Kodi Akristu Ayenera Kukhala Ansanje?
KODI nsanje ndi khalidwe limene Akristu ayenera kukhala nalo? Ife monga Akristu timalimbikitsidwa ‘kutsata chikondi,’ ndipo timauzidwa kuti “chikondi sichidukidwa [kapena kuti sichichita nsanje].” (1 Akorinto 13:4; 14:1) Komanso, timauzidwa kuti “Yehova . . . ali Mulungu wansanje” ndipo amatilamula kuti ‘tikhale akutsanza a Mulungu.’ (Eksodo 34:14; Aefeso 5:1) N’chifukwa chiyani pakuoneka kuti pali kutsutsana?
Zili choncho chifukwa chakuti mawu a Chihebri ndi Chigiriki amene anawamasulira kuti “nsanje” m’Baibulo ali ndi matanthauzo osiyanasiyana. Angakhale ndi tanthauzo la chinthu choyenera kapenanso chosayenera, malinga ndi mmene mawuwo awagwiritsira ntchito. Mwachitsanzo, liwu la Chihebri limene analimasulira kuti “nsanje” lingatanthauze “kuumirira pa kulambira kosagaŵanika; kusalola wina kuukira; changu; chikondi chachikulu; nsanje [yoyenera kapena yoipa]; njiru.” Liwu la Chigiriki la nsanje lilinso ndi matanthauzo ofanana ndi ameneŵa. Mawu ameneŵa angatanthauze kukhala ndi maganizo olakwika kwa munthu amene ukumuganizira kuti akulimbana nawe kapena amene akuganiziridwa kuti akudyerera ena masuku pamutu. (Miyambo 14:30) Mawuŵa angatanthauzenso khalidwe labwino loperekedwa ndi Mulungu, kufuna kuteteza munthu amene akumukonda kuti asavulale.—2 Akorinto 11:2.
Chitsanzo Chabwino Kwambiri
Yehova ndiye chitsanzo chabwino kwambiri posonyeza nsanje yoyenera. Zolinga zake n’zabwino, amazichita chifukwa chofuna kuteteza anthu ake ku zinthu zimene zingawavulaze mwauzimu ndiponso zimene zingaipitse makhalidwe awo. Iye, ponena za anthu ake akale amene mophiphiritsira anawatcha Ziyoni anati: “Ndim’chitira nsanje Ziyoni ndi nsanje yaikulu, ndipo ndim’chitira nsanje ndi ukali waukulu.” (Zekariya 8:2) Monga mmene tate wachikondi nthaŵi zonse amakhalira tcheru kuti ateteze ana ake ku zinthu zovulaza, Yehova ali tcheru kuti ateteze atumiki ake ku zinthu zimene zingavulaze thupi lawo ndi moyo wawo wauzimu.
Pofuna kuteteza anthu ake, Yehova anapereka Mawu ake, Baibulo. Muli mawu ambiri olimbikitsa anthu akewo kuti ayende mwanzeru, ndipo muli zitsanzo zambiri za anthu amene anachitadi zimenezo. Pa Yesaya 48:17, timaŵerenga kuti: “Ine ndine Yehova, Mulungu wako, amene ndikuphunzitsa kupindula, amene ndikutsogolera m’njira yoyenera iwe kupitamo.” N’zolimbikitsatu kudziŵa kuti nsanje yake imam’chititsa kutisamalira ndi kutiyang’anira. Akanakhala kuti alibe nsanje yabwino imeneyi, tikanavutika ndi zinthu zambiri zovulaza chifukwa cha kusadziŵa kwathu zambiri. Nsanje ya Yehova si yadyera.
Ndiyeno, kodi nsanje ya Mulungu ikusiyana bwanji ndi nsanje yosayenera? Kuti tione kusiyana kwake, tiyeni tipende chitsanzo cha Miriamu ndi cha Pinehasi. Onani zimene zinawapangitsa kuchita nsanje.
