Kulanditsidwa ndi Kuloŵa m’Dziko Latsopano Lolungama
“Adzakondwera nawo mtendere wochuluka.”—SALMO 37:11.
1, 2. (a) Kodi chilanditso cha Yehova m’nthaŵi yathu chidzasiyana motani ndi zilanditso zakale? (b) Kodi ndi dziko lotani limene Yehova adzaloŵetsamo anthu ake?
YEHOVA ndi Mulungu wolanditsa. Kale, analanditsa anthu ake nthaŵi zambiri. Zilanditso zimenezo zinali zakanthaŵi, pakuti pazochitika zonsezo Yehova sanapereke ziweruzo zake zachikhalire pa dziko lonse la Satana. Koma m’tsiku lathu, Yehova posachedwa adzadzetsa chilanditso chachikulu koposa zonse m’malo mwa atumiki ake. Tsopano adzawononga mbali iliyonse ya dongosolo la Satana padziko lonse lapansi, ndipo adzaloŵetsa atumiki ake m’dziko latsopano lolungama lachikhalire.—2 Petro 2:9; 3:10-13.
2 Yehova akulonjeza kuti: “Katsala kanthaŵi ndipo woipa adzatha psiti: . . . Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nawo mtendere wochuluka.” (Salmo 37:10, 11) Mpaka liti? “Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.” (Salmo 37:29; Mateyu 5:5) Komabe, zisanachitike zimenezo, dzikoli lidzaona mavuto aakulu koposa, omwe silinaonepo.
“Chisautso Chachikulu”
3. Kodi Yesu anachifotokoza motani “chisautso chachikulu”?
3 Mu 1914 dzikoli linaloŵa ‘m’masiku ake otsiriza.’ (2 Timoteo 3:1-5, 13) Takhala m’nyengoyo zaka 83 tsopano ndipo tili pafupi ndi mapeto ake pamene, malinga ndi ulosi wa Yesu, zotsatirazi zidzachitika: “Padzakhala masauko aakulu [“chisautso chachikulu,” NW], monga sipadakhale otero kuyambira chiyambi cha dziko, kufikira tsopano, inde ndipo sipadzakhalanso.” (Mateyu 24:21) Inde, choposa ngakhale Nkhondo Yadziko II, pamene anthu okwanira ngati 50 miliyoni anafa. Ha, nthaŵi imene ikuyandikira mofulumirayo njogwedeza dziko chotani nanga!
4. Kodi nchifukwa ninji chiweruzo cha Mulungu chikudza pa “Babulo Wamkulu”?
4 “Chisautso chachikulu” chidzafika ndi kudzidzimutsa kodabwitsa, “m’ola limodzi.” (Chivumbulutso 18:10) Chidzayamba mwa kuperekedwa kwa chiweruzo cha Mulungu pa zipembedzo zonse zonyenga, zimene Mawu a Mulungu amatcha “Babulo Waukulu [“Wamkulu,” NW].” (Chivumbulutso 17:1-6, 15) Chinthu chapadera m’Babulo wakale chinali chipembedzo chonyenga. Babulo wamakono ali monga mnzake wakale ndipo amaimira ufumu wa dziko lonse wa chipembedzo chonyenga. Wachita dama mwa kumvana ndi andale. Wachirikiza nkhondo zawo ndipo wadalitsa magulu a nkhondo omenyana kumbali zonse ziŵiri, kuchititsa anthu a chipembedzo chimodzimodzi kuphana. (Mateyu 26:51, 52; 1 Yohane 4:20, 21) Walekerera ntchito zoipa za anthu ake ndipo wazunza Akristu oona.—Chivumbulutso 18:5, 24.
5. Kodi “chisautso chachikulu” chikuyamba motani?
5 “Chisautso chachikulu” chikuyamba pamene andale aukira “Babulo Wamkulu” mwadzidzidzi. ‘Adzadana ndi mkazi wachigololoyo, nadzamkhalitsa wabwinja wausiwa, nadzadya nyama yake, nadzampsereza ndi moto.’ (Chivumbulutso 17:16) Zitatha zimenezo, achirikizi ake akale “adzalira nadzaulira maliro.” (Chivumbulutso 18:9-19) Koma atumiki a Yehova ayembekezera zimenezi nthaŵi yaitali, ndipo adzafuula kuti: “Aleluya; . . . pakuti . . . anaweruza mkazi wachigololo wamkulu, amene anaipsa dziko ndi chigololo chake, ndipo anabwezera chilango mwazi wa akapolo ake padzanja lake la mkaziyo.”—Chivumbulutso 19:1, 2.
