“Mtima Wako Ngwowongoka Kodi?”
“Tiye nane, ukaone changu changa cha kwa Yehova.”—2 MAFUMU 10:16.
1, 2. (a) Kodi ndi motani mmene nkhani yachipembedzo inafikira poipiratu ku Israyeli? (b) Kodi ndi kusintha kosangalatsa kuti kumene kunali pafupi kuchitika mu Israyeli mu 905 B.C.E.?
CHAKA cha 905 B.C.E. chinali chaka chimene zinthu zinasintha kwambiri mu Israyeli. Pafupifupi zaka 100 zisanachitike zimenezi, Yehova anapangitsa kuti ufumu wogwirizana wa Israyeli ukhale wogaŵanika chifukwa cha mpatuko wa Solomo. (1 Mafumu 11:9-13) Kenaka, ufumu wakummwera, Yuda, unayamba kulamuliridwa ndi Rehabiamu, mwana wa Solomo pamene ufumu wakumpoto, Israyeli, unayamba kulamuliridwa ndi Mfumu Yerobiamu, Mwefrati. Zachisoni, ufumu wakumpoto unali ndi chiyambi choipa. Yerobiamu sanafune kuti anthu ake apite ku ufumu wakummwera kukalambirira m’kachisi, poopa kuti mwina anthuwo angaganize zobwerera kunyumba ya Davide. Choncho, iye anayambitsa kulambira ana a ng’ombe mu Israyeli ndipo potero anayambitsa kulambira mafano kumene kunachitika nthaŵi yaitali ndithu m’mbiri yonse ya ufumu wakumpoto.—1 Mafumu 12:26-33.
2 Zinthu zinafika poipa kwambiri pamene Ahabu, mwana wa Omri, analoŵa ufumu. Mkazi wake wakudziko lina, Yezebeli, anachirikiza kulambira Baala ndipo anapha aneneri a Yehova. Mosasamala kanthu za machenjezo osapita m’mbali a mneneri Eliya, Ahabu sanaletse mkazi wakeyo. Komabe, Ahabu anafa mu 905 B.C.E., ndipo Yehoramu, mwana wake, anayamba kulamulira. Tsopano imeneyi inali nthaŵi yoti dzikolo liyeretsedwe. Woloŵa m’malo mwa Eliya, Elisa, anauza kazembe wankhondo, Yehu, kuti Yehova anamdzoza kuti akhale mfumu yotsatira ya Israyeli. Ntchito yake? Kukantha nyumba yochimwa ya Ahabu ndi kubwezera mwazi wa aneneri umene unakhetsedwa ndi Yezebeli!—2 Mafumu 9:1-10.
3, 4. Kodi Yehonadabu anasonyeza motani kuti mtima wake unali ‘wovomerezana ndi mtima wa Yehu’?
3 Mogwirizana ndi lamulo la Mulungu, Yehu anapha Yezebeli woipayo, ndipo pambuyo pake ananyamuka kukayeretsa Israyeli mwa kukantha nyumba ya Ahabu. (2 Mafumu 9:15–10:14, 17) Kenaka iye anakumana ndi womthandiza. “Anakomana naye Yehonadabu mwana wa Rekabu wakudzamchingamira; namlankhula, nanena naye, Mtima wako ngwowongoka kodi, monga mtima wanga uvomerezana nawo mtima wako? Nati Yehonadabu, Momwemo. Ukatero undipatse dzanja lako. Nampatsa dzanja lake, namkweretsa pali iye pagaleta. Nati iye, Tiye nane, ukaone changu changa cha kwa Yehova. M’mwemo anamuyendetsa m’galeta wake.”—2 Mafumu 10:15, 16.
