1 Mbiri
11 Patapita nthawi, Aisiraeli onse anasonkhana kwa Davide ku Heburoni+ nʼkumuuza kuti: “Ife ndi inu ndife magazi amodzi.*+ 2 Kale Sauli ali mfumu, inuyo ndi amene munkatsogolera Aisiraeli kunkhondo.*+ Ndipo Yehova Mulungu wanu anakuuzani kuti, ‘Udzaweta anthu anga Aisiraeli ndipo udzakhala mtsogoleri wa anthu anga Aisiraeli.’”+ 3 Choncho akulu onse a Isiraeli anabwera kwa mfumu ku Heburoni ndipo Davide anachita nawo pangano ku Heburoniko pamaso pa Yehova. Kenako iwo anadzoza Davide kukhala mfumu ya Isiraeli,+ mogwirizana ndi mawu a Yehova amene analankhula kudzera mwa Samueli.+
4 Zitatero Davide ndi Aisiraeli onse anapita ku Yerusalemu, kapena kuti ku Yebusi,+ dziko limene kunkakhala Ayebusi.+ 5 Anthu a ku Yebusi anayamba kunyoza Davide kuti: “Sudzalowa mumzinda uno.”+ Koma Davide analanda malo amene anali mumpanda wolimba kwambiri mu Ziyoni,+ umene panopa ndi Mzinda wa Davide.+ 6 Choncho Davide anati: “Aliyense amene ayambirire kuukira Ayebusi akhala mtsogoleri ndiponso kalonga.” Yowabu+ mwana wa Zeruya ndi amene anayamba kupita, choncho anakhala mtsogoleri. 7 Ndiyeno Davide anayamba kukhala kumalo ovuta kufikako. Nʼchifukwa chake malowo anawapatsa dzina lakuti Mzinda wa Davide. 8 Kenako Davide anayamba kumanga mzinda pamalo onsewo, kuyambira ku Chimulu cha Dothi* mpaka kumadera ozungulira, ndipo Yowabu ndi amene anamalizitsa kumanga mzindawo. 9 Choncho Davide anapitiriza kukhala wamphamvu+ chifukwa Yehova Mulungu wa magulu ankhondo akumwamba anali naye.
10 Awa ndi amene anali atsogoleri a asilikali amphamvu a Davide amene anamuthandiza kwambiri kulimbitsa ufumu wake pamodzi ndi Aisiraeli onse, kuti iye akhale mfumu mogwirizana ndi mawu a Yehova okhudza Aisiraeli.+ 11 Otsatirawa ndi amene anali asilikali amphamvu a Davide: Yasobeamu+ mbadwa ya Hakemoni, mtsogoleri wa amuna atatu.+ Iye anatenga mkondo wake nʼkupha anthu 300 nthawi imodzi.+ 12 Wotsatira wake anali Eliezara+ mwana wa Dodo, mwana wa Ahohi.+ Iye anali mmodzi wa asilikali atatu amphamvuwo. 13 Iye anali ndi Davide ku Pasi-damimu+ kumene Afilisiti anasonkhana kuti amenyane nawo. Kumeneko kunali munda wa balere wambiri ndipo anthu anali atathawa chifukwa choopa Afilisitiwo. 14 Koma iye anaima pakati pa mundawo nʼkuuteteza ndipo anapitiriza kupha Afilisiti, moti Yehova anawathandiza kuti apambane.+
15 Kenako, atatu mwa atsogoleri 30 anapita kwa Davide kuthanthwe, kuphanga la Adulamu.+ Pa nthawiyi asilikali a Afilisiti anali atamanga msasa mʼchigwa cha Arefai.+ 16 Pa nthawi imeneyi nʼkuti Davide ali kumalo ovuta kufikako ndipo asilikali a Afilisiti anali ku Betelehemu. 17 Ndiyeno Davide ananena zimene ankalakalaka kuti: “Ndikanakonda ndikanamwa madzi amʼchitsime chimene chili pageti la ku Betelehemu!”+ 18 Atatero amuna atatu aja analimbana ndi anthu mpaka kulowa mumsasa wa Afilisiti nʼkukatunga madzi mʼchitsime chimene chinali pageti la ku Betelehemu ndipo anapita nawo kwa Davide. Koma iye anakana kumwa madziwo. Mʼmalomwake anawapereka kwa Yehova powathira pansi. 19 Iye anati: “Ndikaiona nkhaniyi mmene Mulungu akuionera, sindingachite zimenezi. Kodi ndimwe magazi a amuna amene anaika moyo wawo pa ngoziwa?+ Chifukwa anaika moyo wawo pa ngozi kuti akatunge madziwa.” Choncho iye anakana kumwa madziwo. Izi nʼzimene asilikali ake atatu amphamvuwo anachita.
