Nsanje ya pa Kulambira Yehova Koyera
“Yehova dzina lake ndiye Wansanje, ali Mulungu wansanje.”—EKSODO 34:14.
1. Kodi ndi uti umene uli mkhalidwe waukulu wa Mulungu, ndipo kodi umagwirizana motani ndi nsanje yake?
YEHOVA amadzitcha “Mulungu wansanje.” Mwina mungadabwe ndi zimenezo, chifukwa chakuti liwu lakuti “nsanje” limapereka lingaliro la mkhalidwe woipa. Ndithudi, mkhalidwe waukulu wa Mulungu ndiwo chikondi. (1 Yohane 4:8) Chotero, malingaliro ake alionse a nsanje ayenera kukhala kaamba ka ubwino wa munthu. Kwenikweni, tidzaona kuti nsanje ya Mulungu njofunika kwambiri kuti pakhale mtendere ndi chigwirizano m’chilengedwe chonse.
2. Kodi mawu Achihebri otembenuzidwa “nsanje” angamasuliridwenso m’njira zina zotani?
2 Mawu ofanana Achihebri otembenuzidwa “nsanje” amapezeka nthaŵi zoposa 80 m’Malemba Achihebri. Pafupifupi theka la malowo limaloza kwa Yehova Mulungu. “Pamene liloza kwa Mulungu,” akufotokoza motero G. H. Livingston, “liwu lakuti nsanje silimakhala ndi lingaliro la mkhalidwe woipa, koma m’malo mwake, limatanthauza kuumirira pa kulambira kumodzi kokha kwa Yehova.” (The Pentateuch in Its Cultural Environment) Chifukwa chake, New World Translation nthaŵi zina imamasulira nauni Yachihebri ya liwulo kuti “kuumirira pa kulambira kosagaŵanika.” (Ezekieli 5:13) Mamasuliridwe ena oyenera ndiwo “kukangalika” kapena “changu.”—Salmo 79:5, NW; Yesaya 9:7.
3. Kodi ndi m’njira zotani zimene nsanje nthaŵi zina ingakhalire yothandiza?
3 Munthu analengedwa ndi chibadwa cha kumva nsanje, koma kuchimwa kwa munthu kunaipitsa nsanje. Komabe, nsanje ya anthu ingakhale yothandiza. Ingachititse wina kutetezera wokondedwa wake ku makhalidwe oipa. Ndiponso, anthu angasonyeze nsanje yoyenera ya pa Yehova ndi kulambiridwa kwake. (1 Mafumu 19:10) Kuti timveketse bwino nsanje imeneyo ya kwa Yehova, nauni Yachihebri ingatembenuzidwe “kusalola mpikisano” ndi iye.—2 Mafumu 10:16, NW.
Mwana wa Ng’ombe Wagolidi
4. Kodi ndi lamulo lotani la nsanje yolungama limene linali lalikulu m’Chilamulo cha Mulungu kwa Israyeli?
4 Chitsanzo cha nsanje yolungama ndicho chimene chinachitika pamene Aisrayeli analandira Chilamulo pa phiri la Sinai. Iwo anachenjezedwa mobwerezabwereza kusalambira milungu yopangidwa ndi anthu. Yehova anawauza kuti: “Ine Yehova Mulungu wako ndili Mulungu wansanje (wachangu), [kapena, Mulungu wofuna kulambira kosagaŵanika; Mulungu wosalola kupikisana naye].” (Eksodo 20:5, yerekezerani ndi Eksodo 20:22, 23; 22:20; 23:13, 24, 32, 33.) Yehova anapangana pangano ndi Aisrayeli, nawalonjeza kuwadalitsa ndi kuwaloŵetsa m’Dziko Lolonjezedwa. (Eksodo 23:22, 31) Ndipo anthu anati: “Zonse zimene Yehova walankhula tidzachita, ndi kumvera.”—Eksodo 24:7.
5, 6. (a) Kodi ndi tchimo lalikulu lotani limene Aisrayeli anachita pamene anali pachigono mmunsi mwa Phiri la Sinai? (b) Kodi Yehova ndi alambiri ake olungama anasonyeza motani nsanje yolungama pa Sinai?
