Chilamulo cha Kristu
“Ine . . . womvera lamulo kwa Kristu.”—1 AKORINTO 9:21.
1, 2. (a) Kodi zambiri za zolakwa za anthu zikanapeŵedwa motani? (b) Kodi nchiyani chimene Dziko Lachikristu linalephera kuphunzira pa mbiri ya Chiyuda?
“ANTHU ndi maboma sanaphunzirepo kalikonse pa mbiri yakale, kapena kutsatira mapulinsipulo opezekamo.” Anatero wafilosofi wachijeremani wa m’zaka za zana la 19. Inde, njira ya mbiri ya anthu yafotokozedwa kukhala “kuguba kwa uchitsiru,” mpambo wa zolakwa zoipa ndi masoka, zimene zambiri zikanapeŵedwa ngati anthu akanangokhala okonzekera kuphunzirapo kanthu pa zolakwa zakale.
2 Kukana kuphunzirapo kanthu pa zolakwa zakale kumodzimodziko kukusonyezedwa m’nkhani ino ya malamulo aumulungu. Yehova Mulungu anachotsa Chilamulo cha Mose naikapo chabwino koposadi—chilamulo cha Kristu. Komabe, atsogoleri a Dziko Lachikristu, amene amati amaphunzitsa ndi kutsatira chilamulo chimenechi, alephera kuphunzirapo kanthu pa uchitsiru woipitsitsa wa Afarisi. Chotero Dziko Lachikristu lapotoza ndi kugwiritsira ntchito molakwa chilamulo cha Kristu monga momwedi Chiyuda chinachitira ndi Chilamulo cha Mose. Kodi zinachitika bwanji zimenezo? Choyamba, tiyeni tikambitsirane chilamulo chimenechi chokha—zimene chili, amene chimalamulira ndi mmene chimawalamulirira, ndi chimene chimachisiyanitsa ndi Chilamulo cha Mose. Ndiyeno tidzapenda mmene Dziko Lachikristu lachigwiritsirira ntchito molakwa. Motero tiphunzirepo kanthu pa mbiri ndi kupindula!
Pangano Latsopano
3. Kodi ndi lonjezo lotani limene Yehova anapanga lokhudza pangano latsopano?
3 Kodi ndani akanatha kuwongolera Chilamulo changwiro kusiyapo Yehova Mulungu? Pangano la Chilamulo cha Mose linali langwiro. (Salmo 19:7) Ngakhale zinali choncho, Yehova analonjeza kuti: “Taonani, masiku adza, . . . ndipo ndidzapangana pangano latsopano ndi nyumba ya Israyeli, ndi nyumba ya Yuda; si monga pangano limene ndinapangana ndi makolo awo.” Malamulo Khumi—maziko a Chilamulo cha Mose—analembedwa pamiyala. Koma ponena za pangano latsopano, Yehova anati: “Ndidzaika chilamulo changa mkati mwawo, ndipo m’mtima mwawo ndidzachilemba.”—Yeremiya 31:31-34.
4. (a) Kodi ndi Israyeli uti amene ali m’pangano latsopano? (b) Kodi ndaninso pambali pa Aisrayeli auzimu amene ali pansi pa chilamulo cha Kristu?
4 Kodi ndani amene akanaloŵetsedwa m’pangano latsopano limeneli? Osati “nyumba ya Israyeli” ayi, imene inakana Nkhoswe ya pangano limeneli. (Ahebri 9:15) M’malo mwake, “Israyeli” watsopano ameneyu anadzakhala “Israyeli wa Mulungu,” mtundu wa Aisrayeli auzimu. (Agalatiya 6:16; Aroma 2:28, 29) Pambuyo pake, kagulu kakang’ono kameneka kodzozedwa ka Akristu kanali kudzagwirizana ndi “khamu lalikulu” lochokera m’mitundu yonse amenenso adzafuna kulambira Yehova. (Chivumbulutso 7:9, 10; Zekariya 8:23) Ngakhale kuti saali mbali ya pangano latsopano, ameneŵanso adzafunikira kumvera lamulo. (Yerekezerani ndi Levitiko 24:22; Numeri 15:15.) Monga “gulu limodzi” pansi pa “mbusa mmodzi,” onse adzakhala “omvera lamulo kwa Kristu,” monga momwe mtumwi Paulo analembera. (Yohane 10:16; 1 Akorinto 9:21) Paulo anatcha pangano latsopano limeneli “pangano labwino loposa.” Chifukwa ninji? Makamaka, ilo lazikidwa pa malonjezo okwaniritsidwa osati pa mthunzi wa zinthu zilinkudza.—Ahebri 8:6; 9:11-14.
