Limbani Mtima pamene Chilanditso Chikuyandikira
“Ine ndili ndi iwe, ati Yehova, kukulanditsa.”—YEREMIYA 1:19.
1, 2. Kodi nchifukwa ninji banja laumunthu likufuna chilanditso?
CHILANDITSO! Liwu limenelo nlotonthoza bwanji! Kulanditsidwa kumatanthauza kupulumutsidwa, kumasulidwa pa mkhalidwe woipa wosakondweretsa. Zimenezi zikuphatikizapo ganizo la kuikidwa mumkhalidwe wabwino kwambiri ndi wokondweretsa.
2 Mmene banja laumunthu likufunira kwambiri chilanditso chimenecho panthaŵi ino! Anthu kulikonse alema ndi kulefuka chifukwa cha mavuto aakulu—a zachuma, kakhalidwe, a m’thupi, m’maganizo, ndi mumtima. Ochuluka sakhutira ndipo ngokhumudwa ndi mmene zinthu zikuyendera m’dziko ndipo angakonde ngati zinthu zingaongokere.—Yesaya 60:2; Mateyu 9:36.
“Nthaŵi Zoŵaŵitsa”
3, 4. Kodi nchifukwa ninji chilanditso chikufunika kwambiri tsopano?
3 Popeza zaka za zana la 20 zino zaona mavuto aakulu kuposa zina zilizonse, chilanditso chikufunika kwambiri tsopano kuposa ndi kalelonse. Lero, anthu oposa mamiliyoni chikwi chimodzi ali amphaŵi adzaoneni, ndipo pachiŵerengero chimenecho pamawonjezeka anthu ngati 25 miliyoni pachaka. Chaka ndi chaka ana ngati 13 miliyoni amafa ndi matenda a njala kapena pazifukwa zina zaumphaŵi—oposa 35,000 patsiku! Ndipo achikulire mamiliyoni ambiri amafa msanga ndi matenda osiyanasiyana.—Luka 21:11; Chivumbulutso 6:8.
4 Nkhondo ndi zipolowe zabutsa mavuto osaneneka. Buku lakuti Death by Government likutero kuti nkhondo, kumenyana kwa mafuko ngakhalenso kwa zipembedzo, ndi kupululutsa anthu awo kumene maboma amachita, zonsezo “zapha anthu oposa 203 miliyoni m’zaka za zana lino.” Likuwonjezanso kuti: “Akufawo angakhale anthu ngati 360 miliyoni. Zili monga ngati mtundu wathu wasakazidwa ndi Chaola chamakono. Ndipo wasakazidwa kumene, koma ndi mliri wa Mphamvu, osati wa tizolombo ayi.” Mlembi Richard Harwood anati: “Tikayerekezera ndi nkhondo zankhalwe pazaka mazana apita, zitsaliratu kutali.”—Mateyu 24:6, 7; Chivumbulutso 6:4.
5, 6. Kodi nchiyani chikupangitsa nthaŵi yathu kukhala yosautsa kwambiri?
5 Pambali pa mikhalidwe yosautsa m’zaka zamakono pakhala kuwonjezeka kwa upandu wachiwawa, chisembwere, ndi kusweka kwa mabanja. Yemwe kale anali Nduna ya Zamaphunziro ku United States, William Bennett, anatero kuti pazaka 30 chiŵerengero cha anthu ku United States chinawonjezeka ndi 41 peresenti, koma upandu wachiwawa unawonjezeka ndi 560 peresenti, ana apathengo 400 peresenti, zisudzulo 300 peresenti, ndi achinyamata odzipha 200 peresenti. Profesa wa pa Yunivesite ya Princeton, John DiIulio, Jr., anachenjeza za magulu omachuluka a achichepere “ankhalwe yonyanyitsa,” amene “amapha anthu, kuwamenya, kuchita mizambi, kulanda, kuthyola nyumba, ndi kuyambitsa zipwirikiti zoopsa m’komboni. Saopa kugwidwa, zoŵaŵa za ndende, ngakhale kuvutika chikumbumtima chawo.” M’dzikolo, mbanda ndiyo chochititsa imfa chachiŵiri pakati pa azaka 15 mpaka 19. Ndipo ana ambiri osakwanitsa zaka zinayi amafa ndi nkhanza osati matenda ayi.