5 Komabe, posapita nthaŵi Aisrayeliwo anachimwira Mulungu. Anali chikhalirebe pachigono mmunsi mwa Phiri la Sinai. Mose anali paphiri masiku ambiri, akumalandira malangizo ena kwa Mulungu, ndipo anthuwo anakakamiza Aroni mbale wake wa Mose kuti awapangire mulungu. Aroni anagonja nawapangira mwana wa ng’ombe ndi golidi amene anthu adampatsa. Ananena kuti fano limeneli linaimira Yehova. (Salmo 106:20) Mmaŵa mwake iwo anapereka nsembe, “namgwadira.” Ndiyeno ‘anaseŵera.’—Eksodo 32:1, 4, 6, 8, 17-19.
6 Mose anatsika m’phirimo pamene Aisrayeli anali pachikondwerero. Ataona kachitidwe konyansako, anafuula nati: “Onse akuvomereza Yehova adze kwa ine.” (Eksodo 32:25, 26) Ana a Levi anasonkhana kwa Mose, ndipo iye anawauza kutenga malupanga ndi kupha apandu amenewo olambira fanowo. Posonyeza nsanje yawo pa kulambira Mulungu koyera, Aleviwo anapha pafupifupi 3,000 mwa abale awo aliwongowo. Yehova anachirikiza kachitidwe kameneka mwa kutumiza mliri pa otsalawo. (Eksodo 32:28, 35) Ndiyeno Mulungu anabwereza lamulolo nati: “Musalambira mulungu wina; popeza Yehova dzina lake ndiye Wansanje, ali Mulungu wansanje.”—Eksodo 34:14.
Baala Peori
7, 8. (a) Kodi ndimotani mmene Aisrayeli anagwera m’kulambira mafano konyansa kwa Baala Peori? (b) Kodi mliri wochokera kwa Yehova unatha motani?
7 Patapita zaka makumi anayi, pamene mtundu wa Israyeli unali pafupi kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa, akazi okongola Achimoabu ndi Achimidyani ananyengerera Aisrayeli ambiri kukawachereza kwawo. Amuna ameneŵa anayenera kukana kuyanjana ndi olambira milungu yonyengawo. (Eksodo 34:12, 15) M’malo mwake, iwo anangopita monga ‘ng’ombe zokaphedwa,’ nakachita chisembwere ndi akaziwo nagwirizana nawo pa kugwadira Baala Peori.—Miyambo 7:21, 22; Numeri 25:1-3.
8 Yehova anatumiza mliri kuti uphe aja amene anadziloŵetsa m’kulambira chigololo kochititsa manyazi kumeneku. Mulungu analamulanso Aisrayeli opanda mlandu kupha abale awo aliwongo. Mwa kunyoza kwamwano, kalonga wina wa mu Israyeli wotchedwa Zimiri analoŵetsa mkazi Wachimidyani m’hema wake kuti agone naye. Poona zimenezi, wansembe Pinehasi wowopa Mulungu anapha achisembwere aŵiriwo. Pamenepo, mliriwo unalekeka, ndipo Mulungu analengeza kuti: “Pinehasi . . . wabweza mkwiyo wanga pa Aisrayeli; wasonyeza pakati pawo mkwiyo wansanje umodzimodzi umene unandisonkhezera, chifukwa chake mwa nsanje yanga sindinawawononge Aisrayeli.” (Numeri 25:11, The New English Bible) Ngakhale kuti mtunduwo unalanditsidwa ku chiwonongeko, Aisrayeli osachepera 23,000 anafabe. (1 Akorinto 10:8) Iwo analephera pa chiyembekezo chawo chimene anachisunga kwa nthaŵi yaitali cha kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa.
Phunziro Lochenjeza
9. Kodi nchiyani chimene chinagwera anthu a Israyeli ndi Yuda chifukwa cha kusachitira nsanje kulambira Yehova koyera?
9 Mwachisoni, Aisrayeliwo anaiŵala mwamsanga maphunziro ameneŵa. Sanachitire nsanje kulambira Yehova koyera. “Namchititsa nsanje [Mulungu] ndi mafano osema.” (Salmo 78:58) Chotulukapo nchakuti, Yehova analola mafuko khumi a Israyeli kutengedwa ukapolo ndi Aasuri mu 740 B.C.E. Ufumu wa Yuda wotsalawo wa mafuko aŵiri unakumana ndi chilango chimodzimodzi, pamene mzinda wa malikulu awo wa Yerusalemu unawonongedwa m’chaka cha 607 B.C.E. Ambiri anaphedwa, ndipo opulumuka anatengedwa ukapolo ku Babulo. Ha, ndi chitsanzo chochenjeza chotani nanga kwa Akristu onse lerolino!—1 Akorinto 10:6, 11.