Aukira Atumiki a Mulungu
6, 7. Kodi nchifukwa ninji atumiki a Yehova adzakhala ndi chidaliro poukiridwa mkati mwa “chisautso chachikulu”?
6 Pokhala atawononga chipembedzo chonyenga, andale aukira atumiki a Yehova. Mu ulosi, Satana, “Gogi, wa ku dziko la Magogi,” akuti: “Ndidzakwera kumka ku dziko la midzi yopanda malinga, ndidzamka kwa iwo amtendere okhala mosatekeseka.” Poganiza kuti iwo sadzavuta, iye akuwaukira ndi “nkhondo yaikulu; . . . ngati mtambo wakuphimba dziko.” (Ezekieli 38:2, 10-16) Anthu a Yehova akudziŵa kuti kuukiraku kudzalephera chifukwa iwo amakhulupirira Yehova.
7 Pamene Farao ndi magulu ake a nkhondo anaganiza kuti atsekereza atumiki a Mulungu ku Nyanja Yofiira, Yehova analanditsa anthu ake mozizwitsa nawononga magulu a nkhondo a Igupto. (Eksodo 14:26-28) Mkati mwa “chisautso chachikulu,” pamene amitundu aganiza kuti atsekereza anthu a Yehova, iye akuwapulumutsanso mozizwitsa: “Tsiku ilo, . . . ukali wanga udzakwera m’mphuno mwanga. Pakuti ndanena [“ndidzanena,” NW] mu nsanje yanga, ndi m’moto wa kuzaza kwanga.” (Ezekieli 38:18, 19) Panthaŵiyo chimake cha “chisautso chachikulu” chidzakhala pafupi!
8. Ndi zinthu zachilendo zotani zomwe zidzachitika Yehova asanawononge oipa, ndipo zotsatira zake zidzakhala zotani?
8 Panthaŵi ina “chisautso chachikulu” chitayamba, koma Yehova asanapereke chiweruzo chake pa mbali yotsala ya dzikoli, kudzachitika zachilendo. Taonani zotsatira zake. “Pomwepo padzaoneka m’thambo chizindikiro cha Mwana wa munthu [Kristu]; ndipo mitundu yonse ya padziko lapansi idzadziguguda pachifuwa, nidzapenya Mwana wa munthu alinkudza pa mitambo yakumwamba, ndi mphamvu ndi ulemerero waukulu.” (Mateyu 24:29, 30) “Kudzakhala zizindikiro pa dzuŵa ndi mwezi ndi nyenyezi; . . . anthu akukomoka ndi mantha, ndi kuyembekezera zinthu zilinkudza kudziko lapansi.”—Luka 21:25, 26.
“Chiomboledwe Chanu Chayandikira”
9. Kodi nchifukwa ninji atumiki a Yehova ‘adzatukula mitu yawo’ pamene zinthu zachilendozo zichitika?
9 Panthaŵi yomweyo, ulosi wa Luka 21:28 udzakwaniritsidwa. Yesu anati: “Poyamba kuchitika izi weramukani, tukulani mitu yanu; chifukwa chiomboledwe chanu chayandikira.” Adani a Mulungu adzanthunthumira ndi mantha chifukwa adzadziŵa kuti zinthu zachilendozo zomwe zikuchitika zachokera kwa Yehova. Koma atumiki a Yehova adzakondwera chifukwa adzadziŵa kuti chiomboledwe chawo chayandikira.
10. Kodi Mawu a Mulungu akuchifotokoza motani chimake cha “chisautso chachikulu”?
10 Ndiyeno Yehova akomola dongosolo la Satana motere: “Ndidzalimbana naye [Gogi] ndi mliri ndi mwazi; ndipo ndidzamvumbitsira iye, ndi magulu ake, . . . mvumbi waukulu, ndi matalala aakulu, moto ndi sulfure. . . . Motero adzadziŵa kuti Ine ndine Yehova.” (Ezekieli 38:22, 23) Mbali zonse za dongosolo la Satana zawonongedwa. Anthu onse onyalanyaza Mulungu afafanizidwa. Imeneyo ndiyo Armagedo, chimake cha “chisautso chachikulu.”—Yeremiya 25:31-33; 2 Atesalonika 1:6-8; Chivumbulutso 16:14, 16; 19:11-21.
