Levitiko
7 “‘Lamulo la nsembe yakupalamula+ ndi ili: Nsembeyi ndi yopatulika koposa. 2 Nyama ya nsembe yakupalamula aziiphera pamalo amene amaphera nyama ya nsembe yopsereza, ndipo magazi ake+ aziwazidwa mbali zonse za guwa lansembe.+ 3 Azipereka mafuta ake onse,+ kuphatikizapo mchira wamafuta, mafuta okuta matumbo, 4 impso ziwiri zimene zili pafupi ndi chiuno komanso mafuta okuta impsozo. Azichotsanso mafuta apachiwindi pamodzi ndi impsozo.+ 5 Wansembe aziwotcha zinthu zimenezi paguwa lansembe monga nsembe yowotcha pamoto yoperekedwa kwa Yehova.+ Imeneyi ndi nsembe yakupalamula. 6 Mwamuna aliyense yemwe ndi wansembe azidya nyamayo+ ndipo aziidyera mʼmalo oyera. Nsembeyi ndi yopatulika koposa.+ 7 Lamulo la nsembe yakupalamula ndi lofanana ndi la nsembe yamachimo. Nyama ya nsembeyi izikhala ya wansembe amene wapereka nsembeyo pophimba machimo.+
8 Wansembe akaperekera munthu nsembe yopsereza, chikopa+ cha nsembeyo chizikhala cha wansembe amene wapereka nsembeyo.
9 Nsembe iliyonse yambewu imene yaphikidwa mu uvuni kapena mʼchiwaya+ izikhala ya wansembe amene wapereka nsembeyo. Izikhala yake.+ 10 Koma nsembe yambewu iliyonse yothira mafuta+ kapena yosathira mafuta+ izikhala ya ana onse aamuna a Aroni, azigawana mofanana.
11 Tsopano lamulo la nsembe yamgwirizano+ imene aliyense azipereka kwa Yehova ndi ili: 12 Ngati akupereka nsembeyo posonyeza kuyamikira,+ azipereka nsembe yoyamikira pamodzi ndi mkate wozungulira woboola pakati, wopanda zofufumitsa, wothira mafuta. Aziperekanso timitanda ta mkate topyapyala topanda zofufumitsa, topaka mafuta komanso mkate wozungulira woboola pakati, wothira mafuta, wophika ndi ufa wosalala wosakaniza bwino ndi mafuta. 13 Azipereka nsembe yake pamodzi ndi mitanda ya mkate yozungulira yoboola pakati, yokhala ndi zofufumitsa. Aziipereka pamodzi ndi nsembe zamgwirizano zimene akuzipereka posonyeza kuyamikira. 14 Pa zinthu zimenezi azipereka mtanda umodzi wa nsembe iliyonse kuti ikhale gawo lopatulika loperekedwa kwa Yehova. Mtandawo uzikhala wa wansembe amene wawaza magazi a nsembe zamgwirizanozo paguwa lansembe.+ 15 Nyama ya nsembe zamgwirizano zimene zaperekedwa monga nsembe yoyamikira aziidya pa tsiku limene waipereka. Asasunge nyama iliyonse mpaka mʼmamawa.+
16 Ngati akupereka nsembe chifukwa cha lonjezo limene anapanga+ kapena ngati akupereka nsembe yaufulu,+ aziidya pa tsiku limene wapereka nsembeyo, ndipo yotsala angathenso kuidya pa tsiku lotsatira. 17 Koma ngati nyama ya nsembeyo yatsala mpaka tsiku lachitatu, ayenera kuiwotcha pamoto.+ 18 Koma ngati nyama iliyonse ya nsembe yamgwirizano yadyedwa pa tsiku lachitatu, wopereka nsembeyo Mulungu sadzasangalala naye. Nsembe yakeyo idzakhala yopanda phindu. Idzakhala chinthu chonyansa, ndipo amene wadya nsembeyo adzayankha mlandu chifukwa cha kulakwa kwake.+ 19 Nyama imene yakhudza chilichonse chodetsedwa, siyenera kudyedwa. Muziiwotcha pamoto. Koma aliyense woyera angathe kudya nyama imene sinadetsedwe.