10. Kodi nchiyani chidzachitika kwa olambira mafano osalapa?
10 Gawo limodzi mwa magawo atatu a chiŵerengero cha anthu pa dziko lapansi—pafupifupi 1,900 miliyoni—tsopano amati ndi Akristu. (1994 Britannica Book of the Year) Ambiri mwa ameneŵa ali m’matchalitchi amene amagwiritsira ntchito zifaniziro, mafano, ndi mitanda polambira. Yehova sanalekerere anthu ake amene anamchititsa nsanje mwa kulambira kwawo mafano. Ndipo sadzalekerera odzitcha Akristu amene amagwiritsira ntchito zinthu zina polambira. “Mulungu ndiye Mzimu; ndipo omlambira iye ayenera kumlambira mumzimu ndi m’choonadi,” anatero Yesu Kristu. (Yohane 4:24) Ndiponso, Baibulo limachenjeza Akristu kupeŵa mafano. (1 Yohane 5:21) Olambira mafano osalapa ali pakati pa awo amene sadzaloŵa Ufumu wa Mulungu.—Agalatiya 5:20, 21.
11. Kodi ndimotani mmene Mkristu angakhalire ndi liwongo la kulambira mafano popanda kugwadira fano, ndipo kodi nchiyani chimene chingathandize munthu kupeŵa kulambira mafano kotero? (Aefeso 5:5)
11 Ngakhale kuti Mkristu woona sangagwadire fano, ayenera kupeŵa chinthu chilichonse chimene Mulungu amachiona kukhala kulambira mafano, chonyansa, ndi chauchimo. Mwachitsanzo, Baibulo limachenjeza kuti: “Fetsani ziŵalozo zili padziko; dama, chidetso, chifunitso cha manyazi, chilakolako choipa, ndi chisiriro, chimene chili kupembedza mafano; chifukwa cha izi zomwe ukudza mkwiyo wa Mulungu.” (Akolose 3:5, 6) Kumvera mawu ameneŵa kumafuna kukana khalidwe losadzisungira. Zimenezi zimafuna kupeŵa zosangulutsa zodzutsa chilakolako chonyansa ndi cha chisembwere. M’malo mokhutiritsa chilakolako choterocho, Akristu oona amachitira nsanje kulambira Mulungu koyera.
Zitsanzo za Pambuyo Pake za Nsanje Yaumulungu
12, 13. Kodi ndimotani mmene Yesu anaperekera chitsanzo chapadera cha kusonyeza nsanje pa kulambira Mulungu koyera?
12 Chitsanzo chapadera koposa cha munthu amene anachitira nsanje kulambira Mulungu koyera anali Yesu Kristu. M’chaka choyamba cha utumiki wake, anaona amalonda aumbombo akumachitira malonda awo m’bwalo la kachisi. Ayuda ochokera kutali mwina ankafuna chithandizo cha osinthitsa ndalama kuti asinthitse ndalama za kwawo ndi ndalama zimene zikanaloledwa monga msonkho wa kachisi. Anayeneranso kugula nyama ndi mbalame zoperekera nsembe zofunika malinga ndi Chilamulo cha Mulungu. Malonda oterowo anayenera kuchitikira kunja kwa bwalo la kachisi. Choipa kwambiri chinali chakuti amalondawo, mwachionekere anali kudyerera pa zofunika za chipembedzo za abale awo mwa kuwalipiritsa mitengo yokwera kwambiri. Atagwidwa ndi nsanje ya kulambira Mulungu koyera, Yesu anagwiritsira ntchito mkwapulo kupitikitsa nkhosa ndi ngo’mbe. Anagubuduzanso magome a osinthitsa ndalama, akumati: “Musamayesa nyumba ya Atate wanga nyumba ya malonda.” (Yohane 2:14-16) Motero Yesu anakwaniritsa mawu a pa Salmo 69:9 akuti: “Changu [kapena, “nsanje,” Byington] cha pa nyumba yanu chandidya.”
