Makolo, Kondwerani mwa Ana Anu
“Atate wako ndi amako akondwere.”—MIYAMBO 23:25.
1. Kodi nchiyani chimene chidzachititsa makolo kukondwera mwa ana awo?
NKWABWINO chotani nanga kuona kamtengo kanthete kakumakula kukhala mtengo waukulu wokongola ndi wopereka mthunzi—makamaka ngati inuyo ndiye amene munauwoka ndi kuusamalira! Mofananamo, makolo amene amasamalira ana amene amakula kukhala atumiki a Mulungu okula msinkhu amakondwera kwambiri mwa iwo, monga momwe mwambi wa Baibulo umanenera kuti: “Atate wa wolungama adzasekeradi; wobala mwana wanzeru adzakondwera naye. Atate wako ndi amako akondwere, amako wakukubala asekere.”—Miyambo 23:24, 25.
2, 3. (a) Kodi makolo angapeŵe bwanji chisoni ndi zoŵaŵa? (b) Kodi timitengo tanthete ndi ana omwe zimafunikiranji kuti zikhale magwero a chikondwerero?
2 Komabe, mwana samangokhala yekha “wolungama” ndi “wanzeru.” Pafunikira kuyesayesa kwakukulu kusachititsa ana kukhala magwero a “chisoni” ndi “zoŵaŵa,” monga momwe ilili ntchito yochititsa kamtengo kanthete kukhala mtengo waukulu. (Miyambo 17:21, 25) Mwachitsanzo, mitengo yochirikizira kamtengo kanthete ingathandizire kukakulitsa mowongoka ndiponso mwamphamvu. Kukathirira ndi madzi nthaŵi zonse nkofunika, ndipo kamtengo kantheteko kangafunikire kutetezeredwa pa tizilombo. Potsirizira pake, kudulira mtengowo kumauchititsa kukhala wokongola.
3 Mawu a Mulungu amasonyeza kuti ana amafunikira zinthu zimenezi zonga chiphunzitso chaumulungu, kukhathamiritsidwa ndi madzi a choonadi cha Baibulo, chitetezero pa makhalidwe oipitsa, ndi chilango chachikondi kuti mudulire zikhoterero zosafunika. Kuti apereke zofunika zimenezi, atate makamaka akulimbikitsidwa kulera ana awo “m’chilango ndi kuwongolera maganizo kwa Yehova.” (Aefeso 6:4, NW) Kodi zimenezi zimaloŵetsamonji?
Chigogomezero pa Mawu a Yehova
4. Kodi makolo ali ndi thayo lotani kulinga kwa ana awo, ndipo nchiyani chimene chikufunika asanachite zimenezi?
4 “Kuwongolera maganizo kwa Yehova” kumatanthauza kuwongolera maganizo athu kuti agwirizane ndi chifuniro cha Yehova. Pamenepo, makolo ayenera kuika maganizo a Yehova pa zinthu mwa ana awo, kuloŵetsa mwa iwo malingaliro ake. Ndipo ayeneranso kutsanzira chitsanzo cha Mulungu cha kupereka chilango chachifundo, kapena maphunziro a kuwongolera. (Salmo 103:10, 11; Miyambo 3:11, 12) Koma makolo asanachite zimenezi, iwo eniwo ayenera kumwerekera m’mawu a Yehova, monga momwe Mose mneneri wa Mulungu analangizira Aisrayeli akale kuti: “Mawu awa [ochokera kwa Yehova] ndikuuzani lero, azikhala pamtima panu.”—Deuteronomo 6:6.
5. Kodi ndi liti ndipo ndi motani mmene makolo achiisrayeli anafunikira kulangizira ana awo, ndipo kodi ‘kuphunzitsa’ kumatanthauzanji?
