Achichepere Amene Amakumbukira Mlengi Wawo
“Kumbukira, tsopano lino, Mlengi wako Wamkulu m’masiku a unyamata wako.”—MLALIKI 12:1, NW.
1. Kodi ndi mawu otani a wazaka 11 wina amene akusonyeza kuti Mlengi wathu ali weniweni kwa iye?
NKOKOMA chotani nanga pamene ana aang’ono alankhula ndi kuchita zinthu m’njira imene imasonyeza kuti amaona Yehova Mulungu monga munthu weniweni amene amamyamikira ndi kufuna kumkondweretsa! Mnyamata wina wazaka 11 anati: “Pamene ndili ndekha ndi kuyang’ana kunja pazenera, ndimaona mmene chilengedwe cha Yehova chilili chodabwitsa. Ndiyeno ndimayerekezera mmene Paradaiso adzakhalira wokongola mtsogolo ndi mmene ndidzakhudzira nyama panthaŵiyo.” (Yesaya 11:6-9) Anawonjezera kuti: “Pamene ndili ndekha, ndimapemphera kwa Yehova. Ndimadziŵa kuti sangaipidwe nane konse chifukwa cha kulankhula naye nthaŵi zonse. Ndimadziŵa kuti nthaŵi zonse amandiona.” Kodi Mlengi wathu ali weniweni kwa inu monga momwe alili kwa mnyamatayu?
Kodi Mulungu Ali Weniweni Motani kwa Inu?
2. (a) Kodi Mlengi wanu angakhale bwanji weniweni kwa inu? (b) Kodi makolo angachite mbali yotani pothandiza ana awo kuzindikira kuti Mulungu ndi munthu weniweni?
2 Kuti Yehova ndi malonjezo ake akhale enieni kwa inu, choyamba muyenera kuphunzira za iye ndi za mtsogolo mwabwino kwambiri mmene iyeyo akukupatsani m’dziko latsopano lolungama limene Baibulo limalongosola. (Chivumbulutso 21:3, 4) Ngati makolo anu akuphunzitsani zinthu zimenezi, muli ndi chifukwa chokhalira othokoza chifukwa chakuti zimenezi zimakukhozetsani kulabadira lamulo louziridwa lakuti: “Kumbukira, tsopano lino, Mlengi wako Wamkulu.” (Mlaliki 12:1, NW) Wachichepere wina ponena za kuphunzitsidwa ndi makolo ake pachiyambi anati: “Nthaŵi zonse zinthu zonse m’moyo zinali kuloza kwa Yehova. Imeneyi inali mfungulo ya kukumbukira kwanga Mlengi wanga.” Msungwana winanso anati: “Ndidzathokoza makolo anga kosatha chifukwa cha kundiphunzitsa kuti Yehova ndi munthu weniweni. Anandisonyeza mmene ndingamkondere ndipo anandiuza za chimwemwe cha kumtumikira nthaŵi zonse.”
3, 4. Kodi nchiyani chimene chingakuthandizeni kuganiza za Yehova monga munthu weniweni?
3 Komabe, ambiri amapeza kukhala kovuta kuona Mulungu monga munthu weniweni amene amasonyeza chidwi mwa iwo. Kodi inu mumatero? Wachichepere wina anathandizidwa kuganiza za Mulungu m’njira yakeyake ndi ndemanga ya mu Nsanja ya Olonda yakuti: “Sitidziŵa mmene ulili ukulu wa thupi la Yehova Mulungu.” Zoonadi, upamwamba wa Yehova sudalira pa ukulu wa thupi lake kapena kaumbidwe ka thupi lake, pakuti chiganizo chotsatira mu Nsanja ya Olonda imeneyo chinati: “Ukulu wake weniweni uli pa mtundu wa Mulungu amene iye ali,” indedi, Mulungu wokhulupirika, wachifundo, wachikondi, ndi wokhululukira.a (Eksodo 34:6; Deuteronomo 32:4; Salmo 86:5; Yakobo 5:11) Kodi mwafikira pa kuona Yehova monga munthu wotero, bwenzi lodalirika limene mungakhale nalo pa unansi wamtengo wapatali?—Yesaya 41:8; Yakobo 2:23.