11. Nchifukwa ninji atumiki a Yehova akulanditsidwa pa “chisautso chachikulu”?
11 Amene adzalanditsidwa pa “chisautso chachikulu” ndi olambira a Yehova mamiliyoni ambiri padziko lonse lapansi. Ameneŵa ndiwo “khamu lalikulu” lomwe ‘lachokera mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe.’ Nchifukwa ninji akulanditsidwa mwanjira yoopsa imeneyo? Chifukwa “amtumikira Iye [Yehova] usana ndi usiku.” Choncho apulumuka mapeto a dzikoli ndi kuloŵetsedwa m’dziko latsopano lolungama. (Chivumbulutso 7:9-15) Motero, aona kukwaniritsidwa kwa lonjezo la Yehova lakuti: “Yembekeza Yehova, nusunge njira yake, ndipo Iye adzakukweza kuti ulandire dziko: pakudulidwa oipa udzapenya.”—Salmo 37:34.
Dziko Latsopano
12. Kodi opulumuka Armagedo adzayembekeza zotani?
12 Mmene nthaŵiyo idzakhalira yosangalatsa nanga—kuipa kudzatha ndipo nyengo yaulemerero woposa m’mbiri yonse ya munthu idzayamba! (Chivumbulutso 20:1-4) Opulumuka Armagedo adzamthokozadi Yehova poloŵa m’chikhalidwe choyera ndi chabwino chopangidwa ndi Mulungu, dziko latsopano, limene lidzasanduka paradaiso! (Luka 23:43) Ndipo sadzamwaliranso nthaŵi yonse! (Yohane 11:26) Inde, kuyambira nthaŵiyo ndi mtsogolo mwake, adzakhala ndi chiyembekezo chabwino chodabwitsa chokhala ndi moyo wautali monga Yehova!
13. Kodi Yesu aiyambanso motani ntchito yochiritsa imene anayamba ali padziko lapansi?
13 Yesu, amene Yehova waika kukhala Mfumu yakumwamba, adzasamalira madalitso ozizwitsa amene olanditsidwawo adzasangalala nawo. Pamene anali padziko lapansi, anatsegula maso akhungu ndi makutu ogontha nachiritsa “nthenda iliyonse ndi zofooka zonse.” (Mateyu 9:35; 15:30, 31) M’dziko latsopano, adzaiyambanso ntchito yake ija yaikulu yochiritsa koma nthaŵiyi padziko lonse. Monga Mtumiki wa Mulungu, adzakwaniritsa lonjezo lotsatirali: “[Mulungu] adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pawo; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena choŵaŵitsa; zoyambazo zapita.” (Chivumbulutso 21:4) Sipadzafunikiranso madokotala kapena osamalira maliro!—Yesaya 25:8; 33:24.
14. Kodi ndi chilanditso chotani chomwe chidzadza kwa atumiki a Yehova omwe anafa kale?
14 Enanso omwe adzalanditsidwa ndiwo atumiki okhulupirika onse a Mulungu amene anafa kalelo. M’dziko latsopano, adzamasulidwa ku nsinga za manda. Yehova akulonjeza kuti: “Kudzakhala kuuka kwa olungama ndi osalungama.” (Machitidwe 24:15) “Olungama” ayenera kuti ndiwo adzayamba kuuka ndi kuthandiza kufutukula Paradaiso. Opulumuka Armagedo adzasangalala chotani nanga kumva zokumana nazo za okhulupirika amenewo omwe anafa kale kwambiri, omwe tsopano ali ndi moyo!—Yohane 5:28, 29.
15. Fotokozani mikhalidwe ina imene idzakhalako m’dziko latsopano.
15 Onse okhala ndi moyo nthaŵiyo adzaona zimene wamasalmo anatchula ponena za Yehova: “Muolowetsa dzanja lanu, nimukwaniritsira zamoyo zonse chokhumba chawo.” (Salmo 145:16) Sikudzakhalanso njala: Mphamvu yobala ya dziko lapansi idzabwezeretsedwa ndipo lidzatulutsa dzinthu dzochuluka. (Salmo 72:16) Sikudzakhalanso anthu osoŵa nyumba: “Iwo adzamanga nyumba ndi kukhalamo,” ndipo munthu yense adzakhala “patsinde pa mpesa wake, ndi patsinde pa mkuyu wake; ndipo sipadzakhala wakuwaopsa.” (Yesaya 65:21, 22; Mika 4:4) Sikudzakhalanso mantha: Nkhondo, chiwawa, kapena upandu sizidzakhalakonso. (Salmo 46:8, 9; Miyambo 2:22) “Dziko lonse lapuma, lili du; iwo ayamba kuimba nyimbo.”—Yesaya 14:7.
