Kuzindikira Pulinsipulo Kumasonyeza Uchikulire
MAYANJANO oipa aipsa makhalidwe okoma. Udzatuta chomwe wachifesa. (1 Akorinto 15:33; Agalatiya 6:7) Kaya mwakuthupi kapena mwauzimu, mawu onse amenewo ali chitsanzo cha choonadi chachikulu—pulinsipulo—ndipo mawu onse amenewo ali maziko a malamulo. Ngakhale zili tero, malamulo amadza ndi kuchoka, ndipo amalunjika pachinthu chakutichakuti. Komabe, mapulinsipulo amakhudza zinthu zambiri ndipo angakhalepo kosatha. Choncho, Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kuti nthaŵi zonse ngati nkotheka tizilingalira za mapulinsipulo.
Webster’s Third New International Dictionary imamasulira pulinsipulo kukhala “choonadi chachidziŵikire kapena chachikulu: lamulo lokhudza zinthu zambiri ndiponso lalikulu, ndiponso chiphunzitso, kapenanso lingaliro pa zimene malamulo, ziphunzitso ndi malingaliro enawo azikidwapo kapena kumene achokera.” Mwachitsanzo, kwa mwana munthu angapereke lamulo lakuti, “Usagwire chitofu.” Koma kwa munthu wamkulu mawu akuti, “Chitofu nchotentha” ngokwanira. Onani kuti mawu achiŵiriwa amakhudza zambiri. Popeza akulamulira zimene ungachite—kaya kuphika, kuotcha kapena kuzima chitofu—kwenikweni amakhala pulinsipulo.
Zoona, mapulinsipulo aakulu a m’moyo ngauzimu; amalamulira kulambira kwathu Mulungu ndi chimwemwe chathu. Komabe ena, amapeŵa kuyesayesa kofunikira kuti aganizire za mapulinsipulo. Pamene ayenera kupanga chosankha, iwo amakonda kusankhapo lamulo. Zimenezi nzosayenera ndipo zimasemphana ndi chitsanzo chimene amuna akale okhulupirika a m’nthaŵi za Baibulo anapereka.—Aroma 15:4.
Amuna a Mapulinsipulo Aumulungu
Mwa anthu opanda ungwiro, Abele angatchedwe kuti munthu woyamba wa mapulinsipulo aumulungu. Ayenera kuti anaganiza kwambiri za lonjezo lonena za “mbewu” ndipo anazindikira kuti kuomboledwa ku uchimo kudzafunikira nsembe yamwazi. (Genesis 3:15) Choncho anapereka kwa Mulungu “mwana woyamba wa nkhosa zake.” Mawu akuti “ndi mafuta omwe” amasonyeza kuti Abele anapatsa Yehova nkhosa zabwino koposa zomwe anali nazo. Komabe, panali kudzapita zaka zikwi ziŵiri pambuyo pa imfa ya Abele kuti Mulungu apereke malangizo atsatanetsatane okhudza nsembe kwa nthaŵi yoyamba. Mosiyana ndi Abele munthu wa mapulinsipulo woopa Mulungu, mbale wake Kaini anapereka nsembe yachiphamaso kwa Mulungu. Koma mzimu wake sunali wokhutiritsa, kanthu kena pansembe zake kanasonyeza mtima wopanda mapulinsipulo.—Genesis 4:3-5.
Nayenso Nowa anali munthu wa mapulinsipulo aumulungu. Pamene kuli kwakuti mbiri ya m’Baibulo imasonyeza kuti Mulungu anangomlamula kuti amange chingalaŵa, sitimaŵerengapo za lamulo lililonse kwa iye lakuti alalikire kwa ena. Komabe, Nowa amatchedwa kuti “mlaliki wa chilungamo.” (2 Petro 2:5) Ngakhale kuti mwina Mulungu anamlangiza Nowa kuti alalikire, mosakayikira kuzindikira kwake pulinsipulo lake ndi chikondi chake cha pa mnansi zinamsonkhezeranso kuchita motero. Popeza tikukhala m’nthaŵi zofanana ndi za Nowa, tiyeni titsatire mzimu wake wabwino ndi chitsanzo chake.
