Chenjerani ndi Kusakhulupirira
“Tapenyani, abale, kuti kapena ukakhale mwa wina wa inu mtima woipa wosakhulupira, wakulekana ndi Mulungu wamoyo.”—AHEBRI 3:12.
1. Kodi mawu a Paulo amene anauza Akristu achihebri ayenera kutidziŵitsa za chiyani chochititsa mantha?
NZOCHITITSA mantha chotani nanga—kuona anthu amene kale anali paunansi wathithithi ndi Yehova kenaka akumakulitsa “mtima woipa” ndiponso “kulekana ndi Mulungu wamoyo”! Ndipo limenelitu ndi chenjezo lofunika! Mawu ameneŵa a mtumwi Paulo sanali kunena za anthu opanda chikhulupiriro ayi, koma anali kunena za anthu amene anali atapatulira miyoyo yawo kwa Yehova pamaziko a chikhulupiriro chawo m’nsembe ya dipo ya Yesu Kristu.
2. Kodi ndi mafunso ati amene tiyenera kuwalingalira?
2 Kodi munthu wodalitsidwa mwauzimu chotero angakulitse motani “mtima woipa wosakhulupira”? Inde, kodi nchiyani chomwe chingapangitse munthu amene analaŵa chikondi ndi chisomo cha Mulungu kulekana naye mwadala? Ndipo kodi zimenezi zingachitike kwa aliyense wa ife? Ameneŵa ndi mafunso ochititsa chidwi, ndipo tifunikira kuzindikira chifukwa chimene iye anaperekera chenjezo limeneli.—1 Akorinto 10:11.
Kodi Nchifukwa Ninji Anapereka Uphungu Wamphamvu Chotere?
3. Fotokozani zinthu zimene zinali kuchitikira Akristu a m’zaka za zana loyamba okhala m’Yerusalemu ndi madera ozungulira mzindawu.
3 Zikuonetsa kuti Paulo analembera kalatayi Akristu achihebri a ku Yudeya mu 61 C.E. Wolemba mbiri wina anafotokoza kuti imeneyi inali nthaŵi imene “kunalibe mtendere kapena chisungiko kwa anthu okonda mtendere, ndiponso oona mtima, okhala mumzinda wa Yerusalemu kapena kwina kulikonse m’chigawo chonsecho.” Inali nthaŵi ya kusayeruzika ndi chiwawa, chomwe chinawonjezeka pamene kunabwera ankhondo achiroma opondereza, Azerote achiyuda ooneka ngati olimba mtima potsutsana ndi Aroma, ndiponso akuba amene anapezerapo mwayi panthaŵi yovuta imeneyi. Zonsezi zinapangitsa kuti zinthu zikhale zovuta kwambiri kwa Akristu, amene anali kuyesetsa zolimba kupeŵa kuloŵerera m’zochitika zimenezo. (1 Timoteo 2:1, 2) Ndithudi, chifukwa cha uchete wawo, ena anali kuwaona monga anthu osayanjana ndi anzawo, ngakhale kuwaonanso monga otsutsa maulamuliro. Akristu nthaŵi zambiri anali kuchitiridwa zoipa, ndipo analandidwa katundu.—Ahebri 10:32-34.
4. Kodi ndi mavuto achipembedzo otani amene Akristu achihebri anayang’anizana nawo?
4 Akristu achihebri analinso kuponderezedwa kwambiri ndi anthu achipembedzo. Changu cha ophunzira okhulupirika a Yesu ndi kuwonjezeka kwakukulu komwe kunatsatirapo mumpingo wachikristu zinapangitsa kuti Ayuda aziwachitira nsanje ndi kukwiya nawo—makamaka atsogoleri awo achipembedzo ndiwo analimbikitsa zimenezo. Iwo anali kuvutitsa ndi kuzunza otsatira Yesu Kristu mulimonse mmene angafunire.a (Machitidwe 6:8-14; 21:27-30; 23:12, 13; 24:1-9) Ngakhale kuti Akristu ena sanazunzidwe, iwo anali kutukwanidwa ndi kunyozedwa ndi Ayuda. Chikristu chinali kunyozedwa ndipo anali kunena kuti nchipembedzo chatsopano chomwe sichinkatsatira Chiyuda, chinalibe kachisi, ansembe, madyerero, sankapereka nsembe zamwambo, ndi zina zotero. Ngakhale mtsogoleri wawo, Yesu, anaphedwa monga mpandu woipitsitsa. Kuti achirimikebe pachipembedzo chawo, Akristu anafunikira kukhala ndi chikhulupiriro, kulimba mtima, ndiponso kupirira.