4 Yesu anathandiza otsatira ake oyambirira kupeza unansi wapafupi ndi Mulungu. Chotero, pamene mtumwi Yohane analemba za chiukiriro chake cha moyo wa kumwamba chimene anali kuyembekezera, Yohane anati: “Tidzakhala ofanana ndi [Mulungu], pakuti tidzamuona iye monga ali.” (1 Yohane 3:2; 1 Akorinto 15:44) Lerolino achichepere angathandizidwenso kuona Mulungu monga munthu weniweni, munthu amene angamdziŵe bwino ngakhale kuti sangathe kumuona. Mnyamata wina anati: “Makolo anga anandithandiza kukumbukira Yehova mwa kufunsa mafunso ambiri, onga akuti, ‘Kodi Yehova anganenenji? Kodi ungazifotokoze motani m’mawu akoako? Zimenezo zikutanthauzanji?’” Kodi mafunso onga ameneŵa samatichititsa kuganiza za unansi wathu wapafupi ndi Mulungu?
Tanthauzo la Kukumbukira
5. Kodi ndi zitsanzo ziti za m’Baibulo zimene zikusonyeza kuti kukumbukira munthu winawake kumaloŵetsamo zambiri kuposa kungokumbukira dzina lake?
5 Kumvera lamulolo, “Kumbukira, tsopano lino, Mlengi wako Wamkulu,” kumatanthauza zambiri kuposa kungoganiza za Yehova. Kumaloŵetsamo ntchito, kuchita zimene zimamkondweretsa. Pamene mpandu wina anachonderera Yesu kuti, ‘Ndikumbukireni mmene muloŵa Ufumu wanu,’ iyeyo anafuna kuti Yesu achite zambiri kuposa pa kungokumbukira dzina lake. Anafuna kuti Yesu adzachitepo kanthu, kumuukitsa. (Luka 23:42) Mofananamo, Yosefe woikidwa m’ndende anayembekezera kuchitiridwa kenakake pamene anapempha wopereka chikho wa Farao kumkumbukira kwa Farao. Ndipo pamene Yobu anapempha Mulungu, ‘Kundikumbukira,’ Yobu anali kupempha kuti panthaŵi ina mtsogolo, Mulungu adzachitapo kanthu mwa kumuukitsa.—Yobu 14:13; Genesis 40:14, 23.
6. Kodi liwu lachihebri la “kumbukira” limapereka motani lingaliro la kukonda chinthu kapena munthu wokumbukiridwayo?
6 Umboni wina umanena kuti liwu lachihebri lotembenuzidwa kuti “kumbukira” kaŵirikaŵiri limapereka lingaliro la “kukonda kwa maganizo ndi mchitidwe zimene zimatsagana ndi chikumbukiro.” Kuloŵetsedwa kwa “kukonda” m’liwu lakuti “kumbukira” kungaonedwe pa kudzuma kwa “khamu losakanikirana” m’chipululu kwakuti: ‘Mmene tikukumbukirira nanga nsomba zimene tinali kudya ku Igupto!’ Monga momwe Yobu anapempherera kuti adzakumbukiridwe mwachiyanjo ndi Mulungu, ndimo mmenenso Hezekiya, Nehemiya, Davide, ndi wamasalmo wina wosatchulidwa dzina anachonderera kuti adzakumbukiridwe mwachikondi ndi Yehova chifukwa cha kukhulupirika kwawo.—Numeri 11:4, 5, NW; 2 Mafumu 20:3; Nehemiya 5:19; 13:31; Salmo 25:7; 106:4.
7. Ngati tikumbukira Mulungu ndi chikondi, kodi zimenezi zingayambukire motani khalidwe lathu?
7 Chotero, tingafunse kuti, ‘Kodi timakumbukira Mlengi wathu ndi chikondi ndi kupeŵa kuchita chilichonse chomchititsa kukhumudwa kapena kumva chisoni?’ Wachichepere wina anati: “Amayi anandithandiza kuzindikira kuti Yehova ali ndi malingaliro, ndipo ndikali wamng’ono, ndinali kuzindikira kuti zochita zanga zinali kumkhudza.” (Salmo 78:40-42) Winanso analongosola kuti: “Ndinali kudziŵa kuti zochita zanga zingathandizire kapena kudodometsa kupereka yankho pa chitokoso chimene Satana anapereka kwa Yehova. Ndinafuna kukondweretsa mtima wa Yehova, chotero zimenezo zinandithandiza ndipo zikundithandizabe lerolino.”—Miyambo 27:11.