5. Kodi chifuno cha pangano latsopano nchiyani, ndipo nchifukwa ninji chidzapambana?
5 Kodi chifuno cha pangano limeneli nchiyani? Ndicho kutulutsa mtundu wa mafumu ndi ansembe odalitsa anthu onse. (Eksodo 19:6; 1 Petro 2:9; Chivumbulutso 5:10) Pangano la Chilamulo cha Mose silinatulutse konse mtundu umenewu m’lingaliro lake lokwanira, pakuti Israyeli yense anapanduka nataya mwaŵi wake. (Yerekezerani ndi Aroma 11:17-21.) Komabe, pangano latsopano lidzapambanatu, pakuti lili logwirizana ndi chilamulo chosiyana kwambiri. Chosiyana m’njira zotani?
Lamulo Laufulu
6, 7. Kodi chilamulo cha Kristu chimapatsa motani ufulu wochuluka kuposa umene Chilamulo cha Mose chinapatsa?
6 Chilamulo cha Kristu mobwerezabwereza chimagwirizanitsidwa ndi ufulu. (Yohane 8:31, 32) Chimatchedwa “lamulo la [anthu a, NW] ufulu” ndi ‘lamulo langwiro, laufulu.’ (Yakobo 1:25; 2:12) Inde, ufulu wonse wa anthu uli ndi malire. Chikhalirechobe, chilamulo chimenechi chimapatsa ufulu woposeratu uja wa choyambirira, Chilamulo cha Mose. Motani?
7 Choyamba, palibe amene amabadwira m’chilamulo cha Kristu. Zinthu zonga fuko ndi malo obadwirako zilibe kanthu. Akristu oona amasankha mwaufulu m’mitima mwawo kulandira goli la kumvera chilamulochi. Mwa kutero, amapeza kuti lili goli lofeŵa, katundu wopepuka. (Mateyu 11:28-30) Ndi iko komwe, Chilamulo cha Mose chinalinganizidwanso kumphunzitsa munthu kuti ali wochimwa ndi kuti amafunikira kwambiri nsembe ya dipo kuti imuwombole. (Agalatiya 3:19) Chilamulo cha Kristu chimaphunzitsa kuti Mesiya anabwera, anapereka mtengo wa dipo ndi moyo wake, natitsegulira njira kuti timasulidwe ku chitsenderezo cha uchimo ndi imfa! (Aroma 5:20, 21) Kuti tipindule, tifunikira ‘kukhulupirira’ m’nsembe imeneyo.—Yohane 3:16.
8. Kodi chilamulo cha Kristu chimaphatikizapo chiyani, koma kodi nchifukwa ninji kuchitsatira sikumafuna kuloŵeza pamtima malamulo mazana ambiri?
8 ‘Kukhulupirira’ kumaphatikizapo kutsatira chilamulo cha Kristu. Zimenezo zimaphatikizapo kumvera malamulo onse a Kristu. Kodi zimenezi zikutanthauza kuwaloŵeza pamtima malamulo mazana ambiri? Ayi. Pamene kuli kwakuti Mose, nkhoswe ya pangano lakale, analemba Chilamulo cha Mose, Yesu, Nkhoswe ya pangano latsopano, sanalembepo lamulo ngakhale limodzi. M’malo mwake, anatsatira chilamulo chimenechi. Mwa njira ya moyo wake wangwiro, anapereka chitsanzo kuti onse achitsatire. (1 Petro 2:21) Mwinamwake nchifukwa chake kulambira kwa Akristu oyambirira kunatchedwa “Njira.” (Machitidwe 9:2; 19:9, 23; 22:4; 24:22) Kwa iwo, chilamulo cha Kristu chinasonyezedwa m’moyo wa Kristu. Kutsanzira Yesu kunali kumvera chilamulo chimenechi. Kumkonda kwawo kwambiri kunatanthauza kuti chilamulo chimenechi chinali cholembedwadi m’mitima mwawo, malinga ndi ulosi. (Yeremiya 31:33; 1 Petro 4:8) Ndipo munthu amene amamvera chifukwa cha chikondi samamva kuponderezedwa—chifukwa chinanso chimene chilamulo cha Kristu chingatchedwere “lamulo la anthu aufulu.”