5. Kodi nchifukwa ninji kunali kofunika kuti Akristu a ku Yudeya akhale atcheru mwauzimu?
5 Vuto lalikulu linali lakuti Akristu achihebri a ku Yudeya anali kukhala m’nthaŵi yovuta ya m’mbiri ya mtundu umenewo. Zinthu zambiri zimene Ambuye wawo, Yesu Kristu, anali atanena kuti zidzakhala zizindikiro za mapeto a dongosolo lachiyuda zinali zitachitika kale. Mapeto anali pafupi kwambiri. Kuti apulumuke, Akristuwo anafunikira kukhalabe tcheru mwauzimu ndiponso kukhala okonzekera ‘kuthaŵira kumapiri.’ (Mateyu 24:6, 15, 16) Kodi iwo adzakhala ndi chikhulupiriro ndiponso nyonga yauzimu yomwe idzawasonkhezera kuchita zinthu mosazengereza, monga momwe Yesu anali atanenera? Zinaonetsa kuti panali kukayikira.
6. Kodi nchiyani chomwe Akristu a ku Yudeya anafunikira mwamsanga?
6 Patatsala zaka khumi kuti dongosolo lonse lachiyuda liwonongedwe, Akristu achihebri mwachionekere anali ndi mavuto ambiri kungoyambira mkati mwa mpingo wachikristu ndiponso kunja kwake. Iwo anafunikira kulimbikitsidwa. Koma anafunikiranso uphungu ndi chitsogozo chowathandiza kuzindikira kuti njira yomwe anali kutsata inali yolongosoka ndiponso kuti kuvutika ndi kupirira kwawo kunali ndi phindu. Mwamwayi, Paulo anadzipereka kuchita zimenezo ndipo anawathandiza.
7. Kodi nchifukwa ninji tiyenera kukhudzidwa ndi zimene Paulo analembera Akristu achihebri?
7 Zimene Paulo analembera Akristu achihebri ziyenera kutikhudza kwambiri. Chifukwa ninji? Chifukwa chakuti tikukhala m’nthaŵi yofanana ndi yawoyo. Tsiku lililonse timavutika ndi mavuto a m’dziko lolamuliridwa ndi Satanali. (1 Yohane 5:19) Maulosi a Yesu ndi atumwi onena za masiku otsiriza ndiponso “mathedwe a nthaŵi ya pansi pano” akukwaniritsidwa m’tsiku lathu. (Mateyu 24:3-14; 2 Timoteo 3:1-5; 2 Petro 3:3, 4; Chivumbulutso 6:1-8) Chofunika kwambiri nchakuti tiyenera kukhalabe atcheru mwauzimu kuti ‘tikalimbike kupulumuka zonse zimene zidzachitika.’—Luka 21:36.
Munthu Wamkulu Kuposa Mose
8. Mwa kunena zimene zinalembedwa pa Ahebri 3:1, kodi Paulo anali kulimbikitsa Akristu anzake kuti achite chiyani?
8 Pofotokoza mfundo yofunika kwambiri, Paulo analemba kuti: “Lingirirani za Mtumwi ndi Mkulu wa ansembe wa chivomerezo chathu, Yesu.” (Ahebri 3:1) “Kulingirira” kumatanthauza “kuzindikira bwino . . . , kudziŵa bwino, kupenda mosamalitsa.” (Vine’s Expository Dictionary of Old and New Testament Words) Choncho, Paulo anali kupempha okhulupirira anzake kuti ayesetse mwakhama kuzindikira bwino za ntchito imene Yesu anagwira pachikhulupiriro ndi chipulumutso chawo. Ngati iwo akanachita zimenezi akanakhala otsimikiza kuchirimika pachikhulupiriro. Nangano, kodi ntchito ya Yesu inali yotani, ndipo nchifukwa ninji tiyenera “kulingirira” za iye?