4 Yehonadabu (kapena kuti, Yonadabu) sanali Mwisrayeli. Komabe, mogwirizana ndi dzina lake (lotanthauza kuti “Yehova Akufunitsitsa,” “Yehova Ngwokwezeka,” kapena kuti “Yehova Ngwooloŵa Manja”) iye anali wolambira Yehova. (Yeremiya 35:6) Ndithudi, iye anasangalala kwambiri pamene anaona “changu cha kwa Yehova” cha Yehu. Kodi tikudziŵa bwanji zimenezi? Ndithudi, kukumana kwake ndi mfumu yodzozedwa ya Israyeli sikunachitike mwangozi. Yehonadabu ‘anamchingamira,’ ndipo panthaŵiyi Yehu anali atapha kale Yezebeli ndi anthu ena a m’nyumba ya Ahabu. Yehonadabu anadziŵa chimene chinali kuchitika pamene Yehu anamuitana kuti akwere m’galeta lake. Mosakayika konse iye anali kumbali ya Yehu—ndiponso ya Yehova—pankhondo imeneyi ya pakati pa kulambira konyenga ndi kulambira koona.
Yehu Wamakono ndi Yehonadabu Wamakono
5. (a) Kodi nkusintha kotani kumene kudzachitikira mtundu wonse wa anthu posachedwapa? (b) Kodi Yehu Wamkulu ndani, ndipo kodi ndani amene amamuimira padziko lapansi?
5 Lerolino, zinthu zidzasintha kwambiri posachedwapa mumtundu wonse wa anthu monga momwe zinachitikira Israyeli kalekale mu 905 B.C.E. Tsopano nthaŵi yayandikira yakuti Yehova ayeretse kuipa konse kwa dziko lapansi kumene kwadza chifukwa cha zotsatirapo zoipa za chisonkhezero cha Satana, kuphatikizapo chipembedzo chonyenga. Kodi Yehu wamakono ndani? Si winanso ayi koma Yesu Kristu, amene ulosi unaneneratu za iye kuti: “Dzimangireni lupanga lanu m’chuuno mwanu, wamphamvu inu, ndi ulemerero wanu ndi ukulu wanu. Ndipo pindulani, mu ukulu wanu yendani, kaamba ka choonadi ndi chifatso ndi chilungamo.” (Salmo 45:3, 4) Yesu akuimiridwa padziko lapansi ndi “Israyeli wa Mulungu,” Akristu odzozedwa “amene asunga malamulo a Mulungu, nakhala nawo umboni wa Yesu.” (Agalatiya 6:16; Chivumbulutso 12:17) Kuyambira mu 1922 abale odzozedwa ameneŵa a Yesu akhala akuchenjeza mopanda mantha za ntchito za Yehova zachiweruzo zimene zikudzazo.—Yesaya 61:1, 2; Chivumbulutso 8:7–9:21; 16:2-21.
6. Kodi ndani amene anachokera mwa mitundu kudzathandizira Akristu odzozedwa, ndipo kodi iwo akwera motani galeta, kunena kwake titero, la Yehu Wamkulu?
6 Akristu odzozedwa sali okha. Mongadi momwe Yehonadabu anachingamirira Yehu, anthu ambiri amitundu abwera kudzathandizira Yesu, Yehu Wamkulu, ndiponso oimira ake a padziko lapansi pakuchirikiza kwawo kulambira koona. (Zekariya 8:23) Yesu anawatcha kuti “nkhosa zina,” ndipo mu 1932 iwo anazindikiridwa kukhala ofanana ndi Yehonadabu wakale ndipo anaitanidwa ‘kukwera galeta’ wa Yehu wamakono. (Yohane 10:16) Motani? Mwa ‘kutsatira malamulo a Mulungu’ ndi kuthandizana ndi odzozedwa “kukhala nawo umboni wa Yesu.” M’nthaŵi zamakono, zimenezi zimaphatikizapo kulalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu wokhazikitsidwawo umene ukulamuliridwa ndi Yesu monga Mfumu. (Marko 13:10) Mu 1935 “Ayonadabu” ameneŵa anazindikiridwa kuti ndiwo “khamu lalikulu” la pa Chivumbulutso 7:9-17.