8. (a) Kodi ndi kulondola chiyani kumene kudzasonyeza kuti timakumbukira Yehova ndi chikondi? (b) Kodi ndi mafunso otani amene achichepere ayenera kulingalira mwanzeru?
8 Zoonadi, m’dziko loipali, nthaŵi zina nkovuta kukumbukira Yehova mwa kukhala ndi phande lokwanira mu ntchito imene imamkondweretsa. Komabe kungakhale kwabwino chotani nanga ngati mungatsanzire Timoteo wachichepere wa m’zaka za zana loyamba—osaphatikizapo zikwi zambiri za achichepere owopa Mulungu lerolino—mwa kulondola utumiki wachikristu wanthaŵi zonse monga mtumiki yemwe ali mpainiya! (Machitidwe 16:1-3; 1 Atesalonika 3:2) Komabe, tingafunse kuti, Kodi mungathe kudzichirikiza mu utumiki waupainiya? Ndipo ngati muloŵa mu ukwati, kodi mudzakhala ndi maluso osamalirira awo a m’banja lanu? (1 Timoteo 5:8) Ameneŵa ndi mafunso ofunika, ndipo nkofunika kuti inu muwalingalire mosamala.
Maphunziro Okhala ndi Cholinga
9. Kodi ndi chosankha chotani chimene achichepere amayang’anizana nacho pa nkhani ya maphunziro akusukulu?
9 Pamene chitaganya cha anthu chikukhala chocholoŵana kwambiri, mlingo wokulirapo wa maphunziro ungafunike kuti mupeze ntchito yoyenera yodzichirikizira mu ntchito ya upainiya. Mwina mwaona kale kuti ngakhale ena amene ali ndi maphunziro a kuyunivesite afunikira kuwonjezera maphunziro kuti apeze maluso atsopano amene olemba ntchito amawafuna lerolino. Chotero achicheperenu ofuna kukondweretsa Mulungu, kodi mudzafuna kupeza maphunziro ochuluka motani? Chosankha chiyenera kupangidwa moyenera mukumakumbukira lamulo louziridwalo lakuti: “Kumbukira, tsopano lino, Mlengi wako Wamkulu.”
10. Kodi maphunziro abwino koposa amene tingalandire ndi ati?
10 Zoonadi, inu mudzafunikira kulondola maphunziro amene ngakhale anthu olemekezeka ambiri akudziko amati ndiwo abwino koposa—aja amene timapeza mwa kuphunzira Mawu a Mulungu mosamalitsa. Wolemba mabuku wachijeremani Johann Wolfgang von Goethe anati: “Pamene [mtundu] upita patsogolo m’zamaphunziro, mpamenenso kumakhala kosavuta kwambiri kugwiritsira ntchito Baibulo ponse paŵiri monga maziko ndi chiŵiya cha maphunziro.” Inde, kuphunzira Baibulo kudzakukonzekeretsani bwino kwambiri kaamba ka moyo kuposa mmene angachitire maphunziro ena alionse!—Miyambo 2:6-17; 2 Timoteo 3:14-17.
11. (a) Kodi ntchito yofunika koposa imene tingachite ndi iti? (b) Kodi nchifukwa ninji wachichepere wina anasankha kupeza mlingo wina wa maphunziro?
11 Popeza kuti kudziŵa Mulungu kuli kopatsa moyo, ntchito yofunika koposa imene mungachite lerolino ndiyo ya kuuza ena chidziŵitso chimenecho. (Miyambo 3:13-18; Yohane 4:34; 17:3) Komabe, kuti muchite zimenezi mogwira mtima, mufunikira kuphunzitsidwa njira zofunika. Mufunikira kukhala wokhoza kuganiza bwino, kulankhula mwanzeru, ndi kuŵerenga ndi kulemba bwino—maluso amene timaphunzira kusukulu. Chotero onani makosi anu a kusukulu mwamphamvu, monga momwe anachitira Tracy, wachichepere wa ku Florida, ku United States of America, amene anamaliza maphunziro pa sukulu yasekondale ndi mamalikisi apamwamba. Anafotokoza chiyembekezo chake kuti: “Nthaŵi zonse ndakhala ndi cholinga cha kukhala mtumiki wanthaŵi zonse wa Mulungu wanga Yehova, ndipo ndikhulupirira kuti maphunziro anga adzandithandiza kukwaniritsa cholinga chimenechi.”