9. Kodi nchifukwa ninji Paulo ananena kuti Yesu ndi “mtumwi” ndiponso “mkulu wa ansembe”?
9 Paulo anagwiritsira ntchito mawu akuti “mtumwi” ndiponso “mkulu wa ansembe” pofotokoza za Yesu. “Mtumwi” ndi munthu wotumidwa ndipo panopo akunena za njira ya Mulungu yolankhulira ndi anthu. “Mkulu wa ansembe” ndi munthu amene anthu angafikire Mulungu kudzera mwa iye. Makonzedwe aŵiri ameneŵa ngofunika kwambiri pa kulambira koona, ndipo Yesu ndiye zonse ziŵirizo. Iye ndiye amene anatumidwa kuchokera kumwamba kudzaphunzitsa anthu za choonadi chonena za Mulungu. (Yohane 1:18; 3:16; 14:6) Yesu anaikidwanso kukhala Mkulu wa Ansembe wophiphiritsira m’makonzedwe a kachisi wauzimu wa Yehova kaamba ka chikhululukiro cha machimo. (Ahebri 4:14, 15; 1 Yohane 2:1, 2) Ngati timadziŵadi madalitso amene tingalandire kudzera mwa Yesu, tidzalimba mtima ndi kutsimikiza kuchirimika pachikhulupiriro.
10. (a) Kodi Paulo anathandiza motani Akristu achihebri kuti azindikire kuti Chikristu nchachikulu kuposa Chiyuda? (b) Kodi ndi choonadi chiti chomwe Paulo anagwiritsira ntchito pogogomezera mfundo yake?
10 Pogogomezera za kufunika kwa chikhulupiriro chachikristu, Paulo anayerekezera Yesu ndi Mose, amene Ayuda anamuona monga mneneri wamkulu koposa mwa makolo awo. Ngati Akristu achihebri anatsimikiza ndi mtima wonse kuti Yesu anali wamkulu kuposa Mose, iwo sakanakayikira zakuti Chikristu nchachikulu kuposa Chiyuda. Ngakhale kuti Paulo anafotokoza kuti Mose anali woyenerera kuikizidwa “nyumba” ya Mulungu—mtundu, kapena mpingo, wa Israyeli—iye anali chabe kalinde, kapena mtumiki wokhulupirika. (Numeri 12:7) Koma Yesu anali Mwana, woyang’anira m’nyumbamo. (1 Akorinto 11:3; Ahebri 3:2, 3, 5) Pogogomezera mfundo yakeyi, Paulo anafotokoza choonadi ichi: “Pakuti nyumba iliyonse ili naye wina woimanga; koma wozimanga zonse ndiye Mulungu.” (Ahebri 3:4) Palibe amene angatsutse kuti Mulungu ngwamkulu kuposa aliyense, chifukwa chakuti iye ndiye Womanga, kapena kuti Mlengi, wa zonse. Choncho, popeza kuti Yesu anali wantchito mnzake wa Mulungu, iye ayenera kukhala wamkulu kuposa cholengedwa chilichonse, kuphatikizapo Mose.—Miyambo 8:30; Akolose 1:15-17.
11, 12. Kodi nchiyani chomwe Paulo analangiza Akristu achihebri kuti achigwiritse “kuchigwira kufikira chitsiriziro,” ndipo kodi tingagwiritsire ntchito motani uphungu umenewu?
11 Zoonadi, Akristu achihebri anali ndi mwayi waukulu. Paulo anawakumbutsa kuti iwo anali “olandirana nawo maitanidwe akumwamba,” mwayi waukulu kwambiri kuposa chilichonse chomwe chinali m’dongosolo lachiyuda. (Ahebri 3:1) Mawu a Paulo ayenera kuti anapangitsa Akristu odzozedwa amenewo kukhala oyamikira chifukwa chakuti anali kuyembekezera choloŵa chatsopano mmalo modzimvera chisoni chifukwa chotaya chilichonse chokhudzana ndi choloŵa chawo chachiyuda. (Afilipi 3:8) Powalangiza kuti agwiritsitse mwayi wawo ndiponso kuti asauone mopepuka, Paulo anati: “Kristu monga mwana, wosunga nyumba yake [ya Mulungu]; ndife nyumba yake, ngati tigwiritsa kulimbika mtima ndi kudzitamandira kwa chiyembekezocho, kuchigwira kufikira chitsiriziro.”—Ahebri 3:6.