20 Munthu aliyense wodetsedwa amene wadya nyama ya nsembe yamgwirizano, imene ndi ya Yehova, aziphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu a mtundu wake.+ 21 Munthu akakhudza chilichonse chodetsedwa, kaya ndi chodetsa chochokera kwa munthu+ kapena nyama yodetsedwa,+ kapenanso chinthu chilichonse chonyansa chodetsedwa,+ nʼkudya ina mwa nyama ya nsembe yamgwirizano, imene ndi ya Yehova, munthu ameneyo aziphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu a mtundu wake.’”
22 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 23 “Uwauze Aisiraeli kuti, ‘Musamadye mafuta alionse+ a ngʼombe, a mwana wa nkhosa kapena a mbuzi. 24 Mafuta a nyama imene mwaipeza yakufa komanso mafuta a nyama imene yaphedwa ndi nyama inzake, mungathe kuwagwiritsa ntchito iliyonse, koma musamawadye ngakhale pangʼono.+ 25 Aliyense amene wadya mafuta a nyama imene waipereka kwa Yehova ngati nsembe yowotcha pamoto, aziphedwa kuti asakhalenso pakati pa anthu a mtundu wake.
26 Musamadye magazi alionse+ kulikonse kumene mungakhale, kaya akhale magazi a mbalame kapena a nyama. 27 Munthu aliyense wodya magazi alionse aziphedwa+ kuti asakhalenso pakati pa anthu a mtundu wake.’”
28 Yehova anapitiriza kulankhula ndi Mose kuti: 29 “Uwauze Aisiraeli kuti, ‘Munthu amene akubweretsa nsembe yake yamgwirizano kwa Yehova,+ azipereka mbali ya nsembe yake yamgwirizanoyo kwa Yehova. 30 Iye azibweretsa yekha mafuta+ pamodzi ndi chidale ngati nsembe yowotcha pamoto yoperekedwa kwa Yehova. Ndipo aziyendetsa zinthu zimenezi uku ndi uku monga nsembe yoyendetsa uku ndi uku+ yoperekedwa kwa Yehova. 31 Wansembe aziwotcha mafutawo paguwa lansembe,+ koma chidalecho chizikhala cha Aroni ndi ana ake.+
32 Mwendo wakumbuyo wakumanja muziupereka kwa wansembe monga gawo lopatulika lochokera pansembe zanu zamgwirizano.+ 33 Mwana wa Aroni amene wapereka kwa Mulungu magazi a nsembe zamgwirizano ndiponso mafuta, azitenga mwendo wakumbuyo wakumanja monga gawo lake.+ 34 Ine ndikutenga chidale cha nsembe yoyendetsa uku ndi uku ndiponso mwendo womwe ndi gawo lopatulika. Ndikutenga zimenezi pansembe zamgwirizano za Aisiraeli nʼkuzipereka kwa Aroni wansembe ndi ana ake. Limeneli ndi lamulo kwa Aisiraeli mpaka kalekale.+
35 Limeneli linali gawo la Aroni ndi ana ake monga ansembe. Gawoli linali lochokera pansembe zowotcha pamoto zoperekedwa kwa Yehova, malinga ndi zimene anawalamula pa tsiku limene anaperekedwa kuti atumikire monga ansembe a Yehova.+ 36 Yehova analamula kuti aziwapatsa gawoli kuchokera kwa Aisiraeli, pa tsiku limene anawadzoza.+ Limeneli ndi lamulo mʼmibadwo yawo yonse mpaka kalekale.’”
37 Limeneli ndi lamulo lokhudza nsembe yopsereza,+ nsembe yambewu,+ nsembe yamachimo,+ nsembe yakupalamula,+ nyama yoperekedwa poika munthu kuti akhale wansembe+ ndiponso nsembe yamgwirizano,+ 38 mogwirizana ndi zimene Yehova analamula Mose paphiri la Sinai,+ pa tsiku limene analamula Aisiraeli kuti azipereka nsembe zawo kwa Yehova mʼchipululu cha Sinai.+