Anachita Chifuniro cha Yehova
Paulo Alaka Mavuto
PAULO ali mu mkhalidwe wosoŵa potulukira. Iye pamodzi ndi anthu ena 275 ali m’ngalawa imene ikuvutika ndi mphepo ya Eurokulo—namondwe wowononga kwambiri panyanja ya Mediterranean. Namondweyo ndi wamphamvu kwambiri kwakuti masana dzuŵa silikuoneka, ngakhalenso usiku nyenyezi sizikuoneka. Ndithudi, anthu amene ali m’ngalawayo akuopa kuti akufa. Komabe, Paulo akuwatonthoza mwa kuwauza zimene Mulungu anamuuza m’maloto: “Sadzatayika wamoyo mmodzi mwa inu, koma ngalawa ndiyo.”—Machitidwe 27:14, 20-22.
Usiku wa tsiku la 14 namondweyo adakali mkati, amalinyerowo akuzindikira chinthu chodabwitsa—madzi ndi akuya mikwamba makumi aŵiri okha.a Atayenda pang’ono, akuyesanso madziwo. Tsopano ndi akuya mikwamba khumi ndi isanu. Atsala pang’ono kufika kumtunda! Koma nkhani yabwino imeneyi ilinso yonjenjemeretsa. Poponyedwa uku ndi uku usiku m’madzi osaya kwambiri, ngalawayo ikhoza kugunda mwala ndi kuwonongeka. Mwanzeru amalinyerowo akuponya anangula. Ena a iwo akufuna kutsitsa bwato laling’ono ndi kukweramo, kuyesa kudzipulumutsa panyanjayo.b Koma Paulo akuwaletsa. Akuuza kenturiyo pamodzi ndi asilikaliwo kuti: “Ngati aŵa sakhala m’ngalawa inu simukhoza kupulumuka.” Kenturiyoyo akumvera zimene Paulo akunena, ndipo tsopano anthu onse 276 amene ali m’ngalawayo akulakalaka kwambiri kuti kuche.—Machitidwe 27:27-32.
Ngalawa Isweka
Kutacha mmaŵa, anthuwo akuona bondo la mchenga. Pokhalanso ndi chiyembekezo, amalinyerowo akutaya anangula nakweza thanga la kulikulu. Ngalawayo ikuyamba kuyenda kuloŵera kugombe—mosakayikira anthu akujowajowa ndi chisangalalo.—Machitidwe 27:39, 40.
Komabe, mwadzidzidzi ngalawayo ikukanika kuyenda pamalo pokumana mafunde aŵiri. Kuwonjezera apo, mafunde amphamvu akukantha kumakaliro kwa ngalawayo ndi kuiswa. Anthu onse afunika kuchokamo m’ngalawayo! (Machitidwe 27:41) Koma izi zikupereka vuto lina. Anthu ambiri amene ali m’ngalawayo—kuphatikizapo Paulo—ndi andende. Mwa malamulo a Aroma, mlonda wodikirira andende amene alola wandende wake kuthaŵa, iyeyo ndiye anali kulandira chilango chimene wandendeyo anayenera kulandira. Mwachitsanzo, ngati munthu amene anapha mnzake athaŵa, mlonda wolekererayo anayenera kulipira ndi moyo wake.
Poopa zimenezi, asilikaliwo akufuna kupha andende onse. Komabe, kenturiyo, amene ndi waubwenzi kwa Paulo, akuloŵererapo. Iye akulamula kuti onse amene angathe adumphire m’madzi ndi kusambira kukafika kumtunda. Amene sangathe kusambira agwirire matabwa kapena zinthu zina za m’ngalawamo. Anthu amene anali m’ngalawa yomwe yawonongekayo akufika kumtunda mmodzimmodzi. Mogwirizanadi ndi mawu a Paulo, palibe aliyense amene wapita ndi madzi!—Machitidwe 27:42-44.
