Nkumpatsiranji Yehova?
PAMENE dzuŵa linali kutentha m’tauni yaing’ono ya Zarefati wa ku Zidoni, mkazi wamasiye anaŵerama kuti atole nkhuni. Anafuna kukoleza moto wakuti aphikepo chakudya chochepa—mwinamwake chinali chakudya chomaliza chimene iye ndi mwana wake wamwamuna anati adye. Anali atayesetsa kudzisunga wamoyo pamodzi ndi mwana wake m’nyengo yonse yaitali ya chirala ndi ya njala, ndipo zinthu zinafika pamkhalidwe woipa umenewu. Iwo anali kufa ndi njala.
Panafika mwamuna wina. Dzina lake anali Eliya, ndipo posapita nthaŵi mkazi wamasiyeyo anaona kuti iyeyo anali mneneri wa Yehova. Zikuoneka kuti iye anali atamvapo za Mulungu ameneyu. Yehova anali wosiyana ndi Baala, amene kulambira kwake koipa kwankhanza kunali kofala m’dziko la mkaziyo la Zidoni. Chotero pamene Eliya anampempha madzi akumwa, iye anafunitsitsa kumthandiza. Mwinamwake anaganiza kuti mwakuchita zimenezo akanapeza chiyanjo cha Yehova. (Mateyu 10:41, 42) Komano Eliya anapemphanso zina—chakudya pang’ono. Mkaziyo anafotokoza kuti anali chabe ndi chakudya chomaliza chokwanira. Komabe, Eliya analimbikira, akumamtsimikiza kuti Yehova adzampatsa chakudya mozizwitsa kufikira chirala chitatha. Kodi mkaziyo anatani? Baibulo limati: “Ndipo iye anakachita monga mwa mawu a Eliya.” (1 Mafumu 17:10-15) Mawu osavuta kumva ameneŵa amafotokoza mchitidwe wa chikhulupiriro chachikulu—kwenikweni, chachikulu kwambiri kwakuti Yesu Kristu anatamanda mkazi wamasiye ameneyo patapita zaka pafupifupi chikwi chimodzi!—Luka 4:25, 26.
Ngakhale zili choncho, zingaoneke kukhala zachilendo kuti Yehova anafuna zochuluka kwambiri kwa mkazi amene anali ndi zochepa kwambiri. Zimenezi zili choncho makamaka pamene tilingalira za pemphero limene linaperekedwapo ndi mwamuna wina wotchuka. Kusonkhanitsa kwa Mfumu Davide zopereka za mwana wake Solomo zogwiritsira ntchito pomanga kachisi kunasonkhezera kuoloŵa manja kwakukulu. Malinga ndi mitengo yamakono, mphatso zoperekedwazo zinakwanira madola mabiliyoni ambiri! Koma Davide anati m’pemphero kwa Yehova: “Ndine yani, ndi anthu anga ndiwo ayani, kuti tidzakhoza kupereka mwaufulu motere? Popeza zonsezi zifuma kwanu; takupatsani zofuma ku dzanja lanu.” (1 Mbiri 29:14) Malinga ndi kunena kwa Davide, zonse nza Yehova. Chotero chilichonse chimene timapereka kuti tipititse patsogolo kulambira koyera, timakhala tikumbwezera zake Yehova. (Salmo 50:10) Chifukwa chake, pakubuka funso lakuti, Kodi nchifukwa ninji Yehova amafunadi kuti tizipatsa?
Mbali Yofunika Kwambiri pa Kulambira Koona
Yankho lapafupi nlakuti kuyambira kale Yehova wapanga kupatsa kukhala mbali yofunika kwambiri ya kulambira koyera. Mwamuna wokhulupirika Abele anapereka nsembe kwa Yehova zina za zifuyo zake za mtengo wapatali. Makolowo Nowa, Abrahamu, Isake, Yakobo, ndi Yobu anapereka nsembe zofanana nayo.—Genesis 4:4; 8:20; 12:7; 26:25; 31:54; Yobu 1:5.