5 Phunziro la Baibulo lokhazikika, kusinkhasinkha, ndi pemphero zimakonzekeretsa makolo kuchita zimene kenako Mose analamulira: “Muziwaphunzitsa [mawu a Yehova] mwachangu kwa ana anu, ndi kuwalankhula awa pokhala pansi m’nyumba zanu, ndi poyenda inu panjira, ndi pogona inu pansi, ndi pouka inu.” Liwu lachihebri lotembenuzidwa kuti “phunzitsa” limatanthauza “kubwereza,” “kunena mobwerezabwereza,” “kukhomereza mwakuya.” Onani mmene Mose anagogomezera mowonjezereka kufunika kwa kusunga mawu a Yehova choyamba: “Muziwamanga padzanja panu ngati chizindikiro, ndipo akhale ngati chapamphumi pakati pa maso anu. Ndipo muziwalembera pa mphuthu za nyumba zanu, ndi pazipata zanu.” Mwachionekere, Yehova amafuna kuti makolo azipereka chisamaliro chachikondi ndi chanthaŵi zonse pa ana awo!—Deuteronomo 6:7-9.
6. Kodi makolo anafunikira kuphunzitsanji ana awo, ndipo ndi phindu lotani?
6 Kodi “mawu awa” a Yehova amene makolo anafunikira kuphunzitsa ana awo ngotani? Mose anali atangobwerezanso kumene kutchula zimene ambiri amatcha kuti Malamulo Khumi, kuphatikizapo malamulo a kusapha, kusachita chigololo, kusaba, kusapereka umboni wonama, ndi kusasirira. Zofunika zimenezo za makhalidwe, ndiponso lamulo la ‘kukonda Yehova Mulungu wanu ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse, ndi mphamvu yanu’ zinali zimene makolo achiisrayeli makamaka anafunikira kuphunzitsa ana awo. (Deuteronomo 5:6-21; 6:1-5) Kodi simungavomereze kuti umenewu ndiwo mtundu wachiphunzitso chimene ana akufunikira lerolino?
7. (a) Kodi ana anayerekezeredwa ndi chiyani m’Baibulo? (b) Kodi nchiyani chimene tsopano tidzapenda?
7 Atate achiisrayeli anauzidwa kuti: “Mkazi wako adzanga mpesa wopatsa m’mbali za nyumba yako; ana ako adzanga timitengo ta azitona pozinga podyera pako.” (Salmo 128:3) Komabe, kuti makolo akondwere mwa ‘timitengo tawo tanthete’ m’malo mwa kuchita chisoni, ayenera kusonyeza chidwi chaumwini cha tsiku ndi tsiku mwa ana awo. (Miyambo 10:1; 13:24; 29:15, 17) Tiyeni tipende mmene makolo angaphunzitsire, kuthirira mwauzimu, kutetezera, ndi kulanga ana awo mwachikondi m’njira imene imawachititsa kupeza chikondwerero chenicheni mwa iwo.
Kuphunzitsa Kuyambira pa Ukhanda
8. (a) Kodi ndani amene anali ngati mitengo yochirikiza kwa Timoteo? (b) Kodi maphunzirowo anayamba liti, ndipo ndi zotulukapo zotani?
8 Lingalirani za Timoteo, amene analandira chichirikizo kuchokera ku mitengo iŵiri yochirikiza yozikika mwamphamvu, titero kunena kwake—amake ndi agogo ake aakazi. Popeza kuti atate a Timoteo anali Mgiriki ndipo mwachionekere osakhulupirira, amake achiyuda, a Yunike, ndi amayi awo a Loisi ndiwo amene anaphunzitsa mnyamatayo ‘malembo opatulika kuyambira ukhanda.’ (2 Timoteo 1:5; 3:15; Machitidwe 16:1) Khama lawo pophunzitsa Timoteo—ngakhale pamene anali khanda—“zodabwiza zake zimene [Yehova] anazichita” linafupidwa kwambiri. (Salmo 78:1, 3, 4) Timoteo anakhala mmishonale ku maiko akutali, mwinamwake pamene anali akali kamnyamata, ndipo anadziŵika pa kulimbitsa mipingo yachikristu yoyambirira—Machitidwe 16:2-5; 1 Akorinto 4:17; Afilipi 2:19-23.