9. Kodi mzimu weniweni wa chilamulo cha Kristu nchiyani, ndipo kodi chilamulo chimenechi chimaphatikizapo motani lamulo latsopano?
9 Ngati chikondi chinali chofunika m’Chilamulo cha Mose, ndicho mzimu weniweni wa chilamulo chachikristu. Chotero chilamulo cha Kristu chimaphatikizapo lamulo latsopano—Akristu ayenera kukhala ndi chikondi chodzimana kwa wina ndi mnzake. Ayenera kukonda monga momwe Yesu anakondera; iye mwaufulu anapereka moyo wake chifukwa cha mabwenzi ake. (Yohane 13:34, 35; 15:13) Chotero kunganenedwe kuti chilamulo cha Kristu ndicho chisonyezero chopambana cha teokrase kuposa Chilamulo cha Mose. Monga momwe magazini ano anenera kumbuyoku: “Teokrase ndi ulamuliro wa Mulungu; Mulungu ndiye chikondi; chotero teokrase ndi ulamuliro wa chikondi.”
Yesu ndi Afarisi
10. Kodi chiphunzitso cha Yesu chinasiyana motani ndi cha Afarisi?
10 Pamenepa, nkosadabwitsa konse kuti Yesu analimbana ndi atsogoleri achipembedzo achiyuda a m’tsiku lake. ‘Lamulo langwiro, laufulu’ silinali konse m’maganizo a alembi ndi Afarisi. Iwo anayesa kulamulira anthu ndi malamulo opangidwa ndi anthu. Chiphunzitso chawo chinakhala chotsendereza, chotsutsa, choipa. Mosiyana kwambiri ndi zimenezo, chiphunzitso cha Yesu chinali chomangirira kwambiri ndiponso chabwino! Iye anali wothandiza ndipo anasamalira zosoŵa zenizeni ndi nkhaŵa za anthu. Anaphunzitsa mosavuta ndipo ndi chifundo chenicheni, akumagwiritsira ntchito mafanizo otengedwa pa moyo wa masiku onse ndi kugwiritsira ntchito ukumu wa Mawu a Mulungu. Chifukwa chake, “makamu a anthu anazizwa ndi chiphunzitso chake.” (Mateyu 7:28) Inde, chiphunzitso cha Yesu chinafika mitima yawo!
11. Kodi Yesu anasonyeza motani kuti Chilamulo cha Mose chikanagwiritsiridwa ntchito mololera ndi mwachifundo?
11 M’malo mowonjezera malamulo enanso ambiri ku Chilamulo cha Mose, Yesu anasonyeza mmene Ayuda akanafunikira kumagwiritsira ntchito Chilamulocho nthaŵi zonse—mololera ndi mwachifundo. Mwachitsanzo, kumbukirani nthaŵi pamene mkazi wodwala nthenda ya kukha mwazi anafika kwa iye. Malinga ndi kunena kwa Chilamulo cha Mose, aliyense womkhudza anali kukhala wodetsedwa, chotero mkaziyo sanafunikire nkomwe kukhala pa khamu la anthu! (Levitiko 15:25-27) Koma iyeyo analakalaka kwambiri kuchiritsidwa kwakuti anayenda m’khamulo nakhudza chovala cha Yesu. Mwaziwo unaleka kukha nthaŵi yomweyo. Kodi iye anamdzudzula chifukwa cha kuswa Chilamulo? Iyayi; m’malo mwake, iye anazindikira mkhalidwe wosautsa wa mkaziyo nasonyeza mfundo yaikulu koposa ya Chilamulo—chikondi. Mwachifundo anauza mkaziyo kuti: “Mwana wamkaziwe, chikhulupiriro chako chakupulumutsa; muka mumtendere, nukhale wochira chivutiko chako.”—Marko 5:25-34.
Kodi Chilamulo cha Kristu Chimalekerera Zinthu?
12. (a) Kodi nchifukwa ninji sitiyenera kuganiza kuti Kristu amalekerera zinthu? (b) Kodi nchiyani chikusonyeza kuti kupanga malamulo ambiri kumachititsa kupangidwa kwa njira zambiri zowazembera?