Chilamulo cha Mose chinalamula kuti mphatso ziperekedwe kwa Yehova ndiponso chinapereka malangizo ake. Mwachitsanzo, Aisrayeli onse analamulidwa kupereka chachikhumi, kapena kupereka limodzi la magawo khumi la mbewu ndi la chiwonjezeko cha zoŵeta zawo. (Numeri 18:25-28) Zopereka zina zinalibe malamulo amphamvu chotero. Mwachitsanzo, Mwisrayeli aliyense anafunikira kupatsa Yehova zoyamba za zoŵeta zake ndi za mbewu zake. (Eksodo 22:29, 30; 23:19) Komabe, Chilamulo chinalola munthu aliyense kusankha unyinji wa zoyamba zake zimene akanapereka, malinga ngati anapereka zabwino koposa. Chilamulo chinafunanso nsembe za chiyamiko ndi za choŵinda, zimene zinali zaufulu kotheratu. (Levitiko 7:15, 16) Yehova analimbikitsa anthu ake kupatsa monga mwa dalitso limene anawapatsa. (Deuteronomo 16:17) Monga momwe zinalili pomanga chihema ndi kachisi pambuyo pake, aliyense anapereka zimene mtima wake unamfulumiza kupereka. (Eksodo 35:21; 1 Mbiri 29:9) Ndithudi zopereka zaufulu zotero zinamkondweretsa koposa Yehova!
Mu “chilamulo cha Kristu,” kupatsa konse kunayenera kukhala kwaufulu. (Agalatiya 6:2; 2 Akorinto 9:7) Zimenezo sizinatanthauze kuti otsatira a Kristu anasiya kupatsa kapena kuti anapatsa zochepa. Ayi! Pamene Yesu ndi ophunzira ake analalikira mu Israyeli, kagulu ka akazi kanawatsata ndi kuwatumikira ndi chuma chawo. (Luka 8:1-3) Momwemonso mtumwi Paulo analandira mphatso zimene zinamthandiza pa ntchito yake yaumishonale, ndipo nayenso analimbikitsa mipingo ina kupereka ndalama kwa ena osoŵa. (2 Akorinto 8:14; Afilipi 1:3-5) Bungwe lolamulira ku Yerusalemu linaika amuna athayo kuti atsimikizire kuti chuma choperekedwa chinagaŵiridwa kwa osoŵa. (Machitidwe 6:2-4) Mwachionekere, Akristu oyambirira anauyesa mwaŵi kuchirikiza kulambira koyera mwanjira zimenezo.
Chikhalirechobe, tingafunebe kudziŵa chifukwa chake Yehova amapanga kupatsa kukhala mbali ya kulambira kwake. Talingalirani zifukwa zinayi.
Chimene Timapatsira
Choyamba, Yehova amapanga kupatsa kukhala mbali ya kulambira koona chifukwa kuchita motero nkwabwino kwa ife. Kumasonyeza chiyamikiro chathu kaamba ka ubwino wa Mulungu. Mwachitsanzo, ngati mwana agulira kholo lake kapena kulipangira mphatso, nchifukwa ninji khololo limakondwera? Kodi mphatsoyo imakwaniritsa chosoŵa china chimene khololo silikanapeza mwanjira ina? Mwinamwake ayi. M’malo mwake, khololo limakondwera kuona mwanayo akukhala ndi mzimu woyamikira ndi wopatsa. Pazifukwa zofananazo Yehova amatilimbikitsa kupatsa ndipo amakondwera pamene titero. Ndi mmene timamsonyezera kuti timayamikiradi kukoma mtima kwake kochuluka ndi kuoloŵa manja kwake kwa ife. Iye ndiye mpatsi wa “mphatso iliyonse yabwino, ndi chininkho chilichonse changwiro,” chotero sitidzasoŵa konse zifukwa zomyamikirira. (Yakobo 1:17) Koposa zonse, Yehova anapereka Mwana wake wokondedwa, kumlola kufa kuti tikhale ndi moyo kosatha. (Yohane 3:16) Kodi tingamthokozenso motani?
Chachiŵiri, ngati tikhala ndi chizoloŵezi cha kupatsa, timaphunzira kutsanzira Yehova ndi Mwana wake, Yesu Kristu, m’mbali yofunika koposa. Yehova samasiya kupatsa, ngwooloŵa manja nthaŵi zonse. Monga momwe Baibulo limanenera, amatipatsa “moyo ndi mpweya ndi zinthu zonse.” (Machitidwe 17:25) Moyenerera tingamthokoze kaamba ka mpweya wonse umene timapuma, chakudya chilichonse chomwe timadya, nthaŵi iliyonse yosangalatsa ndi yokhutiritsa m’moyo. (Machitidwe 14:17) Yesu, monga Atate wake, anasonyeza mzimu wopatsa. Anadzipereka ndi mtima wonse. Kodi mukudziŵa kuti pamene Yesu anachita zozizwitsa, anatero mwa kutaya kanthu kena? Nthaŵi zingapo Malemba amatiuza kuti pamene anachiritsa anthu odwala, mphamvu ‘inatuluka mwa iye.’ (Luka 6:19; 8:45, 46) Yesu anali wooloŵa manja kwambiri kwakuti anathira sou yake, moyo wake, kuimfa.—Yesaya 53:12.
