Mmene Angelo Angakuthandizireni
MAWU a Mulungu amaterodi kuti angelo aliko. Amatiuza kuti zolengedwa zauzimu zimenezi ziliko mamiliyoni ambirimbiri. Danieli, mtumiki wa Yehova Mulungu, anaona masomphenya a zinthu zakumwamba ndipo analemba kuti: “Zikwi zikwi anamtumikira [Mulungu], ndi unyinji wosaŵerengeka unaima pamaso pake.”—Danieli 7:10.
Mwaonatu kuti mawu a Danieli sakungotiuza zoti kuli angelo ambiri. Akutiuzanso kuti angelo amatumikira Mulungu. Ndi atumiki ake. Mogwirizana ndi zimenezi, wamasalmo anaimba kuti: “Lemekezani Yehova, inu angelo ake; a mphamvu zolimba, akuchita mawu ake, akumvera liwu la mawu ake. Lemekezani Yehova, inu makamu ake onse; inu atumiki ake akuchita chomkondweretsa Iye.”—Salmo 103:20, 21.
Baibulo limafotokozanso kuti angelo sanayambe akhalapo anthu padziko lapansi. Yehova analenga angelo kumwamba asanalenge anthu padziko lapansi. Mulungu ‘ataika maziko a dziko lapansi, ana onse aungelo a Mulungu anafuula ndi chimwemwe.’—Yobu 38:4-7.
Angelo ndi zolengedwa zauzimu—zosaoneka, zamphamvu, zanzeru kwambiri. M’Baibulo, liwu lachihebri lakuti mal·ʼakhʹ ndi liwu lachigiriki lakuti agʹge·los onse amatembenuzidwa kuti “mngelo” pamene akunena za cholengedwa chauzimu. Mawu amenewa akupezeka pafupifupi nthaŵi 400 m’Baibulo. Onse aŵiri ali ndi tanthauzo limodzi, ndilo, “mthenga.”
Kuona Angelo
Ndithudi, angelo ndi amithenga. Mwina mumaidziŵa nkhani ya m’Baibulo yonena za nthaŵi pamene mngelo Gabrieli anaonekera kwa Mariya. Mngeloyo anamuuza kuti ngakhale kuti Mariya anali namwali, adzabala mwana wamwamuna amene adzatchedwe Yesu. (Luka 1:26-33) Mngelo anaonekeranso kwa abusa ena amene anali kumabusa. Iye analengeza kuti: “Wakubadwirani inu lero, . . . Mpulumutsi, amene ali Kristu Ambuye.” (Luka 2:8-11) Momwemonso, angelo anafikitsa uthenga kwa Hagara, Abrahamu, Loti, Yakobo, Mose, Gideoni, Yesu ndi enanso amene Baibulo limatchula.—Genesis 16:7-12; 18:1-5, 10; 19:1-3; 32:24-30; Eksodo 3:1, 2; Oweruza 6:11-22; Luka 22:39-43; Ahebri 13:2.
Chochititsa chidwi nchakuti mauthenga onse amenewa operekedwa ndi angelo anali ogwirizana ndi kukwanitsidwa kwa zolinga za Mulungu ndipo osati zolinga za anthu olandira uthengawo. Angelo anaonekera monga oimira Mulungu, malinga ndi chifuniro chake ndi nthaŵi yake. Sanaitanidwe ndi anthu.
Kodi Tiyenera Kuitana Angelo Kuti Adzatithandize?
Kodi zili bwino kuitana angelo pamene zinthu zativuta? Ngati nchoncho, tingafunikire kudziŵa dzina la mngelo amene angatithandize bwino. Ndiye chifukwa chake, mabuku ena amene amagulitsidwa ali ndi mpambo wa maina ambiri amene amati ndi maina a angelo, pamodzi ndi malo awo, maina awo aulemu, ndi ntchito yawo. Buku lina lili ndi mpambo wa amene limati ndiwo “[angelo] khumi oyambirira akumwamba,” “angelo odziŵika koposa kumaiko a Kumadzulo.” Mpambowo ulinso ndi malangizo akuti muzitseka maso anu, kutchula dzina la mngelo pang’onopang’ono kangapo, kupuma mwakuya, kupuma pang’onopang’ono, ndi “kukonzekera kuonana nawo.”