12 Inde, kuti Akristu achihebri apulumuke pa mapeto omwe anayandikira a dongosolo lazinthu lachiyuda, iwo anafunikira kugwiritsitsa chiyembekezo chawo chopatsidwa ndi Mulungu “kuchigwira kufikira chitsiriziro.” Tiyeneranso kuchita zofananazo lerolino ngati tikufuna kupulumuka mapeto a dongosolo lino. (Mateyu 24:13) Tisalole nkhaŵa za m’moyo, mphwayi za anthu, kapena kupanda ungwiro kwathu kugwedeza chikhulupiriro chathu m’malonjezo a Mulungu. (Luka 21:16-19) Kuti tizindikire mmene tingadzilimbitsire, tiyeni timvetsere mwatcheru mawu owonjezereka a Paulo.
“Musaumitse Mitima Yanu”
13. Kodi ndi chenjezo liti limene Paulo anapereka, ndipo kodi iye anagwiritsira ntchito motani Salmo 95?
13 Atafotokoza za mwayi wa Akristu achihebri, Paulo anapereka chenjezo lakuti: “Monga anena Mzimu Woyera, Lero ngati mudzamva mawu ake, Musaumitse mitima yanu, monga m’kupsetsa mtimamo, monga muja tsiku la chiyesero m’chipululu.” (Ahebri 3:7, 8) Paulo anali kugwira mawu Salmo 95, ndiye chifukwa chake anati “anena Mzimu Woyera.”b (Salmo 95:7, 8; Eksodo 17:1-7) Malemba ngouziridwa ndi Mulungu mwa mzimu wake woyera.—2 Timoteo 3:16.
14. Kodi Aisrayeli anachita motani ndi zimene Yehova anawachitira, ndipo nchifukwa ninji?
14 Atamasulidwa mu ukapolo ku Igupto, Aisrayeli analemekezedwa kwambiri mwa kuwaloŵetsa m’pangano launansi ndi Yehova. (Eksodo 19:4, 5; 24:7, 8) Komabe, mmalo moyamikira chifukwa cha zimene Mulungu anawachitira, iwo posapita nthaŵi anapanduka. (Numeri 13:25–14:10) Kodi nchiyani chimene chinapangitsa kuti zimenezo zichitike? Paulo anafotokoza chifukwa chake: kuumitsa mitima yawo. Koma kodi mitima yolabadira ndi kumvera Mawu a Mulungu ingaume motani? Ndipo kodi tiyenera kuchitanji kuti tipeŵe zimenezi?
15. (a) Kodi ‘mawu a Mulungu’ anaperekedwa motani kale, nanga lerolino akuperekedwa motani? (b) Kodi ndi mafunso ati omwe tiyenera kudzifunsa ponena za ‘mawu a Mulungu’?
15 Paulo anayamba kupereka chenjezo lake ndi mawu ogogomezera nkhaniyo akuti “ngati mudzamva mawu ake.” Mulungu analankhula kwa anthu ake mwa Mose ndi aneneri ena. Kenaka, Yehova analankhula kwa iwo mwa Mwana wake, Yesu Kristu. (Ahebri 1:1, 2) Lerolino, tili ndi Mawu onse ouziridwa a Mulungu, Baibulo Loyera. Tilinso ndi “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru,” woikidwa ndi Yesu kuti azipereka “zakudya [zauzimu] panthaŵi yake.” (Mateyu 24:45-47) Choncho, Mulungu akulankhulabe. Koma kodi tikumvera? Mwachitsanzo, kodi timachita motani ndi uphungu wonena za kavalidwe ndi kapesedwe kapena wonena za zosangulutsa ndiponso nyimbo? Kodi ‘timamvera,’ kutanthauza, kulabadira ndi kutsatira zimene tikumva? Ngati tili ndi chizoloŵezi cha kupeza zifukwa zodzikhululukira kapena kulingalira kuti uphunguwo sukutikhudza, tikudziika pangozi yosaoneka ya kuumitsa mitima yathu.