13 Patapita zaka zitatu, Yesu anaonanso amalonda aumbombowo akuchitira malonda awo m’kachisi wa Yehova. Kodi iye anamyeretsanso kachiŵiri? Nsanje yake ya kulambira Mulungu koyera inali yamphamvube monga momwe inalili pamene anayamba utumiki wake. Anapitikitsa ogulitsa ndi ogula omwe. Ndipo anapereka chifukwa champhamvu koposerapo cha zimene anachita, akumati: “Sichilembedwa kodi, Nyumba yanga idzatchedwa nyumba yakupempheramo anthu a mitundu yonse? Koma inu mwaiyesa phanga la achifwamba.” (Marko 11:17) Ha, ndi chitsanzo chabwino chotani nanga cha kuumirira pa kusonyeza nsanje yaumulungu!
14. Kodi nsanje ya Yesu pa kulambira koyera iyenera kutiyambukira motani?
14 Umunthu wa Ambuye Yesu Kristu amene tsopano ali wolemekezeka sunasinthe. (Ahebri 13:8) M’zaka za zana la 20 lino, iye adakali wansanje ya pa kulambira koyera kwa Atate wake monga analili pamene anali pa dziko lapansi. Tikhoza kuona zimenezi m’mauthenga a Yesu ku mipingo isanu ndi iŵiri olembedwa m’buku la Chivumbulutso. Kukwaniritsidwa kwakukulu kwa mauthengaŵa kukuchitika tsopano, mu “tsiku la Ambuye.” (Chivumbulutso 1:10; 2:1–3:22) M’masomphenya, mtumwi Yohane anaona Yesu Kristu wolemekezedwayo ali ndi “maso ake ngati laŵi la moto.” (Chivumbulutso 1:14) Zimenezi zimasonyeza kuti palibe chimene Kristu samaona pamene ayendera mipingo ndi kutsimikizira kuti ikukhalabe yoyera ndi yoyenera kutumikira Yehova. Akristu amakono ayenera kukumbukira chenjezo la Yesu loletsa kutumikira ambuye aŵiri—Mulungu ndi chuma. (Mateyu 6:24) Yesu anauza ziŵalo za mpingo wa Laodikaya zokonda chumazo kuti: “Popeza uli wofunda, wosati wotentha kapena wozizira, ndidzakulavula m’kamwa mwanga. . . . Chita changu, nutembenuke mtima.” (Chivumbulutso 3:14-19) Mwa mawu ndi chitsanzo, akulu oikidwa a mpingo ayenera kuthandiza okhulupirira anzawo kupeŵa msampha wa kukonda chuma. Akulu ayeneranso kutetezera gulu la nkhosa ku makhalidwe oluluza a dzikoli lokhoterera pa chisembwere. Ndiponso, anthu a Mulungu sayenera konse kulekerera mzimu uliwonse wa Yezebeli mumpingo.—Ahebri 12:14, 15; Chivumbulutso 2:20.
15. Kodi mtumwi Paulo anatsanzira motani Yesu pa kusonyeza nsanje ya pa kulambira Yehova?
15 Mtumwi Paulo anali wotsanzira Kristu. Kuti atetezere Akristu obatizidwa chatsopano ku makhalidwe oipa, anati: “Ndichita nsanje pa inu ndi nsanje ya Mulungu.” (2 Akorinto 11:2) Izi zisanachitike, nsanje ya Paulo pa kulambira koyera inamsonkhezera kulangiza mpingo umodzimodziwu kuti uchotse wachigololo wosalapa amene anali ndi makhalidwe odetsa. Malangizo ouziridwa operekedwa pa chochitikacho akhala othandiza kwambiri kwa akulu lerolino pamene akuyesetsa kusunga mipingo ya Mboni za Yehova yoposa 75,500 kukhala yoyera.—1 Akorinto 5:1, 9-13.
Nsanje ya Mulungu Imapindulitsa Anthu Ake
16, 17. (a) Pamene Mulungu analanga Yuda wakaleyo, kodi mitundu inasonyeza mzimu wotani? (b) Pambuyo pa zaka 70 za ukapolo wa Yuda, kodi Yehova anasonyeza motani nsanje yake pa Yerusalemu?
16 Pamene Mulungu analanga anthu a Yuda mwa kuwalola kutengedwa ukapolo ku Babulo, iwo anasekedwa. (Salmo 137:3) Mwa chidani cha nsanje, Aedomu anathandizadi Ababulo kudzetsa tsoka pa anthu a Mulungu, ndipo Yehova anaona zimenezi. (Ezekieli 35:11; 36:15) Ali mu ukapolo kumeneko, opulumukawo analapa, ndipo pambuyo pa zaka 70 Yehova anawabwezeretsa ku dziko la kwawo.