6 Upandu wotero ndi chiwawa sizili chabe m’dziko lokhalo ayi. Maiko ambiri akuti mikhalidwe yotero ilikonso kwawo. Zimene zathandizira zimenezi ndizo kuwonjezeka kwa ogwiritsira ntchito anamgoneka osaloleka ndi lamulo omwe amawononga anthu mamiliyoni ambiri. Sydney Morning Herald ya ku Australia inati: “Malonda a padziko lonse ozembetsa anamgoneka akhala achiŵiri kwa malonda a zida pakupindula kwake.” Chinanso chimene chathandizira ndicho chiwawa ndi chisembwere zochuluka pawailesi yakanema. M’maiko ambiri, pamene mwana akwanitsa zaka 18, amakhala ataona ziwawa zikwi makumi ambiri pa TV ndi zisembwere zosaŵerengeka. Zimenezo zili chisonkhezero champhamvu choipitsa, pakuti umunthu wathu umaumbika ndi zimene timaloŵetsa m’maganizo athu nthaŵi zonse.—Aroma 12:2; Aefeso 5:3, 4.
7. Kodi ulosi wa Baibulo unalosera motani za mikhalidwe yoipa yomwe ilipo tsopano?
7 Baibulo linalosera mosaphonya za mkhalidwe woipa umenewu wa zochitika za m’zaka za zana lathu lino. Linatero kuti kudzakhala nkhondo padziko lonse, miliri ya matenda, njala, ndi kuwonjezeka kwa kusayeruzika. (Mateyu 24:7-12; Luka 21:10, 11) Ndipo pamene tipenda ulosi wolembedwa pa 2 Timoteo 3:1-5, umamveka ngati malipoti oulutsidwa m’nkhani masiku onse. Umasonyeza kuti nyengo yathu ino ndiyo “masiku otsiriza” ndipo umati anthu ndi ‘odzikonda okha, okonda ndalama, osamvera akuwabala, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osakhoza kudziletsa, aukali, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu.’ Ndi mmenedi dziko lakhalira lerolino. Monga anavomereza William Bennett: “Pali zizindikiro zambiri zakuti . . . kutsungula kwavunda.” Anthu afika ngakhale ponena kuti kutsungula kunatha ndi nkhondo yadziko yoyamba.
8. Nchifukwa ninji Mulungu anadzetsa Chigumula m’tsiku la Nowa, ndipo zimenezi zikugwirizana bwanji ndi tsiku lathu?
8 Mkhalidwe tsopano ngwoipa kuposa ndi m’tsiku la Nowa chisanadze Chigumula, pamene ‘dziko lapansi linadzala ndi chiwawa.’ Panthaŵiyo, anthu ambiri anakana kusiya njira zawo zoipa. Chifukwa chake, Mulungu anati: “Dziko lapansi ladzala ndi chiwawa chifukwa cha iwo.” Chigumula chinawononga dziko lachiwawalo.—Genesis 6:11, 13; 7:17-24.
Chilanditso Sichingachokere kwa Anthu
9, 10. Nchifukwa ninji sitiyenera kuyembekezera kuti anthu adzapereka chilanditso?
9 Kodi anthu ndi zochita zawo angatilanditse ku mikhalidwe yoipa imeneyi? Mawu a Mulungu amayankha kuti: “Musamakhulupirira zinduna, kapena mwana wa munthu, amene mulibe chipulumutso mwa iye.” “Sikuli kwa munthu woyenda kulongosola mapazi ake.” (Salmo 146:3; Yeremiya 10:23) Mbiri ya zaka zikwi zambiri yatsimikiza kuti zimenezo nzoona. Anthu ayesa njira iliyonse yandale, zachuma, ndi kakhalidwe yomwe aganiza, koma mikhalidwe ikuipiraipira. Ikanakhalako njira yaumunthu yothetsera mavuto, ikanaoneka kale. M’malo mwake, choonadi nchakuti “wina apweteka mnzake pomlamulira.”—Mlaliki 8:9; Miyambo 29:2; Yeremiya 17:5, 6.