12. Ngati musankha kuwonjezera maphunziro, kodi iwo angakwaniritse chifuno chotani?
12 Kodi munayamba mwalingalirapo chifukwa chimene mumapitira kusukulu? Kodi makamaka mumatero kuti mudzikonzekeretse kudzakhala mtumiki wogwira mtima wa Yehova? Ngati ndi choncho, mufunikira kulingalira mwamphamvu za mmene maphunziro anu adzakwaniritsira chifuno chimenechi. Mutakambitsirana ndi makolo anu, kungasankhidwe kuti muwonjezere maphunziro kuposa pa ofunidwa ndi lamulo. Maphunziro owonjezera amenewo angakuthandizeni kupeza ntchito yodzichirikizira ndi kukupatsanibe nthaŵi ndi nyonga ya kukhala ndi phande mu ntchito ya Ufumu.—Mateyu 6:33.
13. Kodi Akristu aŵiri achirasha amene anawonjezera maphunziro asonyeza motani chifuno chawo m’moyo?
13 Ena amene amawonjezera maphunziro amaloŵa mu utumiki wanthaŵi zonse ngakhale pamene akulandira maphunziro owonjezereka. Lingalirani za Nadia ndi Marina, asungwana aŵiri achichepere ku Moscow, Russia. Aŵiri onsewo anabatizidwa mu April 1994 ndipo anayamba kutumikira monga atumiki ochita upainiya wothandiza. Posapita nthaŵi pambuyo pake anamaliza maphunziro a kusekondale ndipo analembetsa m’programu ya maphunziro a ntchito yoŵerengera ndalama ya zaka ziŵiri. Mu May 1995 anayamba kuchita upainiya wokhazikika, komabe anapezabe avareji ya A m’makalasi awo ophunzira ntchito yoŵerengera ndalama. Ndiponso, pakati pawo, anali okhoza kuchititsa avareji ya maphunziro a Baibulo 14 mlungu uliwonse akumapitabe kusukulu. Asungwanawo akuyembekezera kuti maphunziro awo a ntchito ya kuŵerengera ndalama adzawakhozetsa kupeza ntchito yoyenera, kotero kuti adzichirikize mu utumiki wanthaŵi yonse.
14. Mosasamala kanthu za kuchuluka kwa maphunziro akusukulu amene tasankha, kodi nchiyani chimene chiyenera kukhala chinthu chofunika koposa m’moyo wathu?
14 Ngati muwonjezera maphunziro kuposa pa ofunidwa ndi lamulo, pendani mwanzeru chifukwa chanu chochitira zimenezo. Kodi mukufuna kudzipangira dzina ndi kupeza chuma chakuthupi? (Yeremiya 45:5; 1 Timoteo 6:17) Kapena kodi cholinga chanu ndicho kugwiritsira ntchito maphunziro owonjezera kuti mukhale ndi phande mokwanira mu utumiki wa Yehova? Lydia, wachichepere amene anasankha kuwonjezera maphunziro, analongosola lingaliro labwino pa zinthu zauzimu, akumanena kuti: “Ena amalondola maphunziro apamwamba ndi kulola kukondetsa zakuthupi kuwapinga, ndipo ataya Mulungu. Pa ine ndekha unansi wanga ndi Mulungu ndiwo chinthu chofunika koposa kwa ine.” Ha, ndi maganizo abwino chotani nanga amenewo kwa ife tonse!
15. Kodi ndi kusiyanasiyana kotani m’maphunziro kumene kunalipo pakati pa Akristu a m’zaka za zana loyamba?
15 Mosakayikira, Akristu a m’zaka za zana loyamba anali osiyanasiyana m’maphunziro. Mwachitsanzo atumwiwo Petro ndi Yohane anaonedwa kukhala “osaphunzira ndi opulukira” chifukwa chakuti sanaphunzire m’sukulu za arabi. (Machitidwe 4:13) Komano, mtumwi Paulo analandira maphunziro amene lerolino tingaŵayerekezere ndi a ku yunivesite. Komabe, Paulo sanagwiritsire ntchito maphunziro amenewo kudzidziŵikitsira iye mwini; m’malo mwake, iwo anali chuma pamene anali kulalikira kwa anthu a m’mikhalidwe yosiyanasiyana ya moyo. (Machitidwe 22:3; 1 Akorinto 9:19-23; Afilipi 1:7) Mofananamo, Manayeni, amene ‘anaphunzira ndi Herode wolamulira chigawo,’ anali pakati pa aja amene anatsogolera mumpingo wa Antiokeya.—Machitidwe 13:1, NW.