17 Poyamba, anthu a Yuda anali m’vuto lothetsa nzeru. Mzinda wa Yerusalemu ndi kachisi wake zinali bwinja. Koma mitundu yozungulira inatsutsa kuyesayesa kuli konse kwa kumanganso kachisiyo. (Ezara 4:4, 23, 24) Kodi Yehova anamva motani ndi zimenezi? Cholembedwa chouziridwa chimati: “Atero Yehova wa makamu: Ndichitira nsanje Yerusalemu ndi Ziyoni ndi nsanje yaikulu. Ndipo ndikwiya nawo amitundu okhala osatekeseka ndi mkwiyo waukulu; pakuti ndinakwiya pang’ono, ndipo anathandizira choipa. Chifukwa chake atero Yehova: Ndabwera kudza ku Yerusalemu ndi zachifundo; nyumba yanga idzamangidwamo.” (Zekariya 1:14-16) Malinga ndi lonjezo limeneli, kachisiyo ndi mzinda wa Yerusalemu anamangidwanso bwino lomwe.
18. Kodi Akristu oona anakumana ndi chiyani mkati mwa nkhondo yadziko yoyamba?
18 Mpingo woona Wachikristu unakumana ndi mkhalidwe umodzimodzi m’zaka za zana la 20. Mkati mwa nkhondo yoyamba, Yehova anapereka chilango kwa anthu ake chifukwa chakuti analephera kusunga uchete wokwanira m’nkhondo yadziko imeneyo. (Yohane 17:16) Mulungu analola maulamuliro a ndale kuwapondereza, ndipo atsogoleri achipembedzo a Dziko Lachikristu anakondwa ndi tsoka limeneli. Kwenikweni, atsogoleri achipembedzo ndiwo anali kutsogolo pakusonkhezera andale kuletsa ntchito ya Ophunzira Baibulo, dzina limene Mboni za Yehova zinatchedwa nalo panthaŵiyo.—Chivumbulutso 11:7, 10.
19. Kodi Yehova wasonyeza motani nsanje pa kulambiridwa kwake chiyambire 1919?
19 Komabe, Yehova anasonyeza nsanje pa kulambiridwa kwake ndipo anabwezeretsa anthu ake olapa m’chiyanjo chake m’chaka cha 1919 pambuyo pa nkhondo. (Chivumbulutso 11:11, 12) Monga chotulukapo, chiŵerengero cha atamandi a Yehova chawonjezeka kuchokera pa ochepera pa 4,000 mu 1918 kufika pafupifupi mamiliyoni asanu lerolino. (Yesaya 60:22) Posachedwapa, Yehova adzasonyeza nsanje yake pa kulambiridwa kwake koyera m’njira zazikulu kwambiri.
Zochita Zamtsogolo za Nsanje ya Mulungu
20. Kodi Mulungu adzachitanji posachedwapa kusonyeza nsanje yake pa kulambira koyera?
20 Kwa zaka mazana ambiri, matchalitchi a Dziko Lachikristu alondola njira ya Ayuda ampatuko amene anaputa nsanje ya Yehova. (Ezekieli 8:3, 17, 18) Posachedwapa Yehova Mulungu adzachitapo kanthu mwa kuika lingaliro lalikulu m’maganizo a ziŵalo za United Nations. Chimenechi chidzasonkhezera maulamuliro andale ameneŵa kupasula Dziko Lachikristu ndi chipembedzo chonyenga chonse. (Chivumbulutso 17:16, 17) Olambira oona adzapulumuka chiweruzo chaumulungu chowopsa chimenecho. Iwo adzayankha mawu a zamoyo zakumwamba zimene zikuti: “Aleluya; . . . ndipo anaweruza mkazi wachigololo wamkulu [chipembedzo chonyenga], amene anaipsa dziko ndi chigololo chake [ziphunzitso zake zonyenga ndi kuchirikiza kwake ndale zachinyengo], ndipo anabwezera chilango mwazi wa akapolo ake pa dzanja lake la mkaziyo.”—Chivumbulutso 19:1, 2.
21. (a) Kodi Satana ndi dongosolo lake adzachitanji chitawonongedwa chipembedzo chonyenga? (b) Kodi Mulungu adzachita motani?