Mosiyana ndi atsogoleri achipembedzo a m’tsiku lake, Yesu anaphunzitsa anthu kumalingalira za mapulinsipulo. Ulaliki wake wa pa Phiri ndiwo chitsanzo chake. Mkhalidwe wake wonse umasonyeza kufunika kwa kugwiritsira ntchito mapulinsipulo. (Mateyu, machaputala 5-7) Yesu anaphunzitsa motere chifukwa chakuti, monga Abele ndi Nowa omwe analiko iye asanadze, iye anamdziŵadi Mulungu. Ngakhale pamene anali mnyamata, analemekeza choonadi chachikuluchi: “Munthu sakhala wamoyo ndi mkate wokha, koma . . . ndi zonse zakutuluka mkamwa mwa Yehova.” (Deuteronomo 8:3; Luka 2:41-47) Inde, mfungulo yokhalira munthu wa mapulinsipulo aumulungu ndiyo kumdziŵadi Yehova, kudziŵa zomwe amakonda, zomwe amadana nazo, ndi zifuno zake. Pamene mapulinsipulo aakulu a Mulungu ameneŵa alamulira miyoyo yathu, kwenikweni, amakhala mapulinsipulo ogwiradi ntchito.—Yeremiya 22:16; Ahebri 4:12.
Mapulinsipulo ndi Mtima
Zimatheka kuti nkumvera lamulo koma mosafunitsitsa, mwina chifukwa choopa chilango cha kusamvera. Komabe, kutsatira pulinsipulo kumachotserapotu mzimu umenewu, popeza ndi mmene mapulinsipulo akhalira kuti kuwatsatira ndiko kuwamvera mochokera mumtima. Talingalirani za Yosefe amene, monga Abele ndi Nowa, analiko pangano la Chilamulo cha Mose lisanakhaleko. Mkazi wa Potifara atayesa kumnyengerera, Yosefe anayankha kuti: “Ndikachita choipa chachikulu ichi bwanji ndi kuchimwira Mulungu?” Inde, Yosefe anadziŵa pulinsipulo lakuti mwamuna ndi mkazi wake ndi “thupi limodzi.”—Genesis 2:24; 39:9.
Lerolino dziko lilibiretu mapulinsipulo olungama. Limadya chiwawa ndi makhalidwe oipa monga munthu wosusuka. Ngozi yake njakuti Mkristu angayesedwe kuti adyeko, mwina mwamtseri, zakudya zimodzimodzizo zowononga—mafilimu, mavidiyo, kapena mabuku. Choncho, kuli bwino chotani nanga, pamene monga Yosefe tikana zoipa motsatira mapulinsipulo, pokumbukira kuti pa “chisautso chachikulu” Mulungu adzangosunga okhulupirika okha. (Mateyu 24:21, NW) Inde, ndi zimene timachita kwatokha, osati poyera, zimene kwenikweni zimavumbula kuti ndifedi otani mkati mwathu.—Salmo 11:4; Miyambo 15:3.
Motero ngati timatsogozedwa ndi mapulinsipulo a Baibulo, sitidzafunafuna njira zopeŵera malamulo a Mulungu; ndiponso sitidzayesa kuona kuti tingafike pati tisanaswe lamulo lakutilakuti. Maganizo otero amagwiritsa mwala ife tomwe; pomalizira pake amatipweteka.
Dziŵani Cholinga cha Lamulo
Zoona, malamulo ngofunika kwambiri pamoyo wa Mkristu. Ali ngati alonda othandizira kutiteteza, ndipo pamaziko ake pali mapulinsipulo ambiri ofunika. Kusaona mapulinsipulo ameneŵa kungathetse chikondi chathu cha malamulo okhudzana nawo. Mtundu wakale wa Israyeli unasonyeza zimenezi.
Mulungu anapatsa Israyeli Malamulo Khumi, amene lamulo lake loyamba linaletsa kulambira mulungu aliyense kusiyapo Yehova. Choonadi chachikulu cha lamulo ili ndicho chakuti Yehova ndiye analenga zinthu zonse. (Eksodo 20:3-5) Koma kodi mtunduwo unalitsatira pulinsipulo limeneli? Yehova iye mwini akuyankha kuti: “‘Ndinu atate wathu’ [anatero Aisrayeli] kwa mtengo wosema ndipo [anafuula kuti] ‘Amayi’ kwa mwala. Koma andifulatira ine [Yehova] ndipo andibisa nkhope zawo.” (Yeremiya 2:27, The New English Bible) Ndi kupusa kouma khosi ndi kopanda mapulinsipulo kotani nanga! Ndipo kunapweteketsa mtima wa Yehova chotani nanga!—Salmo 78:40, 41; Yesaya 63:9, 10.