Komano Baibulo limangotiuza maina a angelo a Mulungu okhulupirika aŵiri okha, Mikayeli ndi Gabrieli. (Danieli 12:1; Luka 1:26) Chifukwa choperekera maina aŵiriwa chingakhale kusonyeza kuti mngelo aliyense ndi munthu wauzimu wokhala ndi umunthu wake ndi dzina lake, osati chabe nyonga kapena mphamvu ina yake yopanda umunthu.
Chochititsa chidwi nchakuti angelo ena anakana kuvumbulira anthu maina awo. Yakobo atapempha mngelo kuti amuuze dzina lake, mngeloyo anakana. (Genesis 32:29) Pamene mngelo amene anafikira Yoswa anafunsidwa dzina lake, iye anangoti ndi “kazembe wa ankhondo a Yehova.” (Yoswa 5:14) Makolo a Samsoni atafunsa mngelo dzina lake, iye anati: “Ufunsiranji dzina langa, popeza lili lodabwitsa?” (Oweruza 13:17, 18) Mwa kusatiuza maina a angelowo, Baibulo likutichinjiriza kuti tisapereke ulemu wosayenera kwa angelowo ndi kuwalambira. Monga momwe tidzaonera, silimatiuzanso kuti tizipemphera kwa iwo.
Kuitanira pa Mulungu
Baibulo limatiuza zochitika zonse za kudziko lamizimu zimene tifunikira kudziŵa. Mtumwi Paulo analemba kuti: “Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pachiphunzitso . . . kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino.” (2 Timoteo 3:16, 17) Mulungu akadafuna kuti tidziŵe maina a angelo ambiri, akadawavumbula m’Mawu ake, Baibulo. Ndipo Mulungu akadafuna kutilangiza mmene tingalankhulire ndi angelo m’pemphero, akadatiuza zimenezo m’Malemba.
M’malo mwake, Yesu Kristu anaphunzitsa kuti: “Iwe popemphera, loŵa m’chipinda chako, nutseke chitseko chako, nupemphere Atate wako ali mtseri . . . Chifukwa chake pempherani inu chomwechi: Atate wathu wa Kumwamba, dzina lanu liyeretsedwe.” (Mateyu 6:6, 9) Mfundo ya m’Malemba ndi iyi: Sitiyenera kuitanira pa angelo kapena kupemphera kwa iwo, koma tiyenera kulankhula kwa Mlengi wa angelowo m’pemphero, Mulungu iyemwini. Dzina lake si lachinsinsi, ndipo silochita kufuna woona masomphenya kuti alivumbule. Ngakhale kuti ena ayesayesa kulibisa dzina la Mulungulo, ilo limapezeka nthaŵi zoposa 7,000 m’Baibulo. Mwachitsanzo, wamasalmo anali kunena za Atate wakumwamba pamene anaimba kuti: “Inu nokha, dzina lanu ndinu Yehova, ndinu Wammwambamwamba padziko lonse lapansi.”—Salmo 83:18.
Yehova satanganidwa moti nkusatimva tikamamfikira moyenera m’pemphero. Baibulo limatitsimikizira kuti: “Maso a Yehova ayang’ana uko ndi uko m’dziko lonse lapansi, kudzionetsera wamphamvu kwa iwo amene mtima wawo uli wangwiro ndi Iye.”—2 Mbiri 16:9.
Angelo Ndiponso Makhalidwe Abwino
Mosiyaniratu ndi zimene ofalitsa nkhani amasonyeza, angelo saweruza anthu. Zimenezo nzoyenera, popeza kuti angelo alibe mphamvu yoweruza anthu. Yehova ndiye “Woweruza wa onse,” ngakhale kuti “anapereka kuweruza konse kwa Mwana,” Yesu Kristu. (Ahebri 12:23; Yohane 5:22) Komabe, sitinganene kuti angelo alibe chidwi ndi mmene timakhalira m’moyo wathu. Yesu anati: “Kuli chimwemwe pamaso pa angelo a Mulungu chifukwa cha munthu wochimwa mmodzi amene atembenuka mtima.”—Luka 15:10.
Komano angelo sangopenyerera zochitika. Kalelo, anatumikira monga akupha, opereka ziweruzo za Mulungu. Mwachitsanzo, Mulungu anagwiritsa ntchito angelo poweruza Aigupto akale. Malinga nkunena kwa Salmo 78:49, “anawatumizira mkwiyo wake wotentha, kuzaza, ndi kupsa mtima, ndi nsautso, ndizo gulu la amithenga ochita zoipa [“odzetsa tsoka,” NW].” Momwemonso, Baibulo limasimba kuti usiku wina mngelo mmodzi anawononga asilikali 185,000 a Asuri.—2 Mafumu 19:35.