16. Nchifukwa ninji dziko latsopano lidzadzala ndi chilungamo?
16 M’dziko latsopano, njira ya Satana youlutsira manenanena idzachotsedwamo. M’malo mwake, “okhala m’dziko lapansi adzaphunzira chilungamo.” (Yesaya 26:9; 54:13) Polandira malangizo auzimu oyenera chaka ndi chaka, “dziko lapansi lidzadzala ndi odziŵa Yehova, monga madzi adzaza nyanja.” (Yesaya 11:9) Malingaliro ndi zochita za anthu onse zidzakhala zomangirira. (Afilipi 4:8) Talingalirani, chitaganya cha anthu cha dziko lonse chopanda upandu, kudzitukumula, nsanje—ubale wa dziko lonse umene onse asonyezapo zipatso za mzimu wa Mulungu. Inde, ngakhale tsopano mikhalidwe yotero akuikulitsa akhamu lalikulu.—Agalatiya 5:22, 23.
Zatenga Bwanji Nthaŵi Yaitali Chonchi?
17. Nchifukwa ninji Yehova wayembekeza nthaŵi yaitali chonchi kuti athetse kuipa?
17 Komabe, nchifukwa ninji Yehova wayembekeza nthaŵi yaitali chonchi kuti achotsepo kuipa ndi kulanditsa anthu ndi kuwaloŵetsa m’dziko latsopano? Lingalirani zimene zinayenera kukwaniritsidwa. Chofunika koposa ndicho kutsimikiza uchifumu wa Yehova, kuyenera kwake kulamulira. Mwa kulola nthaŵi yokwanira kupitapo, wasonyeza motsimikiza ndithu kuti kulamulira kwa munthu popanda uchifumu wake kwalephera koopsa. (Yeremiya 10:23) Choncho tsopano Yehova ayeneradi kuchotsapo ulamuliro wa anthu ndi kuikapo ulamuliro wa Ufumu wake wakumwamba mwa Kristu.—Danieli 2:44; Mateyu 6:9, 10.
18. Kodi ndi liti pamene mbadwa za Abrahamu zinayenera kutenga dziko la Kanani?
18 Zimene zachitika pazaka mazana ambiri zonsezi zikufanana ndi zomwe zinachitika m’nthaŵi ya Abrahamu. Yehova anauza Abrahamu kuti mbadwa zake zidzatenga dziko la Kanani—koma patapita zaka mazana anayi “pakuti mphulupulu za Aamori sizinakwaniridwe.” (Genesis 12:1-5; 15:13-16) Panopa liwulo “Aamori” (mtundu wamphamvu) liyenera kuti linaimira mitundu yonse ya Akanani. Choncho panayenera kupita zaka mazana anayi kuti Yehova alole anthu ake kulanda Kanani. Mkati mwa nthaŵiyo, Yehova analola mitundu ya ku Kanani kutukula dziko lawo. Kodi panatsatira zotani?
19, 20. Kodi ndi zitaganya zotani zomwe Akanani anamanga?
19 Bible Handbook, yolembedwa ndi Henry H. Halley, imatero kuti ku Megido, ofukula mabwinja anapeza mabwinja a kachisi wa Asitaroti, mulungu wamkazi, mkazi wake wa Baala. Akulemba kuti: “Pafupi kwambiri ndi kachisiyo panali manda, amene anapezamo mitsuko yambiri, imene munali mafupa a makanda amene anaperekedwa nsembe m’kachisi ameneyu . . . Aneneri a Baala ndi Asitaroti anali kudziŵika monga akupha ana aang’ono.” “Chizoloŵezi china chonyansa ndi [chija] ankatcha ‘nsembe za maziko.’ Pamene anafuna kumanga nyumba, anali kupereka nsembe mwana, ndipo mtembo wake anali kuuika m’khoma ndi kumangira pamodzi.”