Kodi Nchifukwa Ninji Muyenera Kugwiritsira Ntchito Mwanzeru Ndalama Zanu?
16. (a) Kodi nchifukwa ninji kungakhale kovutirapo kukumbukira Mlengi wathu ngati tili m’ngongole? (b) Kodi ndi motani mmene limodzi la mafanizo a Yesu limasonyezera kufunika kwa kuganiza bwino tisanagwiritsire ntchito ndalama?
16 Ngati mulephera kusamalira mwanzeru ndalama zanu, kungakhale kovutirapo kukumbukira Mlengi wanu mwa kuchita zimene zimamkondweretsa. Pakuti ngati muloŵa m’ngongole, tinganene kuti muli ndi mbuye wina. Baibulo limalongosola kuti: “Kongola ndalama ndipo udzakhala kapolo wa wokukongoletsa.” (Miyambo 22:7, Today’s English Version) Limodzi la mafanizo a Yesu limasonyeza kufunika kwa kuganiza tisanagwiritsire ntchito ndalama. “Ndani wa inu,” Yesu anatero, “amene akafuna kumanga nsanja yaitali, sathanga wakhala pansi, naŵerengera mtengo wake, aone ngati ali nazo zakuimaliza? Kuti kungachitike, pamene atakhazika pansi miyala ya ku maziko ake, osakhoza kuimaliza, anthu onse akuyang’ana adzayamba kumseka iye.”—Luka 14:28, 29.
17. Kodi nchifukwa ninji kaŵirikaŵiri kumakhala kovuta kulamulira kugwiritsira ntchito ndalama kwa munthuwe?
17 Chotero, mwanzeru muyenera kuyesa kuchita mogwirizana ndi pulinsipulo la m’Malemba ‘la kusakhala ndi mangawa kwa munthu aliyense, koma kukondana ndiko.’ (Aroma 13:8) Koma kuchita zimenezi nkovuta, makamaka pamene tiyang’anizana ndi zinthu zatsopano zopangidwa mosalekeza zimene osatsa malonda amanena kuti mufunikiradi kukhala nazo. Kholo lina, limene layesa kuthandiza ana ake kusonyeza luntha, linati: “Tathera nthaŵi yambiri tikumakambitsirana pa zimene zili zofunikira ndi zimene zili zokhumba.” Sukulu zambiri zalephera kuphunzitsa nkhani zimenezo, mwina zikumangopereka malangizo ochepa kwambiri onena za njira yosamalirira ndalama mwanzeru. “Timamaliza maphunziro ku sukulu yasekondale tikumadziŵa kwambiri masamu kuposa mmene tingasungire ndalama,” anatero wantchito zothandiza anthu wina. Nangano, nchiyani chimene chingakuthandizeni kugwiritsira ntchito ndalama mwanzeru?
18. Kodi mfungulo ya kusamalira ndalama mwanzeru nchiyani, ndipo chifukwa ninji?
18 Kulabadira chisonkhezerocho, “Kumbukira, tsopano lino, Mlengi wako Wamkulu,” kuli mfungulo ya kusamalira ndalama zanu mwanzeru. Zimenezi zili chifukwa chakuti pamene mumvera lamulo limenelo, chinthu chanu choyamba ndicho kukondweretsa Yehova, ndipo chikondi chanu kwa iye chimayambukira mmene mumagwiritsirira ntchito ndalama zanu. Motero, simudzayesa kulola zokhumba zanu kudodometsa kudzipereka kwa Mulungu ndi mtima wonse. (Mateyu 16:24-26) Mudzayesayesa kuchititsa diso lanu kukhala “la kumodzi,” ndiko kuti, lolunjika bwino pa Ufumu wa Mulungu ndi kuchita chifuniro chake. (Mateyu 6:22-24) Motero mudzafikira pa kuona chilangizo cha Mulungu cha ‘kulemekeza Yehova ndi chuma chanu’ kukhala mwaŵi wosangalatsa.—Miyambo 3:9.