Chozizwitsa pa Melita
Gulu lotopalo likupulumukira pa chisumbu chotchedwa Melita. Anthu a pamenepo ndi “anthu olankhula zachilendo,” m’chenicheni “barbarians” m’Chingelezi (Chigiriki, barʹba·ros).c Koma anthu a pa Melita sali ngati zinyama ayi. Mosiyana kwambiri, Luka, yemwe anali kuyenda ndi Paulo, anati “anatichitira zokoma zosachitika pena ponsepo; pakuti anasonkha moto, natilandira ife tonse, chifukwa cha mvula inalinkugwa, ndi chifukwa cha chisanu.” Paulo akuthandizana ndi anthu a pa Melitapo kutola nkhuni ndi kuziika pamoto.—Machitidwe 28:1-3, NW, mawu a mtsinde.
Mwadzidzidzi, njoka ikuluma dzanja la Paulo! Anthu a pachisumbucho akuganiza kuti Paulo ayenera kukhala wambanda. Iwo mwinamwake akuganiza kuti Mulungu amalanga ochimwa mwa kudwalitsa chiŵalo cha thupi lawo chimene chinawapangitsa kuchimwa. Koma taonani! Paulo akukutumulira njokayo pamoto zomwe zikudabwitsa kwambiri anthu a pachisumbucho. Monga momwe Luka yemwe anali kuona zimenezi ananenera, iwo “anayesa kuti [Paulo] adzatupa, kapena mwiniwake kugwa kufa pomwepo.” Anthu a pachisumbucho akusintha maganizo awo ndi kuyamba kunena kuti Paulo ayenera kukhala mulungu.—Machitidwe 28:3-6.
Paulo akutha miyezi itatu ali pa Melita, ndipo m’nthaŵiyi akuchiritsa atate ake a Popliyo, mkulu wa pachisumbucho amene anamulandira bwino Paulo, ndi anthu enanso amene akuvutika ndi matenda. Ndiponso, Paulo akufesa mbewu za choonadi, zomwe zikutulutsa madalitso ambiri kwa anthu ocherezawo a pa Melita.—Machitidwe 28:7-11.
Phunziro kwa Ife
Paulo anakumana ndi mavuto ambiri pochita utumiki wake. (2 Akorinto 11:23-27) M’nkhani yangofotokozedwayi, anali wandende chifukwa cha uthenga wabwino. Ndiyeno, anakumana ndi ziyeso zina zomwe sanaziyembekezere: namondwe woopsa ndiyeno kusweka kwa ngalawa. M’zochitika zonsezi, Paulo sanagwedezeke pakukhala kwake wotsimikiza kukhala mlaliki wachangu wa uthenga wabwino. Kuchokera pa zimene anakumana nazo, iye analemba kuti: “M’zinthu zonse ndaloŵa mwambo wakukhuta, ndiponso wakumva njala; wakusefukira, ndiponso wakusoŵa. Ndikhoza zonse mwa Iye wondipatsa mphamvuyo.”—Afilipi 4:12, 13.
Mavuto amoyo asatifooketse pa kukhala atumiki achangu a Mulungu woona! Pamene chiyeso chadzidzidzi chitifikira, timataya nkhaŵa yathu pa Yehova. (Salmo 55:22) Kenako, mopirira timadikira kuti tione mmene adzachitira kuti kukhale kotheka kwa ife kupirira chiyesocho. Zili choncho, timapitiriza kumutumikira mokhulupirika, tili ndi chidaliro chakuti amatisamalira. (1 Akorinto 10:13; 1 Petro 5:7) Mwa kukhala olimba, zivute zitani, ife—mofanana ndi Paulo—tingalake mavuto.
[Mawu a M’munsi]
a Kaŵirikaŵiri mkwamba umodzi umatengedwa kukhala mikono inayi, kapena pafupifupi mamita 1.8.
b Bwato laling’ono linali kugwiritsidwa ntchito kukafikira kumtunda pamene ngalawa inachirikizidwa ndi anangula pafupi ndi gombe. Mwachionekere, amalinyerowo anali kuyesa kudzipulumutsa mosaganizira anthu amene akanawasiya m’ngalawamo, amene anali osazoloŵera kuyendetsa ngalawa.
c Buku lotchedwa Word Origins (Chiyambi cha Mawu) la Wilfred Funk limati: “Agiriki anali kunyoza zinenero za anthu ena, ndipo anali kunena kuti amamveka ngati akuti ‘bar-bar’ ndipo aliyense amene anali kuyankhula zinenero zoterozo anali kumutcha kuti barbaros.”