9. Kodi ana angaphunzire motani kupeŵa misampha ya kukonda chuma?
9 Makolo, kodi ndinu mitengo yochirikiza yotani? Mwachitsanzo, kodi mukufuna kuti ana anu akulitse lingaliro loyenera la zinthu zakuthupi? Pamenepo muyenera kupereka chitsanzo chabwino cha kusalondola ziŵiya zonse zamakono kapena zinthu zina zimene simukufunikira kwenikweni. Ngati musankha kulondola mapindu akuthupi, musadabwe pamene ana anu akukutsanzirani. (Mateyu 6:24; 1 Timoteo 6:9, 10) Indedi, ngati mitengo yochirikizira ili yosawongoka, kodi kamtengo kanthete kangakule bwanji mowongoka?
10. Kodi makolo ayenera kufuna chitsogozo cha yani nthaŵi zonse, ndipo ayenera kukhala ndi maganizo otani?
10 Makolo amene amakondwera mwa ana awo amafunafuna thandizo la Mulungu mosalekeza powaphunzitsa, nthaŵi zonse akumalingalira mkhalidwe wauzimu wabwino koposa wa ana awo. Nakubala wina wa ana anayi anasimba kuti: “Ngakhale pamene ana athu anali asanabadwe, tinali kupemphera kwa Yehova nthaŵi zonse kuti atithandize kukhala makolo abwino, kutsogoleredwa ndi Mawu ake, ndi kuwagwiritsira ntchito m’moyo wathu.” Anawonjezera kuti: “Mawu akuti ‘Yehova ndiye woyamba’ sanangokhala mawu wamba koma moyo umene tinatsatira.”—Oweruza 13:8.
Kuthirira “Madzi” Nthaŵi Zonse
11. Kodi timitengo tanthete ndi ana omwe zimafuna chiyani kuti zikule?
11 Timitengo tanthete makamaka timafuna kuthirira madzi kosalekeza, monga momwe mitengo yomakula bwino m’mbali mwa mtsinje imasonyezera. (Yerekezerani ndi Chivumbulutso 22:1, 2.) Nawonso makanda amakula bwino mwauzimu ngati akuthiriridwa nthaŵi zonse ndi madzi a choonadi cha Baibulo. Koma makolo afunikira kulingalira za utali wa nyengo ya kupereka chisamaliro cha kumvetsera cha mwana wawo. Mwinamwake nyengo zazifupi zochitidwa moŵirikiza za malangizo zingakhale zothandiza kwambiri kuposa nyengo zoŵerengeka zazitali. Musaderere phindu la nyengo zazifupi zimenezo. Kuthera nthaŵi pamodzi kwa kholo ndi mwana nkofunika kwambiri kuti pakhale chikondi chomangirira pakati pawo, kuyandikirana kumene Malemba amalimbikitsa mobwerezabwereza.—Deuteronomo 6:6-9; 11:18-21; Miyambo 22:6.
12. Kodi phindu la kupemphera ndi ana nlotani?
12 Imodzi ya nyengozo ndi ana ingakhaleko nthaŵi yokagona. Wachichepere wina akukumbukira kuti: “Makolo anga anali kukhala kumapeto kwa mbedi wathu usiku uliwonse ndi kutimvetsera popereka mapemphero athu.” Ponena za phindu la kuchita zimenezi, wina anati: “Zimenezo zinayambitsa mwa ine chizoloŵezi cha kupemphera kwa Yehova usiku uliwonse ndisanagone.” Pamene ana amva makolo awo akulankhula za Yehova ndi kupemphera kwa iye tsiku ndi tsiku, amakhala munthu weniweni kwa iwo. Mnyamata wina anati: “Ndinkatseka maso anga popemphera kwa Yehova ndi kuona munthu wonga agogo aamuna enieni. Makolo anga anandithandiza kuona kuti Yehova amachita mbali yaikulu mu zonse zimene timachita ndi kunena.”