12 Kodi pamenepa tiyenera kuganiza kuti chifukwa chakuti chilamulo cha Kristu ‘nchaufulu,’ ndiye kuti chimalekerera zinthu, pamene kuli kwakuti Afarisi, ndi miyambo yawo yonse ya pakamwa, anakhoza kuchititsa khalidwe la anthu kusapambana malire? Iyayi. Mitundu ya malamulo a boma lerolino imasonyeza kuti nthaŵi zambiri ngati pali malamulo ambiri, anthu amapeza njira zambiri zowazembera.a M’tsiku la Yesu kuchuluka kwa malamulo a Afarisi kunalimbikitsa anthu kufunafuna njira zowazembera, kuchita ntchito zachiphamaso zopanda chikondi, ndi kudzionetsera ngati olungama kunja, kubisa kuipa kwa mkati.—Mateyu 23:23, 24.
13. Kodi nchifukwa ninji chilamulo cha Kristu chimatulutsa muyezo wopambana wa khalidwe kuposa malamulo alionse olembedwa?
13 Chilamulo cha Kristu, mosiyana ndi zimenezo, sichimalimbikitsa mzimu wotero. Kunena zoona, kumvera lamulo lozikidwa pa chikondi cha Yehova ndiponso limene limamvedwa mwa kutsanzira chikondi chodzimana cha Kristu kwa ena kumachititsa munthu kukhala ndi muyezo wopambana wa khalidwe kuposa kutsatira mpambo wa malamulo olembedwa. Chikondi sichimafunafuna njira zozembera; chimatiletsa kuchita zinthu zoipa zimene mwina mpambo wa malamulo sungaletse kwenikweni. (Onani Mateyu 5:27, 28.) Motero, chilamulo cha Kristu chimatisonkhezera kuchitira ena zinthu—kukhala woolowa manja, kuchereza alendo, ndi kusonyeza chikondi—mwa njira imene lamulo lolembedwa lililonse silingachitire.—Machitidwe 20:35; 2 Akorinto 9:7; Ahebri 13:16.
14. Kodi chinatulukapo nchiyani pamene mpingo wachikristu wa m’zaka za zana loyamba unatsatira chilamulo cha Kristu?
14 Pamene ziŵalo zake zinatsatira chilamulo cha Kristu, mpingo woyambirira wachikristu unakhala ndi mkhalidwe wabwino, wachikondi, wopanda mzimu waliuma ndi wokonda kuweruza ena, ndi wachinyengo wofala kwambiri m’masunagoge apanthaŵiyo. Anthu a m’mipingo yatsopanoyo ayenera kuti anaonadi kuti anali kutsatira “lamulo la anthu aufulu”!
15. Kodi zina za zoyesayesa zoyambirira za Satana za kuipitsa mpingo wachikristu zinali zotani?
15 Komabe, Satana anali kulakalaka kuipitsa mpingo wachikristu kuchokera mkati mwake, monga momwe anaipitsira mtundu wa Israyeli. Mtumwi Paulo anachenjeza za anthu onga mimbulu amene ‘adzalankhula zokhotakhota’ ndi kusautsa gulu la Mulungu. (Machitidwe 20:29, 30) Anachita kulimbana ndi Ayuda Osunga Mwambo, amene anafuna kusinthanitsa ufulu wokhala ndi malire wa chilamulo cha Kristu ndi ukapolo wa Chilamulo cha Mose, chimene chinali chitakwaniritsidwa mwa Kristu. (Mateyu 5:17; Machitidwe 15:1; Aroma 10:4) Atamwalira womaliza wa atumwi, panalibenso choletsa mpatuko umenewo. Chotero kuipa kunafalikira.—2 Atesalonika 2:6, 7.
Dziko Lachikristu Liipitsa Chilamulo cha Kristu
16, 17. (a) Kodi kuipitsako kunakhala kwa mitundu yotani m’Dziko Lachikristu? (b) Kodi ndi motani mmene malamulo a Tchalitchi cha Katolika anachirikizira lingaliro lopotoka la kugonana?