Miriamu ndi Pinehasi
Miriamu anali mlongo wamkulu wa Mose ndi Aroni, atsogoleri a Israyeli pamene mtunduwu unali paulendo. Pamene Aisrayeli anali m’chipululu, Miriamu anachitira nsanje mlongo wake, Mose. Nkhani ya m’Baibulo imati: “Ndipo Miriamu ndi Aroni anatsutsana naye Mose chifukwa cha mkazi mtundu wake Mkusi amene adam’tenga . . . Ndipo anati, Kodi Yehova wanena ndi Mose yekha? Sananenanso ndi ife nanga?” Mwachionekere, Miriamu ndi amene anayambitsa kutsutsana ndi Mose, chifukwa Yehova analanga Miriamu osati Aroni, mwa kum’chititsa khate kwa mlungu wathunthu chifukwa cha kupanda kwake ulemu.—Numeri 12:1-15.
Kodi n’chiyani chinachititsa Miriamu kutsutsana ndi Mose? Kodi anali kudera nkhaŵa kulambira koona ndi kufuna kuteteza Aisrayeli anzake ku ngozi? Ayi ndithu. Zikuoneka kuti Miriamu analola chikhumbo choipa chofuna ulemu ndi ulamuliro waukulu kukula mumtima mwake. Iye monga mneneri wamkazi mu Israyeli, anthu anali kum’lemekeza kwambiri makamaka akazi. Iye anawatsogolera poimba nyimbo pamene Aisrayeli anapulumuka mozizwitsa pa Nyanja Yofiira. Komano kenako, Miriamu ayenera kuti anayamba kuganiza molakwika kuti kutchuka kwake kudzatha chifukwa cha mkazi wa Mose amene anali kumuganizira kuti akufuna kulimbana naye. Chifukwa cha nsanje yadyera imeneyi, iye anayamba kutsutsana ndi Mose, munthu amene Yehova anamuika.—Eksodo 15:1, 20, 21.
Koma chifukwa chimene Pinehasi anachitira nsanje chinali chosiyana kwambiri. Atangotsala pang’ono kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa, pamene Aisrayeli anamanga misasa m’Chigwa cha Moabu, akazi achimoabu ndi achimidyani anakopa amuna achiisrayeli ambiri ndi kuchita nawo zachiwerewere ndiponso kulambira mafano. Pofuna kuyeretsa msasawo ndi kuimitsa mkwiyo waukulu wa Yehova, oweruza a Israyeli analamulidwa kupha amuna onse amene anapanduka. Zimri, kalonga wachisimeoni, mopanda manyazi anabweretsa Kozibi mkazi wachimidyani mumsasa “pamaso pa khamu lonse la ana a Israyeli” kuti achite naye zachiwerewere. Pinehasi anachitapo kanthu mwamsanga. Chifukwa cha nsanje, kapena changu cha kulambira Yehova ndi kufuna kuti pamsasapo pakhale chiyero, iye anapha anthu adamawo mu hema wawo. Yehova anayamikira Pinehasi chifukwa cha “mkwiyo [wake] wa nsanje,” “osalolera m’pang’ono pomwe kuukira” Yehova. Kuchitapo kanthu mwansanga kwa Pinehasi kunaimitsa mlili umene unali kulanga anthu womwe unali utapha anthu 24,000, ndipo Yehova anam’patsa mphoto mwa kupanga naye pangano lakuti unsembe udzakhalabe kwa iye ndi ana ake mpaka kalekale.—Numeri 25:4-13; The New English Bible.
Kodi nsanje ziŵiri zimenezi zinasiyana bwanji? Miriamu anatsutsana ndi mbale wake chifukwa cha nsanje yadyera pamene Pinehasi anachita chilungamo chifukwa cha nsanje ya Mulungu. Pali nthaŵi zina zimene ife, monga anachitira Pinehasi, tiyenera kuona kuti tifunika kufotokoza maganizo athu mosapita m’mbali kapena kuchitapo kanthu pofuna kuteteza dzina la Yehova, kulambira kwake ndi anthu ake.