13. Kodi nyengo za malangizo zokhazikika zingaphatikizeponji?
13 Kuti athandize ana kuloŵetsa madzi a choonadi cha Baibulo, makolo angaphatikizepo zinthu zambiri zothandiza m’nyengo zokhazikika za malangizo. Makolo ena a ana aŵiri omasinkhuka anati: “Ana aŵiri onse anayamba kuphunzitsidwa kukhala chete m’Nyumba ya Ufumu kuyambira pa milungu yawo yoyamba yoŵerengeka ya moyo.” Atate wina anafotokoza zimene banja lake linachita kuti: “Tinalemba mabuku onse a Baibulo pa makhadi ndi kuyeseza kuwaika m’dongosolo lake, tonsefe tikumalandizana. Ana nthaŵi zonse anali kuyembekezera zimenezi.” Mabanja ambiri panyengo za chakudya kapena pambuyo pake amaphatikizapo malangizo achidule. Atate wina anati: “Nthaŵi ya chakudya chamadzulo yakhala bwino kwa ife pa kukambitsirana lemba latsiku.”
14. (a) Kodi ndi zochita ziti zofupa mwauzimu zimene mungachite ndi ana? (b) Kodi ana akhoza kuphunzira zotani?
14 Achichepere amakondanso kumvetsera nkhani za m’Baibulo zotenga mtima za mu Bukhu Langa la Nkhani za Baibulo.a “Pamene anawo anali aang’ono,” akutero makolo ena, “tinali kuphunzira nkhani ya m’buku la Nkhani za Baibulo, ndipo anawo anali kuvala mikanjo namayesezera anthu ake monga seŵero laling’ono. Anakonda zimenezi ndipo kaŵirikaŵiri anali kuumirira kuti tichite nkhani zoposa pa imodzi m’phunziro limodzi.” Musaderere kukhoza kwa kuphunzira kwa mwana wanu! Ana a zaka zinayi aloŵeza pamtima mitu yathunthu ya m’buku la Nkhani za Baibulo ndipo aphunzira kuŵerenga ngakhale Baibulo! Wachichepere wina akukumbukira kuti pamene anali ndi zaka ngati zitatu ndi theka, anali kubwerezabwereza kutchula mawuwo “maweruzo” molakwa, koma atate wake anamlimbikitsa kupitiriza kuyeseza.
15. Kodi ndi zinthu zotani zimene mungaphatikize m’kukambitsirana ndi ana, ndipo pali umboni wotani wosonyeza kuti kukambitsirana kotero kuli kwaphindu?
15 Nyengo zimene mumalinganiza ndi ana anu mungazigwiritsirenso ntchito kuwakonzekeretsa kuti agaŵire ena madzi a choonadi, monga ngati mwa kupereka ndemanga pamisonkhano. (Ahebri 10:24, 25) “Mkati mwa nyengo zathu za kuyeseza, ndinali kupereka ndemanga m’mawu angaanga,” akukumbukira motero wachichepere wina. “Sindinaloledwe kungoŵerenga mosazindikira.” Ndiponso, ana angaphunzitsidwe kukhala ndi phande latanthauzo mu utumiki wakumunda. Mkazi wina amene analeredwa ndi makolo owopa Mulungu analongosola kuti: “Sitinali ongotsatira makolo athu chabe mu ntchito yawo. Tinadziŵa kuti tinafunikira kukhalamo ndi phande, ngakhale ngati kunali kuliza belu chabe ndi kusiya handibilu. Mwa kukonzekera mosamala pasadakhale zochita pa kutha kwa mlungu uliwonse, tinkadziŵa zimene titi tikalankhule. Sitinadzukepo mmaŵa wa Loŵeruka uliwonse tikumafunsa kaya ngati tidzapita ku utumiki. Tinkadziŵa kuti tipita.”
16. Kodi nchifukwa ninji kusadumphadumpha pochititsa phunziro labanja ndi ana kuli kofunika?
16 Kufunika kwa kuthirira ana ndi madzi a choonadi cha Baibulo nthaŵi zonse sitingakugogomezere mwina, zimene zimatanthauza kuti phunziro la Baibulo la banja nlofunika kwambiri. Atate wina wa ana aŵiri akunena kuti “chinthu chachikulu chimene chimakwiyitsa ana ndicho kudumphadumpha.” (Aefeso 6:4) Iyeyo anati: “Ine ndi mkazi wanga tinasankha tsiku ndi nthaŵi ndipo tinachita phunziro labanja mokhulupirika mogwirizana ndi mndandanda umenewo. Sikunatenge nthaŵi yaitali kuti ana ayambe kuliyembekezera panthaŵiyo.” Kuphunzitsa konseko kuyambira paukhanda nkofunika, mogwirizana ndi choonadi chakuti, ‘Mtengo umakula molingana ndi mmene mphukira yake imasamaliridwira.’