10 Zaka zingapo zapitazo, yemwe kale anali phungu wa zachitetezo wa dziko la United States, Zbigniew Brzezinski, anati: “Zimene munthu mosapeŵeka anganene atapenda mwanjira iliyonse zochitika za padziko lonse moona mtima nzakuti kusokonezeka kwa kakhalidwe ka anthu, chipolowe cha ndale, mavuto a zachuma, ndi kugwebana kwa maiko zidzafalikira kwambiri.” Anawonjeza kuti: “Chinthu choopsa chomwe anthu akuyang’anizana nacho [ndi] chipwirikiti padziko lonse.” Mawu amenewo osonyeza mkhalidwe wa dzikoli ngatanthauzo kwambiri lerolino. Ponena za nyengo ino ya chiwawa chochuluka, nkhani ya mkonzi m’nyuzipepala ya ku New Haven, Connecticut, ya Register inati: “Zikuoneka kuti tafika patali kwambiri kwakuti sitikhoza kuziletsa.” Inde, kunyonyotsoka kwa dzikoli sikudzaletseka ayi, pakuti ulosiwo wa ‘masiku ano otsiriza’ unanenanso kuti: “Anthu oipa ndi onyenga, adzaipa chiipire, kusokeretsa ndi kusokeretsedwa.”—2 Timoteo 3:13.
11. Nchifukwa ninji anthu ndi khama lawo sadzasintha mikhalidwe yomaipiraipirayi?
11 Anthu sangasinthe mikhalidwe imeneyi chifukwa Satana ndiye “mulungu wa nthaŵi ino ya pansi pano.” (2 Akorinto 4:4) Inde, “dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.” (1 Yohane 5:19; onaninso Yohane 14:30.) Chifukwa chake Baibulo limati za tsiku lathu: “Tsoka mtunda ndi nyanja, chifukwa Mdyerekezi watsikira kwa inu, wokhala nawo udani waukulu, podziŵa kuti kamtsalira kanthaŵi.” (Chivumbulutso 12:12) Satana akudziŵa kuti kulamulira kwake ndi dziko lake zili pafupi kutha, choncho ali monga “mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire.”—1 Petro 5:8.
Chilanditso Chayandikira—Cha Yani?
12. Kodi nchilanditso cha yani chimene chayandikira?
12 Mikhalidwe yomavuta kwambiri padziko lapansi ili umboni wapadera wakuti kusintha kwakukulu—inde, chilanditso chopambana—chayandikira kwambiri! Cha yani? Chilanditso chikuyandikira cha aja osamala machenjezo amenenso akuchitapo kanthu moyenera. Yohane woyamba 2:17 akusonyeza zomwe ayenera kuchita: ‘Dziko lapansi [dongosolo la zinthu la Satana] lipita, ndi chilakolako chake; koma iye amene achita chifuniro cha Mulungu akhala ku nthaŵi zonse.’—Onaninso 2 Petro 3:10-13.
13, 14. Kodi Yesu anasonyeza motani kuti tifunika kudikira?
13 Yesu analosera kuti anthu oipa alero adzasesedwa posachedwa panthaŵi ya mavuto “monga sipadakhale otero kuyambira chiyambi cha dziko, kufikira tsopano, inde ndipo sipadzakhalanso.” (Mateyu 24:21) Nchifukwa chake anachenjeza kuti: “Mudziyang’anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha; pakuti lidzatero ndi kufikira anthu onse akukhala pankhope pa dziko lonse lapansi. Koma inu dikirani nyengo zonse, ndi kupemphera, kuti mukalimbike kupulumuka zonse zimene zidzachitika.”—Luka 21:34-36.
14 Amene ‘akudziyang’anira’ ndi ‘kudikira’ adzafunafuna chifuniro cha Mulungu ndi kuchichita. (Miyambo 2:1-5; Aroma 12:2) Ameneŵa ndiwo ‘adzalimbika kupulumuka’ chiwonongeko chimene posachedwa chidzadza pa dongosolo la Satana. Ndipo ali ndi chidaliro chonse chakuti adzalanditsidwa.—Salmo 34:15; Miyambo 10:28-30.
Mlanditsi Wamkulu
15, 16. Kodi Mlanditsi wamkulu ndani, ndipo nchifukwa ninji tikutsimikiza kuti ziweruzo zake zidzakhala zolungama?
15 Kuti atumiki a Mulungu alanditsidwe, Satana ndi dongosolo lake lonse la zinthu padziko ayenera kuchotsedwapo. Zimenezi zidzafuna mlanditsi wamphamvu kwambiri kuposa anthu. Ameneyo ndi Yehova Mulungu, Mfumu Yaikulu, Mlengi wamphamvuyonse wa chilengedwe chonse choopsachi. Iyeyo ndiye Mlanditsi wamkulu: “Ine, Inetu ndine Yehova; ndipo palibe Mpulumutsi, koma Ine ndekha.”—Yesaya 43:11; Miyambo 18:10.
