemerero wa Yehova pa dziko lapansi
[Chithunzi patsamba 18]
Kukwaniritsidwa kotsiriza kwa Eksodo 19:6 ndiko Ufumu