M’tsogolonso, angelo adzawononga aja amene akusokoneza mtendere wa ena mwa kukana kutsatira malamulo olungama a Mulungu. Yesu adzadza “pamodzi ndi angelo a mphamvu yake, m’laŵi lamoto, ndi kubwezera chilango kwa iwo osamdziŵa Mulungu, ndi iwo osamvera Uthenga Wabwino.”—2 Atesalonika 1:7, 8.
Choncho Malemba akusonyeza kuti angelo okhulupirika a Mulungu nthaŵi zonse amachita chifuniro chake mwa kutsatira malangizo ake ndi kuchirikiza malamulo ake olungama. Ndithudi, ngati tikufuna kuti angelo a Mulungu atithandize, tifunikira kudziŵa kuti chifuniro cha Mulungu nchiyani ndi kuyesetsa ndi mtima wonse kuchichita.
Angelo Oyang’anira
Kodi angelo amasamalira anthu ndi kuwateteza? Mtumwi Paulo anafunsa kuti: “Kodi [angelo] siili yonse mizimu yotumikira, yotumidwa kuti itumikire iwo amene adzaloŵa chipulumutso?” (Ahebri 1:14) Ndithudi, yankho la funso la Paulo ndilo inde.
Chifukwa chakuti anakana kugwadira fano lagolide loimikidwa ndi Mfumu Nebukadinezara wa Babulo, Ahebri atatu aja Sadrake, Mesake, ndi Abedinego anaponyedwa m’ng’anjo yamoto wadzaoneni. Komabe, atumiki okhulupirika amenewo a Mulungu sanatenthedwe ndi motowo. Mfumuyo itayang’ana m’ng’anjoyo, inaona “amuna anayi,” ndipo inati “maonekedwe a wachinayi [ananga] mwana wa milungu.” (Danieli 3:25) Patapita zaka zambiri, Danieli anaponyedwa m’dzenje la mikango chifukwa cha kukhulupirika kwake. Iyenso sanavulazidwe ndipo anati: “Mulungu wanga watuma mthenga wake, natseka pakamwa pa mikango.”—Danieli 6:22.
Mpingo wa otsatira Kristu utakhazikitsidwa m’zaka za zana loyamba C.E., angelo anaonekeranso, namasula atumwi m’ndende. (Machitidwe 5:17-24; 12:6-12) Ndipo moyo wa Paulo utakhala pangozi panyanja, mngelo anamtsimikizira kuti adzafika bwino ku Roma.—Machitidwe 27:13-24.
Atumiki amakono a Yehova Mulungu amakhulupirira ndi mtima wonse kuti makamu osaoneka a angelo a Mulungu alikodi ndipo amatha kupereka chitetezo, monga momwe anachitira kwa Elisa ndi mnyamata wake. (2 Mafumu 6:15-17) Zoonadi, “mngelo wa Yehova azinga kuwachinjiriza iwo akuopa Iye, nawalanditsa iwo.”—Salmo 34:7; 91:11.
Uthenga Umene Angelo Ali Nawo
Pamene angelo amasamala za ubwino wa anthu amene akutumikira Yehova Mulungu, iwo akuonetsetsanso kuti anthu akuphunzira za iye ndi zolinga zake. Mtumwi Yohane analemba kuti: “Ndinaona mngelo wina alikuuluka pakati pa mlengalenga, wakukhala nawo Uthenga Wabwino wosatha, aulalikire kwa iwo akukhala padziko, ndi kwa mtundu uliwonse ndi fuko ndi manenedwe ndi anthu; ndi kunena ndi mawu aakulu, Opani Mulungu, mpatseni ulemerero.”—Chivumbulutso 14:6, 7.
Kodi mukufuna kudziŵa zimene “Uthenga Wabwino wosatha” umenewu ukunena? Ngati mukufuna, funsani Mboni za Yehova. Nzofunitsitsa kukuuzani.
[Zithunzi patsamba 7]
Mngelo amene ali pakati pa mlengalenga akulengeza uthenga wabwino. Kodi mukufuna kuudziŵa?