Chotero pamene tipatsa, kaya ndi nthaŵi yathu, nyonga yathu, kapena chuma chathu, timatsanza Yehova ndi kukondweretsa mtima wake. (Miyambo 27:11; Aefeso 5:1) Timatsatiranso chitsanzo changwiro cha khalidwe laumunthu chimene Yesu Kristu anatisiyira.—1 Petro 2:21.
Chachitatu, kupatsa kumakwaniritsa zosoŵa zenizeni ndiponso zofunika. Zoonadi, Yehova akhoza kukwaniritsa zosoŵa pa zinthu za Ufumu popanda thandizo lathu, monga momwe angalinganizire kuti miyala ifuule m’malo mwa kutigwiritsira ntchito kulalikira mawu. (Luka 19:40) Koma wasankha kutilemekeza mwa kutipatsa mwaŵi umenewu. Chotero pamene tipereka chuma chathu kuchirikiza zinthu za Ufumu, timapeza chikhutiro chachikulu podziŵa kuti tikuchita mbali yaikuludi m’ntchito yofunika koposa imene ikuchitika m’dzikoli.—Mateyu 24:14.
Sipafunikira kuchita kunena kuti ndalama zikufunika zolipirira ntchito ya padziko lonse ya Mboni za Yehova. M’chaka chautumiki cha 1995, Sosaite inawononga pafupifupi $60 miliyoni posamalira chabe apainiya apadera, amishonale, ndi oyang’anira oyendayenda m’magawo awo a utumiki wakumunda. Komabe, zimenezo ndi ndalama zazing’ono poziyerekezera ndi zolipirira ntchito yomanga ndi ya maofesi anthambi ndi malo osindikizira kuzungulira dziko lonse. Komabe, zonsezo zikutheka ndi zopereka zaufulu!
Anthu a Yehova samangoganiza kuti ngati ali osauka, angangosiyira ena kuti asenze mtolowo. Maganizo otero angatiphonyetse mbali imeneyi ya kulambira kwathu. Malinga ndi kunena kwa mtumwi Paulo, Akristu ku Makedoniya anali ‘osauka kwenikweni.’ Komabe, iwo anaumirira mwaŵi wa kupatsa. Ndipo zimene anapereka, Paulo anachitira umboni, zinali ‘zoposa mphamvu yawo’!—2 Akorinto 8:1-4.
Chachinayi, Yehova wapanga kupatsa kukhala mbali ya kulambira koona chifukwa kupatsa kudzatithandiza kukhala achimwemwe. Yesu mwiniyo anati: “Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.” (Machitidwe 20:35) Ndi mmene Yehova anatilengera. Ndicho chifukwa chinanso chimene mwina tingaganizire kuti kaya zimene timampatsa zichuluke motani, sizingathe kukhala zolingana ndi chiyamikiro chodzala m’mitima yathu. Komabe, chosangalatsa nchakuti Yehova samayembekezera kulandira zoposa zimene tingampatse. Tingakhale ndi chidaliro chakuti iye amakondwa pamene mwachimwemwe timpatsa zimene tingathe!—2 Akorinto 8:12; 9:7.
Madalitso Amadza Chifukwa cha Kusonyeza Mzimu Wopatsa
Titabwerera ku chitsanzo chathu choyamba chija, tayerekezerani kuti mkazi wamasiye uja wa ku Zarefati anangopondereza nkhaniyi ndi kuti munthu wina akanathetsa njala ya chakudya ya Eliya. Akanaphonya dalitso lalikulu chotani nanga!
Mosakayikira Yehova amadalitsa awo amene amasonyeza mzimu wopatsa. (Miyambo 11:25) Mkazi wamasiye wa ku Zarefati sanafunikire kuvutika chifukwa cha kupatsa wina chakudya chake chimene anaganiza kuti chinali chomaliza. Yehova anamfupa ndi chozizwitsa. Malinga ndi lonjezo la Eliya, ufa ndi mafuta sizinathe m’zotengera zake kufikira chirala chitapita. Koma analandiranso mfupo yaikulu kwambiri. Pamene mwana wake anadwala ndi kufa, Eliya, munthu wa Mulungu woona, anamuukitsa nambwezera kwa iye. Zimenezo ziyenera kukhala zitammangirira mwauzimu chotani nanga!—1 Mafumu 17:16-24.