17. Kodi nchiyani chimene chili chofunika mofanana ndi kugaŵira ana choonadi cha Baibulo?
17 Kuphunzitsa ana choonadi cha Baibulo nkofunika, koma chitsanzo chamakolo nachonso nchofunika mofananamo. Kodi ana anu amakuonani mukuphunzira, kufika pamisonkhano mokhazikika, kukhala ndi phande mu utumiki wakumunda, inde, kukondwera ndi kuchita chifuniro cha Yehova? (Salmo 40:8) Nkofunika kwambiri kuti azitero. Chifukwa chake, mwana wina wamkazi wa nakubala amene anapirira chitsutso cha mwamuna wake ndi amene analera ana asanu ndi mmodzi nakhala Mboni zokhulupirika anati ponena za amake: “Chimene chinatichititsa chidwi koposa chinali chitsanzo cha Amayi iwo eni.—chinapereka uthenga wamphamvu kuposa mawu.”
Kutetezera Anawo
18. (a) Kodi makolo angapereke motani kwa ana awo chitetezero chimene amafuna? (b) Kodi ana a mu Israyeli analandira malangizo amtundu wanji onena za ziŵalo zathupi zobalira?
18 Monga momwe timitengo tanthete timafunira chitetezero pa tizilombo tangozi, ana amafunikira kutetezeredwa pa “anthu oipa” m’dongosolo lino la zinthu loipa. (2 Timoteo 3:1-5, 13) Kodi makolo angapereke motani chitetezero chimenechi? Mwa kuwathandiza kupeza nzeru ya Mulungu! (Mlaliki 7:12) Yehova analamulira Aisrayeli—kuphatikizapo “ana” awo—kumvetsera kuŵerengedwa kwa Chilamulo chake, chimene chinaphatikizapo kudziŵikitsidwa kwa khalidwe la kugonana loyenera ndi losayenera. (Deuteronomo 31:12; Levitiko 18:6-24) Ziŵalo zathupi zobalira zikutchulidwa mobwerezabwereza, kuphatikizapo “mavalo” ndi “mpheto.” (Levitiko 15:1-3, 16, NW; 21:20, NW; 22:24, NW; Numeri 25:8; Deuteronomo 23:10) Chifukwa cha kuipa komkitsa kwa dziko lamakono, ana afunikira kuzindikira kugwiritsiridwa ntchito koyenera ndi kosayenera kwa ziŵalo zimenezo za m’thupi zimene zaphatikizidwa m’chilengedwe chimene Mulungu anatcha kuti ‘chabwino kwambiri.’—Genesis 1:31, NW; 1 Akorinto 12:21-24.
19. Kodi ndi malangizo oyenera otani amene ana ayenera kupatsidwa onena za ziŵalo zawo zathupi zobisika?
19 Moyenerera makolo onse aŵiri, kapena munthu wokula msinkhu wolera mwana, ayenera kudziŵitsa mwanayo ziŵalo zake zathupi zobisika. Ndiyeno ayenera kulongosola kuti palibe munthu wina amene ayenera kuloledwa kugwira ziŵalo zimenezi. Popeza kuti ogona ana kaŵirikaŵiri amafuna kuona mmene mwana angachitire ndi njira zamachenjera, mwana ayenera kuphunzitsidwa kukana mwamphamvu ndi kunena kuti, “Ndidzakunenerani!” Phunzitsani ana anu kuti nthaŵi zonse ayenera kukuuzani za aliyense amene amayesa kuwagwiragwira mwa njira imene samafuna, mosasamala kanthu za ziwopsezo zimene anganene.
Kupereka Chilango Chachikondi
20. (a) Kodi chilango chimafanana motani ndi kudulira? (b) Kodi chilango chimakhala chotani poyamba, koma kodi zipatso zake zimakhala zotani?