16 Yehova ali ndi mphamvu zonse, nzeru, chilungamo, ndi chikondi. (Salmo 147:5; Miyambo 2:6; Yesaya 61:8; 1 Yohane 4:8) Chotero pamene adzapereka ziweruzo zake, tikutsimikiza kuti zochita zake zidzakhala zolungama. Abrahamu anafunsa nati: “Kodi sadzachita zoyenera woweruza wa dziko lonse lapansi?” (Genesis 18:24-33) Paulo anafuula nati: “Kodi chilipo chosalungama ndi Mulungu? Msatero ayi.” (Aroma 9:14) Yohane analemba kuti: “Inde, Ambuye Mulungu, Wamphamvuyonse, maweruziro anu ali oona ndi olungama.”—Chivumbulutso 16:7.
17. Kodi atumiki a Yehova akale anasonyeza motani chidaliro pamalonjezo ake?
17 Pamene Yehova alonjeza chilanditso, iye sadzalephera kukuchita ayi. Yoswa anati: ‘Sikadasoŵa kanthu konse ka zinthu zokoma zonse Yehova adazinena.’ (Yoswa 21:45) Solomo anati: “Sanatayika mawu amodzi a mawu ake onse abwino, amene analankhula.” (1 Mafumu 8:56) Mtumwi Paulo anatero kuti Abrahamu “sanagwedezeka chifukwa cha kusakhulupirira, . . . nakhazikikanso mumtima kuti, chimene Iye [Mulungu] analonjeza, anali nayonso mphamvu ya kuchichita.” Momwemonso Sara “anamŵerengera wokhulupirika Iye [Mulungu] amene adalonjeza.”—Aroma 4:20, 21; Ahebri 11:11.
18. Nchifukwa ninji atumiki a Yehova lerolino ali ndi chidaliro chakuti adzawalanditsa?
18 Kusiyana ndi anthu, Yehova ngwodalirika kotheratu, amasunga mawu ake. “Yehova wa makamu walumbira, nati, Ndithu monga ndaganiza, chotero chidzachitidwa; ndipo monga ndapanga uphungu, chotero chidzakhala.” (Yesaya 14:24) Chotero pamene Baibulo linena kuti “Ambuye adziŵa kupulumutsa opembedza poyesedwa iwo, ndi kusunga osalungama kufikira tsiku loweruza akalangidwe,” tingakhale ndi chidaliro chonse chakuti zimenezi zidzachitika. (2 Petro 2:9) Ngakhale pamene adani amphamvu afuna kuwononga atumiki a Yehova, iwo amalimba mtima chifukwa cha mzimu wake, wosonyezedwa ndi lonjezo lake kwa mmodzi wa aneneri ake: “Adzamenyana ndi iwe; koma sadzakuposa; chifukwa Ine ndili ndi iwe, ati Yehova, kukulanditsa.”—Yeremiya 1:19; Salmo 33:18, 19; Tito 1:2.
Zilanditso Zakale
19. Kodi Yehova anamlanditsa motani Loti, ndipo zidzafanana motani ndi nthaŵi yathu?
19 Kusimba zina za ntchito zopulumutsa za Yehova zakale kungatilimbikitse kwambiri. Mwachitsanzo, Loti ‘analema mtima’ ndi kuipa kwa Sodomu ndi Gomora. Koma Yehova anamva “kulira” kodandaulira midziyo. Panthaŵi yake, anatumiza amithenga kuti afulumize Loti ndi banja lake kutulukamo m’dera limenelo mwamsanga. Zotsatira zake? Yehova “anapulumutsa Loti wolungamayo,” ‘naisandutsa makala midzi ya Sodoma ndi Gomora.’ (2 Petro 2:6-8; Genesis 18:20, 21) Lerolinonso, Yehova akumva kulira kodandaula chifukwa cha kuipitsitsa kwa dzikoli. Amithenga ake amakono akamaliza ntchito ya umboni yofulumirayo kufikira pamene akufuna, iye adzawononga dzikoli ndi kulanditsa atumiki ake monga anachita ndi Loti.—Mateyu 24:14.