20 Abisai+ mchimwene wake wa Yowabu+ anali mtsogoleri wa amuna atatu. Iye anatenga mkondo wake nʼkupha anthu 300 ndipo anali wotchuka ngati amuna atatu aja.+ 21 Pa amuna atatu ena aja, iye anali wolemekezeka kwambiri kuposa awiri enawo ndipo anali mtsogoleri wawo. Koma sankafanana ndi amuna atatu oyambirira aja.
22 Benaya+ mwana wa Yehoyada, anali munthu wolimba mtima* ndipo anachita zinthu zambiri ku Kabizeeli.+ Iye anapha ana awiri a Ariyeli wa ku Mowabu komanso analowa mʼchitsime chopanda madzi pa tsiku lomwe kunagwa sinowo* nʼkupha mkango umene unali mʼchitsimemo.+ 23 Benaya anaphanso munthu wamkulu modabwitsa wa ku Iguputo, yemwe anali wamtali mikono 5.*+ Ngakhale kuti munthuyu anali ndi mkondo mʼmanja mwake, waukulu ngati mtengo wogwiritsa ntchito powomba nsalu,+ Benaya anapita kukakumana naye atanyamula ndodo ndipo analanda mkondowo nʼkumupha ndi mkondo wake womwewo.+ 24 Zimenezi nʼzimene Benaya mwana wa Yehoyada anachita. Iye anali wotchuka ngati asilikali atatu amphamvu aja. 25 Ngakhale kuti anali wolemekezeka kwambiri kuposa amuna 30 aja, sankafanana ndi amuna atatu aja.+ Koma Davide anamuika kukhala mmodzi wa asilikali ake omulondera.
26 Asilikali amphamvu a magulu ankhondo anali Asaheli+ mchimwene wake wa Yowabu, Elihanani mwana wa Dodo wa ku Betelehemu,+ 27 Samoti wa ku Harodi, Helezi wa ku Peloni, 28 Ira+ mwana wa Ikesi wa ku Tekowa, Abi-ezeri+ wa ku Anatoti, 29 Sibekai+ wa ku Husa, Ilai wa ku Ahohi, 30 Maharai+ wa ku Netofa, Heledi+ mwana wa Bana wa ku Netofa, 31 Ifai mwana wa Ribai wa ku Gibeya wa fuko la Benjamini,+ Benaya wa ku Piratoni, 32 Hurai wa kuzigwa* za Gaasi,+ Abiyeli wa ku Beti-araba, 33 Azimaveti wa ku Bahurimu, Eliyaba wa ku Saaliboni, 34 ana a Hasemu mbadwa ya Gizoni, Yonatani mwana wa Sage wa ku Harari, 35 Ahiyamu mwana wa Sakari wa ku Harari, Elifali mwana wa Uri, 36 Heferi mbadwa ya Mekera, Ahiya wa ku Peloni, 37 Heziro wa ku Karimeli, Naarai mwana wa Ezibai, 38 Yoweli mchimwene wake wa Natani, Mibari mwana wa Hagiri, 39 Zeleki mbadwa ya Amoni, Naharai wa ku Beeroti yemwe anali wonyamula zida za Yowabu mwana wa Zeruya, 40 Ira mbadwa ya Itiri, Garebi mbadwa ya Itiri, 41 Uriya+ Muhiti, Zabadi mwana wa Alai, 42 Adina mwana wa Siza wa fuko la Rubeni yemwe anali mtsogoleri wa anthu a fuko la Rubeni okwana 30, 43 Hanani mwana wa Maaka, Yosafati mbadwa ya Mitini, 44 Uzia wa ku Asitaroti, Sama ndi Yeyeli ana a Hotamu wa ku Aroweli, 45 Yediyaeli mwana wa Simuri, mchimwene wake wa Yoha wa ku Tizi, 46 Elieli wa ku Mahavi, Yeribai ndi Yosaviya ana a Elinaamu, Itima wa ku Mowabu, 47 Elieli, Obedi ndiponso Yaasiyeli wa ku Zoba.