16 Mofanana ndi Chiyuda, kuipa m’Dziko Lachikristu kunali ndi mitundu yosiyanasiyana. Nalonso linaloŵereredwa ndi ziphunzitso zonama ndi makhalidwe osadziletsa. Ndipo kuyesayesa kwake kutetezera nkhosa zake ku chisonkhezero chakunja nthaŵi zambiri kunawononga mbali zilizonse zotsala za kulambira koyera. Malamulo ouma ndi osakhala amalemba anachuluka.
17 Tchalitchi cha Katolika chakhala patsogolo kupanga malamulo a tchalitchi ambirimbiri. Malamulo ameneŵa anali opotoka kwambiri ponena za kugonana. Malinga ndi kunena kwa buku lakuti Sexuality and Catholicism, tchalitchi chinalandira filosofi yachigiriki ya Chistoiki, chimene chinakayikira zokondweretsa za mtundu uliwonse. Tchalitchi chinayamba kuphunzitsa kuti chisangalalo chonse cha kugonana, kuphatikizapo chija choyenera cha muukwati, chinali choipa. (Siyanitsani ndi Miyambo 5:18, 19.) Anati ntchito ya kugonana inali kubala ana basi, osati kupatsa chisangalalo. Chifukwa chake lamulo la tchalitchi linanena kuti njira ya mtundu uliwonse yoletsa kubala inali tchimo lalikulu, limene nthaŵi zina linafuna kudzilanga zaka zambiri. Ndiponso, ansembe anawaletsa kukwatira, lamulo limene lachititsa kugonana kochuluka kosaloledwa, kuphatikizapo kugona ana.—1 Timoteo 4:1-3.
18. Kodi chinatulukapo nchiyani chifukwa cha kuchuluka kwa malamulo a tchalitchi?
18 Pamene malamulo a tchalitchi anachuluka, anakonzedwa kukhala mabuku. Ameneŵa m’kupita kwa nthaŵi anayamba kuphimba Baibulo ndi kuloŵa m’malo mwake. (Yerekezerani ndi Mateyu 15:3, 9.) Monga Chiyuda, Chikatolika sichinakhulupirire zolemba zakudziko ndipo chinaona zambiri za izo kukhala zangozi. Lingaliro limeneli posapita nthaŵi linapitirira ndi chenjezo lanzeru la Baibulo pankhaniyi. (Mlaliki 12:12; Akolose 2:8) Jerome, wolemba za tchalitchi wa m’zaka za zana lachinayi C.E., anati: “O Ambuye, ndikakhalanso ndi mabuku akudziko kapena kuwaŵerenga, ndiye kuti ndakukanani.” M’kupita kwa nthaŵi, tchalitchi chinayamba kulamulira zolemba m’mabuku—ngakhale aja a nkhani za dziko. Chotero wopenda zakuthambo wa m’zaka za zana la 17 Galileo anadzudzulidwa chifukwa cha kulemba kuti dziko lapansi limazungulira dzuŵa. Kuumirira kwa tchalitchi kunena kuti ndicho chinali ndi ulamuliro wonse pa kalikonse—ngakhale pankhani yopenda zakuthambo—m’kupita kwa nthaŵi kunadzachepetsa chikhulupiriro m’Baibulo.
19. Kodi ndi motani mmene nyumba za amonke zinachirikizira malamulo otsendereza?
19 Kupanga malamulo kwa tchalitchi kunafala m’nyumba za amonke, kumene amonke anadzilekanitsa ndi dzikoli akumadzikana. Nyumba zambiri za amonke zachikatolika zinatsatira “Malamulo a St. Benedict.” Abbot (liwu lotengedwa ku liwu lachiaramaiki la “atate”) anali ndi ulamuliro wonse. (Yerekezerani ndi Mateyu 23:9.) Ngati mmonke analandira mphatso kwa makolo ake, abbot ndiye anali kusankha ngati mmonkeyo kapena wina adzailandira. Kuwonjezera pa kutsutsa zamwano, lamulo lina linaletsa manenanena ndi njerengo, likumati: “Wophunzira aliyense asamalankhule zotero.”