20 Ana amapindula ndi chilango chachikondi, monga momwe mtengo umapindulira ndi kuduliridwa. (Miyambo 1:8, 9, NW; 4:13, NW; 13:1, NW) Pamene nthambi zosafunika zidulidwa, zina zimasonkhezereka kukula. Chotero ngati ana anu akuika malingaliro kwambiri pa chuma chakuthupi kapena kukhoterera pa mayanjano oipa kapena zosangulutsa zoipa, zikhoterero zoipa zimenezi zili ngati nthambi zofunikira kudulidwa. Ngati zidulidwa, mudzathandiza ana anu kukula m’njira yauzimu. Poyamba chilango chimenecho chingaoneke kukhala chosakondweretsa, monga momwe mtengo ungasokonezekere pamene uduliridwa. Koma zipatso zabwino za chilango ndizo kukula kosonkhezeredwa chatsopano m’njira imene mukufuna kuti mwana wanu akuliremo.—Ahebri 12:5-11.
21, 22. (a) Kodi nchiyani chimene chimasonyeza kuti chilango sichimakhala chokondweretsa kuchipereka ngakhalenso kuchilandira? (b) Kodi nchifukwa ninji makolo sayenera kuleka kupereka chilango?
21 Anthu amavomereza kuti chilango sichimakhala chokondweretsa kuchipereka ngakhalenso kuchilandira. “Mwana wanga anali kuthera nthaŵi yochulukirapo ndi wachichepere wina amene akulu anandichenjeza kuti sanali woyanjana naye wabwino,” anatero atate wina. “Ndikanayenera kuchitapo kanthu mwamsanga kuposa mmene ndinachitira. Ngakhale kuti mwana wangayo sanaloŵetsedwe m’tchimo lina loonekeratu, kumsintha maganizo ake kunatenga nthaŵi.” Mwanayo anati: “Pamene anandiletsa kuyanjana ndi bwenzi langa lapamtima, ndinapsinjika mtima kwambiri.” Koma anawonjezera kuti: “Chimenechi chinali chosankha chabwino, pakuti pambuyo pake pasanapite nthaŵi iyeyo anachotsedwa.”
22 “Zidzudzulo za mwambo ndizo njira ya moyo,” amatero Mawu a Mulungu. Chotero mosasamala kanthu za mmene kungakhalire kovuta kupereka chilango, musaleke kuchipereka kwa ana anu. (Miyambo 6:23; 23:13; 29:17) M’kupita kwa nthaŵi, adzayamikira kuti munawawongolera. “Ndikukumbukira kuti ndinali kuwakwiyira kwambiri makolo anga akandilanga,” wachichepere wina akukumbukira choncho. “Ndikanakwiya kwambiridi tsopano ngati makolo anga anali atandimana chilango chimenecho.”
Mphotho Yoyenerera Kuyesayesako
23. Kodi nchifukwa ninji chisamaliro chonse chimene chimaikidwa pa ana chili choyenerera kuyesayesako?
23 Palibe chikayikiro konse pa zimenezi, ana amene makolo ndi ena, amakondwera nawo ali zipatso za kupereka chisamaliro chachikulu chachikondi chatsiku ndi tsiku. Komabe, kuyesayesa konse kumene amapereka pa iwo—kaya akhale ana akuthupi kapena ana auzimu—nkoyenerera mfupo imene angalandire. Mtumwi Yohane wokalambayo anasonyeza zimenezi pamene analemba kuti: “Ndilibe chimwemwe choposa ichi, chakuti ndimva za ana anga kuti alikuyenda m’choonadi.”—3 Yohane 4.
[Mawu a M’munsi]
a Lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
Kodi Mukukumbukira?
◻ Kodi timitengo tanthete ndi ana omwe zimafunikiranji kuti zikhale zoyamikika?
◻ Kodi ndi motani, kwenikweni, mmene makolo angakhalire monga mitengo yochirikizira yogwira mtima?
◻ Kodi nchiyani chimene chingaphatikizidwe m’nyengo za kulangiza ana achichepere, ndipo ayenera kuphunzitsidwa kukananji?
◻ Kodi mwana amapindula motani ndi chilango, monga momwe mtengo umapindulira ndi kuduliridwa?
[Mawu a Chithunzi patsamba 10]
Mwachilolezo cha Green Chimney’s Farm