Nsanje Yolakwika
Koma kodi n’zotheka kukhala ndi nsanje yolakwika? Inde. Ndi mmene zinalili ndi Ayuda ambiri m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino. Iwo anateteza mwansanje Chilamulo chimene Mulungu anawapatsa ndiponso miyambo yawo. Pofuna kuteteza Chilamulo, iwo anapanga malamulo ndi zoletsa zambirimbiri zimene zinali mtolo wolemera kwa anthuwo. (Mateyu 23:4) Polephera kapena posafuna kuzindikira kuti tsopano Mulungu m’malo mwa Chilamulo cha Mose waika zimene chilamulocho chinachitira chithunzi, nsanje yawo yolakwika inawachititsa kusonyeza mkwiyo wosalamulirika kwa otsatira a Yesu Kristu. Mtumwi Paulo amene nayenso poyamba anakhulupirika pochitira nsanje molakwika Chilamulo, anafotokoza kuti anthu amene anali kukhalira kumbuyo Chilamulo anali ndi “changu cha [nsanje ya] kwa Mulungu, koma si monga mwa chidziŵitso.”—Aroma 10:2; Agalatiya 1:14.
Ngakhale Ayuda ambiri amene anakhala Akristu zinawavuta kuti amasuke pa kuchitira changu Chilamulo molakwika. Paulo atamaliza ulendo wake wachitatu waumishonale, anapereka lipoti ku bungwe lolamulira la m’zaka 100 zoyambirira za Nyengo Yathu Ino za kutembenuka kwa amitundu. Panthaŵi imeneyo, Akristu achiyuda ambirimbiri anali nacho “changu onseŵa, cha pa chilamulo.” (Machitidwe 21:20) Zimenezi zinachitika patapita zaka zambiri kuchokera pamene bungwe lolamulira linalamula kuti Akristu Achikunja sanafunikire kudulidwa. Nkhani zokhudza kusunga Chilamulo zinali kuyambitsa mikangano mumpingo. (Machitidwe 15:1, 2, 28, 29; Agalatiya 4:9, 10; 5:7-12) Posamvetsa bwino mmene Yehova anali kuchitira zinthu ndi anthu ake panthaŵiyi, Akristu ena achiyuda anali kuumirira maganizo awo ndiponso kusuliza anzawo.—Akolose 2:17; Ahebri 10:1.
Ifenso tiyenera kupeŵa msampha wofuna kuteteza mwansanje maganizo kapena njira zathu zimene tikuzikonda zomwe zilibe zifukwa zokwanira za m’Mawu a Mulungu. Tiyenera kuvomereza kamvedwe katsopano koongoleredwa ka Mawu a Mulungu kamene timalandira kudzera m’njira imene Yehova akugwiritsa ntchito masiku ano.
Chitirani Nsanje Yehova
Komabe, nsanje ya Mulungu ili ndi malo ake pa kulambira koona. Ngati sitikudera nkhaŵa mosayenera za mbiri yathu kapena ufulu wathu, nsanje ya Mulungu imatichititsa kuika maganizo athu pa Yehova. Imatichititsa kufunafuna njira zosiyanasiyana zolengezera choonadi chonena za iye, kukhalira kumbuyo njira zake ndi anthu ake.
Akiko, mtumiki wamkazi wa nthaŵi zonse wa Mboni za Yehova, anakanidwa kwamtuwagalu ndi mwininyumba wina wamkazi amene anali ndi maganizo olakwika pa lamulo la Mulungu lonena za magazi. Akiko anakhalira kumbuyo Mawu a Mulungu mosamala, ndiponso anatchula mavuto a zaumoyo amene amakhalapo munthu akaikidwa magazi. Chifukwa chofunitsitsa kulankhula za Yehova, iye anasintha zokambiranazo n’kuyamba kulankhula za vuto limene anaona kuti n’limene linachititsa mkaziyo kutsutsa. Iye sanali kukhulupirira kuti kuli Mlengi. Akiko analankhula ndi mwininyumbayo mmene chilengedwe chimalimbikitsira kukhulupirira Mlengi. Kuteteza kwake Mawu a Mulungu molimba mtima kunathandiza kuthetsa maganizo olakwika ndi opanda mazikowo ndiponso anayamba kuphunzira Baibulo ndi mkaziyo panyumba pake. Lerolino mwininyumba ameneyu yemwe poyamba anali waukali tsopano ndi wotamanda Yehova.