Akristu nawonso ali ndi malamulo ochokera kwa Mulungu. Mwachitsanzo, ayenera kupeŵa kulambira mafano, chisembwere, ndi kugwiritsira ntchito mwazi mosayenera. (Machitidwe 15:28, 29) Mutalingalira zimenezi, titha kuona mapulinsipulo ake, monga akuti: Mulungu amafuna kulambira kwathu kosagaŵanika; tiyenera kukhala okhulupirika kwa mnzathu wa muukwati; ndiponso Yehova ndiye Wotipatsa Moyo. (Genesis 2:24; Eksodo 20:5; Salmo 36:9) Ngati timazindikira ndi kumvetsanso kwambiri mapulinsipulo a malangizo ameneŵa, timaona kuti ndi otipindulitsa ife eni. (Yesaya 48:17) Kwa ife, “malamulo [a Mulungu] sali olemetsa.”—1 Yohane 5:3.
Pamene kuli kwakuti nthaŵi ina yake Aisrayeli ananyalanyaza malamulo a Mulungu, podzafika m’nthaŵi ya Yesu “akatswiri [awo] a lamulo,” alembi, anali atawonjezerapo malamulo ambirimbiri. Iwo anapanga malamulo ambirimbiri ndi miyambo zimene zinaphimba kulambira koyera ndi kubisa mapulinsipulo aumulungu. (Mateyu 23:2, NEB) Anthu anangolefuka, kusoŵeratu chiyembekezo, kapena anangokhala akapolo a chinyengo. (Mateyu 15:3-9) Ndipo malamulo ambiri opangidwa ndi anthu anali osachitira chifundo ena. Pamene anali pafupi kuchiritsa mwamuna wina wadzanja lopuwala, Yesu anafunsa Afarisi amene analipo kuti: “Kodi nkuloledwa dzuŵa la Sabata kuchita zabwino.” Kusayankha kwawo kunasonyeza kuti akana, kupangitsa Yesu kumva “chisoni chifukwa cha kuuma kwa mitima yawo.” (Marko 3:1-6) Afarisi ankatha kuthandiza chiŵeto (chimene chili chuma) chotayika kapena chovulala pa Sabata koma osati kuthandiza mwamuna kapena mkazi—koma mwina atakhala pafupi kufa. Ndithudi, iwo anakondetsa malamulo a anthu moti monga nyerere zothamangathamanga pachithunzithunzi, analephera kuona chithunzithunzi chonse—mapulinsipulo a Mulungu.—Mateyu 23:23, 24.
Komabe, ngakhale ana aang’ono, pamene ali oona mtima, angadzetse ulemerero kwa Yehova mwa kuzindikira kwawo mapulinsipulo a Baibulo. Mwachitsanzo, pali Rebecca wazaka khumi ndi zitatu. Mphunzitsi wake anafunsa kalasi amene angatchove juga. Ambiri ananena kuti sangatchove. Komabe, pamene anatchula mikhalidwe yosiyanasiyana, onse kusiyapo Rebecca yekha anavomereza kuti angatchove juga m’njira ina yake. Mphunzitsiyo anafunsa Rebecca ngati angagule tikiti ya masenti 20 yochitira mpikisano kuti ndalamazo zikagwiritsiridwe ntchito pachinthu chopindulitsa. Rebecca anakana ndipo anapereka zifukwa za m’Malemba zosonyeza chifukwa chake kumeneko kungakhale kutchova juga kwa mtundu wina. Kenako mphunzitsi wake anati kwa kalasi lonse: ‘Kwa ineyo, Rebecca ndiye yekha muno amene ali ndi zimene ndimati “mapulinsipulo” enieni.’ Inde, Rebecca akanangoyankha kuti, “Chipembedzo changa sichilola zimenezo,” koma anaganiza kwambiri kuposa zimenezo; anatha kuyankha chifukwa chake kutchova juga nkulakwa ndi chifukwa chimene anakanira kutengamo mbali.
Zitsanzo monga za Abele, Nowa, Yosefe, ndi Yesu zimatisonyeza mmene timapindulira mwa kugwiritsira ntchito “luso [lathu] la kulingalira” ndi “mphamvu [yathu] ya kulingalira” polambira Mulungu. (Miyambo 2:11, NW; Aroma 12:1, NW) Akulu achikristu amachita bwino kutsanzira Yesu pamene ‘akuŵeta gulu la Mulungu lili mwa iwo.’ (1 Petro 5:2) Monga momwe Yesu anaperekera chitsanzo chabwino, amene amakonda mapulinsipulo aumulungu ndiwo amapita patsogolo mu uchifumu wa Yehova.—Yesaya 65:14.