Kodi Angelo Ndi Otani?
Yankho la m’Baibulo
Angelo ndi zolengedwa zomwe zili ndi mphamvu kwambiri komanso amachita zinthu kuposa anthu. (2 Petulo 2:11) Angelo amakhala kumwamba, kumalo omwe kumakhala zolengedwa zauzimu, komwe n’kutali kwambiri kuposa komwe tingathe kuona ndi maso. (1 Mafumu 8:27; Yohane 6:38) N’chifukwa chake angelo amatchedwanso kuti mizimu.—1 Mafumu 22:21; Salimo 18:10.
Kodi angelo anachokera kuti?
Mulungu analenga angelo pogwiritsa ntchito Yesu yemwe Baibulo limamutcha kuti “woyamba kubadwa wa chilengedwe chonse.” Pofotokoza mmene Mulungu anagwiritsira ntchito Yesu polenga zinthu, Baibulo limati: “Kudzera mwa [Yesu] zinthu zina zonse zinalengedwa, zakumwamba ndi zapadziko lapansi. Inde, zinthu zooneka ndi zinthu zosaoneka,” kuphatikizapo angelo. (Akolose 1:13-17) Angelo sakwatira kapena kuberekana. (Maliko 12:25) M’malo mwake, aliyense wa “ana a Mulungu woona” amenewa analengedwa mwachindunji.—Yobu 1:6.
Angelo analengedwa kalekale kwambiri, dziko lapansi lisanalengedwe. Mulungu atalenga dziko lapansi, angelo “anayamba kufuula ndi chisangalalo.”—Yobu 38:4-7.
Kodi angelo alipo angati?
Baibulo silitchula chiwerengero chenicheni cha angelo, koma limasonyeza kuti alipo ochuluka kwambiri. Mwachitsanzo, mtumwi Yohane anaona mamiliyoni ambiri a angelo m’masomphenya.—Chivumbulutso 5:11.
Kodi angelo ali ndi mayina komanso makhalidwe osiyanasiyana?
Inde. Baibulo limatchula mayina awiri a angelo: Mikayeli komanso Gabirieli. (Danieli 12:1; Luka 1:26)a Angelo enanso anavomereza kuti anali ndi mayina koma sanafune kuwatchula.—Genesis 32:29; Oweruza 13:17, 18.
Angelo ndi osiyanasiyana ndipo amatha kulankhulana. (1 Akorinto 13:1) Amatha kuganiza komanso kupanga mawu otamanda Mulungu. (Luka 2:13, 14) Ndipo ali ndi ufulu wotha kusankha pakati pa chabwino ndi cholakwika, monga mmene zinalili pamene angelo ena anachimwa n’kupandukira Mulungu limodzi ndi Satana Mdyerekezi.—Mateyu 25:41; 2 Petulo 2:4.
Kodi pali magulu osiyanasiyana a angelo?
Inde. Mikayeli, yemwe ndi mkulu wa angelo, ndi amene ali ndi ulamuliro komanso mphamvu zambiri. (Yuda 9; Chivumbulutso 12:7) Aserafi ndi angelo apamwamba kwambiri omwe amakhala pafupi ndi mpando wachifumu wa Yehova. (Yesaya 6:2, 6) Akerubi ndi gulu linanso la angelo apamwamba omwe amagwira ntchito zapadera. Mwachitsanzo, akerubi ndi amene ankalondera khomo lolowera m’munda wa Edeni panthawi imene Adamu ndi Hava anathamangitsidwa m’mundawo.—Genesis 3:23, 24.
Kodi angelo amathandiza anthu?
Inde, Mulungu amagwiritsa ntchito angelo ake okhulupirika pothandiza anthu masiku ano.
Mulungu amagwiritsa ntchito angelo potsogolera atumiki ake pa ntchito yolalikira uthenga wabwino wa Ufumu wa Mulungu. (Chivumbulutso 14:6, 7) Zimenezi zimathandiza anthu amene akulalikirawo komanso amene akumvetsera uthenga wabwino.—Machitidwe 8:26, 27.
Angelo amathandiza kuti mpingo wa Chikhristu ukhale wosadetsedwa ndi anthu oipa.—Mateyu 13:49.