7. Kodi Akristu lerolino asonyeza motani kuti ‘mtima wawo ngwowongokabe’ mogwirizana ndi mtima wa Yesu?
7 Chiyambire m’zaka za m’ma 1930, a khamu lalikulu ndi abale awo odzozedwa asonyeza molimba mtima kuchirikiza kwawo kulambira koona. Ambiri a iwo m’maiko ena monga ku Eastern ndi Western Europe, Far East, ndiponso ku Afirika, anafa chifukwa cha chikhulupiriro chawo. (Luka 9:23, 24) M’maiko ena, iwo anaikidwa m’ndende, kuzunzidwa ndi magulu ozunza, kapena kuzunzidwa m’njira zina. (2 Timoteo 3:12) Iwo apanga mbiri yachikhulupiriro yotani nanga! Ndipo Lipoti la Chaka Chautumiki cha 1997 likusonyeza kuti iwo ali ofunitsitsabe kutumikira Mulungu, mosasamala kanthu kuti adzakumana ndi zotani. ‘Mitima yawo ili yowongokabe’ mogwirizana ndi mtima wa Yesu. Zimenezi zinaoneka m’chaka cha 1997, pamene ofalitsa Ufumu okwanira 5,599,931, pafupifupi onse a “Ayonadabu” ameneŵa, anathera maola okwanira 1,179,735,841 m’ntchito yochitira umboni wa Yesu.
Akulalikirabe Mwachangu
8. Kodi Mboni za Yehova zimasonyeza motani changu chawo cha kulambira koona?
8 Yehu anali ndi mbiri yakuti anali kuyendetsa galeta lake paliŵiro lalikulu—umboni wa changu chake pofuna kuchita ntchito yake mwachipambano. (2 Mafumu 9:20) Yesu, Yehu Wamkulu, amadziŵika kuti ‘anadyedwa’ ndi changu. (Salmo 69:9) Choncho, nzosadabwitsa kuti Akristu oona lerolino amadziŵika bwino chifukwa cha changu chawo. Ponse paŵiri, mumpingo ndiponso kwina kulikonse, iwo ‘amalalikira mawu panthaŵi yake, popanda nthaŵi yake.’ (2 Timoteo 4:2) Changu chawo chinasonyezedwa makamaka kuchiyambi kwa 1997 pamene nkhani ina mu Utumiki Wathu Waufumu inalimbikitsa kuti anthu ochuluka achite utumiki waupainiya wothandiza. M’dziko lililonse anakhazikitsa chiŵerengero cha apainiya amene anafunikira kuchita utumikiwo. Kodi zotsatirapo zake zinali zotani? Zodabwitsa! Nthambi zambiri zinapyola chiŵerengero chimene zinakhazikitsa. Ku Ecuador anakhazikitsa chiŵerengero cha 4,000 koma m’March anachitira lipoti apainiya othandiza okwanira 6,936. Ku Japan anachitira lipoti apainiya othandiza okwanira 104,215 m’miyezi yonse itatuyo. Ku Zambia, kumene anakhazikitsa chiŵerengero cha 6,000, anachitira lipoti apainiya othandiza okwanira 6,414 m’March; 6,532 mu April; ndiponso 7,695 m’May. Kuzungulira dziko lonse, chiŵerengero chapamwamba koposa cha apainiya othandiza ndi okhazikika onse pamodzi chinali 1,110,251, chiwonjezeko cha 34.2 peresenti kuposa 1996!
9. Kuwonjezera pantchito ya kunyumba ndi nyumba, kodi Mboni za Yehova zimafikira anthu m’njira zina ziti pofuna kuwauza uthenga wabwino?
9 Mtumwi Paulo anauza akulu a ku Efeso kuti: “Sindinakubisirani zinthu zopindulira, osazilalikira kwa inu, ndi kukuphunzitsani inu pabwalo ndi m’nyumba m’nyumba.” (Machitidwe 20:20) Lerolino Mboni za Yehova zimatsanzira chitsanzo cha Paulo ndipo zimalalikira uthenga wabwino mwachangu kunyumba ndi nyumba. Komabe, nthaŵi zina kumakhala kovuta kupeza anthu panyumba zawo. Choncho, “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” amalimbikitsa ofalitsa Ufumu kuti azifikira anthu m’malo awo a ntchito, m’misewu, pamagombe, m’mapaki—kulikonse kumene kungapezeke anthu. (Mateyu 24:45-47) Zotsatirapo zake zakhala zosangalatsa kwambiri.