Lerolino sitimayembekezera kudalitsidwa ndi zozizwitsa. (1 Akorinto 13:8) Koma Yehova amatitsimikizira kuti adzachirikiza iwo akumtumikira ndi mtima wonse. (Mateyu 6:33) Chotero tingakhale monga mkazi wamasiye wa ku Zarefati mwanjira imeneyo, tikumapatsa mwaufulu, ndi chidaliro chakuti Yehova adzatisamalira. Momwemonso, tingapeze mfupo zazikulu zauzimu. Ngati kupatsa kwathu kuli chizoloŵezi, osati kwakamodzikamodzi, kotengeka maganizo, kudzatithandiza kukhala ndi diso langwiro ndi kusumika maganizo pa zinthu za Ufumu, monga momwe Yesu analangizira. (Luka 11:34; yerekezerani ndi 1 Akorinto 16:1, 2.) Kudzatithandizanso kumva kuti tili oyandikana kwambiri ndi Yehova ndi Yesu monga antchito anzawo. (1 Akorinto 3:9) Ndipo kudzawonjezera mzimu wopatsa waufulu umene olambira a Yehova padziko lonse adziŵika nawo kale.
[Bokosi patsamba 31]
NJIRA ZIMENE ENA AMASANKHA KUPATSIRAMO
ZOPEREKA ZA NTCHITO YA PADZIKO LONSE
Ambiri amaika pambali kapena kulinganiza ndalama zimene amaika m’mabokosi a zopereka olembedwa kuti: “Zopereka za Ntchito ya Padziko Lonse ya Sosaite—Mateyu 24:14.” Mwezi uliwonse mipingo imatumiza ndalamazi ku malikulu a dziko lonse ku Brooklyn, New York, kapena ku ofesi ya nthambi yakwawo.
Zopereka zaufulu za ndalama zingatumizidwenso mwachindunji ku Treasurer’s Office, Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania, 25 Columbia Heights, Brooklyn, New York 11201-2483, kapena ku ofesi ya Sosaite ya m’dziko lanu. Majuwelo kapena zinthu zina zamtengo wapatali zingaperekedwenso. Kalata yachidule yofotokoza kuti zimenezo zaperekedwa monga mphatso yeniyeni iyenera kutsagana ndi zoperekazo.
CHOPEREKA CHOTCHEDWA CONDITIONAL-DONATION
Ndalama zingaperekedwe ku Watch Tower Society kuziikizira kufikira imfa ya woperekayo, limodzi ndi makonzedwe akuti ngati pakhala kusoŵa kwaumwini, zidzabwezeredwa kwa woperekayo. Kuti mudziŵe zambiri, lemberani ku Treasurer’s Office pakeyala yosonyezedwayo.
KUPATSA KOLINGANIZA
Kuwonjezera pa mphatso zenizeni za ndalama ndi zopereka za ndalama za conditional, pali njira zina zopatsiramo kuti tithandizire utumiki wa Ufumu wa padziko lonse. Zimenezo zimaphatikizapo:
Inshuwalansi: Watch Tower Society ingalembetsedwe kuti ndiyo idzapatsidwa mapindu a inshuwalansi kapena penshoni. Sosaite iyenera kudziŵitsidwa za makonzedwe alionse otero.
Maakaunti a ku Banki: Maakaunti a ku banki, zikalata zoikizira ndalama, kapena maakaunti a anthu opuma pantchito angaikiziridwe kapena kulipiridwa pambuyo pa imfa ku Watch Tower Society, mogwirizana ndi malamulo a mabanki akwanu. Sosaite iyenera kudziŵitsidwa za makonzedwe alionse otero.
Stock ndi Bond: Stock ndi bond ingapatsidwe monga chopereka ku Watch Tower Society monga mphatso yeniyeni kapena mwa kakonzedwe kamene woperekayo angapitirize kumalipiridwa ndalama zopindulidwa.
Malo: Malo okhoza kugulitsidwa angaperekedwe ku Watch Tower Society monga mphatso yeniyeni kapena mwa kusunga malowo mwini wake, amene angapitirizebe kukhalapo pamene ali ndi moyo. Munthuyo ayenera kudziŵitsa Sosaite asanailoŵetse m’pangano la malo alionse.
Chuma cha Masiye ndi Choikizira: Chuma kapena ndalama zingakhale choloŵa cha Watch Tower Society kudzera mwa pangano la amene adzatenga chuma cha masiye lochitidwa mwa lamulo, kapena Sosaite ingalembetsedwe kukhala yodzapindula ndi pangano loikizira chuma. Pangano loikizira chuma lopindulitsa gulu la chipembedzo lingakhale ndi mapindu ena akuchepetsa msonkho. Kope la pangano la chuma cha masiye kapena choikizira liyenera kutumizidwa ku Sosaite.
Awo amene akufuna kugwiritsira ntchito alionse a makonzedwewa a kupatsa kolinganiza ayenera kulembera ku ofesi ya Sosaite ya m’dziko lawo. Sosaite iyenera kulandira makope a zikalata zofunikira zokhudza makonzedwe alionse ameneŵa.