20 Halley akuti: “Kulambira Baala, Asitaroti, ndi milungu ina yachikanani kunaphatikizapo mapwando onkitsa; akachisi awo anali nyumba zochitiramo zoipa. . . . Akanani analambira, mwa kuchita chisembwere, . . . ndiyeno, mwa kupha ana awo achisamba, monga nsembe kwa milungu imeneyo. Kukuoneka kuti, pamlingo waukulu, dziko lonselo la Kanani lidafikira kukhala monga Sodomu ndi Gomora. . . . Kodi chitaganya chauve chonyansa motero ndi nkhanza zake chinayenera konse kupitiriza kukhalapo? . . . Ofukula m’mabwinja amene amakumba mabwinja a mizinda ya Kanani amadabwa chifukwa chake Mulungu sanawawononge mwamsanga koposa ndi mmene Anachitira.”—Yerekezerani ndi 1 Mafumu 21:25, 26.
21. Kodi mkhalidwe wa Akanani ufanana bwanji ndi wa m’tsiku lathu?
21 Kuipa kwa Aamori kunali ‘kutakwanira.’ Choncho Yehova tsopano anayeneradi kuwapululutsa. Zilinso chimodzimodzi lerolino. Dzikoli ladzala ndi chiwawa, chisembwere, ndi kunyozera malamulo a Mulungu. Ndipotu popeza timachitadi kakasi ndi nsembe zonyansa za ana m’Kanani wakale, bwanji nanga za nsembe za achichepere mamiliyoni makumi ambiri m’nkhondo za dzikoli, zoposeratu kutali za ku Kanani? Inde, Yehova ayeneradi kuwononga dongosolo ili loipa.
Kukukwaniritsanso Kanthu Kena
22. Kodi kuleza mtima kwa Yehova m’nthaŵi yathu kukukwaniritsanji?
22 Kuleza mtima kwa Yehova m’masiku ano otsiriza kukukwaniritsanso kanthu kena. Walola nthaŵi yosonkhanitsa ndi kuphunzitsa khamu lalikulu, omwe aposa kale mamiliyoni asanu. Motsogozedwa ndi Yehova, iwo apanga gulu lomapitabe patsogolo. Amuna, akazi, ndi achichepere akuphunzitsidwa mmene angaphunzitsire ena choonadi cha Baibulo. M’misonkhano yawo ndi m’zofalitsa zofotokoza Baibulo, amaphunzira za njira zachikondi za Mulungu. (Yohane 13:34, 35; Akolose 3:14; Ahebri 10:24, 25) Ndiponso, akupeza maluso a zomanga, zamagetsi, kusindikiza, ndi ntchito zina kuti achirikize ulaliki wa ‘uthenga wabwino.’ (Mateyu 24:14) Maluso akuphunzitsa ndi kumanga otero angadzagwire ntchito kwambiri m’dziko latsopano.
23. Kodi nchifukwa ninji uli mwaŵi kukhala ndi moyo nthaŵi ino?
23 Inde, Yehova akukonzekeretsa atumiki ake lerolino kuti akapulumuke “chisautso chachikulu” ndi kuloŵa m’dziko latsopano lolungama. Mmenemo Satana ndi dziko lake loipa sadzakhalamonso kuti iwo azilimbana naye, ngakhalenso matenda, chisoni, ndi imfa sizidzakhalamo. Ndi chisangalalo chachikulu ndi chikondwerero, anthu a Mulungu adzapitiriza ndi ntchito yosangalatsa yomanga paradaiso, mmene tsiku lililonse lidzakhala ‘lokondweretsa.’ Ati mwaŵi kukula umene tili nawo wa kukhala ndi moyo pachimakechi cha nyengo, kumdziŵa Yehova ndi kumtumikira, ndi kudziŵa kuti posachedwapa ‘tidzatukula mitu yathu chifukwa chiomboledwe chathu chayandikira’!—Luka 21:28; Salmo 146:5.
Mafunso Obwereramo
◻ Kodi “chisautso chachikulu” nchiyani, ndipo chiyamba motani?
◻ Nchifukwa ninji kuukira atumiki a Yehova kwa Gogi kudzalephera?
◻ Kodi “chisautso chachikulu” chikutha motani?
◻ Kodi ndi mapindu otani abwino kwambiri amene dziko latsopano lidzapereka?
◻ Nchifukwa ninji Yehova wayembekeza nthaŵi yaitali chonchi kuti abweretse mapeto a dongosololi?
[Chithunzi patsamba 16]
Dziko lonse lapansi lidzasanduka paradaiso