10, 11. Kodi ofalitsa m’maiko ena aŵiri asonyeza motani njira yofunika yopezera okondwerera amene sangapezeke panyumba?
10 Ku Copenhagen, Denmark, gulu laling’ono la ofalitsa lakhala likuchitira umboni m’misewu ya kunja kwa malo okwerera sitima zapamtunda. Kuyambira m’January mpaka m’June, anagaŵira magazini okwanira 4,733, anachezera anthu ambiri, ndipo anapanga maulendo ambiri obwereza. Ofalitsa angapo m’dzikolo anakhazikitsa njira zamagazini m’masitolo. M’tauni ina mumakhala msika waukulu Lachisanu lililonse, ndipo pamabwera anthu zikwi zambiri. Choncho, mpingowo unapanga makonzedwe a kuchitira umboni pamsika nthaŵi zonse. M’dera lina amakachezera masukulu pogwiritsira ntchito zofalitsa zosiyanasiyana zimene makamaka zili zofunika kwa aphunzitsi a sukulu.
11 Ku Hawaii akuyesetsanso kufikira anthu amene sangapezeke panyumba. Ali ndi magawo ena apadera monga m’malo a anthu onse (m’misewu, m’mapaki, pamalo oimika galimoto, ndiponso pamalo okwerera basi), m’misika ya m’matauni, m’masitolo ndi m’mabwalo a ndege, kuchitira umboni wapatelefoni, m’zoyendera za onse (kulalikira m’mabasi), ndiponso m’makoleji. Amaonetsetsa kuti asamatumize Mboni zochulukitsitsa m’gawo lililonse ndipo otumizidwawo amaphunzitsidwa bwino. Maiko ambiri achitiranso lipoti kuti ayesetsanso mofananamo. Chotsatirapo chake, anthu okondwerera amene mwinamwake sakanapezeka mu utumiki wa kunyumba ndi nyumba akufikiridwa.
Kuimabe Osasunthika
12, 13. (a) Kodi Satana anagwiritsira ntchito njira yamachenjera iti potsutsa Mboni za Yehova mu 1997? (b) Kodi malipoti abodza anathandiza motani m’dziko lina?
12 M’maiko ambiri mu 1997, Mboni za Yehova anazinenera malipoti abodza ndi achiŵembu ncholinga chakuti boma liwaimbe mlandu. Koma iwo sanabwerere mmbuyo! (Salmo 112:7, 8) Iwo anakumbukira pemphero la wamasalmo lakuti: “Odzikuza anandipangira bodza: ndidzasunga malangizo anu ndi mtima wanga wonse.” (Salmo 119:69) Malipoti abodza oterowo ali umboni wakuti iwo ali Akristu oona amene akudedwa monga momwe Yesu analoserera. (Mateyu 24:9) Ndipo nthaŵi zina zotsatirapo za malipotiwo zimakhala zothandiza. Mwamuna wina ku Belgium anaŵerenga nkhani yonyoza Mboni za Yehova m’nyuzipepala ina ya tsiku ndi tsiku yodziŵika bwino. Atavutika maganizo ndi zinenezo zimenezo, iye anakafika pamsonkhano ku Nyumba ya Ufumu Lamlungu lotsatira. Iye anapempha kuti aziphunzira Baibulo ndi Mboni ndipo anapita patsogolo mofulumira. Poyamba, mwamuna ameneyu anali mmodzi wa gulu lina laupandu. Phunziro lake la Baibulo linamthandiza kuyeretsa moyo wake, ndipo anthu anaonadi zimenezi. Ndithudi, wolemba nkhani yabodzayo sanalingalire nkomwe kuti zoterezi zingachitike!