21 Kodi nchiyani chidzachitika pambuyo pa kuwonongedwa kwa ufumu wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga? Satana adzasonkhezera maulamuliro andale kuukira anthu a Yehova padziko lonse. Kodi Mulungu woona ameneyu adzachitaponji pamene Satana adzayesa kufafaniza kulambira koona pankhope ya dziko lapansi? Ezekieli 38:19-23 amatiuza kuti: “Ndanena [ine Yehova] mu nsanje yanga, ndi m’moto wa kuzaza kwanga, . . . Ndipo ndidzalimbana naye [Satana] ndi mliri ndi mwazi; ndipo ndidzamvumbitsira iye, ndi magulu ake, ndi mitundu yambiri ya anthu okhala naye mvumbi waukulu, ndi matalala akulu, moto ndi sulfure. Momwemo ndidzadzikuzitsa, ndi kudzizindikiritsa woyera, ndipo ndidzadziŵika pamaso pa amitundu ambiri; motero adzadziŵa kuti Ine ndine Yehova.”—Onaninso Zefaniya 1:18; 3:8.
22. Kodi tingasonyeze motani kuti tili ndi nsanje ya pa kulambira Yehova koyera?
22 Nkotonthoza mtima chotani nanga kudziŵa kuti Mfumu ya chilengedwe chonse imasamalira mwansanje alambiri ake oona! Kaamba ka chiyamikiro chathu chachikulu cha chisomo chake, tiyeni tichitire nsanje kulambira koyera kwa Yehova Mulungu. Ndi changu, tiyeni tipitirize kulalikira uthenga wabwino ndi kuyembekezera mwachidaliro tsiku lalikulu pamene Yehova adzakwezetsa ndi kuyeretsa dzina lake lalikululo.—Mateyu 24:14.
Mfundo Zofuna Kusinkhasinkha
◻ Kodi kukhala ndi nsanje ya pa Yehova kumatanthauzanji?
◻ Kodi tingaphunzirenji pa chitsanzo cha Aisrayeli akale?
◻ Kodi tingapeŵe motani kuputa nsanje ya Yehova?
◻ Kodi Mulungu ndi Kristu asonyeza motani nsanje ya pa kulambira koyera?
[Bokosi patsamba 12]
Chikondi Chilibe Nsanje
PONENA za njiru, katswiri wa Baibulo wa m’zaka za zana la 19, Albert Barnes analemba kuti: “Chili chimodzi cha zisonyezero zofala kwambiri za kuipa, ndipo chimasonyeza poyera kuipa kozama kwa munthu.” Anapitiriza kuti: “Munthu amene angakhoze kupeza chochititsa chenicheni cha nkhondo zonse ndi mikangano yonse ndi zolinga za dziko—chochititsa chenicheni cha zolingalira zonse ndi zifuno ngakhale za otchedwa Akristu, zimene zimaipitsa kwambiri chipembedzo ndi kuwachititsa kukhala ndi maganizo a dziko—angadabwe kupeza kuti chochititsa chachikulu ndicho njiru. Zimatipweteka mtima kuona kuti ena ali olemera kuposa ife; timakhumba kukhala ndi zimene ena ali nazo, ngakhale kuti sizili zathu; ndipo zimenezi zimatichititsa kutenga njira zosiyanasiyana zoipa zimene zimachepetsa kusangalala kwawo ndi zinthuzo, kapena zochititsa kuti zinthuzo zikhale zathu, kapena zosonyeza kuti saali ndi zochuluka monga momwe ambiri amaonera. . . . pakuti mwakutero mzimu wa njiru m’mitima mwathu umakhutiritsidwa.”—Aroma 1:29; Yakobo 4:5.
Mosiyana ndi zimenezo, Barnes anapereka ndemanga ina yosangalatsa ponena za chikondi, chimene “chilibe njiru.” (1 Akorinto 13:4, King James Version) Iye analemba kuti: “Chikondi sichidukidwa ndi chimwemwe cha ena; chimakondwa ndi ubwino wawo; ndipo pamene chimwemwe chawo chikula . . . aja amene chikondi chimawasonkhezera . . . samachepetsa chisangalalo cha enawo; samawachititsa manyazi chifukwa cha zimene ali nazo; samasokoneza chimwemwe chawo; samaŵiringula kapena kukhumudwa poona kuti iwo sanapeze mwaŵi waukulu wotero. . . . Ngati tikondadi ena—ngati tikondwa ndi chimwemwe chawo, sitidzawachitira njiru.”
[Chithunzi patsamba 10]
Pinehasi anali ndi nsanje ya pa kulambira Yehova koyera