16. Kodi mitima yathu ingaume m’njira ina iti?
16 Mitima yathu ingaumenso ngati tili ndi chizoloŵezi chosafuna kuchita zinthu zimene tingachite ndiponso zimene tiyenera kuchita. (Yakobo 4:17) Ngakhale kuti Yehova anachitira zambiri Aisrayeli, iwo analephera kukhala ndi chikhulupiriro, anapandukira Mose, anasankha kumvera mawu oipa onena za Kanani, ndipo anakana kuloŵa m’Dziko Lolonjezedwa. (Numeri 14:1-4) Choncho, Yehova analamula kuti iwo adzakhala zaka 40 m’chipululu—nthaŵi yaitali ndithu pofuna kuti anthu onse osakhulupirira a mumbadwowo afe. Atakwiya nawo, Mulungu anati: “Nthaŵi zonse amasokera mumtima; koma sanazindikira njira zanga iwowa; monga ndinalumbira mu ukali wanga: Ngati adzaloŵa mpumulo wanga [“Sadzaloŵa mpumulo wanga,” NW]!” (Ahebri 3:9-11) Kodi tatengapo phunziro pamenepa?
Phunziro kwa Ife
17. Ngakhale kuti anaona ntchito zamphamvu za Yehova ndi kumva zilengezo zake, kodi nchifukwa ninji Aisrayeli sanakhulupirire?
17 Mbadwo wa Aisrayeli umene unatuluka mu Igupto unaona ndi maso awo ntchito zamphamvu za Yehova ndipo unamvanso ndi makutu awo zilengezo zake. Komabe, iwo sanakhulupirire kuti Mulungu angawatsogolere bwino kuwaloŵetsa m’Dziko Lolonjezedwa. Chifukwa ninji? “Sanazindikira njira zanga,” anatero Yehova. Anadziŵa zimene Yehova ananena ndi kuchita, koma analibe chidaliro ndi chitsimikizo chakuti iye angawasamalire. Iwo anadera nkhaŵa kwambiri zosoŵa ndi zokhumba zawo kotero kuti sanalingalire kwenikweni njira za Mulungu ndi chifuno chake. Inde, sanakhulupirire lonjezo lake.
18. Malinga nkunena kwa Paulo, kodi ndi khalidwe liti lomwe limadza chifukwa cha “mtima woipa wosakhulupira”?
18 Mawu owonjezerekawa opita kwa Ahebri akugwiranso ntchito mofananamo kwa ife: “Tapenyani, abale, kuti kapena ukakhale mwa wina wa inu mtima woipa wosakhulupira, wakulekana ndi Mulungu wamoyo.” (Ahebri 3:12) Paulo anagogomezera mfundoyo mwa kunena kuti “mtima woipa wosakhulupira” umadza chifukwa cha “kulekana ndi Mulungu wamoyo.” Poyambirira m’kalata imeneyi, iye ananena za ‘kutengedwa kusiyana nazo’ chifukwa cha kusamvetsera. (Ahebri 2:1) Komabe, mawu achigiriki otembenuzidwa kuti “kulekana” amatanthauza “kuchoka” ndipo ngogwirizana ndi mawu akuti “mpatuko.” Amasonyeza kukana dala ndiponso mofunitsitsa, kupatuka ndi kuloŵa gulu lina, ukumanyoza gulu loyambalo.
19. Kodi kulephera kumvera uphungu kungadzetse motani mavuto? Perekani chitsanzo.
19 Choncho, phunziro lake nlakuti ngati tikhala ndi chizoloŵezi cholephera ‘kumva mawu ake,’ kunyalanyaza uphungu wochokera kwa Yehova woperekedwa kudzera m’Mawu ake ndi kagulu ka kapolo wokhulupirika, mitima yathu sidzachedwa kuuma. Mwachitsanzo, mwina mwamuna ndi mkazi osakwatirana angazoloŵerane kwambiri moti nkuchita zinthu zopyola malire pang’ono. Kodi chingachitike nchiyani atangonyalanyaza nkhaniyo? Kodi kunyalanyazako kungawatetezere kuti asadzabwerezenso zimene anachita, kapena kodi kudzangowapangitsa kuti abwerezenso mosavuta zimene anachitazo? Mofananamo, pamene kagulu ka kapolo kapereka uphungu woti tizipenda bwino nyimbo zimene timamvetsera ndiponso zosangulutsa, ndi zina zotero, kodi timavomereza moyamikira ndi kuwongolera ngati kuli kofunika? Paulo anatilangiza kuti ‘tisaleke kusonkhana kwathu pamodzi.’ (Ahebri 10:24, 25) Ngakhale kuti pali uphungu umenewu, ena sadera nkhaŵa kwenikweni za misonkhano yachikristu. Iwo angalingalire kuti ngati alephera kupita kumisonkhano ina kapena ngakhale kungosiyiratu kupita kumisonkhano ina palibe chimene chidzachitika.