13 Anthu ena oona mtima ku Belgium analankhula molimba mtima potsutsa nkhani zabodzazo. Mmodzi wa iwo ndi amene kale anali nduna yaikulu amene anavomereza kuti anasangalala kwambiri ndi zimene Mboni za Yehova zimachita. Ndipo wachiŵiri wake analemba kuti: “Mosiyana ndi nkhani zabodza zimene zimafalitsidwa nthaŵi zina, palibe umboni uliwonse wakuti [Mboni za Yehova] zingapereke chiopsezo ku Boma. Iwo ndi nzika zokonda mtendere, anthu a chikumbumtima chabwino, ndiponso olemekeza maulamuliro.” Ndithudi, mawu awa a mtumwi Petro ngolondola: “Mayendedwe anu mwa amitundu akhale okoma, kuti, mmene akamba za inu ngati ochita zoipa, akalemekeze Mulungu pakuona ntchito zanu zabwino, m’tsiku la kuyang’anira.”—1 Petro 2:12.
Phwando Lachikumbutso Losaiŵalika
14. Kodi ndi malipoti ena osangalatsa ati onena za chiŵerengero cha anthu opezeka pa Chikumbutso mu 1997?
14 Nkoyenerera kuti awo amene amachita umboni wa Yesu aziona Chikumbutso cha imfa yake monga chochitika chofunika kwambiri cha pachaka. Mu 1997, anthu okwanira 14,322,226 anasonkhana pa March 23 kuchita phwandoli. Chiŵerengero chimenechi chinaposa cha mu 1996 ndi 1,400,000. (Luka 22:14-20) M’maiko ambiri, chiŵerengero cha anthu opezeka pa Chikumbutso chinapitirira kwambiri chiŵerengero cha ofalitsa Ufumu, kusonyeza kuti pali chiyembekezo chakuti ofalitsawo adzawonjezereka mtsogolo muno. Mwachitsanzo, chiŵerengero chapamwamba cha ofalitsa ku Haiti mu 1997 chinali 10,621, pamene anthu okwanira 67,259 ndiwo anapezeka pa Chikumbutsocho. Ngati mufuna mungaone lipoti lapachaka kuchokera patsamba 18 mpaka tsamba 21 ndipo mungaone mmene anthu ochuluka kuposa chiŵerengero cha ofalitsa anapezekera paphwando limeneli m’maiko ena.
15. Kodi abale athu m’maiko ena anathetsa motani mavuto aakulu pofuna kuchita phwando la Chikumbutso?
15 Ena anavutika kwambiri kuti apezeke pa Chikumbutso. Ku Albania analengeza kuti pasapezeke munthu woyenda itangokwana 7 koloko madzulo chifukwa chakuti kunali chipolowe. Magulu ang’onoang’ono okwanira 115 m’dziko lonselo anayamba Chikumbutsocho pa 5:45 madzulo. Nisan 14 inayamba pa 6:08, dzuŵa litaloŵa. Zizindikiro zinayamba kuyendetsedwa cha m’ma 6:15. Ambiri anapereka pemphero lomaliza cha m’ma 6:30, ndipo amene anapezekapo anapita kunyumba mofulumira 7 koloko isanakwane. Komabe, chiŵerengero cha anthu opezeka pa Chikumbutso chinali 3,154, poyerekezera ndi chiŵerengero chapamwamba cha ofalitsa chokwanira 1,090. M’dziko lina ku Afirika, anthu sanathe kupita ku Nyumba ya Ufumu chifukwa cha chipolowe, choncho akulu aŵiri anaganiza zokasonkhana m’nyumba ya mkulu wachitatu kuti akapange makonzedwe akuti phwandolo lichitikire m’magulu ang’onoang’ono. Kuti akafike kunyumbako, akulu aŵiriwo anayenera kuwoloka ngalande ya madzi. Komabe, m’deralo anali kuomberana, ndipo anali kuombera aliyense wofuna kuwoloka ngalandeyo. Mkulu mmodzi anathamanga nawoloka popanda chochitika. Mkulu wachiŵiriyo anamva kuombera kwa mfuti pamene anali kuwoloka. Iye anadzigwetsa pansi nakwaŵa, kupeŵa zipolopolo zimene zinali kudutsa pamwamba pa mutu wake. Msonkhano wa akuluwo unachitika bwinobwino, ndipo zosoŵa za mpingowo zinasamaliridwa.