20. Fotokozani mmene Yehova analanditsira Israyeli wakale kwa Igupto.
20 Mu Igupto wakale anthu a Mulungu mamiliyoni ambiri anali akapolo. Yehova anati za iwo: “Ndamvanso kulira kwawo . . . ndidziŵa zoŵaŵitsa zawo; ndipo ndatsikira kuwalanditsa.” (Eksodo 3:7, 8) Komabe, Farao atalola anthu a Mulungu kupita, anasintha maganizo ake nawalondola pamodzi ndi asilikali ake amphamvu. Aisrayeli anaoneka ngati asoŵa kopita pa Nyanja Yofiira. Koma Mose anati: “Musaope, chirimikani, ndipo penyani chipulumutso cha Yehova, chimene adzakuchitirani lero.” (Eksodo 14:8-14) Yehova anagaŵa Nyanja Yofiira, ndipo Aisrayeli anathaŵa. Asilikali a Farao anawalondola, koma Yehova anagwiritsira ntchito mphamvu yake koti “nyanja inawamiza; anamira m’madzi aakulu ngati mtovu.” Zitatha zimenezo, Mose anafuula kuimbira Yehova nyimbo: “Afanana ndi inu ndani, wolemekezedwa, woyera, woopsa pomyamika, wakuchita zozizwa?”—Eksodo 15:4-12, 19.
21. Kodi anthu a Yehova anapulumutsidwa motani kwa Amoni, Moabu, ndi Seiri?
21 Panthaŵi ina, mitundu ya adani ya Amoni, Moabu, ndi Seiri (Edomu) inafuna kuwononga anthu a Yehova. Yehova anati: “Musaope musatenge nkhaŵa chifukwa cha [adani] aunyinji ambiri awa; pakuti nkhondoyi si yanu, koma ya Mulungu. . . . Si kwanu kuchita nkhondo. . . . Imani, nimupenye chipulumutso cha Yehova pa inu.” Yehova analanditsa anthu ake mwa kusokoneza gulu la nkhondo la adani koti anaphana okhaokha.—2 Mbiri 20:15-23.
22. Kodi ndi chilanditso chozizwitsa chotani chimene Yehova anapereka kwa Israyeli kuchokera kwa Asuri?
22 Pamene Ulamuliro wa Dziko Lonse wa Asuri unalalira Yerusalemu, Mfumu Sanakeribu anatonza Yehova mwa kuuza anthu okhala palinga kuti: “Mwa milungu yonse ya maiko awa [amene ndagonjetsa], inapulumutsa dziko lawo m’manja mwanga ndi iti, kuti Yehova adzapulumutsa Yerusalemu m’manja mwanga?” Kwa atumiki a Mulungu anati: “Musaleke Hezekiya akhulupiritse inu kwa Yehova, ndi kunena, Yehova adzatipulumutsa ndithu.” Ndiyeno Hezekiya anapempherera chilanditso mwaphamphu “kuti maufumu onse a dziko adziŵe, kuti Inu ndinu Yehova, Inu nokha.” Yehova anakantha asilikali a Asuri okwanira 185,000, ndipo atumiki a Mulungu analanditsidwa. Pambuyo pake, pamene Sanakeribu anali kulambira mulungu wake wonyenga, ana ake anamupha.—Yesaya, machaputala 36 ndi 37.
23. Kodi ndi mafunso ati okhudza chilanditso chalero amene afunika mayankho?
23 Kunena zoona tingalimbedi mtima poona mmene Yehova kale analanditsira anthu ake modabwitsa. Nanga bwanji ponena za lero? Kodi atumiki ake okhulupirika posachedwa adzaloŵa mumkhalidwe woopsa wotani umene udzafuna kuti awalanditse mozizwitsa? Nchifukwa ninji wayembekezera mpaka tsopano kuti awalanditse? Kodi mawu a Yesu adzakwaniritsidwa motani akuti: “Poyamba kuchitika izi weramukani, tukulani mitu yanu; chifukwa chiwomboledwe chanu chayandikira”? (Luka 21:28) Ndipo kodi chilanditso chidzadza motani kwa atumiki a Mulungu amene ali akufa? Nkhani yotsatira idzayankha mafunso ameneŵa.
Mafunso Obwereramo
◻ Nchifukwa ninji chilanditso chikufunika kwambiri?
◻ Nchifukwa ninji sitiyenera kuyembekezera chilanditso kwa anthu?
◻ Kodi ndani adzalanditsidwa posachedwapa?
◻ Nchifukwa ninji tili ndi chidaliro m’chilanditso cha Yehova?
◻ Kodi pali zitsanzo ziti zolimbikitsa za zilanditso zakale?
[Chithunzi patsamba 10]
Abrahamu anali pakati pa aja omwe anali ndi chidaliro chonse mwa Yehova