Angelo amatsogolera komanso kuteteza anthu amene ndi okhulupirika kwa Mulungu.—Salimo 34:7; 91:10, 11; Aheberi 1:7, 14.
Posachedwapa, angelo adzamenya nkhondo limodzi ndi Yesu yochotsa anthu onse oipa ndipo zimenezi zidzathandiza kuti anthu azisangalala.—2 Atesalonika 1:6-8.
Kodi munthu aliyense ali ndi mngelo amene amamuteteza?
Ngakhale kuti angelo amachita chidwi ndi zinthu zauzimu zimene atumiki a Mulungu akuchita, zimenezi sizikutanthauza kuti Mulungu amapereka mngelo kwa Mkhristu aliyense n’cholinga choti azimuteteza.b (Mateyu 18:10) Angelo sateteza atumiki a Mulungu ku mavuto kapena mayesero onse. Baibulo limasonyeza kuti nthawi zambiri Mulungu ‘amapereka njira yopulumukira’ ku mayeserowo popatsa munthu nzeru komanso mphamvu kuti athe kupirira.—1 Akorinto 10:12, 13; Yakobo 1:2-5.
Maganizo olakwika okhudza angelo
Maganizo olakwika: Angelo onse ndi abwino.
Zoona zake: Baibulo limanena za “makamu a mizimu yoipa” komanso “angelo amene anachimwa.” (Aefeso 6:12; 2 Petulo 2:4) Angelo oipawa ndi ziwanda zomwe zinakhala kumbali ya Satana n’kupandukira Mulungu.
Maganizo olakwika: Angelo safa.
Zoona zake: Angelo oipa, kuphatikizapo Satana Mdyerekezi, adzawonongedwa.—Yuda 6.
Maganizo olakwika: Anthu akafa amasanduka angelo.
Zoona zake: Angelo ndi zolengedwa zapadera za Mulungu, osati anthu amene afa kenako n’kuukitsidwa. (Akolose 1:16) Anthu amene aukitsidwa kuti akakhale ndi moyo kumwamba, Mulungu amawapatsa mphatso ya moyo womwe sungafe. (1 Akorinto 15:53, 54) Iwo adzakhala ndi malo apamwamba kuposa angelo.—1 Akorinto 6:3.
Maganizo olakwika: Angelo analengedwa kuti azitumikira anthu.
Zoona zake: Angelo amatsatira malamulo a Mulungu, osati athu. (Salimo 103:20, 21) Ngakhale Yesu pa nthawi ina ananena kuti akanatha kupempha thandizo kwa Mulungu, osati kwa angelo.—Mateyu 26:53.
Maganizo olakwika: Tingathe kupemphera kwa angelo kuti atithandize.
Zoona zake: Kupemphera ndi mbali ya kulambira kwathu, ndipo tiyenera kulambira Yehova Mulungu basi. (Chivumbulutso 19:10) Tiyenera kupemphera kwa Mulungu yekha, kudzera mwa Yesu.—Yohane 14:6.
a Pa Yesaya 14:12, ma Baibulo ena amagwiritsa ntchito mawu oti “Lusifala” omwe anthu ena amati ndi dzina la mngelo yemwe anakhala Satana Mdyerekezi. Komabe, mawu a Chiheberi oyambirira omwe anagwiritsidwa ntchito palembali amatanthauza kuti ‘wonyezimira.’ Nkhaniyi sikusonyeza kuti mawuwa akunena za Satana, koma akunena za mzera wa mafumu a Babulo, omwe Mulungu anali kudzawachititsa manyazi chifukwa cha kunyada kwawo. (Yesaya 14:4, 13-20) Mawu oti “wonyezimirawe” anawagwiritsa ntchito panthawi imene mafumu a Babulo anachotsedwa paudindo, posonyeza kuti anali opusa.
b Anthu ena amaganiza kuti nkhani yofotokoza za kutulutsidwa m’ndende kwa Petulo ikutanthauza kuti Petulo anali ndi mngelo wake womuteteza. (Machitidwe 12:6-16) Komabe, pamene ophunzirawo ananena kuti “mngelo [wa Petulo]”, n’kutheka kuti anaganiza molakwika kuti mngelo yemwe anali mthenga woimira Petulo wabwera, osati Petulo weniweniyo.