“Ochokera mwa Mtundu Uliwonse, ndi Mafuko . . . ndi Manenedwe”
16. Kodi gulu la kapolo wokhulupirika ndi wanzeru lapanga makonzedwe otani pofuna kuti uthenga wabwino ulalikidwe m’magulu ang’onoang’ono a zinenero?
16 Mtumwi Yohane anafotokoza kuti khamu lalikulu lidzachokera “mwa mtundu uliwonse, ndi mafuko ndi anthu ndi manenedwe.” (Chivumbulutso 7:9) Choncho, Bungwe Lolamulira limapanga makonzedwe akuti mabuku azipezeka m’zinenero zowonjezereka—kuphatikizapo zinenero zolankhulidwa ndi mitundu yosadziŵika kwambiri ndi magulu ang’onoang’ono a anthu. Mwachitsanzo, ku Mozambique, trakiti lakuti Moyo m’Dziko Latsopano la Mtendere linatulutsidwa m’zinenero zisanu zowonjezereka. Ku Nicaragua, brosha lakuti Sangalalani ndi Moyo pa Dziko Lapansi Kosatha! linatulutsidwa m’chinenero cha Miskito—chofalitsa choyamba cha Watch Tower Society m’chinenero chimenecho. Amwenye ambiri achimiskito analandira broshalo mwachisangalalo ataona chofalitsa cha m’chinenero chawocho. Mu 1997 Sosaite inapereka chilolezo chakuti mabuku afalitsidwe m’zinenero 25 zowonjezereka ndiponso inasindikiza magazini oposa 1000,000,000.
17. Kodi ndi gulu lachinenero liti limene linathandizidwa ku Korea, ndipo ndi motani mmene mavidiyo anathandizira kwambiri gulu limeneli la anthu?
17 Ku Korea gulu lina la chinenero linathandizidwa kwambiri. Mu 1997, ku Korea kunachitika msonkhano woyamba wachigawo wa m’chinenero chachikoreya cholankhula ndi manja. Ku Korea kuli mipingo 15 ya chinenero cholankhula ndi manja ndi ofalitsa 543, koma anthu 1,174 anapezeka pamsonkhano wachigawowo, ndipo anthu 21 anabatizidwa. Kuti athandize anthu ogontha amene sangamvetsetse mawu olankhulidwa kapena olembedwa, zofalitsa zina zikuikidwa pavidiyo m’zinenero zolankhula ndi manja 13 zosiyanasiyana. Choncho, anthu ogontha akuphunzitsidwa “kuŵerenga” ngakhalenso kuphunzira uthenga wabwino mwachipambano. Ku United States, poyambirira nthaŵi zambiri munthu wogontha anali kutha zaka zisanu kuti afike pakubatizidwa. Tsopano, popeza kuti kuli mavidiyo ambiri a m’Chinenero Cholankhula ndi Manja cha ku America, anthu ena ogontha akutha kubatizidwa patangotha pafupifupi chaka chimodzi chokha.
‘Kukhalabe m’Galeta’
18. Atakumana ndi Yehonadabu, kodi Yehu anayamba kuchita chiyani?
18 Kalelo mu 905 B.C.E., atagwirizana ndi Yehonadabu, Yehu anayamba kusakaza kulambira konyenga. Iye anapempha olambira Baala onse kuti: “Lalikirani msonkhano wopatulika wa Baala.” Kenaka iye anatumiza anthu kuti ayendere dziko lonselo pofuna kutsimikizira kuti palibe wolambira Baala aliyense amene anasiyidwa. Pamene makamuwo analoŵa m’kachisi wamkulu wa mulungu wonyenga, iwo anaonetsetsa kuti mmenemo munalibe wolambira Yehova. Pomaliza, Yehu ndi ankhondo ake anakantha olambira Baala. “Momwemo Yehu anawononga Baala m’Israyeli.”—2 Mafumu 10:20-28.