Nsanje yoyenera, kapena kuti changu cha pa kulambira koona imatichititsa kukhala tcheru ndi kugwiritsa ntchito mipata yolankhula ndi kukhalira kumbuyo chikhulupiriro chathu kuntchito, kusukulu, kumasitolo, ndiponso poyenda ulendo. Mwachitsanzo, Midori, yemwe ndi wamkazi, amaonetsetsa kuti akuuza anthu amene amagwira nawo ntchito za chikhulupiriro chake. Wogwira naye ntchito wina wamkazi amene anali ndi zaka za m’ma 40 ananena kuti sankafuna kulankhula ndi Mboni za Yehova. Kenako, akucheza naye ulendo wina, mkaziyo anadandaula kuti mwana wake wamkazi anayamba kusonyeza makhalidwe ena oipa. Midori anamusonyeza mayiyu buku lakuti Mafunso Achichepere Akufunsa—Mayankho Amene Amathandiza,a ndipo ananena kuti angakonze zophunzira bukulo ndi mwanayo. Phunziro linayambika koma mayiyo sankakhala nawo paphunziropo. Midori anaganiza zomusonyeza mayiyo vidiyo yakuti Jehovah’s Witnesses—The Organization Behind the Name.b Zimenezi zinathetsa maganizo ambiri olakwika amene anali nawo. Chifukwa cha zimene anaona, mkaziyo anati: “Ndikufuna kukhala ngati Mboni za Yehova.” Anayamba kuphunzira Baibulo limodzi ndi mwana wakeyo.
Nsanje yoyenera ilinso ndi malo ake mumpingo wachikristu. Imalimbikitsa mtima wabwino wachikondi ndi kuderana nkhaŵa ndipo imatichititsa kupeŵa miseche ndi maganizo a mpatuko zimene zingasokoneze ndi kuwononga abale athu auzimu. Nsanje ya Mulungu imatichititsa kugwirizana ndi zimene akulu asankha kuchita, omwe nthaŵi zina amaona kuti n’koyenera kudzudzula olakwa. (1 Akorinto 5:11-13; 1 Timoteo 5:20) Polemba za nsanje yake kwa okhulupirira anzake a mumpingo wa ku Korinto, Paulo anati: “Ndichita nsanje pa inu ndi nsanje ya Mulungu; pakuti ndinakupalitsani ubwenzi mwamuna mmodzi, kuti ndikalangize inu ngati namwali woyera mtima kwa Kristu.” (2 Akorinto 11:2) Chimodzimodzinso ife, nsanje imatilimbikitsa kuchita zonse zimene tingathe kuti titeteze onse mumpingo kuti akhale oyera pankhani ya ziphunzitso, moyo wauzimu, ndiponso makhalidwe.
Inde, nsanje yoyenera—nsanje ya Mulungu—imathandiza ena. Imachititsa Yehova kutiyanja ndipo iyenera kukhala imodzi mwa makhalidwe amene Akristu ayenera kukhala nawo masiku ano.—Yohane 2:17.
[Mawu a M’munsi]
a Zofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
b Zofalitsidwa ndi Mboni za Yehova.
[Zithunzi patsamba 29]
Zimene Pinehasi anachita, anatero chifukwa cha nsanje ya Mulungu
[Zithunzi patsamba 30]
Peŵani msampha wa nsanje yolakwika
[Zithunzi patsamba 31]
Nsanje ya Mulungu imatichititsa kuuza ena chikhulupiriro chathu ndi kusamalira ubale wathu