Achichepere Oyenera Kuwatsanzira
19. Kodi achichepere kalelo anakumbukira motani Mlengi wawo?
19 Mwamwaŵi, achichepere ambiri, akale ndi amakono, akumbukira Mlengi wawo. Samueli wachichepere anachirimika mu ntchito ya pachihema ngakhale kuti panali zisonkhezero zoipa za aja amene anali kutumikira nawo. (1 Samueli 2:12-26) Mkazi wa Potifara woyesayesa kunyengererayo, analephera kukola Yosefe wachichepere kuti achite chisembwere. (Genesis 39:1-12) Ngakhale kuti anali “mwana,” Yeremiya analalikira molimba mtima poyang’anizana ndi chitsutso cholimba. (Yeremiya 1:6-8) Buthu lachiisrayeli mopanda mantha linalangiza kazembe wa khamu la nkhondo lamphamvu kukafuna thandizo ku Israyeli, kumene anadziŵako za Yehova. (2 Mafumu 5:1-4) Danieli wachichepere ndi anzake anasunga chikhulupiriro chawo pamene anayesedwa pa malamulo a chakudya a Mulungu. Ndipo anyamatawo Sadrake, Mesake, ndi Abedinego anasankha kuponyedwa m’ng’anjo ya moto m’malo mwa kulolera kutaya kukhulupirika kwawo kwa Mulungu mwa kulambira fano.—Danieli 1:8, 17; 3:16-18; Eksodo 20:5.
20. Kodi achichepere ambiri akumbukira motani Mlengi wawo lerolino?
20 Lerolino achichepere oposa 2,000 azaka zakubadwa 19 mpaka 25 akutumikira pa malikulu adziko lonse a Mboni za Yehova mu New York State, ku United States of America. Iwo ali chigawo chochepa chokha cha achichepere zikwi zambiri amene akukumbukira Mlengi wawo padziko lonse. Monga momwe analili Yosefe wakale, iwo akana kulolera kutaya chiyero chawo cha makhalidwe abwino. Ambiri amvera Mulungu m’malo mwa anthu pamene akakamizidwa kusankha amene ayenera kumtumikira. (Machitidwe 5:29) Ku Poland mu 1946, Henryka Zur wazaka zakubadwa 15 anazunzidwa pamene anakana kusonyeza mchitidwe wa kulambira mafano kwachipembedzo. “Ganiza chilichonse chimene ukufuna mumtima,” mmodzi wa omzunza ake anatero, “komano ingosonyeza chizindikiro cha mtanda chachikatolika.” Chifukwa chakuti anakana, anamkwakwazira mu nkhalango ndi kumuwombera mfuti, chiyembekezo chake chotsimikizirika cha moyo wosatha chili chosagwedera!b
21. Kodi ndi chiitano chotani chimene chingakhale chanzeru kuchilandira, ndi chotulukapo chotani?
21 Mmene mtima wa Yehova uyenera kukhala utakondwerera nanga ndi achichepere amene amkumbukira m’zaka mazana ambiri zapitazo! Kodi inu mudzalabadira chiitano chake chakuti, “Kumbukira, tsopano lino, Mlengi wako Wamkulu”? Kunena zoona iyeyo ngwoyenerera kuti inu mumkumbukire! Ganizani tsiku ndi tsiku za zinthu zonse zimene wakuchitirani ndi zimene ati adzachite, ndipo landirani chiitano chake chakuti: “Mwananga, khala wanzeru, nukondweretse mtima wanga; kuti ndimuyankhe yemwe anditonza.”—Miyambo 27:11.
[Mawu a M’munsi]
a Nsanja ya Olonda yachingelezi ya, December 15, 1953, tsamba 750.
b Onani 1994 Yearbook of Jehovah’s Witnesses, masamba 217-18, yofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi achichepere angathandizidwe motani kuona Mulungu monga munthu weniweni?
◻ Kodi kukumbukira Mlengi wanu kumatanthauzanji?
◻ Kodi maphunziro athu ayenera kutumikira chifuno chotani?
◻ Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kugwiritsira ntchito mwanzeru ndalama zathu?
◻ Kodi ndi achichepere ati amene muyenera kutsanzira?
[Chithunzi patsamba 17]
Kodi munayamba mwalingalirapo chifukwa chimene mumapitira kusukulu?
[Chithunzi patsamba 18]
Kodi mukuphunzira mmene mungagwiritsirire ntchito ndalama mwanzeru?