Kwa Afilipi
3 Pomalizira abale anga, pitirizani kusangalala monga otsatira a Ambuye.+ Kubwereza kulemba zinthu zimene ndinakulemberani kale si vuto kwa ine, koma ndi chitetezo kwa inu.
2 Chenjerani ndi anthu amene amachita zinthu ngati agalu. Chenjerani ndi anthu amene amavulaza anzawo. Chenjerani ndi anthu amene amachita mdulidwe.+ 3 Chifukwa ife tinachita mdulidwe weniweni,+ ife amene tikuchita utumiki wopatulika motsogoleredwa ndi mzimu wa Mulungu. Timadzitamandira mwa Khristu Yesu+ ndipo sitidalira zinthu zimene anthu amaziona kuti ndi zofunika, 4 ngakhale kuti ineyo, kuposa wina aliyense, ndili ndi zifukwa zodalira zinthu zimene anthu amaziona kuti ndi zofunika.
Ngati pali munthu wina amene akuganiza kuti ali ndi zifukwa zodalira zinthu zimene anthu amaziona kuti ndi zofunika, ine ndikuposa ameneyo, chifukwa: 5 ndinadulidwa pa tsiku la 8,+ ndine wa mtundu wa Isiraeli, wa fuko la Benjamini, ndine Mheberi wobadwa kwa Aheberi.+ Kunena za chilamulo, ndine Mfarisi.+ 6 Kunena za kudzipereka, ndinkazunza mpingo.+ Kunena zochita chilungamo potsatira chilamulo, ndinasonyeza kuti ndilibe chifukwa chondinenezera. 7 Koma zinthu zimene zinali zaphindu kwa ine ndikuziona kuti ndi zopanda phindu* chifukwa cha Khristu.+ 8 Zoonadi, ndimaona kuti zinthu zonse nʼzosapindulitsa chifukwa chakuti ndinadziwa Khristu Yesu Ambuye wanga, chimene ndi chinthu chamtengo wapatali kwambiri. Chifukwa cha iye, ndinataya zinthu zonse ndipo ndimaziona ngati mulu wa zinyalala, kuti ndikhale pa ubwenzi weniweni ndi Khristu, 9 ndiponso kuti ndizionedwa kuti ndine wotsatira wake. Sikuti ndine wolungama chifukwa chakuti ndikuchita zonse moyenera potsatira Chilamulo, koma chifukwa chakuti ndimakhulupirira+ Khristu.+ Chilungamo chimenechi ndi chochokera kwa Mulungu ndipo chimabwera chifukwa cha chikhulupiriro.+ 10 Cholinga changa nʼchoti ndimudziwe komanso kuti ndidziwe mphamvu za amene anamuukitsa kwa akufa.+ Ndikufunanso kuti ndivutike ngati mmene iye anavutikira,+ mpaka kulolera kufa ngati mmene iye anafera.+ 11 Ndachita zimenezi kuti ngati nʼkotheka ndidzapeze mwayi wodzauka kwa akufa pa kuuka koyamba.+
12 Sikuti ndalandira kale mphotoyo, kapena kuti ndakhala kale wangwiro ayi. Koma ndikuyesetsabe+ kuti ndikalandire mphoto chifukwa ndikudziwa kuti cholinga cha Khristu Yesu pondisankha chinali chimenechi.+ 13 Abale, ine sindikudziona ngati ndalandira kale mphotoyo ayi. Koma pali chinthu chimodzi chimene ndikuchita: Ndikuiwala zinthu zakumbuyo+ ndipo ndikuyesetsa kuti ndikapeze zakutsogolo.+ 14 Ndikuyesetsa kuti ndikwaniritse cholinga changa chokalandira mphoto.+ Mphoto imeneyi ndi kukakhala ndi moyo kumwamba+ ndipo Mulungu adzaipereka kwa anthu amene anawaitana kudzera mwa Khristu Yesu. 15 Choncho, tiyeni tonse amene tili olimba mwauzimu+ tikhale ndi maganizo amenewa. Ndipo ngati muli ndi maganizo osiyana ndi amenewa pambali ina iliyonse, Mulungu adzakuululirani maganizo oyenerawo. 16 Komabe, mulimonse mmene tapitira patsogolo, tiyeni tipitirize kupita patsogolo pochita zomwe tikuchitazo.
17 Abale, nonsenu muyesetse kumanditsanzira+ ndipo muzionetsetsa amene akuchita zinthu mogwirizana ndi chitsanzo chimene tinakupatsani. 18 Chifukwa pali anthu ambiri amene akuchita zinthu ngati adani a mtengo wozunzikirapo* wa Khristu. Kale ndinkawatchula pafupipafupi koma pano ndimawatchula ndikugwetsa misozi. 19 Anthu amenewo akuyembekezera kuwonongedwa ndipo mulungu wawo ndi mimba zawo. Iwo amanyadira zinthu zimene akuyenera kuchita nazo manyazi ndipo amangoganizira zinthu zapadziko lapansi.+ 20 Koma ife ndife nzika+ zakumwamba+ ndipo tikuyembekezera mwachidwi mpulumutsi wochokera kumeneko amene ndi Ambuye Yesu Khristu.+ 21 Iye adzasintha thupi lathu lonyozekali kuti lifanane* ndi thupi lake laulemerero.+ Adzachita zimenezi pogwiritsa ntchito mphamvu zake zazikulu zimene zimamuthandiza kugonjetsa zinthu zonse kuti zikhale pansi pake.+