20. Kodi nchifukwa ninji kuli kofunika kumvera uphungu wa m’Malemba?
20 Ngati sitilabadira “mawu” a Yehova, ofotokozedwa momveka bwino m’Malemba ndiponso m’zofalitsa zozikidwa pa Baibulo, sitidzachedwa ‘kulekana naye Mulungu wamoyo.’ Ngati tinyalanyaza dala uphungu kungakhale kosavuta kuuchepsa, kuuona ngati wosayenera, ndiponso kuukana. Ngati sitithetsa khalidwe limeneli, chotsatirapo chake chidzakhala “mtima woipa wosakhulupira,” ndipo nthaŵi zambiri kumakhala kovuta kuthetsa khalidwe limeneli. (Yerekezerani ndi Aefeso 4:19.) Yeremiya analemba molondola kuti: “Mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika, ndani angathe kuudziŵa?” (Yeremiya 17:9) Nchifukwa chake Paulo analangiza okhulupirira anzake achihebri kuti: “Dandauliranani nokha tsiku ndi tsiku, pamene patchedwa, Lero; kuti angaumitsidwe wina wa inu ndi chenjerero la uchimo.”—Ahebri 3:13.
21. Kodi tonsefe tikulangizidwa kuchitanji, ndipo kodi tili ndi ziyembekezo zotani?
21 Tili okondwa chotani nanga kuti Yehova akutilankhulabe lerolino, kudzera m’Mawu ake ndiponso gulu lake! Tili oyamikira chifukwa chakuti “kapolo wokhulupirika ndi wanzeru” akupitirizabe kutithandiza ‘kugwiritsa chiyambi cha kutama kwathu kuchigwira kufikira chitsiriziro.’ (Ahebri 3:14) Ino ndiyo nthaŵi yolabadira chikondi ndi chitsogozo cha Mulungu. Ngati tichita zimenezo, tingakhalenso ndi lonjezo lina losangalatsa la Yehova—lonjezo la ‘kuloŵa’ mpumulo wake. (Ahebri 4:3, 10) Imeneyo ndiyo nkhani yotsatira imene Paulo anakambitsirana ndi Akristu achihebri, ndipo ndiyo imenenso tidzakambitsirana m’nkhani yotsatira.
[Mawu a M’munsi]
a Josephus anasimba kuti atangofa Festo, Ananus (Hananiya) wa m’kagulu ka Asaduki anakhala mkulu wa ansembe. Iye anatenga Yakobo, mbale wake wa Yesu mwa atate ena, ndi ophunzira ena napita nawo ku bungwe la Sanhedrin ndipo anaweruzidwa kuti aphedwe ndi kuponyedwa miyala.
b Mwachionekere, Paulo anagwira mawu mu Septuagint yachigiriki, yomwe inatembenuza mawu achihebri otanthauza “Meriba” monga “kukangana” ndiponso mawu otanthauza “Masa” monga “kuyesa.” Onani tsamba 350 ndi tsamba 379 mu Voliyumu 2 ya buku la Insight on the Scriptures, lofalitsidwa ndi Watchtower Bible and Tract Society of New York, Inc.
Kodi Mungafotokoze?
◻ Kodi nchifukwa ninji Paulo analemba uphungu wamphamvu chotere kwa Akristu achihebri?
◻ Kodi ndi motani mmene Paulo anathandizira Akristu achihebri kuti azindikire kuti anali ndi chinthu chabwino kwambiri kuposa kukhala m’Chiyuda?
◻ Kodi mtima wa munthu ungaume motani?
◻ Kodi tiyenera kuchitanji kuti tipeŵe kukhala ndi “mtima woipa wosakhulupira”?
[Chithunzi patsamba 10]
Kodi mumakhulupirira Yesu, Mose Wamkulu?