20. Kodi nchiyani chimene chikusonyeza kuti Chiprotesitanti nachonso chinakangalika kuchirikiza malamulo otsendereza?
20 Chiprotesitanti, chimene chinafuna kusintha zinthu zomkitsa za Chikatolika zosakhala zamalemba, posapita nthaŵi chinakhala chokangalika mofananamo kupanga malamulo otsendereza osazikidwa pa chilamulo cha Kristu. Mwachitsanzo, wotsogolera pa kusintha kumeneko, John Calvin, anatchedwa “wopanga malamulo wa Tchalitchi chokonzedwanso.” Analamulira Geneva ndi malamulo ochuluka ovuta osungitsidwa ndi “Akulu” amene “udindo” wawo, anatero Calvin, “ndiwo kuyang’anira moyo wa aliyense.” (Siyanitsani ndi 2 Akorinto 1:24.) Tchalitchi chinayang’anira nyumba za alendo ndi kusankha nkhani zimene zinali zololeka kukamba. Zilango zankhanza zinaperekedwa kaamba ka zolakwa zonga kuimba nyimbo zachabe kapena kuvina.b
Kuphunzirapo Kanthu pa Zolakwa za Dziko Lachikristu
21. Kodi zotulukapo zonse za mzimu wa Dziko Lachikristu wa ‘kupitirira zimene zinalembedwa’ nzotani?
21 Kodi malamulo onse ameneŵa athandiza kutetezera Dziko Lachikristu kuti lisaipe? Kutalitali! Lerolino Dziko Lachikristu lagaŵanika kukhala mipatuko mazana ambiri, kuyambira youmitsa zinthu kwambiri mpaka yolekerera zinthu kowopsa. Yonseyo, mwa njira ina yake, ‘yapitirira zimene zinalembedwa,’ ikumalola malingaliro a anthu kulamulira gulu la nkhosa ndi kusokoneza chilamulo chaumulungu.—1 Akorinto 4:6.
22. Kodi nchifukwa ninji kupanduka kwa Dziko Lachikristu sikunatanthauze mapeto a chilamulo cha Kristu?
22 Komabe, mbiri ya chilamulo cha Kristu siili yatsoka. Yehova Mulungu sadzalola anthu wamba kufafaniza chilamulo chaumulungu. Chilamulo chachikristu chikugwirabe ntchito lerolino pakati pa Akristu oona, ndipo ameneŵa ali ndi mwaŵi waukulu wakuchitsatira. Koma pambuyo pa kupenda zimene Chiyuda ndi Dziko Lachikristu zachita ndi chilamulo chaumulungu, moyenerera tingafunse kuti, ‘Kodi tingachitsatire bwanji chilamulo cha Kristu pamenenso tikupeŵa msampha wa kuipitsa Mawu a Mulungu ndi malingaliro a anthu ndi malamulo amene amaluluza mzimu weniweni wa chilamulo chaumulungu? Kodi ndi lingaliro loyenera liti limene chilamulo cha Kristu chiyenera kutipatsa lerolino?’ Nkhani yotsatira idzayankha mafunso ameneŵa.
[Mawu a M’munsi]
a Afarisi kwenikweni ndiwo anali ndi thayo la kuyambitsa mtundu wa Chiyuda chimene chiliko lerolino, chotero nkosadabwitsa kuti Chiyuda chimafunabe njira zozembera ziletso zake za Sabata zambiri zowonjezedwa. Mwachitsanzo, mlendo ku chipatala cha Ayuda amwambo pa Sabata angapeze kuti chikepe chimaima chokha pamalo alionse kuti okweramo asachite “ntchito” yauchimo ya kusinika batani ya chikepe. Madokotala ena achiyuda amalemba mapepala otengerapo mankhwala ndi inki imene imazimirira pambuyo pa masiku angapo. Chifukwa ninji? Mishnah imati kulemba ndi “ntchito,” koma imamasulira kuti “kulemba” ndiko kusiya chilembo chachikhalire.
b Servetus, amene anatsutsa ena a malingaliro a zaumulungu a Calvin, anatenthedwa pamtengo monga wampatuko.
Kodi Mungayankhe Motani?
◻ Kodi mzimu weniweni wa chilamulo cha Kristu nchiyani?
◻ Kodi kaphunzitsidwe ka Yesu kanasiyana motani ndi ka Afarisi?
◻ Kodi ndi motani mmene Satana anagwiritsirira ntchito mzimu wopanga malamulo mwaliuma kuipitsira Dziko Lachikristu?
◻ Kodi zina za zotulukapo zabwino za kutsatira chilamulo cha Kristu nzotani?
[Chithunzi patsamba 16]
Yesu anagwiritsira ntchito Chilamulo cha Mose mololera ndi mwachifundo