19. Polingalira zimene mtundu wa anthu ukuyembekezera kuyang’anizana nazo mtsogolomu, kodi tiyenera kusonyeza mzimu wotani, ndipo ndi ntchito iti imene tiyenera kuichita mwachangu?
19 Lerolino, chiweruzo chomaliza cha chipembedzo chonyenga chili pafupi kwambiri. Motsogozedwa ndi angelo, Akristu akulengeza uthenga wabwino kwa mtundu wonse wa anthu, kuwalimbikitsa kuti aziopa Mulungu ndiponso kuti asayanjane ndi chipembedzo chonyenga. (Chivumbulutso 14:6-8; 18:2, 4) Anthu ofatsa akulimbikitsidwa kuti adzipereke ku Ufumu wa Mulungu wolamuliridwa ndi Mfumu yokhazikitsidwa ya Yehova, Yesu Kristu. (Chivumbulutso 12:10) Panthaŵi ino yochititsa nthumanzi, tiyenera kusamala kuti changu chathu chisafooke pamene tikupitirizabe kuchirikiza kulambira koona.
20. Kodi mudzatsimikiza kuchita chiyani m’chaka chautumiki cha 1998?
20 Nthaŵi ina, pamene Mfumu Davide anavutika kwambiri mtima, iye anapemphera kuti: “Mtima wanga wakhazikika, Mulungu, ndakhazika mtima; ndidzaimba, inde, ndidzaimba zolemekeza. Ndidzakuyamikirani mwa anthu, Ambuye.” (Salmo 57:7, 9) Nafenso tikhaletu okhazikika mtima. M’chaka chautumiki cha 1997, kunamveka kufuula kwakukulu kwa chitamando ku ulemerero wa Yehova Mulungu, ngakhale kuti panali zovuta zambiri. Tiyenitu timveketsenso kufuula kofananako, ngakhale koposerapo m’chaka chino chautumiki. Ndipo zimenezi zichitiketu mosasamala kanthu za zoyesayesa za Satana za kutifooketsa kapena kutitsutsa. Potero, tidzasonyezadi kuti mitima yathu njowongoka mogwirizana ndi mtima wa Yehu Wamkulu, Yesu Kristu, ndipo tidzayankhadi ndi mtima wathu wonse pempho lakuti: “Sekerani mwa Yehova, ndimo kondwerani inu olungama mtima; ndipo fuulani mokondwera nonsenu oongoka mtima.”—Salmo 32:11.
Kodi Mungafotokoze?
◻ Kodi nkusintha kotani kumene kunachitika ku Israyeli mu 905 B.C.E.?
◻ Kodi Yehu wamakono ndani, ndipo kodi a “khamu lalikulu” asonyeza motani kuti ‘mtima wawo ngwowongoka’ mogwirizana ndi mtima wake?
◻ Kodi ndi ziŵerengero ziti zapachaka zimene zikusonyeza changu cha Mboni za Yehova chosonyezedwa m’chaka chautumiki cha 1997?
◻ Kodi tidzasonyeza mzimu wotani m’chaka chautumiki cha 1998, mosasamala kanthu za chitsutso chilichonse cha Satana?
[Tchati patsamba 18-21]
LIPOTI LA CHAKA CHAUTUMIKI CHA 1997 LA MBONI ZA YEHOVA PADZIKO LONSE
(Onani m’magazini yeniyeni kuti mumvetse izi)
[Chithunzi patsamba 15]
Chiŵerengero chachikulu cha anthu opezeka pa Chikumbutso chikusonyeza kuti pali chiyembekezo chabwino cha chiwonjezeko mtsogolo muno
[Chithunzi patsamba 16]
Monga momwe Yehonadabu anathandizira Yehu, choncho a “khamu lalikulu” lerolino akuthandiza Yehu Wamkulu, Yesu Kristu, ndi abale ake odzozedwa